Peŵani Chinyengo
Peŵani Chinyengo
“Penyani kuti pasakhale wina wakulanda inu ngati chuma, mwa . . . chinyengo chopanda pake.”—AKOLOSE 2:8.
1-3. (a) Kodi ndi zitsanzo ziti zomwe zikusonyeza kuti chinyengo chaloŵerera pafupifupi pa chinthu chilichonse m’moyo watsiku ndi tsiku? (b) N’chifukwa chiyani sitiyenera kudabwa ndi chinyengo chomwe chili m’dzikoli?
“NDI anthu angati mwa inu amene sananamizidwepo ndi munthu wofuna thandizo?” Zaka zingapo zipatazo, pulofesa wina wa zamalamulo anachita kafukufuku pogwiritsa ntchito funso limeneli. Yankho lake linali lotani? Iye anafotokoza kuti: “Mwa maloya zikwi zambiri, loya mmodzi yekha ndi amene anali asananamizidwepo.” Chifukwa chake chinali chiyani? “Loyayo anali atangoyamba kumene ntchito pakampani ina yaikulu ndipo anali asanalankhule ndi munthu wofuna thandizo.” Izi zikusonyeza mfundo yomvetsa chisoni kwambiri, yakuti kunama ndiponso chinyengo n’zofala kwambiri m’dziko la masiku ano.
2 Chinyengo chimachitika m’njira zambiri ndipo chaloŵerera pafupifupi pa chilichonse chomwe anthu akuchita masiku ano. Malipoti a nkhani ngodzala ndi zitsanzo za nkhaniyi, monga andale akumanama pa zochita zawo, akatswiri oŵerengera chuma pamodzi ndi maloya akumanama kuti kampani yapanga phindu lalikulu, otsatsa malonda akumasokeretsa ogula, wosuma kapena kusumiridwa mlandu akumanamiza kampani ya inshuwalansi, ndipo izi n’zitsanzo zochepa chabe. Ndiyeno pali chinyengo chomwe zipembedzo zikuchita. Atsogoleri achipembedzo akusokeretsa anthu mwa kuwaphunzitsa zinthu zabodza, monga za mzimu wosafa, moto wa helo, ndiponso Utatu.—2 Timoteo 4:3, 4.
3 Kodi tiyenera kudabwa ndi chinyengo chonsechi? Osati kwenikweni. Ponena za “masiku otsiriza,” Baibulo linachenjeza kuti: “Anthu oipa ndi onyenga, adzaipa chiipire, kusokeretsa ndi kusokeretsedwa.” (2 Timoteo 3:1, 13) Monga Akristu, tiyenera kuchenjera ndi malingaliro osokeretsa omwe angatisiyitse choonadi. Izi zikutipatsa mafunso aŵiri: N’chifukwa chiyani chinyengo chafala kwambiri masiku ano, ndipo kodi tingatani kuti tipeŵe kunyengedwa?
N’chifukwa Chiyani Chinyengo Chafala Kwambiri Masiku Ano?
4. Kodi Baibulo limafotokoza motani chifukwa chomwe chinyengo chafalira m’dzikoli?
4 Baibulo limafotokoza momveka bwino chifukwa chomwe chinyengo chafalira kwambiri m’dzikoli. Mtumwi Yohane analemba kuti “dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19) “Woipayo” ndi Satana Mdyerekezi. Ponena za Satana, Yesu anati: “Sanaima m’choonadi, pakuti mwa iye mulibe choonadi. Pamene alankhula bodza, alankhula za mwini wake; pakuti ali wabodza, ndi atate wake wa bodza.” Motero, kodi n’zodabwitsa kuti dzikoli likusonyeza mzimu, makhalidwe ndiponso njira zachinyengo za wolamulira wake?—Yohane 8:44; 14:30; Aefeso 2:1-3.
