Atumiki a Yehova Ali ndi Chiyembekezo Chenicheni
Atumiki a Yehova Ali ndi Chiyembekezo Chenicheni
“Otsala a Yakobo adzakhala pakati pa mitundu yambiri ya anthu, ngati mame ochokera kwa Yehova . . . yosachedwera [“yosayembekeza,” NW] munthu.”—MIKA 5:7.
1. Kodi Israyeli wauzimu akutitsitsimula bwanji?
YEHOVA ndiye Mlengi wamkulu wa mvula ndi mame. N’kupanda nzeru kudalira anthu kuti atipatse mame kapena mvula. Mneneri Mika analemba kuti: “Otsala a Yakobo adzakhala pakati pa mitundu yambiri ya anthu, ngati mame ochokera kwa Yehova, ngati mvula paudzu, yosachedwera [“yosayembekeza”] munthu, yosalindira ana a anthu.” (Mika 5:7) Kodi “otsala a Yakobo” ndani masiku ano? Iwo ndi Aisrayeli auzimu, otsalira a “Israyeli wa Mulungu.” (Agalatiya 6:16) Kwa “mitundu yambiri ya anthu” padziko lapansi ali ngati “mame [otsitsimula] ochokera kwa Yehova” ndiponso ngati “mvula paudzu.” Ndithudi, Akristu odzozedwa lerolino ali dalitso kwa anthu lochokera kwa Mulungu. Monga olengeza Ufumu, Yehova akuwagwiritsa ntchito kupatsa anthu uthenga wake wa chiyembekezo chenicheni.
2. Ngakhale kuti tikukhala m’dziko la mavuto, n’chifukwa chiyani tili ndi chiyembekezo chenicheni?
2 N’zosadabwitsa kuti dzikoli lilibe chiyembekezo chenicheni. M’dziko lino lomwe likulamulidwa ndi Satana Mdyerekezi muli mavuto a zandale, kupanda khalidwe, upandu, mavuto a zachuma, uchigawenga, ndi nkhondo. (1 Yohane 5:19) Anthu ambiri ali ndi mantha kuti m’tsogolo zinthu zidzakhala bwanji. Komabe, ifeyo monga olambira a Yehova sitichita mantha chifukwa chakuti chiyembekezo chathu cha m’tsogolo n’chodalirika. Chiyembekezo chathuchi n’chenicheni chifukwa n’chozikidwa pa Mawu a Mulungu. Tili ndi chikhulupiriro mwa Yehova ndi Mawu ake chifukwa zimene iye amanena zimachitikadi nthaŵi zonse.
3. (a) N’chifukwa chiyani Yehova anati adzalanga Israyeli ndi Yuda? (b) N’chifukwa chiyani mawu a Mika akugwiranso ntchito masiku ano?
3 Ulosi wa Mika wouziridwa ndi Mulungu umatilimbikitsa kuyenda m’dzina la Yehova ndipo umatipatsa maziko okhala ndi chiyembekezo chenicheni. M’zaka za m’ma 700 B.C.E., panthaŵi imene Mika analosera, anthu a pangano a Mulungu anali ogaŵikana maufumu aŵiri, Israyeli ndi Yuda, ndipo onse anali kunyalanyaza pangano la Mulungu. Chifukwa cha zimenezi, munali makhalidwe oipa, mpatuko wachipembedzo, ndi kukondetsa chuma. Motero, Yehova anawachenjeza kuti adzawalanga. N’zoona kuti Mulungu anali kuchenjeza anthu a m’nthaŵi ya Mika. Koma mmene zinthu zilili masiku ano n’chimodzimodzi ndi m’nthaŵi ya Mika ndipo mawu ake akugwiranso ntchito masiku ano. Tiona bwinobwino zimenezi pamene tikukambirana mfundo zina zazikulu za m’machaputala asanu ndi aŵiri a buku la Mika.
