Kodi Muli ndi Mtima Wodikira?
Kodi Muli ndi Mtima Wodikira?
“Muyenera inu kukhala anthu otani nanga m’mayendedwe opatulika ndi m’chipembedzo [“m’ntchito zosonyeza kudzipereka kwa Mulungu,” NW], akuyembekezera ndi kufulumira kwa kudza kwake kwa tsiku la Mulungu.” —2 PETRO 3:11, 12.
1, 2. Kodi kudikira tsiku la Yehova tingakuyerekezere ndi chiyani?
TAYEREKEZERANI banja limene likuyembekezera kulandira alendo oti adzadye nawo chakudya chamadzulo. Nthaŵi imene afike ikuyandikira kwambiri. Mayi wa m’banjalo watanganidwa kumalizitsa zina ndi zina zofunika pa chakudyacho. Mwamuna wake ndi ana awo akuthandizira kuti aonetsetse kuti zonse zili bwino. Aliyense ndi wosangalala. Inde, onse m’banjamo akuyembekezera mwachidwi kufika kwa alendowo ndipo akuyembekezera kudya chakudya chokoma ndiponso kucheza bwino ndi alendowo.
2 Ife monga Akristu, tikuyembekezera chinthu chofunika kwambiri kuposa zimenezo. Tikuyembekezera chiyani? Tonsefe tikuyembekezera “tsiku la Mulungu.” Mpaka pamene tsikulo lidzafika, tifunika kukhala ngati mneneri Mika amene anati: “Ndidzadikira Yehova; ndidzalindira Mulungu wa chipulumutso changa.” (Mika 7:7) Kodi zimenezi zikutanthauza kuti tidzangokhala osachita china chilichonse? Ayi. Pali ntchito yambiri yoti tichite.
3. Malinga ndi 2 Petro 3:11, 12, kodi Akristu ayenera kukhala ndi maganizo otani?
3 Mtumwi Petro akutithandiza kukhala ndi maganizo oyenera pamene tikudikira. Iye anati: “Muyenera inu kukhala anthu otani nanga m’mayendedwe opatulika ndi m’chipembedzo [“m’ntchito zosonyeza kudzipereka kwa Mulungu,”], akuyembekezera ndi kufulumira kwa [“kukumbukira,” NW] kudza kwake kwa tsiku la Mulungu.” (2 Petro 3:11, 12) Onani kuti m’mawu ameneŵa, Petro sanali kufunsa mmene tiyenera kukhalira. M’makalata aŵiri amene iye analemba mouziridwa ndi Mulungu, anafotokoza mmene Akristu ayenera kukhalira. Anawalangizanso kupitiriza kuyenda “m’mayendedwe opatulika ndi m’ntchito zosonyeza kudzipereka kwa Mulungu.” Ngakhale kuti panali patapita zaka pafupifupi 30 kuyambira pamene Yesu Kristu anafotokoza chizindikiro “cha mathedwe a nthaŵi ya pansi pano,” Akristu anayenera kukhalabe maso. (Mateyu 24:3) Anayenera ‘kuyembekeza ndi kukumbukira’ kudza kwa tsiku la Yehova.
4. Kodi n’chiyani chikufunika pa “kukumbukira kudza kwake kwa tsiku la Mulungu”?
4 Liwu la Chigiriki limene analimasulira apa kuti “kukumbukira” kwenikweni limatanthauza Mateyu 24:36; 25:13) Buku lina laumboni linanena kuti verebu limene lili tsinde la mawu akuti “kufulumiza” panopa limatanthauza “‘kuchititsa chinthu kufulumira’ ndipo motero n’lofanana kwambiri ndi ‘kuchita changu, kudera nkhaŵa chinachake.’” Motero, Petro anali kulimbikitsa okhulupirira anzake kuti azifunitsitsa kudza kwa tsiku la Yehova. Akanachita zimenezi mwa kukumbukira tsikuli nthaŵi zonse. (2 Petro 3:12) Popeza tsopano “tsiku la Yehova lalikulu ndi loopsa” layandikira kwambiri, ifenso tiyenera kukhala ndi maganizo ameneŵa.—Yoweli 2:31.