5. Kodi Satana walimbikitsa motani zochita zake zachinyengo m’masiku otsiriza ano, ndipo kwenikweni iye akufuna ndani?
5 M’masiku otsiriza ano, Satana walimbikitsa zochita zake. Iye anaponyedwa padziko lapansi. Akudziŵa kuti yam’tsalira nthaŵi yochepa, ndipo ali ndi “udani waukulu.” Pofunitsitsa kuwononga anthu ambiri momwe angathere, iye ‘akunyenga dziko lonse.’ (Chivumbulutso 12:9, 12) Sikuti Satana amanyenga anthu mwa apa ndi apo. Ndi nkhakamira pantchito yake yosokeretsa anthu. * Amagwiritsa ntchito njira iliyonse yonyenga yomwe ali nayo, kuphatikizapo ukamberembere ndiponso kusakhulupirika, n’cholinga chochititsa khungu maganizo a anthu osakhulupirira ndi kuwapangitsa kutalikirana ndi Mulungu. (2 Akorinto 4:4) Katswiri wachinyengoyu akufunitsitsa atalikwira anthu omwe akulambira Mulungu “mumzimu ndi m’choonadi.” (Yohane 4:24; 1 Petro 5:8) Osaiwala kuti Satana, kwenikweni, ananena kuti: ‘Ndingathe kuchotsa munthu aliyense m’manja mwa Mulungu.’ (Yobu 1:9-12) Tiyeni tione zina mwa “njira zachinyengo” za Satana ndiponso mmene tingazipeŵere.—Aefeso 6:11, Jewish New Testament.
Peŵani Kunyengedwa ndi Ampatuko
6, 7. (a) Kodi anthu ampatuko anganene kuti amachitanji? (b) Kodi ndi motani mmene Malemba amasonyezera bwino zolinga za ampatuko?
6 Kwanthaŵi yaitali Satana wakhala akugwiritsa ntchito ampatuko pofuna kunyengerera atumiki a Mulungu. (Mateyu 13:36-39) Ampatuko angathe kunena kuti amalambira Yehova ndiponso kuti amakhulupirira Baibulo, koma amakana gulu lake looneka ndi maso. Ena amafika mpaka potsatira ziphunzitso zonyozetsa Mulungu za ‘Babulo Wamkulu,’ yemwe ndi ufumu wadziko lonse wa chipembedzo chonyenga. (Chivumbulutso 17:5; 2 Petro 2:19-22) Mouziridwa ndi Mulungu, olemba Baibulo anagwiritsa ntchito mawu amphamvu posonyeza poyera zolinga ndiponso njira zomwe ampatuko amagwiritsa ntchito.
7 Kodi cholinga cha ampatuko n’chiyani? Ambiri saupeza mtima kungosiya okha chipembedzo chomwe mwina panthaŵi ina ankaona kuti ndi choona. Nthaŵi zambiri, amafuna kuchoka limodzi ndi anthu ena. M’malo mokafunafuna ndi kupanga ophunzira awo, ampatuko ambiri amafuna ‘kupatutsa ophunzira [kutanthauza ophunzira a Kristu] kuti awatsate.’ (Machitidwe 20:29, 30) Ponena za aphunzitsi onyenga, mtumwi Paulo anapereka chenjezo lofunika kwambiri ili: “Penyani kuti pasakhale wina wakulanda inu ngati chuma.” (Akolose 2:8) Kodi izi sizikufotokoza zimene ampatuko ambiri amachita? Mofanana ndi munthu woba anthu amene amatenga munthu wongodzikhalira n’kupita naye kutali ndi banja lake, ampatuko amafuna mumpingo anthu amene angakhulupirire zomwe iwo akunena, n’cholinga chowachotsa pa gulu lankhosa.
8. Kodi ampatuko amagwiritsa ntchito njira ziti pofuna kukwaniritsa zolinga zawo?
8 Kodi ampatuko amagwiritsa ntchito njira ziti pofuna kukwaniritsa zolinga zawo? Nthaŵi zambiri amaphunzitsa zinthu zopotoka, zinthu zomwe sizoona kwenikweni, komanso mabodza Mateyu 5:11) Otsutsa ankhanza ameneŵa anali oti azidzanena zabodza n’cholinga chonyenga ena. Mtumwi Petro anachenjeza za ampatuko omwe anali kudzagwiritsa ntchito “mawu onyenga,” kufalitsa “ziphunzitso zonyenga” (NW), ndiponso ‘kupotoza Malemba’ mogwirizana ndi zolinga zawo. (2 Petro 2:3, 13; 3:16) N’zomvetsa chisoni kuti ampatuko ‘akumapasula chikhulupiriro cha ena.’—2 Timoteo 2:18.