Zimene Zili M’bukuli
4. Kodi machaputala 1 mpaka 3 a Mika akufotokoza chiyani?
4 Tiyeni tione mwachidule zimene zili M’chaputala 1, Yehova anavumbula kupanduka kwa Israyeli ndi Yuda. Chifukwa cha kulakwa kwawo, Israyeli adzawonongedwa ndipo chilango cha Yuda chidzafika mpaka kuzipata za Yerusalemu. Chaputala 2 chikufotokoza kuti anthu olemera ndiponso amphamvu anali kupondereza anthu ofooka ndi osoŵa thandizo. Komabe, m’chaputalachi mulinso lonjezo la Mulungu. Anthu a Mulungu adzawasonkhanitsa pamodzi. Chaputala 3 chikunena kuti Yehova anadzudzula atsogoleri a mtunduwo ndi aneneri oipa. Atsogoleriŵa anali kupotoza chilungamo ndipo aneneri anali kunama. Ngakhale izi zinali choncho, mzimu woyera unapatsa mphamvu Mika kuti alengeze chiŵeruzo cha Yehova chimene chinali kubwera.
m’buku la Mika.5. Kodi mfundo yaikulu m’machaputala 4 ndi 5 a Mika ndi yotani?
5 Chaputala 4 chikulosera kuti m’masiku otsiriza, mitundu yonse idzapita kuphiri lokwezeka la nyumba ya Yehova kuti iye akaiphunzitse. Komabe zimenezo zisanachitike, Yuda adzapita ku Babulo, koma Yehova adzam’landitsa. Chaputala 5 chikusonyeza kuti Mesiya adzabadwira ku Betelehemu wa mu Yuda. Iye adzaŵeta anthu ake ndi kuwalanditsa ku mitundu imene inali kuwapondereza.
6, 7. Kodi ndi mfundo zotani zomwe zili m’machaputala 6 ndi 7 a ulosi wa Mika?
6 M’chaputala 6 cha Mika, Yehova akudzudzula anthu ake powaimba mlandu. Kodi iye wachita chiyani kuti iwo apanduke? Palibe. Ndipo zimene iye amafuna n’zotheka. Amafuna kuti olambira ake azichita chilungamo ndi chifundo ndipo azikhala odzichepetsa poyenda ndi iye. Koma m’malo mochita zimenezo, Israyeli ndi Yuda anapanduka ndipo anali kudzavutika chifukwa cha kupanduka kwawoko.
7 M’chaputala chomaliza cha ulosi wake, Mika anatsutsa kuipa kwa anthu a m’nthaŵi yake. Komabe, iye sanataye mtima chifukwa anatsimikiza ‘kulindira’ Yehova. (Mika 7:7) Bukuli likumaliza ndi mawu olimbitsa mtima akuti Yehova adzachitira chifundo anthu Ake. Mbiri imasonyeza kuti zimenezi zinachitika. Yehova atatha kulanga anthu ake mu 537 B.C.E., mwachifundo anabwezera otsalira kudziko lawo.
8. Kodi mungafotokoze bwanji mwachidule zimene zili m’buku la Mika?
8 Zimene Yehova akuvumbula kudzera mwa Mika n’zabwino kwambiri! Buku louziridwa limeneli lili ndi zitsanzo zochenjeza. Zimenezi
zimasonyeza zimene Mulungu amachita kwa anthu amene amati amamutumikira koma ali osakhulupirika. Likunena zinthu zimene zikuchitika masiku ano. Ndiponso lili ndi uphungu wa Mulungu pa zimene tiyenera kuchita m’nthaŵi zovuta zino kuti chiyembekezo chathu chikhale cholimba.Ambuye Mfumu Yehova Alankhula
9. Malinga ndi kunena kwa Mika 1:2, kodi n’chiyani chimene Yehova anali kudzachita?
9 Tsopano tiyeni tikambirane buku la Mika mwatsatanetsatane. Pa Mika 1:2, tikuŵerenga kuti: “Imvani, mitundu ya anthu, inu nonse; tamvera, dziko lapansi, ndi zonse zili m’mwemo; ndipo Ambuye Yehova akhale mboni yakutsutsa inu, Ambuye m’Kachisi wake wopatulika.” Mukanakhalako m’nthaŵi ya Mika, mosakayika mukanachita chidwi ndi mawu amenewo. Ndipotu tikuchita nawo chidwi chifukwa Yehova akulankhulira m’kachisi wake wopatulika ndipo akulankhula kwa anthu onse osati kwa Israyeli ndi Yuda yekha. M’nthaŵi ya Mika, anthu anali atanyalanyaza Ambuye Mfumu Yehova kwa nthaŵi yaitali kwambiri. Zimenezo zinali kudzasintha posachedwa. Yehova anatsimikiza mtima kuti adzachitapo kanthu.
