Kodi Yehova Amafuna Chiyani kwa Ife?
Kodi Yehova Amafuna Chiyani kwa Ife?
“Yehova afunanji nawe koma kuti uchite cholungama, ndi kukonda chifundo ndi kuyenda modzichepetsa ndi Mulungu wako?”—MIKA 6:8.
1, 2. Kodi n’chifukwa chiyani atumiki ena a Yehova angataye mtima, koma n’chiyani chingawathandize?
VERA ndi Mkristu wokhulupirika wazaka pafupifupi 75 ndipo amadwaladwala. Iye akuti: “Nthaŵi zina ndikayang’ana kunja pawindo, ndimaona abale anga ndi alongo achikristu akulalikira kunyumba ndi nyumba. Ndikaona zimenezi ndimagwetsa misozi chifukwa ndimafuna kukhala nawo koma kudwala kumandilepheretsa kutumikira Yehova mokwanira.”
2 Kodi munayamba mwamvapo choncho? Ndithudi, onse amene amakonda Yehova amafuna kuyenda m’dzina lake ndipo amachita zofuna zake. Komabe, bwanji ngati thanzi lathu silili bwino, ndife okalamba, kapena tili ndi maudindo osamalira banja? Mwina tingataye mtima chifukwa chakuti zinthu zimenezi zikutilepheretsa kuchita zonse zimene mtima wathu umafuna kuti tichite potumikira Mulungu. Ngati moyo wathu uli wotero, n’kutheka kuti kukambirana kwathu machaputala 6 ndi 7 a Mika kudzatilimbikitsa. Machaputala ameneŵa akusonyeza kuti zimene Yehova amafuna kwa ife si zopambanitsa ndipo tingathe kuzichita.
Zimene Mulungu Amachita ndi Anthu Ake
3. Kodi Yehova anachita bwanji ndi Aisrayeli opandukawo?
3 Choyamba, tiyeni titsegule pa Mika 6:3-5 ndi kuona zimene Yehova amachita ndi anthu ake. Kumbukirani kuti m’nthaŵi ya Mika, Aisrayeli anali atapanduka. Ngakhale anatero, Yehova anawalankhula ndi mawu achifundo akuti, “Anthu anga.” Iye anachonderera kuti: “Anthu anga, kumbukilanitu.” M’malo mowaimba mlandu mwaukali, anayesetsa kuwafika pamtima mwa kuwafunsa kuti, “Ndakuchitirani chiyani?” Moti mpaka anawalimbikitsa ‘kuchita umboni wom’tsutsa.’
4. Kodi chitsanzo cha Mulungu chosonyeza chifundo chiyenera kutikhudza bwanji?
4 Mulungu ndiye chitsanzo chathu chabwino kwambiri. Iye mwachifundo anatcha ngakhale anthu opanduka a Israyeli ndi Yuda a m’nthaŵi ya Mika kuti “anthu anga” ndipo anawachonderera. Mosakayikira, ifenso tiyenera kukhala achifundo ndi okoma mtima pamene tikuchita zinthu ndi anthu amene tili nawo mumpingo. N’zoona kuti ena n’ngovuta kugwirizana nawo, kapena angakhale ofooka mwauzimu. Komabe, ngati amakonda Yehova, tifunika kuwathandiza ndi kuwachitira chifundo.
5. Kodi ndi mfundo yofunika iti imene ikupezeka pa Mika 6:6, 7?
5 Tsopano tiyeni tione Mika 6:6, 7. Mika anafunsa mafunso angapo. Anati: “Ndidzafika kwa Yehova ndi chiyani, ndi kuwerama kwa Mulungu Wam’mwamba? Kodi ndifike kwa Iye ndi nsembe zopsereza, ndi ana a ng’ombe a chaka chimodzi? Kodi Yehova adzakondwera nazo nkhosa zamphongo zikwi, kapena ndi mitsinje ya mafuta zikwi khumi? Kodi ndipereke mwana wanga woyamba chifukwa cha kulakwa kwanga, chipatso cha thupi langa chifukwa cha kuchimwa kwa moyo wanga?” Ayi, n’zosatheka kukondweretsa Yehova ndi “nkhosa zamphongo zikwi, kapena ndi mitsinje ya mafuta zikwi khumi.” Komabe chilipo chimene chingamukondweretse. Kodi n’chiyani chimenecho?
