Atumiki a Mulungu Ali Ngati Mitengo Motani?
Atumiki a Mulungu Ali Ngati Mitengo Motani?
PONENA za munthu amene amasangalala ndi mfundo za m’Baibulo komanso amazigwiritsa ntchito pamoyo wake, wamasalmo anati: “Akunga mtengo wooka pa mitsinje ya madzi; wakupatsa chipatso chake pa nyengo yake, tsamba lake lomwe losafota; ndipo zonse azichita apindula nazo.” (Salmo 1:1-3) N’chifukwa chiyani kuyerekezera kumeneku n’koyenera?
Mitengo imatha kukhala nthaŵi yaitali zedi. Mwachitsanzo, mitengo ina ya azitona ku dera la Mediterranean akuti ili ndi zaka pakati pa 1,000 ndi 2,000. Chimodzimodzinso mitengo ya malambe m’mayiko apakati pa Africa imakhala zaka zambiri, ndipo anthu amakhulupirira kuti mtengo wa bristlecone pine ku California wakhala zaka pafupifupi 4,600. M’nkhalango, nthaŵi zambiri mitengo yokhwima imathandiza zinthu zimene zili pafupi ndi mitengoyo. Mwachitsanzo, timitengo tanthete timatetezeka mu mthunzi wa mitengo italiitali, ndipo masamba amene amagwa m’mitengoyo amapangitsa dothi kukhala lachonde.
Mitengo yaitali kwambiri padziko lapansi pano nthaŵi zambiri imakulira limodzi m’nkhalango, ndipo mtengo uliwonse umathandiza unzake. Popeza mizu yake imatha kukhala yopiringidzana, mitengo ingapo pamodzi ingakhalebe yolimba kutawomba mphepo yamkuntho kusiyana ndi mtengo womera pawokhawokha muudzu. Mizu yambiri imathandizanso mtengo kutenga madzi ndi chakudya chokwanira mu dothi. Nthaŵi zina, mizu ingaloŵe pansi kuposa kutalika kwa mtengowo, kapena mizu ingatambalale kuposa kumene nthambi za mtengowo zafika.
Mtumwi Paulo ayenera kuti anali kunena za mtengo pamene anafotokoza kuti Akristu ayenera ‘kuyenda mwa Iye [Kristu], ozika mizu ndi omangirika mwa Iye, ndi okhazikika m’chikhulupiriro.’ (Akolose 2:6, 7) Ndithudi, Akristu angakhale olimba m’chikhulupiriro ngati ali ozika mizu kwambiri mwa Kristu.—1 Petro 2:21.
Ndi motaninso mmene atumiki a Mulungu alili ngati mitengo? Chabwino, monga momwe mitengo imene ili pamodzi imathandizidwira ndi mitengo imene ili nayo pafupi, chotero onse amene amakhala pafupi kwambiri ndi mpingo wachikristu amathandizidwa ndi okhulupirira anzawo. (Agalatiya 6:2) Akristu okhulupirika ndi okhwima mwauzimu amene ali ndi mizu yauzimu yaitali amathandiza okhulupirira atsopano kukhala olimba m’chikhulupiriro, ngakhale pamene akukumana ndi chitsutso changati mphepo ya mkuntho. (Aroma 1:11, 12) Akristu atsopano angakule ndi kutetezeka mu “mthunzi” wa atumiki a Mulungu odziŵa zambiri. (Aroma 15:1) Ndipo anthu onse a mu mpingo wachikristu wapadziko lonse amapindula ndi chakudya chauzimu chopatsa mphamvu chimene “mitengo [yaikulu, NW] ya chilungamo” yomwe ndi otsalira odzozedwa imapereka.—Yesaya 61:3.
N’zosangalatsa kwambiri kuti atumiki onse a Mulungu akuyembekezera kudzaona lonjezo la pa Yesaya 65:22 likukwaniritsidwa. Lonjezolo limati: “Monga masiku a mtengo adzakhala masiku a anthu anga.”
[Mawu a Chithunzi patsamba 28]
Godo-Foto