Kudziŵa Chilombo ndi Chizindikiro Chake
Kudziŵa Chilombo ndi Chizindikiro Chake
KODI mumakonda kufufuza mayankho a mafunso oimitsa mutu? Kuti muthe kutero, mumaona mawu olondolera kuti mupeze mayankhowo. M’Mawu ake ouziridwa, Mulungu anapereka mawu otilondolera kuti tidziŵe tanthauzo la chiŵerengero cha 666, dzina, kapena kuti chizindikiro cha chilombo cha m’buku la Chivumbulutso chaputala 13.
M’nkhaniyi, tiona mfundo zikuluzikulu zinayi—mawu ofunika kwambiri olondolera—zomwe zitidziŵitse tanthauzo la chizindikiro cha chilombo. Tiona (1) mmene mayina a m’Baibulo ankasankhidwira nthaŵi zina, (2) kodi chilombo n’chiyani, (3) zimene zikutanthauza ponena kuti 666 ndi ‘chiŵerengero cha munthu,’ ndi (4) tanthauzo la nambala ya 6 ndiponso chifukwa chake yalembedwa mobwereza katatu, komwe ndi 600 kuphatikizapo 60 n’kuphatikizaponso 6, kapena kuti 666.—Chivumbulutso 13:18.
Mayina a M’Baibulo Si Zizindikiro Chabe
Mayina ambiri a m’Baibulo ali ndi matanthauzo apadera, makamaka mayina operekedwa ndi Mulungu. Mwachitsanzo, chifukwa chakuti Abramu anali kudzakhala kholo la mitundu yambiri, Mulungu anasintha dzina lake kukhala Abrahamu, kutanthauza kuti Tate wa Namtindi. (Genesis 17:5) Mulungu anauza Yosefe ndi Mariya kuti mwana amene Mariya adzabereke adzamutche Yesu, dzina lotanthauza kuti “Yehova Ndiye Chipulumutso.” (Mateyu 1:21; Luka 1:31) Mogwirizana ndi dzina latanthauzo limenelo, mwa utumiki ndi imfa ya nsembe ya Yesu, Yehova anapangitsa kuti kukhale kotheka kuti tipulumutsidwe.—Yohane 3:16.
Mogwirizana ndi zimenezi, dzina lopatsidwa ndi Mulungu lakuti 666 liyenera kuimira zomwe Mulungu amaona kuti ndi makhalidwe akuluakulu a chilombo. N’zachidziŵikire kuti tifunika kudziŵa chilombocho ndiponso zochita zake kuti tithe kumvetsa makhalidwe amenewo.
Tanthauzo la Chilombo
Buku la m’Baibulo la Danieli limafotokoza zambiri zokhudza tanthauzo la zilombo zophiphiritsira. Chaputala 7 chimafotokoza mwatsatanetsatane za “zilombo zazikulu zinayi”—mkango, chimbalangondo, nyalugwe, ndi chilombo china choopsa kwambiri cha mano akuluakulu achitsulo. (Danieli 7:2-7) Danieli akutiuza kuti zilombo zimenezi zikuimira “mafumu,” kapena maufumu andale, olamulira madera akuluakulu moloŵana m’malo.—Danieli 7:17, 23.
Pankhani ya chilombo cha pa Chivumbulutso 13:1, 2, buku lakuti The Interpreter’s Dictionary of the Bible limanena kuti chilombochi “chatenga makhalidwe onse a zilombo zinayi za m’masomphenya a Danieli . . . Motero, chilombo choyamba chimenechi [cha m’buku la Chivumbulutso] chikuimira mphamvu zonse za maulamuliro onse andale otsutsana ndi Mulungu padziko lapansili.” Lemba la Chivumbulutso 13:7 likuphera mphongo mfundo imeneyi. Ponena za chilombochi lembali limati: ‘Anachipatsa ulamuliro wa pa fuko lililonse, ndi anthu, ndi manenedwe, ndi mitundu.’ *
N’chifukwa chiyani Baibulo limagwiritsa ntchito Mlaliki 8:9) Chifukwa chachiŵiri n’chakuti “chinjoka [Satana] chinam’patsa iye [chilombo] mphamvu yake, ndi mpando wachifumu wake, ndi ulamuliro waukulu.” (Chivumbulutso 12:9; 13:2) Motero, Mdyerekezi ndi amene anayambitsa ulamuliro wa anthu, ndipo n’chifukwa chake maulamulirowo amasonyeza makhalidwe a zilombo monga njoka.—Yohane 8:44; Aefeso 6:12.