Tiyenera Kuchita Chilungamo
6. Kodi ndi zinthu zitatu ziti zimene Mulungu amafuna zopezeka pa Mika 6:8?
6 Pa Mika 6:8, tikuphunzira zimene Yehova amafuna kwa ife. Mika anafunsa kuti: “Yehova afunanji nawe koma kuti uchite cholungama, ndi kukonda chifundo ndi kuyenda modzichepetsa ndi Mulungu wako?” Zinthu zitatu zofunika zimenezi zikukhudza mmene timamvera mumtima mwathu, mmene timaganizira, ndi mmene timachitira zinthu. Tiyenera kuyesetsa kukhala ndi makhalidwe ameneŵa, kusinkhasinkha mmene tingawasonyezere, ndi mmene tingawagwiritsire ntchito. Tiyeni tikambirane zinthu zitatu zofunika zimenezi, chimodzi ndi chimodzi.
7, 8. (a) Kodi ‘kuchita chilungamo’ kumatanthauzanji? (b) Kodi n’zinthu ziti zosalungama zimene zinachuluka m’nthaŵi ya Mika?
7 ‘Kuchita chilungamo’ kumatanthauza kuchita zabwino. Mmene Mulungu amachitira zinthu ndiwo muyezo wa chilungamo. Koma anthu a m’nthaŵi ya Mika sanachite chilungamo, m’malo mwake anachita zosalungama. Kodi anatero m’njira zotani? Taonani pa Mika 6:10. Kumapeto kwa vesi limenelo, akufotokoza kuti amalonda anali kugwiritsa ntchito “muyeso wochepa.” Vesi 11 likuwonjezera kuti anagwiritsa ntchito “miyala yonyenga.” Ndipo vesi 12 likuti “lilime lawo limachita monyenga.” Motero, miyeso yonama, miyala yonyenga, ndi kulankhula mabodza zinali zofala m’malonda panthaŵi ya Mika.
8 Komabe, kupanda chilungamoku sikunali kuchitika kumsika kokha ayi. Zinali kuchitikanso m’makhoti. Pa Mika 7:3 akuti: “Kalonga apempha, ndi woweruza aweruza chifukwa cha mphoto.” Anthu ankapereka ziphuphu kwa oweruza kuti aweruze anthu osalakwa mopanda chilungamo. “Wamkuluyo,” kapena kuti munthu wodziŵika, ankachitanso nawo zosalungamazi. Ndipotu, Mika anati kalonga, woweruza, ndi wamkulu “achiluka pamodzi,” kapena kuti anali kugwirizana pokonza, zoipa zawozo.
9. Kodi kupanda chilungamo kwa oipa kunakhudza bwanji Yuda ndi Israyeli?
9 Kupanda chilungamo kumene atsogoleri oipa ankachita kunakhudza Yuda ndi Israyeli yense. Mika 7:5 akufotokoza kuti chifukwa cha kupanda chilungamoko anthu, mabwenzi enieni, ngakhale anthu okwatirana, anasiya kukhulupirirana. Vesi 6 likusonyeza kuti zimenezi zinachititsa kuti anthu apachibale monga ana aamuna ndi atate awo, ana aakazi ndi amayi awo, azidana.