“kufulumiza.” Inde, ‘sitingafulumize’ tsiku la Yehova m’lingaliro lenileni. Ndipotu, ‘sitidziŵa tsiku ndi nthaŵi yake’ pamene Yesu Kristu adzabwera kudzaweruza adani a Atate wake. (Dikirani mwa “Mayendedwe Opatulika”
5. Kodi tingasonyeze bwanji kuti tikufunitsitsa kudzaona “tsiku la Mulungu”?
5 Ngati tikufunitsitsa kudzapulumuka tsiku la Yehova, tidzasonyeza zimenezo mwa “mayendedwe [athu] opatulika ndi ntchito zosonyeza kudzipereka kwa Mulungu.” Mawu akuti “mayendedwe opatulika” angatikumbutse langizo la Petro lakuti: “Monga ana omvera osadzifanizitsanso ndi zilakolako zakale, pokhala osadziwa inu; komatu monga Iye wakuitana inu ali woyera mtima, khalani inunso oyera mtima m’makhalidwe anu onse; popeza kwalembedwa, Muzikhala oyera mtima, pakuti Ine ndine woyera mtima.”—1 Petro 1:14-16.
6. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tikhale oyera?
6 Kuti tikhale oyera, tiyenera kukhala aukhondo, a maganizo abwino, a makhalidwe abwino, ndiponso kukhala ndi moyo wabwino wauzimu. Kodi tikukonzekera “tsiku la Mulungu” mwa kukhala oyera monga anthu amene tili ndi dzina la Yehova? Masiku ano sizophweka kukhala oyera moteromo chifukwa miyezo ya makhalidwe m’dzikoli ikuipiraipira. (1 Akorinto 7:31; 2 Timoteo 3:13) Kodi tikuona kuti kusiyana kwa miyezo ya makhalidwe athu ndi ya dzikoli kukukulirakulira? Ngati sizikutero, tiyenera kuganizapo bwino. Kodi zingakhale kuti miyezo yathu ikumaloŵa pansi ngakhale kuti ndi yapamwamba kuposa ya dzikoli? Ngati ndi choncho, tifunika kuchitapo kanthu kukonza vutolo kuti tikondweretse Mulungu.
7, 8. (a) Kodi tingaiŵale bwanji kufunika koyendabe “m’mayendedwe opatulika”? (b) Kodi tingafunike kuchita chiyani kuti tikonze vutolo?
7 Popeza zithunzi zolaula zikupezeka pa Intaneti ndiponso munthu amatha kuonera ali yekhayekha, ena amene kale sankatha kupeza zinthu zoipa zoterozo tsopano akupeza “zinthu zambiri zokhudza kugonana,” anatero dokotala wina. Ngati tingafunefune zinthu zoipa zimenezi pa Intaneti, tidzakhala tikunyalanyaza lamulo la m’Baibulo lakuti ‘tisakhudze kanthu kodetsa.’ (Yesaya 52:11) Kodi tingakhale ‘tikukumbukira kudza kwake kwa tsiku la Mulungu’ ngati tichita zimenezi? Kapena kodi tingakhale tikutalikitsa tsikulo m’maganizo mwathu, kuganiza kuti ngakhale titaipitsa maganizo athu ndi zinthu zonyansa, tidakali ndi nthaŵi yodziyeretsa? Ngati tili ndi vuto pankhani imeneyi, tipemphe Yehova mwamsanga kuti ‘achititse mlubza maso athu asapenye zachabe, ndi kutipatsa moyo mu njira yake.’—Salmo 119:37.