10. N’chifukwa chiyani mawu a pa Mika 1:2 ali ofunika kwa ife?
10 N’chimodzimodzinso masiku ano. Chivumbulutso 14:18-20 chikusonyeza kuti Yehova akulankhuliranso m’kachisi wake wopatulika. Posachedwapa adzachitapo kanthu, ndipo zinthu zoopsa zimene zidzachitike anthu adzasokonezeka nazo. Panthaŵi imeneyi, ‘mpesa [woipa] wa dziko lonse’ adzauponya moponderamo mphesa mwamukulu mwa mkwiyo wa Yehova, kuwonongeratu dongosolo la Satana la zinthu.
11. Kodi mawu a pa Mika 1:3, 4 akutanthauzanji?
11 Tamvani zimene Yehova adzachita. Mika 1:3, 4 amati: “Taonani, Yehova alikutuluka m’malo mwake, nadzatsika, nadzaponda pa misanje ya dziko lapansi. Ndi mapiri adzasungunuka pansi pa Iye, ndi zigwa zidzang’ambika, ngati sera pamoto, ngati madzi otsanulidwa potsetseremba.” Kodi Yehova adzachoka kumwamba kusiya malo ake n’kudzapondadi mapiri ndi zigwa za Dziko Lolonjezedwa? Ayi. Iye safunikira kuchita zimenezo. M’malo mwake iye adzangoganiza za dziko lapansi ndi cholinga chakuti akwaniritse chifuno chake. Ndiponso, anthu ndi amene adzaona zoopsa zimene azifotokozazo osati dziko lenilenili. Yehova akadzachitapo kanthu, zotsatira zake zidzakhala zomvetsa chisoni kwa anthu osakhulupirika. Zidzakhala ngati kuti mapiri asungunuka monga sera ndipo zigwa zang’ambika ndi chivomezi.
12, 13. Mogwirizana ndi 2 Petro 3:10-12, kodi chofunika n’chiyani kuti chiyembekezo chathu chikhale chodalirika?
12 Mawu aulosi a pa Mika 1:3, 4 angakukumbutseni ulosi wina wouziridwa wonena za masoka amene adzachitika padziko lapansi. Mtumwi Petro analemba pa 2 Petro 3:10 kuti: “Tsiku la Ambuye lidzadza ngati mbala; mmene miyamba idzapita ndi chibumo chachikulu, ndi zam’mwamba zidzakanganuka ndi kutentha kwakukulu, ndipo dziko ndi ntchito zili momwemo zidzatenthedwa.” Monganso mmene ulili ulosi wa Mika, mawu a Petro sakutanthauza kumwamba kwenikweni ndi dziko lapansi lenilenili. Akutanthauza chisautso chachikulu chimene chidzawononga dongosolo lino loipa la zinthu.
13 Ngakhale kuti masoka amenewo akubwera, Akristu mofanana ndi Mika saopa za m’tsogolo. Chifukwa chiyani? Chifukwa chotsatira malangizo amene ali m’mavesi otsatira a kalata ya Petro. Mtumwiyo akuti: “Muyenera inu kukhala anthu otani nanga m’mayendedwe opatulika ndi m’chipembedzo, akuyembekezera ndi kufulumira kwa kudza kwake kwa tsiku la Mulungu.” (2 Petro 3:11, 12) Chiyembekezo chathu cha m’tsogolo chingakhale chodalirika ngati tikhala ndi mtima womvera ndi kuonetsetsa kuti khalidwe lathu n’loyera ndiponso tikuchita ntchito za chipembedzo pamoyo wathu. Kuti chiyembekezo chathu chikhale chodalirika, tiyeneranso kukumbukira kuti tsiku la Yehova lidzafikadi.
14. Kodi n’chifukwa chiyani Israyeli ndi Yuda anafunika kulangidwa?
14 Yehova akufotokoza chifukwa chake anthu Mika 1:5 akuti: “Chichitika ichi chonse chifukwa cha kulakwa kwa Yakobo, ndi machimo a nyumba ya Israyeli. Kulakwa kwa Yakobo n’kotani? Sindiko Samariya? Ndi misanje ya Yuda ndi iti? Sindiyo Yerusalemu?” Yehova ndi amene anachititsa kuti Israyeli ndi Yuda akhaleko. Komabe anamulakwira ndipo kulakwa kwawo kunafika mpaka m’mizinda yawo yaikulu, Samariya ndi Yerusalemu.
ake akale anafunika kuwalanga.Zoipa Zichuluka
15, 16. Anthu a m’nthaŵi ya Mika anali ndi mlandu chifukwa cha zoipa ziti?