10. Kodi Akristu ali ndi khalidwe lotani m’dziko lopanda chilungamo lino?
10 Nanga bwanji lerolino? Kodi sitikuonanso zinthu ngati zimenezi? Ifenso monga Mika, tikukhala m’dziko lopanda chilungamo, anthu sakukhulupirirana, ndipo mmene iwo akukhalira, ngakhale mabanja, n’chisokonezo chokhachokha. Koma ife atumiki a Mulungu amene tili m’dziko lopanda chilungamo lino, sitilola mzimu wa dziko wochita zosalungama kuloŵa mumpingo wachikristu. M’malo mwake, timayesetsa kutsatira mfundo za makhalidwe abwino za kuona mtima ndi kukhulupirika, ndipo timasonyeza zimenezi pa moyo wathu wa tsiku ndi tsiku. Ndithudi, ‘timakhala oona mtima m’zinthu zonse.’ (Ahebri 13:18, NW) Kodi simukuvomereza kuti mwa kuchita chilungamo timapeza madalitso ochuluka chifukwa cha ubale wathu umene umapereka umboni wakuti timakhulupiriranadi?
Kodi Anthu Amamva Bwanji “Mawu a Yehova”?
11. Kodi Mika 7:12 akukwaniritsidwa bwanji?
11 Mika analosera kuti ngakhale kuti anthu ankachita zinthu zosalungama, chilungamo chidzafikira anthu a mitundu yonse. Mneneriyo analosera kuti anthu adzasonkhanitsidwa “kuyambira kunyanja kufikira kunyanja, ndi kuyambira kuphiri kufikira kuphiri” kuti akhale olambira Yehova. (Mika 7:12) Lerolino, pamene ulosiwu ukukwaniritsidwa komaliza, anthu a mitundu yonse, osati a mtundu umodzi wokha, akupindula ndi chilungamo cha Mulungu chopanda tsankho. (Yesaya 42:1) Kodi zimenezi zikuchitika bwanji?
12. Kodi anthu akumva bwanji “mawu a Yehova” lerolino?
12 Kuti tipeze yankho, taganizirani mawu a Mika oyambirira. Mika 6:9 akuti: “Mawu a Yehova aitana mudzi, ndi wanzeru aopa dzina lanu.” Kodi anthu a mitundu yonse akumva bwanji “mawu a Yehova,” ndipo zimenezi zikugwirizana bwanji ndi kuchita chilungamo kwathu? Inde, anthu samva mawu enieni a Mulungu. Komabe, anthu a mitundu yosiyanasiyana kaya olemera kapena osauka, akumva mawu a Yehova kudzera m’ntchito yathu yolalikira imene ikuchitika padziko lonse. Motero, amene akumvetsera ‘akuopa dzina la Mulungu’ ndipo akulilemekeza. Timachitadi zinthu mwachilungamo ndiponso mwachikondi potumikira monga olengeza Ufumu achangu. Mwa kudziŵitsa aliyense dzina la Mulungu mopanda tsankho, ‘timachita chilungamo.’
Tikhale Okonda Kukoma Mtima
13. Kodi kukoma mtima kumasiyana bwanji ndi chikondi?
13 Tsopano tiyeni tikambirane chinthu chachiŵiri chofunika chimene chili pa Mika 6:8. Yehova amafuna kuti ‘tikonde chifundo.’ Liwu lachihebri limene analimasulira kuti “chifundo” amalimasuliranso kuti “kukoma mtima,” kapena “chikondi chokhulupirika.” Kukoma mtima ndiko kusamala ena mwa kuwachitira zinthu kapena kuwadera nkhaŵa. Kukoma mtima n’kosiyana ndi chikondi. Motani? Chikondi chimakhudza mbali zambiri chifukwa munthu angakonde zinthu kapena mfundo zinazake. Mwachitsanzo, Malemba amanena za munthu “wokonda vinyo ndi mafuta” ndiponso munthu “wokonda nzeru.” (Miyambo 21:17; 29:3) Komano, kukoma mtima nthaŵi zonse kumakhudza anthu, makamaka amene amatumikira Mulungu. N’chifukwa chake pa Mika 7:20 akufotokozapo za ‘kupatsa chifundo [‘kukomera mtima,’ NW] Abrahamu’—munthu amene anatumikira Yehova Mulungu.
14, 15. Kodi kukoma mtima kumasonyezedwa bwanji, ndipo pali umboni wotani wa zimenezi?
