Malonjezo Amene Mungadalire
Malonjezo Amene Mungadalire
MNENERI wa Mulungu Mika anadziŵa kuti nthaŵi zambiri malonjezo akhoza kukhala osadalirika. M’masiku ake, ngakhale mabwenzi okondana kwambiri sanali odalirana nthaŵi zonse kuti asunga mawu awo. Choncho Mika anachenjeza kuti: “Musakhulupirira bwenzi, musatama bwenzi loyanja; usam’tsegulire pakhomo pakamwa pako, ngakhale kwa iye wogona m’fukato mwako.”—Mika 7:5.
Kodi Mika analola zochitika zomvetsa chisonizi kum’pangitsa kukayikira malonjezo onse? Ayi. Iye anasonyeza kudalira kwambiri malonjezo a Mulungu wake, Yehova. Mika analemba kuti: “Koma ine, ndidzadikira Yehova; ndidzalindirira Mulungu wa chipulumutso changa.”—Mika 7:7.
N’chifukwa chiyani Mika anali ndi chidaliro chimenechi? Chifukwa ankadziŵa kuti Yehova nthaŵi zonse amasunga mawu ake. Zonse zimene Mulungu analumbirira makolo a Mika zinachitikadi. (Mika 7:20) Kukhulupirika kwa Yehova m’mbuyomo kunam’patsa Mika chifukwa chomveka chokhulupirira kuti Yehova adzasunga mawu ake m’tsogolo.
“Sanasoŵapo Mawu Amodzi”
Mwachitsanzo, Mika anadziŵa kuti Yehova anapulumutsa Aisrayeli ku ukapolo ku Igupto. (Mika 7:15) Yoswa, amene anali nawo pagulu la anthu opulumutsidwawo, analimbikitsa Aisrayeli anzake kukhulupirira malonjezo onse a Mulungu. Chifukwa chiyani? Yoswa anawakumbutsa kuti: “Mudziŵa m’mitima yanu yonse, ndi m’moyo mwa inu nonse, kuti pa mawu okoma onse Yehova Mulungu wanu anawanena za inu sanagwa padera mawu amodzi; onse anachitikira inu, sanasoŵapo mawu amodzi.”—Yoswa 23:14.
Aisrayeli ankadziŵa bwino kuti Yehova anawachitira zinthu zodabwitsa. Iye anakwaniritsa zimene analonjeza Abrahamu, kholo lawo loopa Mulungu, kuti adzakhala ndi ana ngati nyenyezi ndipo adzatenga dziko la Kanani. Yehova anauzanso Abrahamu kuti mbadwa zake zidzazunzika zaka 400 koma zidzabwerera ku Kanani mu “mbadwo wachinayi.” Zonsezi zinachitikadi.—Genesis 15:5-16; Eksodo 3:6-8.
Aisrayeli analandiridwa bwino ku Igupto m’masiku a Yosefe, mwana wa Yakobo. Kenako Aigupto anayamba kuwazunza powagwiritsa ntchito yathangata, koma monga momwe Mulungu analonjezera, patatha mibadwo inayi kuchokera nthaŵi imene anapita ku Igupto, mbadwa za Abrahamu zimenezi zinamasulidwa ku ukapolo wa ku Igupto. *
Kwa zaka 40 zotsatira, Aisrayeli anali ndi umboni winanso wakuti Yehova nthaŵi zonse amasunga malonjezo ake. Aamaleki ataukira Aisrayeli popanda chifukwa, Mulungu anamenyera nkhondo ndi kuteteza anthu ake. Anawapatsa zinthu zonse zimene anali kufunika paulendo wawo wa zaka 40 wa m’chipululu ndipo pomaliza anawapatsa Dziko Lolonjezedwa. Yoswa ataona mbiri ya zimene Yehova anachitira mbadwa za Abrahamu zimenezi, ananena ndi mtima wonse kuti: “Sikadasoŵa kanthu konse ka zinthu zokoma zonse Yehova adazinenera nyumba ya Israyeli; zidachitika zonse.”—Yoswa 21:45.