zilombo monga zizindikiro za ulamuliro wa anthu? Pali zifukwa zosachepera ziŵiri. Choyamba ndi chifukwa cha mbiri yosakaza miyoyo ya anthu yomwe maboma apanga m’zaka mazanamazana zapitazi, ndipo zimenezi n’zofanana ndi zimene zilombo zingachite. Will ndi Ariel Durant, omwe ndi akatswiri a mbiri yakale, analemba kuti: “Nkhondo ndi chimodzi mwa zinthu zimene zakhala zikuchitika nthaŵi zonse m’mbiri, ndipo sizinachepe chifukwa cha kutukuka kwa anthu kapena demokalase.” Ndi zoonadi kuti “wina apweteka mnzake pom’lamulira.” (Koma izi sizikutanthauza kuti munthu aliyense wolamulira amatsogoleredwa ndi Satana mwachindunji. Ndipotu n’zoona kuti pa zinthu zina maboma a anthu amakhala “mtumiki wa Mulungu,” chifukwa amathandiza kuti anthu akhale mwabata, zomwe sizingachitike popanda maboma. Ndipo atsogoleri ena ateteza mfundo zikuluzikulu za ufulu wa munthu, kuphatikizapo ufulu wa kulambira koona—zimene Satana safuna. (Aroma 13:3, 4; Ezara 7:11-27; Machitidwe 13:7) Komabe, chifukwa cha mphamvu za Mdyerekezi, palibe munthu kapena bungwe limene lathandiza anthu kukhala mwamtendere ndiponso mwabata kwamuyaya. *—Yohane 12:31.
‘Chiŵerengero cha Munthu’
Njira yachitatu yopezera tanthauzo la 666 yagona pamfundo yonena kuti nambalayi ndi ‘chiŵerengero cha munthu.’ Mawu ameneŵa sangakhale akunena za munthu mmodzi, chifukwa chakuti Satana—osati munthu aliyense—ndiye akulamulira chilombochi. (Luka 4:5, 6; 1 Yohane 5:19; Chivumbulutso 13:2, 18) M’malomwake, mfundo yakuti chilombochi chili ndi chiŵerengero kapena chizindikiro cha munthu, ikusonyeza kuti chilombochi chikuimira anthu osati ziwanda, ndipo chifukwa cha zimenezi chimasonyeza makhalidwe ena a anthu. Kodi angakhale makhalidwe otani? Baibulo limayankha funsoli mwa kunena kuti: “[Anthu] onse anachimwa, napereŵera pa ulemerero wa Mulungu.” (Aroma 3:23) Motero, kunena kuti chilombochi chili ndi ‘chiŵerengero cha munthu,’ kukusonyeza kuti maboma amasonyeza kulephera kwa anthu, chizindikiro cha uchimo ndi kupanda ungwiro.
Mbiri ili ndi umboni wosonyeza kuti zimenezi n’zoona. “Moyo uliwonse wotukuka kwambiri womwe anthu anakhalapo nawo unatha,” anatero Henry Kissinger, nduna yakale ya za m’dziko ku Yeremiya 10:23.
United States. “Mbiri ili ndi nkhani zochuluka za zinthu zimene zinalephereka, zolinga zomwe sizinakwaniritsidwe . . . Choncho, monga katswiri wa mbiri yakale, munthu ayenera kudziŵa kuti tsoka n’losapeŵeka.” Mfundo yosabisa mawu ya Kissinger imeneyi ikuphera mphongo mfundo iyi ya m’Baibulo: “Njira ya munthu siri mwa iye mwini; sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.”—Popeza tsopano tachidziŵa chilombochi ndipo taona mmene Mulungu amachionera, tsopano tingayambe kuona mbali yomaliza ya nkhani yathuyi—nambala ya sikisi ndi chifukwa chake yalembedwa mobwereza katatu—kukhala 666, kapena kuti 600 kuphatikizapo 60 n’kudzaphatikizaponso 6.
N’chifukwa Chiyani Sikisi Am’bwereza Katatu
M’Malemba, manambala ena ali ndi matanthauzo apadera. Mwachitsanzo, seveni amam’gwiritsa ntchito kaŵirikaŵiri kuimira chinthu chokwanira bwino, kapena changwiro, m’maso mwa Mulungu. Mwachitsanzo, mlungu umene Mulungu anagwira ntchito yolenga uli ndi ‘masiku’ kapena kuti nthaŵi zazitali seveni, pamene Mulungu anakwaniritsa cholinga chake chokhudza kulenga dziko lapansi. (Genesis 1:3–2:3) “Mawu” a Mulungu ali ngati siliva ‘woyeretsedwa kasanu ndi kaŵiri,’ motero ndi oyengedwa mwangwiro. (Salmo 12:6; Miyambo 30:5, 6) Namani wakhate anauzidwa kuti akasambe mu mtsinje wa Yordano maulendo asanu ndi aŵiri, ndipo atatero anachiriratu.—2 Mafumu 5:10, 14.