enieni. Yesu anadziŵa kuti otsatira ake adzavutika ndi anthu ‘owanenera monama zoipa zilizonse.’ (9, 10. (a) Kodi tingapeŵe bwanji kunyengedwa ndi ampatuko? (b) N’chifukwa chiyani sitikhumudwa ngati kamvedwe kathu ka cholinga cha Mulungu kakufunika kusintha?
9 Kodi tingapeŵe bwanji kunyengedwa ndi ampatuko? Mwa kutsatira malangizo a m’Mawu a Mulungu, akuti: “Yang’anirani iwo akuchita zopatutsana ndi zopunthwitsa, kosalingana ndi chiphunzitsocho munachiphunzira inu; ndipo potolokani pa iwo.” (Aroma 16:17) ‘Timapotoloka’ mwa kukaniratu zonena zawo, kaya zomwe anena pakamwa, m’zosindikiza zawo, kapena pa Intaneti. N’chifukwa chiyani timatero? Choyamba, ndi chifukwa chakuti Mawu a Mulungu amatiuza kuti tizitero, ndipo timakhulupirira kuti Yehova amatifunira zabwino nthaŵi zonse.—Yesaya 48:17, 18.
10 Chifukwa chachiŵiri n’chakuti timakonda gulu lomwe latiphunzitsa choonadi chamtengo wapatali, chomwe chimatisiyanitsa kwambiri ndi Babulo Wamkulu. Komanso timazindikira kuti sitidziŵa bwinobwino zolinga zonse za Mulungu; kamvedwe kathu kakhala kakusintha m’zaka zapitazi. Akristu okhulupirika ngofunitsitsa kuyembekezera Yehova pankhani yomveketsa bwino zinthu imeneyi. (Miyambo 4:18) Pamene tikuyembekezera, sitidzasiya gulu lomwe Mulungu akusangalala kuligwiritsira ntchito, chifukwa timaona umboni wokwanira wakuti iye akulidalitsa.—Machitidwe 6:7; 1 Akorinto 3:6.
Peŵani Kudzinyenga Nokha
11. N’chifukwa chiyani anthu opanda ungwiro ali ndi chizoloŵezi chodzinyenga okha?
11 Anthu opanda ungwiro ali ndi chizoloŵezi china chomwe Satana amapezerapo mwayi mwamsanga ndipo chizoloŵezi chimenechi ndicho kudzinyenga okha. “Mtima ndiwo wonyenga koposa, ndi wosachiritsika,” pamatero pa Yeremiya 17:9. Ndipo Yakobo analemba kuti: “Munthu aliyense ayesedwa pamene chilakolako chake cha iye mwini chim’kokera, nichim’nyenga.” (Yakobo 1:14) Ngati mtima wathu wakokedwa, pamenepo ungathe kutinyenga kuchita tchimo, polionetsa ngati losangalatsa ndiponso losaopsa. Malingaliro oterowo ndi onyenga, chifukwa chakuti munthu akachita tchimo amakumana ndi mavuto pamapeto pake.—Aroma 8:6.
12. Kodi ndi njira zotani zimene zingatikope kugwidwa mu msampha wodzinyenga tokha?
12 M’posavuta kukodwa mu msampha wodzinyenga tokha. Mtima wonyenga ungakometse vuto lalikulu la khalidwe lathu kapena ungadzikhululukire tikachita tchimo lalikulu. (1 Samueli 15:13-15, 20, 21) Mtima wathu wosachiritsika ukhozanso kupeza njira zokometsera khalidwe loipa. Taganizani, mwachitsanzo, nkhani ya zosangalatsa. Zosangalatsa zina ndi zabwino ndipo n’zosangalatsadi. Koma, zinthu zambiri zomwe dzikoli limasonyeza, m’mavidiyo ndi m’mapulogalamu a pa TV, ndiponso pa Intaneti, n’zotukwana komanso zachiwerewere. N’zosavuta kuti tikhulupirire kuti tikhoza kuonerera zinthu zoipa popanda vuto lililonse. Ena amafika mpaka ponena kuti, “Chikumbumtima changa sichikunditsutsa, ndiye vuto n’chiyani?” Koma anthu amenewo ‘akudzinyenga okha [ndi malingaliro abodza, NW].’—Yakobo 1:22.
