“Mawu A Mulungu Ngamphamvu Bwanji!”
“Mawu A Mulungu Ngamphamvu Bwanji!”
“MAWU a Mulungu ali amoyo, ndi ochitachita.” (Ahebri 4:12) Potsimikizira kuti mphamvu ya Mawu a Mulungu silephera, Kalendala ya 2003 ya Mboni za Yehova inali ndi nkhani zisanu ndi imodzi za padziko lonse zofotokoza zochitikadi zenizeni. Pa mutu wakuti “Asanaphunzire ndi Ataphunzira,” kalendalayi inasonyeza mmene ntchito yophunzitsa ya Mboni za Yehova ikuthandizira anthu kukhala ndi makhalidwe abwino, kusiya makhalidwe oika moyo pachiswe, kulimbitsa moyo wawo wabanja, ndi kusamalira ubwenzi wawo ndi Mulungu.
Tinalandira makalata angapo oyamikira kalendala ya 2003 imeneyi. Naŵa ena mwa mawu a m’makalatawo:
“Kalendala imeneyi ndi umboni kwa Akristu oona kuti pali anthu ngati iwo omwe anafunika kumenya zolimba nkhondo ya chikhulupiriro. Tsopano angamaone zithunzizi monga zowakumbutsa zinthu zimene ena asintha.”—Steven, United States.
“Ndinafunitsitsa n’takulemberani mawu ochepa aŵa kuti mudziŵe mmene kalendala ya 2003 yandikhudzira mtima. Kalendala sinandikhudzepo mtima chonchi. Nkhani zofotokoza miyoyo ya anthu zimenezi zikhala pa zinthu zimene ndimayenda nazo m’chikwama changa chimene ndimapita nacho kolalikira kuti ndizisonyeza anthu umboni weniweni ndi wamphamvu kwambiri wa mmene Baibulo lingakhudzire anthu.”—Marc, Belgium.
“Kalendalayi inandikhudza kwambiri. Zinanditenga mtima kwambiri kuŵerenga ndi kuona mmene Yehova wawasinthira anthu ameneŵa. Izi zandilimbikitsa kupitirizabe kusintha moyo wanga. Panopo tsopano kusiyana n’kale lonseli, ndikumvadi kuti ndili nawo m’gulu la ubale wapadziko lonse.”—Mary, United States.
“Yesu anakhudzidwa mtima kwambiri ndi mkhalidwe wauzimu womvetsa chisoni wa anthu. Zikomo chifukwa chotsatira chitsanzo cha Kristu mwa kufotokoza nkhani za miyoyo ya anthu zomwe zili m’kalendala yathu ya 2003. Ndinali ndisanalirepo ndi mfundo za m’kalendala.”—Cassandra, United States.
“Pamene ndinali ndi zaka 11, ndinayamba kusuta; kenako ndinayamba kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo. Nthaŵi zambiri ndinkaganiza zongodzipha. Nditadziŵa Yehova, ndinathandizidwa kusiya zinthu zimenezi. Kalendala imeneyi njofunika kwambiri kwa ine. Zitsanzo za abale ndi alongo anga apadziko lonse zikundilimbikitsa. Ndadziŵa tsopano kuti sindili ndekha pankhondoyi ndiponso kuti kukonda Yehova ndi kum’tumikira ndi mtima wonse ndiye chinthu chofunika kwambiri kwambiri.”—Margaret, Poland.
“Mawu a Mulungu ngamphamvu bwanji! Nditalandira kalendala ya 2003, ndinayesetsa kudzilimbitsa kuti ndisalire. Nkhanizi, pamodzi ndi zithunzizi, n’zolimbitsa chikhulupiriro kwambiri.”—Darlene, United States.
“Moyo wakale wa ena mwa anthuŵa ukufanana kwambiri ndi moyo wanga wakale. Yehova anandipatsa mphamvu kuti ndisiye makhalidwe ooneka ngati osatheka kuwasiya. Zikomo kwambiri chifukwa cha nkhani za zochitika zenizeni pa moyo wa anthu zimenezi.”—William, United States.