14 Pa Mika 7:18, mneneriyo ananena kuti Mulungu “akondwera nacho chifundo [“kukoma mtima,” NW].” Pa Mika 6:8 sakungotiuza kuti tikhale okoma mtima koma kuti tikonde khalidwe limeneli. Kodi tikuphunzira chiyani pa malemba ameneŵa? Timakomera mtima anthu ena mwaufulu chifukwa chakuti tikufuna kutero. Monga Yehova, timasangalala kapena kukondwera pokomera mtima anthu amene akusoŵa thandizo.
15 Lerolino, kukoma mtima kumeneku ndiko chizindikiro cha anthu a Mulungu. Taonani chitsanzo chimodzi ichi. M’chaka cha 2001, mwezi wa June, mvula ya mkuntho inakokolola zinthu ku Texas, ku America, ndipo inawononga nyumba zikwi zambiri ngakhale nyumba mazana angapo za Mboni za Yehova. Pofuna kuthandiza abale awo achikristu, Mboni pafupifupi 10,000 zinagwiritsa ntchito nthaŵi ndi nyonga zawo mwaufulu. Anthu odziperekawa anagwira ntchito mosalekeza kwa nthaŵi yoposa miyezi isanu ndi umodzi. Anali kugwira ntchito usana, usiku, ndiponso Loŵeruka ndi Lamlungu lomwe kuti amangirenso abale awo achikristu Nyumba za Ufumu 8 ndiponso nyumba zawo zoposa 700. Amene sanathe kugwira ntchitoyo, anapereka zakudya, zipangizo, ndi ndalama. N’chifukwa chiyani Mboni zikwizikwi zonsezi zinathandiza abale awo? Chifukwa chakuti ‘zimakonda kukoma mtima.’ Ndipotu n’zosangalatsa kwambiri kuona kuti abale athu padziko lonse akusonyeza kukoma mtima kotereku! Inde, ‘kukonda kukoma mtima’ kumene Mulungu amafuna kwa ife sikolemetsa, koma n’kosangalatsa!
Khalani Odzichepetsa Poyenda ndi Mulungu
16. Kodi ndi fanizo liti limene likutithandiza kuona bwino kufunika kokhala wodzichepetsa poyenda ndi Mulungu?
16 Chinthu chachitatu chofunika chimene chili pa Mika 6:8 ndicho “kuyenda modzichepetsa ndi Mulungu wako.” Zimenezi zikutanthauza kuzindikira kuti pali zinthu zina zimene sitingathe kuchita ndipo tifunika kudalira Mulungu. Mwachitsanzo: Tayerekezerani kuti mwana wamkazi wamng’ono wagwira dzanja la bambo ake molimbika ndipo akuyenda pamene chimvula chadzaoneni chikugwa. Mwanayo akudziŵa kuti ali ndi mphamvu zochepa, koma akudalira bambo ake. Ifenso tiyenera kudziŵa kuti pali zinthu zina zimene sitingathe kuchita ndipo tiyenera kudalira Atate wathu wakumwamba. Kodi tingatani kuti tikhalebe ndi chidaliro chimenechi? Njira imodzi ndiyo kukumbukira chifukwa chake n’kwanzeru kukhalabe pafupi ndi Mulungu. Mika akutikumbutsa zifukwa zitatu: Yehova ndiye Mlanditsi, Mtsogoleri, ndi Mtetezi wathu.
17. Kodi Yehova analanditsa, kutsogolera ndi kuteteza bwanji anthu ake a m’nthaŵi zakale?
17 Pa Mika 6:4, 5, Mulungu anati: “Ndinakukwezani kukutulutsani m’dziko la Aigupto.” Inde, Yehova anali Mlanditsi wa Aisrayeli. Yehova anapitiriza kuti: “Ndinatuma akutsogolereni Mose, Aroni, ndi Miriamu.” Mose ndi Aroni anawagwiritsa ntchito kutsogolera mtunduwo, ndipo Miriamu anatsogolera akazi achiisrayeli povina kukondwerera kupambana kwawo. (Eksodo 7:1, 2; 15:1, 19-21; Deuteronomo 34:10) Yehova anawatsogolera pogwiritsa ntchito atumiki ake. M’vesi 5, Yehova anakumbutsa Aisrayeli kuti anawateteza kwa Balaki ndi Balamu, ndi kutinso anawateteza m’chigawo chomaliza cha ulendo wawo kuyambira ku Sitimu ku Moabu kufikira ku Giligala m’Dziko Lolonjezedwa.