13, 14. (a) N’chitsanzo chiti cha m’Malemba chosonyeza kuti sinthaŵi zonse pamene chikumbumtima chathu chingatitsogolere bwino? (b) Kodi tingapeŵe motani kudzinyenga tokha?
13 Kodi tingatani kuti tipeŵe kudzinyenga tokha? Choyambirira, tifunika kukumbukira kuti chikumbumtima cha munthu sichodalirika nthaŵi zonse. Taganizirani zomwe zinachitikira Machitidwe 9:1, 2) N’kutheka kuti panthaŵiyo chikumbumtima chake sichinkam’tsutsa. Komabe, n’zodziŵikiratu kuti chikumbumtimacho chinali chitasokeretsedwa. “Ndinazichita wosazindikira, wosakhulupirira,” anatero Paulo. (1 Timoteo 1:13) Motero mfundo yokha yakuti chikumbumtima chathu sichikutitsutsa pa zinthu zina zosangalatsa si umboni wakuti tikuchita zolondola. Chikumbumtima chokhacho chomwe chili bwino ndiponso chophunzitsidwa bwino pogwiritsa ntchito Mawu a Mulungu n’chimene chingatitsogolere bwino.
mtumwi Paulo. Asanakhale Mkristu, iye anali kuzunza otsatira a Kristu. (14 Kuti tisadzinyenge tokha, pali mfundo zina zabwino zofunika kumazikumbukira. Dzipendeni mwapemphero. (Salmo 26:2; 2 Akorinto 13:5) Kudzipenda moona mtima kungakuzindikiritseni kuti mukufunika kusintha maganizo kapena mmene mumachitira zinthu. Mverani ena. (Yakobo 1:19) Popeza kuti tingathe kukondera pamene tikudzipenda, ndi bwino kumvera mawu osakondera a Akristu anzathu achikulire. Mukaona kuti mukusankha zochita kapena mukuchita zinthu zomwe okhulupirira anzanu oganiza ndiponso odziŵa bwino zinthu amazikayikira, mungadzifunse kuti, “Kodi n’kutheka kuti chikumbumtima changa sindinachiphunzitse bwino kapena mtima wanga ukundinyenga?” Nthaŵi zonse ŵerengani Baibulo ndiponso mabuku ofotokoza Baibulo. (Salmo 1:2) Kuchita zimenezi kudzakuthandizani kuti maganizo, mtima ndiponso zolinga zanu zizigwirizana ndi mfundo za Mulungu.
Peŵani Mabodza a Satana
15, 16. (a) Pofuna kutinyenga, kodi Satana amagwiritsa ntchito mabodza ati? (b) Kodi tingatani kuti tisanyengedwe ndi mabodza amenewo?
15 Satana amagwiritsa ntchito mabodza osiyanasiyana pofuna kutinyenga. Amafuna kuti tikhulupirire kuti chuma chimapatsa chimwemwe komanso kukhala wokhutira, koma nthaŵi zambiri zimenezi zimakhala bodza lenileni. (Mlaliki 5:10-12) Amafuna kuti tizikhulupirira kuti dziko loipali likhalapobe mpaka muyaya, ngakhale kuti pali umboni woonekeratu wakuti tikukhala ‘m’masiku otsiriza.’ (2 Timoteo 3:1-5) Satana amalimbikitsa mfundo yakuti palibe choopsa chilichonse kukhala moyo wachiwerewere, ngakhale kuti anthu ongofuna zosangalatsa amatuta mavuto nthaŵi zonse. (Agalatiya 6:7) Kodi tingapeŵe motani kunyengedwa ndi mabodza ameneŵa?