8 Mboni za Yehova zambiri, zachichepere ndi zachikulire zomwe, zikutsatirabe miyezo ya makhalidwe abwino yapamwamba ya Mulungu ndipo zikupeŵa zokopa zoipa za dzikoli. Pozindikira kuti nthaŵi imene tikukhala ino ndi yofunika kuchitapo kanthu mwamsanga ndiponso pozindikira chenjezo la Petro lakuti “tsiku la Ambuye lidzadza ngati mbala,” Mboni zimapitiriza kuyenda “m’mayendedwe opatulika.” (2 Petro 3:10) Zochita zawo zimasonyeza kuti “akuyembekezera ndi kukumbukira kudza kwake kwa tsiku la Mulungu.” *
Dikirani mwa “Ntchito Zosonyeza Kudzipereka kwa Mulungu”
9. Kodi kudzipereka kwa Mulungu kuyenera kutilimbikitsa kuchita chiyani?
9 “Ntchito zosonyeza kudzipereka kwa Mulungu” n’zofunikanso kwambiri kuti tizikumbukira tsiku la Yehova. “Kudzipereka kwa Mulungu” kumafuna kulemekeza kwambiri Mulungu, kumene kumatipangitsa kuchita zinthu zimene zingamusangalatse. Kukhulupirika kwathu kwa Yehova n’kumene kumatilimbikitsa kuchita ntchito zosonyeza kudzipereka kwathu kwa Mulungu koteroko. Cholinga cha Mulungu n’chakuti “anthu onse apulumuke, nafike pozindikira choonadi.” (1 Timoteo 2:4) Iye ‘safuna kuti ena awonongeke, koma kuti onse afike kukulapa.’ (2 Petro 3:9) Motero, kodi kudzipereka kwathu kwa Mulungu sikuyenera kutilimbikitsa kuchita khama kwambiri kuthandiza anthu kuphunzira za Yehova ndi kumutsanzira?—Aefeso 5:1.
10. N’chifukwa chiyani tiyenera kupeŵa “chinyengo cha chuma”?
10 Moyo wathu udzadzala ndi ntchito zosonyeza kudzipereka kwa Mulungu ngati tifunafuna Ufumu wa Mulungu choyamba. (Mateyu 6:33) Zimenezi zimafuna kuti tiziziona moyenera zinthu zakuthupi. Yesu anachenjeza kuti: “Yang’anirani, mudzisungire kupewa msiriro uliwonse; chifukwa moyo wake wa munthu sulingana ndi kuchuluka kwa zinthu zake ali nazo.” (Luka 12:15) Ngakhale kuti sitingaganizire zoti tingachititsidwe khungu ndi kukonda ndalama, tingachite bwino kukumbukira kuti ‘kulabadira kwa dziko lapansi, ndi chinyengo cha chuma zingatsamwitse mawu’ a Mulungu. (Mateyu 13:22) Kungakhale kovuta kupeza zinthu zofunika pa moyo. Chifukwa cha zimenezi, ambiri m’mayiko ena amaganiza zoti kuti akhale ndi moyo wabwinopo, afunika kusamukira ku mayiko olemera, mwina n’kusiya banja lawo kwa zaka zingapo. Anthu a Mulungu enanso aganiza choncho. Akapita ku mayiko ena, angathe kupezera banja lawolo zinthu zamakono. Koma kodi n’chiyani chingachitikire moyo wauzimu wa okondedwa awo amene awasiya kwawoko? Popanda utsogoleri woyenera panyumbapo, kodi adzakhala ndi moyo wauzimu umene ukufunika kuti adzapulumuke tsiku la Yehova?
11. Kodi munthu wina amene anachoka m’dziko la kwawo kukagwira ntchito ku dziko lina anasonyeza bwanji kuti kuchita ntchito zosonyeza kudzipereka kwa Mulungu n’kofunika kwambiri kuposa chuma?