18. Kodi Mulungu wakhala bwanji Mlanditsi, Mtsogoleri, ndi Mtetezi wathu lerolino?
18 Pamene tikuyenda ndi Mulungu, amatilanditsa
ku dziko la Satana, amatitsogolera pogwiritsa ntchito Mawu ake ndi gulu lake, ndiponso amatiteteza monga gulu pamene otsutsa atiukira. Motero, tili ndi zifukwa zokwanira zogwirira dzanja la Atate wathu wakumwamba molimbika pamene tikuyenda naye m’chigawo chovuta chomaliza cha ulendo wathu wokaloŵa m’dziko latsopano lolungama la Mulungu loposa Dziko Lolonjezedwa lakale.19. Kodi kudzichepetsa kumagwirizana bwanji ndi zinthu zimene sitingathe kuchita?
19 Kuyenda modzichepetsa ndi Mulungu kumatithandiza kuona moyo wathu moyenera. Zimenezi zili choncho chifukwa kusonyeza kudzichepetsa kumaphatikizapo kuzindikira zinthu zimene sitingathe kuchita. Ukalamba kapena matenda zingatipangitse kuti tisamathe kuchita zinthu zina muutumiki wa Yehova. Koma m’malo molola zimenezi kutikhumudwitsa, tizikumbukira kuti Mulungu amalandira zoyesayesa zathu ndi kudzimana kwathu ‘monga momwe tili nazo, si monga tilibe.’ (2 Akorinto 8:12) Inde, Yehova amafuna kuti tim’tumikire ndi mtima wonse, kuchita zimene tingathe. (Akolose 3:23) Mulungu amatidalitsa kwambiri ngati tikuchita mwakhama ndiponso mwachangu zonse zimene tingathe muutumiki wake.—Miyambo 10:22.
Mtima Wodikira Umadzetsa Madalitso
20. Kodi tiyenera kudziŵa chiyani chimene chingatithandize kukhala ndi mtima wodikira mofanana ndi Mika?
20 Kulandira madalitso a Yehova kumatilimbikitsa kutsanzira mtima wa Mika. Iye anati: “Ndidzalindirira Mulungu wa chipulumutso changa.” (Mika 7:7) Kodi mawu ameneŵa akugwirizana bwanji ndi kuyenda kwathu modzichepetsa ndi Mulungu? Kudikira, kapena kuti kuleza mtima, kumatithandiza kuti tisataye mtima poona kuti tsiku la Yehova silinafikebe. (Miyambo 13:12) Kunena zoona, tonsefe tikulakalaka kuti dziko loipali lithe. Komabe, mlungu uliwonse pali anthu zikwizikwi amene akungoyamba kumene kuyenda ndi Mulungu. Kudziŵa zimenezi kumatipatsa chifukwa chokhalira ndi mtima wodikira. Pankhani imeneyi, Mboni ina imene yatumikira kwa nthaŵi yaitali inati: “Ndikayang’ana m’mbuyo pa zaka 55 zimene ndakhala ndikugwira ntchito yolalikira, ndikuona kuti sindinagwiritsidwe mwala chifukwa choyembekeza Yehova. M’malo mwake, ndapeŵa mavuto ambiri.” Kodi zofanana ndi zimenezi zakuchitikirani?
21, 22. Kodi Mika 7:14 akukwaniritsidwa bwanji masiku ano?