16 Phunzirani pa zitsanzo za m’Baibulo. Baibulo lili ndi zitsanzo zochenjeza za anthu amene ananyengedwa ndi mabodza a Satana. Ankakonda chuma, sanalingalire za nthaŵi yomwe analimo, kapena anachita zachiwerewere, ndipo zonsezi zinali ndi zotsatirapo zoipa kwambiri. (Mateyu 19:16-22; 24:36-42; Luka 16:14; 1 Akorinto 10:8-11) Phunzirani pa zitsanzo zamakono. N’zomvetsa chisoni kuti nthaŵi zina Akristu ena amasiya kukhala tcheru ndi kuyamba kukhulupirira kuti akumanidwa zinthu zabwino chifukwa chotumikira Mulungu. Angathe kusiya choonadi pofuna kuti akhale ndi moyo umene anthu amati ndi wosangalatsa. Koma anthu ameneŵa ali “poterera,” chifukwa posachedwapa adzaona zotsatira za khalidwe lawo loipalo. (Salmo 73:18, 19) Ndi bwino kwambiri kutengera phunziro pa zolakwa za ena.—Miyambo 22:3.
17. N’chifukwa chiyani Satana amalimbikitsa bodza lakuti Yehova satikonda ndiponso sationa ngati anthu ofunika?
17 Pali bodza linanso limene Satana waligwiritsa ntchito bwino kwambiri. Ili ndi bodza lakuti Yehova satikonda ndiponso sationa ngati anthu ofunika. Satana wakhala akuphunzira anthu opanda ungwiro kwa zaka zikwi zambiri. Akudziŵa kuti tingafooke mwauzimu ngati talefulidwa. (Miyambo 24:10) Motero amalimbikitsa bodza lakuti Mulungu sationa ngati ofunika. ‘Tikagwetsedwa’ ndi kukhulupirira kuti Yehova satisamalira, tingakopeke kuti ndi bwino kungosiya kum’khulupirira. (2 Akorinto 4:9) Zimenezi n’zomwe Wonyenga wamkuluyu amafuna. Ndiye tingatani kuti tipeŵe kunyengedwa ndi bodza la Satana limeneli?
18. Kodi Baibulo limatitsimikizira motani kuti Yehova amatikonda?
18 Sinkhasinkhani zomwe Baibulo limanena zosonyeza kuti Mulungu amatikonda. Mawu a Mulungu amagwiritsa ntchito mafanizo omveka bwino pofuna kutitsimikizira kuti Yehova amationa ndiponso amatikonda payekhapayekha. Amasunga misozi yanu “m’nsupa” yake Salmo 56:8) Amadziŵa ‘mukasweka mtima’ ndipo amakhala pafupi nanu panthaŵi zoterozo. (Salmo 34:18) Amadziŵa chilichonse chokhudza inu, kuphatikizapo kuchuluka kwa ‘tsitsi lonse la m’mutu mwanu.’ (Mateyu 10:29-31) Koposa zonsezi, Mulungu “anapatsa Mwana wake wobadwa yekha” chifukwa cha inu. (Yohane 3:16; Agalatiya 2:20) Nthaŵi zina zingakuvuteni kukhulupirira kuti malemba ngati ameneŵa amagwira ntchito pa inuyo panokha. Koma tiyenera kukhulupirira mawu a Yehova. Amafuna kuti tizikhulupirira kuti amatikonda, osati monga gulu basi koma monga munthu payekhapayekha.
kutanthauza kuti amaona ndipo amakumbukira misozi yomwe mumakhetsa pamene mukuyesetsa kuti mukhale wokhulupirika. (19, 20. (a) N’chifukwa chiyani mufunika kuzindikira ndi kukana bodza la Satana lakuti Yehova sakukondani? (b) Kodi woyang’anira woyendayenda wina wathandiza motani anthu otaya mtima?