11 Munthu wina wa ku Philippines amene anapita kukagwira ntchito ku Japan anaphunzira choonadi cha m’Baibulo kwa Mboni za Yehova komweko. Ataphunzira za udindo wa umutu umene Malemba amafotokoza, anaona kuti anafunika kuthandiza anthu a m’banja lake kukhala olambira Yehova. (1 Akorinto 11:3) Mkazi wake yemwe anali kwawoko anatsutsa kwambiri chikhulupiriro chake chatsopanocho ndipo anafuna kuti azipitiriza kumutumizira ndalama m’malo mobwerera kunyumba kuti akawaphunzitse zikhulupiriro zake za m’Baibulo. Komabe, polimbikitsidwa ndi mfundo yakuti nthaŵi ino ndi yofunika kuchitapo kanthu mwamsanga ndiponso podera nkhaŵa okondedwa akewo, iye anabwerera kwawo. Kuchita zinthu moleza mtima ndi a m’banja mwakewo kunapindula. Patapita nthaŵi, banja lake linagwirizana pa kulambira koona, ndipo mkazi wake anayamba utumiki wa nthaŵi zonse.
12. N’chifukwa chiyani tiyenera kuika zinthu zauzimu pamalo oyamba?
12 Mmene zinthu zilili kwa ife zingafanane ndi mmene zingakhalire kwa anthu amene ali m’nyumba imene ikupsa. Kodi kungakhale kwanzeru kutanganidwa kutulutsa katundu m’nyumba imene moto uli laŵilaŵi ndipo yangotsala pang’ono kugwa? Kodi m’malo mwake sikungakhale kofunika kwambiri kupulumutsa moyo wathu ndi wa a m’banja lathu ndi ena amene ali m’nyumbayo? Inde, dongosolo la zinthu loipa lino latsala pang’ono kugwa ndipo anthu ali pangozi. Pozindikira zimenezi, mosakayika tiyenera kuika zinthu zauzimu pamalo oyamba ndi kuika maganizo kwambiri pa ntchito yopulumutsa moyo yolalikira za Ufumu.—1 Timoteo 4:16.
Tifunika Kukhala “Opanda Banga”
13. Kodi tifunika kukhala otani pamene tsiku la Yehova likufika?
13 Potsindika kufunika kokhalabe ndi mtima wodikira, Petro anati: “Okondedwa, popeza muyembekeza izi, chitani changu kuti mupezedwe ndi Iye [Mulungu] mumtendere, opanda banga ndi opanga chilema.” (2 Petro 3:14) Kuwonjezera pa langizo lake loyenda m’mayendedwe opatulika ndi m’ntchito zosonyeza kudzipereka kwathu kwa Mulungu, Petro anatsindika kufunika koti Yehova adzatipeze tili anthu oyeretsedwa ndi mwazi wamtengo wapatali wa Yesu. (Chivumbulutso 7:9, 14) Zimenezi zimafuna kuti munthu akhulupirire nsembe ya Yesu ndi kukhala mtumiki wa Yehova wodzipatulira ndiponso wobatizidwa.
14. Kodi kukhala “opanda banga” kumafuna chiyani?
14 Petro akutilimbikitsa kuchita zonse zimene tingathe kuti adzatipeze “opanda banga.” Kodi tikuyesetsa kuti zovala zathu za makhalidwe achikristu ndiponso za mtima wathu zisakhale ndi banga, zisaipitsidwe ndi dzikoli? Tikaona banga pa chovala chathu, timalichotsa mwamsanga. Ngati bangalo lili pa chovala chimene timachikonda kwambiri, timasamala kwambiri kuti tilichotse bwinobwino. Kodi timachitanso chimodzimodzi zovala zathu zachikristu zikakhala ndi banga, titero kunena kwake, chifukwa cha zofooka zimene zili mumtima mwathu kapena khalidwe lathu?
15. (a) N’chifukwa chiyani Aisrayeli anafunika kuomba mphonje m’mphepete mwa zovala zawo? (b) N’chifukwa chiyani atumiki a Yehova a masiku ano ndi osiyana kwambiri ndi dzikoli?
