M’tsogolomu Muli Dziko Lopanda Upandu
M’tsogolomu Muli Dziko Lopanda Upandu
INGOYEREKEZERANI, ngati mungathe kutero, kuti padziko lonse palibenso apandu! Sipangafunikenso apolisi, ndende, kapenanso njira zopezera apandu ndi kuwalanga zomwe zimafuna ndalama zambiri komanso n’zovuta kwambiri. Lingakhale dziko lomwe aliyense akulemekeza moyo ndiponso katundu wa ena. Kodi izi zikumveka kuti n’zosatheka? Mungaganize choncho, komatu kusintha kochititsa chidwi kumeneku ndi komwe Baibulo limalonjeza. Bwanji osaona zomwe Malemba ananena pankhani ya upandu ndiponso zoipa zina zochitika padziko pano?
M’buku la Masalmo, timaŵerenga kuti: “Usavutike mtima chifukwa cha ochita zoipa, usachite nsanje chifukwa cha ochita chosalungama. Pakuti adzawamweta msanga monga udzu, ndipo adzafota monga msipu wauwisi. Koma ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.” (Salmo 37:1, 2, 11) Kunena zoona, palibe munthu amene angalepheretse Mulungu kukwaniritsa lonjezoli ndiponso malonjezo ake ena onse osangalatsa kwambiri.
Mulungu adzadzetsa madalitso ameneŵa pogwiritsa ntchito Ufumu wake. M’pemphero la Ambuye, Yesu Kristu anaphunzitsa om’tsatira ake kupemphera kuti Ufumu umenewu udze ndiponso kuti chifuno cha Mulungu chichitike “monga Kumwamba chomwecho pansi pano.” (Mateyu 6:9, 10) Posachedwapa, mu Ufumu umenewu, padziko lapansi pano sipadzapezeka munthu aliyense wofuna kuchita zaupandu chifukwa cha umphaŵi, kuponderezedwa, kapena dyera. M’malomwake, Mawu a Mulungu amati: “M’dzikomo mudzakhala dzinthu dzochuluka pamwamba pa mapiri.” (Salmo 72:16) Inde, Yehova Mulungu adzapatsa aliyense padziko pano zinthu zosatha. Chinthu chabwino kwambiri n’chakuti anthu azidzakonda Mulungu ndiponso anansi awo, ndipo dzikoli silidzasokonezedwanso ndi upandu.