19 Zindikirani bodza ndi kulikana. Mukadziŵa kuti winawake akukunamizani, mungathe kudziteteza kuti musanyengedwe. Momwemonso, kungodziŵa kokhako kuti Satana amafuna kuti mukhulupirire bodza lakuti Yehova sakukondani, kungakhale kothandiza kwambiri. Malinga ndi zimene inanena nkhani ya mu Nsanja ya Olonda ina yomwe inachenjeza za njira za Satana, Mkristu wina anati: “Sindinkadziŵa kuti Satana amafuna kugwiritsa ntchito malingaliro anga kuti andilefule. Kudziŵa zimenezi kumandipatsa mphamvu zolimbanirana ndi malingaliro ameneŵa.”
20 Taonani chokumana nacho cha woyang’anira woyendayenda m’dziko lina la ku South America. Akamachita ulendo waubusa kwa okhulupirira anzake omwe ataya mtima, nthaŵi zambiri amawafunsa kuti, ‘Kodi mumakhulupirira Utatu?’ Munthu wolefulidwayo nthaŵi zambiri amayankha kuti, ‘Ayi,’ pozindikira kuti limeneli ndi limodzi mwa mabodza a Satana. Kenako mkulu woyendayendayo amafunsa kuti, ‘Kodi mumakhulupirira moto wa helo?’ Apa amayankhanso kuti, ‘Ayi!’ Akatero, mkulu woyendayendayo amawauza kuti palinso bodza lina la Satana lomwe nthaŵi zambiri silidziŵika kuti ndi bodza. Amapita nawo patsamba 249, ndime 21, ya buku lakuti Yandikirani kwa Yehova, * imene imasonyeza bodza lakuti Yehova satikonda monga munthu payekhapayekha. Woyang’anira woyendayendayu akuti pamakhala zotsatira zabwino pothandiza anthu olefulidwa mwanjirayi, imene imathandiza olefulidwawo kuzindikira ndi kukana bodza limeneli la Satana.
Dzitchinjirizeni ku Chinyengo
21, 22. N’chifukwa chiyani sitili mu mdima pankhani ya njira zachinyengo za Satana, ndipo titsimikize mtima kuchitanji?
21 M’chigawo chomaliza chino cha masiku otsiriza, tiyembekezere kuti Satana apitiriza kufalitsa mabodza ambiri ndiponso kuchita zachinyengo zankhaninkhani. Tikuyamikira kuti Yehova sanatisiye mu mdima pankhani ya njira zachinyengo za Satana. Baibulo pamodzi ndi mabuku ofotokoza Baibulo a “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” amasonyeza poyera zochita zoipa za Mdyerekezi. (Mateyu 24:45) Kulandiriratu chenjezo n’kothandiza kwambiri kuti tithane ndi vuto likafika.—2 Akorinto 2:11.
22 Ndiyetu tiyeni tipitirize kupeŵa zonena za ampatuko. Tiyeni tikhale otsimikiza kupeŵa msampha wosaoneka wa kudzinyenga tokha. Ndipo tiyeni tizindikire ndi kukana mabodza onse a Satana. Mwa kuchita zimenezi, tidzatchinjiriza ubwenzi wathu ndi “Mulungu wa choonadi,” amene amanyansidwa ndi chinyengo.—Salmo 31:5; Miyambo 3:32.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 5 Pamfundo ya kapangidwe ka mneni amene anam’tembenuza kuti “wonyenga” pa Chivumbulutso 12:9, buku lina linanena kuti “amasonyeza ntchito yopitirira yomwe yakhala chizoloŵezi.”
^ ndime 20 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
Kodi Mukukumbukira?
• N’chifukwa chiyani chinyengo chafala kwambiri m’dzikoli masiku ano?
• Kodi tingapeŵe motani kuyengedwa ndi ampatuko?
• Kodi tingapeŵe motani chizoloŵezi chilichonse chodzinyenga tokha?
• Kodi tingapeŵe motani kunyengedwa ndi mabodza a Satana?
[Mafunso]
[Chithunzi patsamba 17]
Musadzinyenge pankhani ya zosangalatsa
[Zithunzi patsamba 18]
Popeŵa kudzinyenga nokha, dzipendeni mwapemphero, mverani ena, ndiponso ŵerengani Mawu a Mulungu nthaŵi zonse