15 Mika 2:1, 2 akufotokoza momveka bwino chitsanzo cha kuipa kwa anthu a m’nthaŵi yake, pamene akuti: “Tsoka iwo akulingirira chinyengo, ndi kukonza choipa pakama pawo! Kutacha m’maŵa achichita, popeza chikhozeka m’manja mwawo. Ndipo akhumbira minda, nailanda; ngakhale nyumba, nazichotsa; asautsa mwamuna ndi nyumba yake, inde munthu ndi choloŵa chake.”
16 Anthu adyera sankagona usiku chifukwa choganiza mmene angalandire minda ndi nyumba za anansi awo. M’maŵa ankafulumira kuchita zimene aganizazo. Akanakhala kuti anali kukumbukira pangano la Yehova sakanachita zoipa ngati zimenezo. M’Chilamulo cha Mose munali malamulo oteteza osauka. Panali lamulo lakuti banja lililonse silinayenera kulandidwa choloŵa chawo mpaka kalekale. Komabe, anthu adyerawo analibe nazo ntchito zimenezo. Ananyalanyaza mawu amene ali pa Levitiko 19:18 akuti: “Uzikonda mnansi wako monga udzikonda wekha.”
17. Kodi n’chiyani chimene chingachitike ngati anthu amene amati amatumikira Mulungu aika zinthu zakuthupi pamalo oyamba pamoyo wawo?
17 Zimenezi zikusonyeza zomwe zingachitike ngati anthu amene amati amatumikira Mulungu anyalanyaza zinthu zauzimu ndi kufunafuna choyamba zinthu zakuthupi. Paulo anachenjeza Akristu a m’nthaŵi yake kuti: “Iwo akufuna kukhala achuma amagwa m’chiyesero ndi m’msampha, ndi m’zilakolako zambiri zopusa ndi zopweteka, zotere zonga zimiza anthu m’chiwonongeko ndi chitayiko.” (1 Timoteo 6:9) Ngati munthu cholinga chachikulu pa moyo wake chikhala kupeza ndalama, iye kwenikweni amalambira mulungu wonyenga—Chuma. Mulungu wonyenga ameneyo sapereka chiyembekezo chodalirika cha m’tsogolo.—Mateyu 6:24.
18. Kodi n’chiyani chimene chinali kudzachitikira anthu okonda chuma m’nthaŵi ya Mika?
18 Anthu ambiri m’nthaŵi ya Mika anaphunzira ataona mavuto kuti kudalira chuma n’kwachabe. Pa Mika 2:4 Yehova anati: “Tsiku ilo adzanena fanizo lakunena inu, nadzalira maliro olemerera, ndi kuti, Tapasuka konse; iye asintha gawo la anthu anga; ha! Andichotsera ili! Agaŵira opikisana minda yathu.” Inde, amene anali kuba nyumba ndi mindawo, anali kudzalandidwa choloŵa cha banja lawo. Adzawatengera ku dziko lachilendo, ndipo zinthu zawozo zidzakhala zofunkha za “opikisana,” kapena kuti amitundu. Chiyembekezo chonse choti adzakhala ndi tsogolo labwino chidzathera pomwepo.
19, 20. Kodi n’chiyani chinachitikira Ayuda amene anakhulupirira Yehova?
19 Koma chiyembekezo cha amene anakhulupirira Yehova sichinawagwiritse mwala. Yehova anakhulupirika pa pangano lake ndi Abrahamu ndi Davide, ndipo anachitira chifundo anthu amene anali ngati Mika omwe anali kum’konda ndi kumva chisoni chifukwa chakuti anzawo anapandukira Mulungu. Panthaŵi yake, Mulungu adzabwezeretsa zinthu chifukwa cha anthu olungama.