21 Mosakayikira kuyenda ndi Yehova kumatipindulitsa. Tikaŵerenga pa Mika 7:14, Iye anayerekezera anthu a Mulungu ndi nkhosa zimene zakhala pamodzi ndi mbusa wawo motetezeka. Lerolino, ulosi umenewu ukukwaniritsidwa mokulirapo pamene otsalira a Israyeli wauzimu pamodzi ndi a “nkhosa zina” amapeza chitetezo kwa Mbusa wawo wokhulupirika, Yehova. Iwo akukhala ‘paokha m’nkhalango pakati pa Karimeli [“munda wa zipatso,” NW],’ olekana mwauzimu ndi dziko lino limene mavuto ake ndi kuopsa kwake zikukulirakulira.—Yohane 10:16; Deuteronomo 33:28; Yeremiya 49:31; Agalatiya 6:16.
22 Anthu a Yehova ndi olemera, monganso mmene Mika 7:14 analoserera. Mika anafotokoza za nkhosa, kapena kuti anthu a Mulungu, kuti: “Zidye m’Basana ndi m’Gileadi.” Mofanana ndi nkhosa za ku Basana ndi Gileadi zimene zinali kudya msipu m’mabusa achonde ndiponso zinali kuchuluka, anthu a Mulungu masiku ano ndi olemera mwauzimu. Limeneli ndi dalitso linanso la anthu amene akuyenda modzichepetsa ndi Mulungu.—Numeri 32:1; Deuteronomo 32:14.
23. Kodi kupenda kwathu Mika 7:18, 19 kungatiphunzitse chiyani?
23 Pa Mika 7:18, 19 mneneriyo anafotokoza kuti Yehova amafunitsitsa kukhululukira anthu amene alapa. Vesi 18 likuti Yehova ndiye “wakukhululuka mphulupulu” ndiponso “wakupitirira zolakwa.” Monga mmene afotokozera m’vesi 19, iye ‘adzataya zochimwa zawo zonse m’nyanja yakuya.’ Kodi ndi phunziro limodzi lotani limene tikupezapo pamenepa? Tingadzifunse ngati tikutsanzira Yehova pankhani imeneyi. Kodi timakhululukira ena akatilakwira? Ngati iwo ali olapa ndipo akufuna kuti tikonze zinthu kuti pakhalenso mtendere, ifenso tiyenera kusonyeza mtima ngati wa Yehova wofuna kukhululuka kotheratu.
24. Kodi mwapindula chiyani ndi ulosi wa Mika?
24 Kodi tapindulapo chiyani pokambirana ulosi wa Mika? Ulosi umenewu watikumbutsa kuti Yehova amapereka chiyembekezo chenicheni kwa anthu amene amadza kwa iye. (Mika 2:1-13) Talimbikitsidwa kuchita zonse zimene tingathe kupititsa patsogolo kulambira koona kuti tiyende m’dzina la Mulungu kosatha. (Mika 4:1-4) Ndiponso tatsimikizidwa kuti mulimonse mmene zinthu zingakhalire pamoyo wathu, tingathe kuchita zimene Yehova amafuna. Inde, ulosi wa Mika umatilimbikitsadi kuti tiyende m’dzina la Yehova.
Kodi Mungayankhe Bwanji?
• Malinga ndi kunena kwa Mika 6:8, kodi Yehova amafuna chiyani kwa ife?
• Kodi chofunika n’chiyani kuti ‘tichite chilungamo’?
• Kodi tingasonyeze bwanji kuti ‘timakonda kukoma mtima’?
• Kodi “kuyenda modzichepetsa ndi Mulungu” kumatanthauza chiyani?
[Mafunso]
[Zithunzi patsamba 21]
Ngakhale kuti zinthu zinali zoipa m’nthaŵi ya Mika, iye anachita zofuna za Yehova. Inunso mungatero
[Chithunzi patsamba 23]
Chitani chilungamo mwa kulalikira kwa anthu osiyanasiyana kaya olemera kapena osauka
[Zithunzi patsamba 23]
Sonyezani kuti ndinu wokoma mtima mwa kuthandiza ena
[Chithunzi patsamba 23]
Chitani zimene mungathe modzichepetsa pozindikira kuti pali zinthu zina zimene simungathe kuchita