Dalirani Malonjezo a Mulungu
Kodi mungatani kuti muzikhulupirira malonjezo a Yehova, monga mmene anachitira Mika ndi Yoswa? Chabwino, kodi mumayamba bwanji kudalira anthu ena? Mumayesetsa kuwadziŵa bwino mmene mungathere. Mwachitsanzo, mungaone kuti ndi odalirika bwanji mwa kuona kuti amayesetsa kwambiri kukwaniritsa zonse zimene alonjeza. Pamene mukuwadziŵa bwino anthuwo, mumayamba kuwadalira pang’onopang’ono. Mungachite zomwezo pankhani yokhulupirira malonjezo a Mulungu.
Njira imodzi imene mungachitire zimenezi ndi yosinkhasinkha za chilengedwe ndi malamulo amene chimayendera. Asayansi amadalira malamulo ameneŵa, monga amene amalamulira mmene selo limodzi la munthu limagaŵikira ndi kuchulukana kuti lipange maselo ambirimbiri amene amapanga thupi lanu. Ndiponso, malamulo amene amalamulira khalidwe la zinthu ndiponso mphamvu m’chilengedwe chonsechi ayenera kuti anaikidwa ndi munthu Wopanga Malamulo wodalirika kwambiri. Ndithudi mungadaliredi Salmo 139:14-16; Yesaya 40:26; Ahebri 3:4.
malonjezo ake, monga momwe mumadalirira malamulo amene chilengedwe chake chimayendera.—Mwa mneneri Yesaya, amene anakhalako nthaŵi imodzi ndi Mika, Yehova anagwiritsa ntchito kusaphonya kwa nyengo nthaŵi zonse ndi kusintha kodabwitsa zedi kwa madzi kuchoka padziko ndi kukapanga mitambo n’kudzagwa ngati mvula kusonyeza kudalirika kwa mawu ake. Chaka chilichonse kumagwa mvula. Imafeŵetsa nthaka ndipo imapangitsa anthu kubzala mbewu zawo ndi kukolola zimene alima. Pambali imeneyi, Yehova anati: “Monga mvula imagwa pansi ndi matalala, kuchokera kumwamba yosabwerera komweko, koma ikhamiza nthaka ndi kuibalitsa, ndi kuiphukitsa, ndi kuipatsitsa mbewu kwa wobzala, ndi chakudya kwa wakudya; momwemo adzakhala mawu anga amene atuluka m’kamwa mwanga, sadzabwerera kwa Ine chabe, koma adzachita chimene ndifuna, ndipo adzakula m’mene ndinawatumizira.”—Yesaya 55:10, 11.
Malonjezo Odalirika a Paradaiso
Kupenda chilengedwe kungathandize kudalira Mlengi, koma pali chinanso chofunika kuchita ngati mukufuna kudziŵa malonjezo amene ndi mbali ya ‘mawu otuluka m’kamwa mwake.’ Kuti mudziŵe malonjezo ameneŵa ndi kuwadalira, mufunika kupenda nkhani ya m’Malemba youziridwa ndi Mulungu yonena za cholinga cha Mulungu polenga dziko lapansi ndiponso zochita zake ndi anthu.—2 Timoteo 3:14-17.
Mneneri Mika anali kudalira malonjezo a Yehova. Ndipo inu muli ndi nkhani zambiri zouziridwa ndi Mulungu kusiyana ndi zimene Mika anali nazo. Pamene mukuŵerenga Baibulo ndi kusinkhasinkha zimene mwaŵerenga, inunso mungakhulupirire kuti malonjezo a Mulungu adzakwaniritsidwa. Malonjezo ameneŵa si okhudza mbadwa zenizeni za Abrahamu zokha ayi, koma anthu onse. Yehova analonjeza kholo loopa Mulungu limeneli kuti: “M’mbewu zako mitundu yonse ya dziko lapansi idzadalitsidwa: chifukwa wamvera mawu anga.” (Genesis 22:18) Mbali yofunika kwambiri ya “mbewu” ya Abrahamu ndi Mesiya, Yesu Kristu.—Agalatiya 3:16.