20 Zimenezo zinachitika mu 537 B.C.E., pamene Babulo anagwa ndiponso pamene Ayuda otsalira anabwerera kwawo. Panthaŵi imeneyo, mawu a pa Mika 2:12 anakwaniritsidwa koyamba. Pamenepo Yehova akuti: “Ndidzakumemezani ndithu, Yakobo, inu nonse; ndidzasonkhanitsa ndithu otsala a Israyeli; ndidzawaika pamodzi ngati nkhosa za ku Bozira; ngati zoweta pakati pa busa pawo adzachita phokoso chifukwa cha kuchuluka anthu.” Ndithudi, Yehova ndi wachikondi. Atawalanga anthu ake, analola otsalira kubwerera ndi kum’tumikira m’dziko limene iye anapatsa makolo awo.
Pali Kufanana Kwambiri ndi Zimene Zikuchitika
21. Kodi mmene zinthu zilili masiku ano zikufanana bwanji ndi m’nthaŵi ya Mika?
21 Pokambirana machaputala aŵiri oyambirira a buku la Mika, kodi munachita chidwi ndi mmene zinthu masiku ano zikufananira ndi masiku a Mika? Anthu ambiri masiku ano, monganso m’nthaŵi ya Mika, amati amatumikira Mulungu. Komabe, mofanana ndi Yuda ndi Israyeli, iwo ndi ogaŵanika ndipo mpaka achita nkhondo pakati pawo. Anthu ambiri olemera m’Matchalitchi Achikristu apondereza osauka. Atsogoleri achipembedzo ambiri amavomereza zinthu zimene Baibulo limaletsa mosapita m’mbali. N’chifukwa chake Matchalitchi Achikristu adzawonongedwa posachedwapa, pamodzi ndi ‘Babulo Wamkulu’ yense, ufumu wa dziko lonse wa chipembedzo chonyenga. (Chivumbulutso 18:1-5) Komabe, monganso mmene zinalili m’nthaŵi ya Mika, Yehova adzakhala ndi atumiki okhulupirika amene adzatsala padziko lapansi.
22. Kodi ndi magulu aŵiri ati amene chiyembekezo chawo ndi Ufumu wa Mulungu?
22 Mu 1919 Akristu odzozedwa okhulupirika anadzipatula kotheratu ku Matchalitchi Achikristu ndipo anayamba kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu ku mitundu yonse. (Mateyu 24:14) Anayamba ndi kufunafuna otsalira a Israyeli wauzimu. Ndiyeno anayamba kusonkhanitsa a “nkhosa zina,” ndipo magulu aŵiriŵa anakhala “gulu limodzi, mbusa mmodzi.” (Yohane 10:16) Ngakhale kuti tsopano akutumikira Mulungu m’mayiko 234, olambira okhulupirika a Yehova onseŵa alidi “pamodzi.” Ndipo pakalipano, m’khola la nkhosalo ‘mukuchitika phokoso chifukwa cha kuchuluka kwa anthu,’ amuna, akazi, ndi ana. Iwo saika chiyembekezo chawo m’dongosolo la zinthu lino koma mu Ufumu wa Mulungu umene udzabwezeretsa paradaiso padziko lapansi.
23. N’chifukwa chiyani mukutsimikiza kuti chiyembekezo chanu n’chodalirika?
23 Ponena za olambira okhulupirika a Yehova, vesi lomaliza la Mika chaputala 2 likuti: “Mfumu yawo yapita pamaso pawo, ndipo Yehova awatsogolera.” Kodi muli nawo pa chionetsero cha kupambana, potsatira Mfumu yanu, Yesu Kristu, ndi Yehova amene akutsogolera? Ngati ndi choncho, tsimikizani kuti mudzapambana ndi kuti chiyembekezo chanu n’chodalirika. Mumvetsa bwino zimenezi pamene tikambirana mfundo zazikulu zina za ulosi wa Mika.
Kodi Mungayankhe Bwanji?
• M’nthaŵi ya Mika, n’chifukwa chiyani Yehova analanga Yuda ndi Israyeli?
• Kodi n’chiyani chimene chingachitike ngati anthu amene amati amatumikira Mulungu aika zinthu zakuthupi pamalo oyamba pamoyo wawo?
• Pambuyo pokambirana machaputala 1 ndi 2 a Mika, kodi n’chifukwa chiyani mukutsimikiza kuti chiyembekezo chanu n’chodalirika?
[Mafunso]
[Chithunzi patsamba 9]
Ulosi wa Mika ungatilimbitse mwauzimu
[Zithunzi patsamba 10]
Mofanana ndi Ayuda otsalira mu 537 B.C.E., Aisrayeli auzimu ndi anzawo akupititsa patsogolo kulambira koona