15 Aisrayeli ankafunika kuomba “mphonje m’mphepete mwa zovala zawo” ndiponso ‘kuika pamphonje m’mphepetemo thonje lamadzi.” Chifukwa chiyani anafunika kuchita zimenezi? Kuti azikumbukira malamulo a Yehova, kuwamvera, ndi ‘kukhala opatulika’ kwa Mulungu wawo. (Numeri 15:38-40) Ife monga atumiki a Yehova masiku ano, timasiyana kwambiri ndi dzikoli chifukwa timatsatira malamulo ndi mfundo za makhalidwe abwino za Mulungu. Mwachitsanzo, timakhala ndi makhalidwe abwino, timalemekeza kupatulika kwa magazi, ndiponso timapewa kulambira mafano kwa mtundu uliwonse. (Machitidwe 15:28, 29) Ambiri amatilemekeza chifukwa cha kutsimikiza mtima kwathu kusafuna kudetsedwa.—Yakobo 1:27.
Tifunika Kukhala “Opanda Chilema”
16. Kodi n’chiyani chimafunika kuti tikhalebe “opanda chilema”?
16 Petro ananenanso kuti tifunika adzatipeze “opanda chilema.” Kodi n’zotheka bwanji zimenezo? Nthaŵi zambiri banga limatheka kulichotsa kapena kuliyeretsa koma osati chilema. Chilema chimasonyeza kuti pali chinachake Afilipi 2:14, 15) Tikatsatira langizo limenelo, tidzapewa kudandaula ndi makani ndipo tidzatumikira Mulungu ndi cholinga chabwino. Kukonda kwathu Yehova ndi anzathu n’kumene kudzatilimbikitsa kulalikira “uthenga uwu wabwino wa Ufumu.” (Mateyu 22:35-40; 24:14) Ndiponso, tidzapitiriza kulalikira uthenga wabwino ngakhale kuti anthu ambiri sangamvetse chifukwa chake timathera nthaŵi yathu pofuna kuthandiza ena kuphunzira za Mulungu ndi Mawu ake, Baibulo.
chimene chalakwika mkati. Mtumwi Paulo analangiza Akristu anzake a ku Filipi kuti: “Chitani zonse kopanda madandaulo ndi makani, kuti mukakhale osalakwa ndi oona, ana a Mulungu opanda chilema pakati pa mbadwo wokhotakhota ndi wopotoka, mwa iwo amene muonekera monga mauniko m’dziko lapansi.” (17. Kodi cholinga chathu pofuna maudindo mumpingo wachikristu chiyenera kukhala chotani?
17 Popeza kuti tikufuna kuti adzatipeze “opanda chilema,” tiyenera kupenda zolinga zathu pa zonse zimene timachita. Tinasiya kuchita zinthu mwadyera monga mmene dziko limachitira, monga kufuna kukhala wolemera kapena wolamulira. Ngati tikufuna udindo mumpingo wachikristu, zolinga zathu ziyenera kukhala zoyenera ndipo tiyeni nthaŵi zonse tichite zimenezi chifukwa chokonda Yehova ndi anthu ena. N’zosangalatsa kuona amuna auzimu “a[ku]khumba udindo wa woyang’anira” mwachimwemwe ndiponso ali ndi cholinga chabwino choti atumikire Yehova ndi okhulupirira anzawo. (1 Timoteo 3:1; 2 Akorinto 1:24) Inde, amene amayenerera kutumikira monga akulu, ‘amaweta gulu la Mulungu mwaufulu; osatsata phindu lonyansa, koma mwachangu; osati monga ochita ufumu pa iwo a udindo wawo, koma okhala zitsanzo za gululo.’—1 Petro 5:1-4.
Tifunika Kukhala “Mumtendere”