Mwa Yesu Kristu, Yehova adzatsimikizira kuti anthu omvera alandira madalitso. Ndipo kodi Mulungu walonjeza kuchita chiyani m’masiku athu ano? Mika 4:1, 2 akuyankha ndi mawu aulosi akuti: “Kudzachitika masiku otsiriza, kuti phiri la nyumba ya Yehova lidzakhazikika pamwamba pa mapiri, nilidzakuzika pamwamba pa zitunda, ndi mitundu ya anthu idzayendako. Ndipo amitundu ambiri adzamuka, nadzati, Tiyeni, tikwere ku phiri la Yehova, ndi ku nyumba ya Mulungu wa Yakobo; kuti Iye atiphunzitse njira zake, ndipo tidzayenda m’mabande ake.”
Amene aphunzira njira za Yehova ‘asula malupanga awo kukhala makasu, ndi mikondo yawo kukhala mazenga.’ Safunanso kumenya nkhondo. Posachedwa dzikoli lidzakhala ndi anthu oongoka mtima okhaokha, ndipo sipadzakhala wowawopseza. (Mika 4:3, 4) Inde, Mawu a Mulungu akulonjeza kuti mu ulamuliro wa Ufumu umene uli m’manja mwa Yesu Kristu, Yehova adzachotsa padziko lapansili anthu onse amene amapondereza anzawo.—Yesaya 11:6-9; Danieli 2:44; Chivumbulutso 11:18.
Ngakhale anthu amene avutika ndiponso kufa chifukwa chakuti anthu anapandukira Mulungu adzaukitsidwa ndi kuyembekezera kukhala ndi moyo kosatha padziko lapansi. (Yohane 5:28, 29) Satana ndi ziwanda zake, amene amayambitsa kuipa, sadzakhalakonso, ndipo zotsatira za kuchimwa kwa Adamu zidzachotsedwa mwa nsembe ya dipo ya Yesu. (Mateyu 20:28; Aroma 3:23, 24; 5:12; 6:23; Chivumbulutso 20:1-3) Kodi zinthu zidzawayendera bwanji anthu omvera? Adzadalitsidwa ndi moyo wosatha komanso thanzi langwiro padziko lapansi la paradaiso.—Salmo 37:10, 11; Luka 23:43; Chivumbulutso 21:3-5.
Ameneŵatu ndi madalitso abwino zedi! Koma kodi mungawakhulupirire? Inde. Awa si malonjezo a anthu amene angakhale ndi zolinga zabwino koma amene amasoŵa mphamvu zochitira zimene alonjezazo. Ndi malonjezo a Mulungu Wamphamvuyonse, amene sanama ndiponso ‘sazengereza lonjezo.’ (2 Petro 3:9; Ahebri 6:13-18) Mungadalire kwambiri malonjezo onse a m’Baibulo, chifukwa chakuti Gwero lake ndi “Yehova, Mulungu wa choonadi.”—Salmo 31:5.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 8 Onani Insight on the Scriptures, voliyumu 1, masamba 911 mpaka 912, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
[Mawu Otsindika patsamba 6]
“Pa mawu okoma onse Yehova Mulungu wanu anawanena za inu sanagwa padera mawu amodzi.”—YOSWA 23:14
[Zithunzi pamasamba 4, 5]
Pa Nyanja Yofiira ndi m’chipululu, Yehova anakwaniritsa zimene analonjeza Aisrayeli
[Chithunzi patsamba 7]
Yehova anakwaniritsa zimene analonjeza Abrahamu. Mbewu yake, Yesu Kristu, idzapatsa anthu madalitso