18. Kodi Mboni za Yehova zimadziŵika ndi makhalidwe ati?
18 Petro akutiuzanso kuti tidzapezedwe “mumtendere.” Kuti tikwanitse kuchita zimenezi, tifunika kukhala pamtendere ndi Yehova ndi anzathu. Petro anatsindika kufunika kokhala ndi ‘chikondano chenicheni mwa ife tokha’ ndi kukhalabe pamtendere ndi Akristu anzathu. (1 Petro 2:17; 3:10, 11; 4:8; 2 Petro 1:5-7) Kuti tikhalebe pamtendere, tifunika kukondana. (Yohane 13:34, 35; Aefeso 4:1, 2) Chikondi chathu ndi mtendere wathu zimaonekera kwambiri makamaka tikamachita misonkhano ya mayiko. Pamsonkhano umene unachitikira ku Costa Rica mu 1999, wogulitsa malonda wina pabwalo la ndege anakwiya chifukwa chakuti Mboni za m’dzikolo zimene zinali kulandira nthumwi, zinatchingira malonda ake mosadziŵa. Koma pa tsiku lachiŵiri, iye anaona chikondi ndi mtendere zimene zinaonekera polandira nthumwizo mosangalala, ngakhale kuti Mboni za m’dzikolo sizinkadziŵana kale ndi nthumwizo. Patsiku lomaliza, wogulitsa malondayo nayenso analandira nawo nthumwizo ndipo anapempha kuti aziphunzira Baibulo.
19. N’chifukwa chiyani n’kofunika kwambiri kuyesetsa kukhala pamtendere ndi okhulupirira anzathu?
19 Ngati sitifunitsitsa kuchokera pansi pa mtima kuti tikhale pamtendere ndi abale ndi alongo athu auzimu, zingasonyeze kuti sitikudikira ndi mtima wonse tsiku la Yehova ndi dziko latsopano limene walonjeza. (Salmo 37:11; 2 Petro 3:13) Tiyerekeze kuti zikutivuta kukhala pamtendere ndi wokhulupira mnzathu wina. Kodi tingaganizire zodzakhala naye limodzi mwamtendere m’Paradaiso? Ngati mbale ali nafe chifukwa, tiyenera ‘kuyanjana naye’ mwamsanga. (Mateyu 5:23, 24) Kuchita zimenezo n’kofunika kwambiri kuti tikhale pamtendere ndi Yehova.—Salmo 35:27; 1 Yohane 4:20.
20. Kodi tiyenera kusonyeza mtima wodikira m’njira ziti?
20 Kodi ‘tikuyembekezera ndi kukumbukira kudza kwake kwa tsiku la Mulungu’? Timasonyeza kufunitsitsa kwathu kudzaona kutha kwa zoipa mwa kukhalabe oyera m’dziko la makhalidwe oipali. Ndiponso, kufunitsitsa kwathu kubwera kwa tsiku la Yehova ndiponso kudzakhala ndi moyo moyang’aniridwa ndi ulamuliro wa Ufumu kumaonekera mwa ntchito zosonyeza kudzipereka kwathu kwa Mulungu. Ndiponso timasonyeza kuyembekezera kwathu kudzakhala m’dziko latsopano la mtendere mwa kuyesetsa kukhala pamtendere ndi olambira anzathu pakalipano. Mwa kuchita zimenezi, timasonyeza kuti tili ndi mtima wodikira ndiponso kuti ‘tikukumbukira kudza kwake kwa tsiku la Mulungu.’
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 8 Onani zitsanzo mu Nsanja ya Olonda ya January 1, 2000, tsamba 16 ndi mu buku la 1997 Yearbook of Jehovah’s Witnesses, tsamba 51.
Kodi Mukukumbukira?
• Kodi “kukumbukira kudza kwake kwa tsiku la Mulungu” kumatanthauza chiyani?
• Kodi mayendedwe athu amasonyeza bwanji kuti tili ndi mtima wodikira?
• N’chifukwa chiyani “ntchito zosonyeza kudzipereka kwa Mulungu” n’zofunika?
• Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti Yehova adzatipeze “mumtendere, opanda banga ndi opanda chilema”?
[Mafunso]
[Chithunzi patsamba 11]
Mtima wodikira umaonekera m’mayendedwe opatulika
[Zithunzi patsamba 12]
Ntchito yolalikira Ufumu ndi yopulumutsa moyo
[Chithunzi patsamba 14]
Pamene tikuyembekezera tsiku la Yehova, tiyeni tiziyesetsa kukhala pamtendere ndi anthu ena