Sikisi akupereŵera ndi wani kuti akwane seveni. Kodi sangakhale chizindikiro choyenera cha chinthu chopanda ungwiro, kapena chomwe chili ndi vuto, m’maso mwa Mulungu? Inde, ndi woyenerera! (1 Mbiri 20:6, 7) Komanso, kubwereza sikisi maulendo atatu, kukhala 666, kukutsindika kupanda ungwiro kumeneko. Umboni wosonyeza kuti imeneyi ndi mfundo yolondola ndi wakuti 666 ndi ‘chiŵerengero cha munthu,’ monga momwe taonera muja. Motero zomwe chilombochi chachita m’mbuyomu, ‘chiŵerengero [chake] cha munthu,’ ndiponso nambala ya 666 zonsezi zikusonyeza mfundo imodzi yoona—chilibiretu ungwiro ndiponso chalephera m’maso mwa Yehova.
Kuona zolephera za chilombochi kukutikumbutsa zomwe zinanenedwa zokhudza mfumu Belisazara ya Babulo wakale. Kudzera mwa Danieli, Yehova anauza mfumuyi kuti: “Mwayesedwa pamiyeso, nimupezeka mwapereŵera.” Usiku womwewo Belisazara anaphedwa, ndipo ufumu wamphamvu wa a Babulo unagwa. (Danieli 5:27, 30) N’chimodzimodzinso ndi chiweruzo cha Mulungu kwa chilombo chandale ndiponso anthu omwe ali ndi chizindikiro chake. Chiweruzocho chikusonyeza mapeto a chilombocho pamodzi ndi ochikhalira mbali. Koma panthaŵiyi, sikuti Mulungu adzangowononga gulu limodzi lokha landale koma adzawononga chilichonse cha ulamuliro wa munthu. (Danieli 2:44; Chivumbulutso 19:19, 20) Ndiye m’pofunika kwambiri kuti tipeŵe chizindikiro choopsa kwambiri cha chilombochi!
Tanthauzo la Chizindikiro
Buku la Chivumbulutso litangotha kutchula za nambala ya 666, linatchula anthu 144,000 otsatira Mwana Wankhosa, Yesu Kristu, omwe analembedwa pamphumi zawo dzina la Yesu pamodzi ndi dzina la Luka 20:25; Chivumbulutso 13:4, 8; 14:1) Motani? Mwa kupereka ulemu wolambira ku maboma andale, zizindikiro zake, ndiponso asilikali ake, ndipo amadalira zimenezi kuti n’zimene zidzawapatsa chiyembekezo ndiponso chipulumutso. Kulambira kulikonse komwe amachitira Mulungu woona ndi kwapakamwa chabe.
Atate wake, Yehova. Mayina ameneŵa akusonyeza kuti anthu omwe alembedwawo ndi a Yehova ndi Mwana wake, ndipo anthuwo amawachitira umboni monyadira. N’chimodzimodzinso ndi anthu amene ali ndi chizindikiro cha chilombo, iwo amasonyeza poyera kuti akutumikira chilombocho. Motero chizindikiro, kaya chili padzanja lamanja kapena pamphumi, ndi mkuluwiko wa chizindikiro chosonyeza kuti munthuyo ali pambuyo pa dongosolo landale la dzikoli lomwe likuchita zinthu monga chilombo ndipo akuchita zinthu molilambira. Anthu omwe ali ndi chizindikiro amapatsa “Kaisara” zinthu zomwe ndi za Mulungu. (Mosiyana ndi zimenezi, Baibulo limatilimbikitsa kuti: “Musamakhulupirira zinduna, kapena mwana wa munthu, amene mulibe chipulumutso mwa iye. Mpweya wake uchoka, abwerera kumka ku nthaka yake; tsiku lomwelo zotsimikiza mtima zake zitayika.” (Salmo 146:3, 4) Anthu olabadira langizo lanzeru limeneli sasokonezeka maganizo maboma akalephera kukwaniritsa malonjezo awo kapena atsogoleri achikoka akalephera kupeza mipando yapamwamba.—Miyambo 1:33.
Izi sizikutanthauza kuti Akristu oona amangokhala, osachita chilichonse pa mavuto a anthu. Mosiyana ndi zimenezi, iwo akulengeza za boma lomwe lidzathetsa mavuto a anthu—Ufumu wa Mulungu, womwe iwo amaimira.—Mateyu 24:14.
Zinthu Zidzawayendera Bwino Anthu mu Ufumu wa Mulungu Wokha
Yesu ali padziko lapansi pano, mfundo yaikulu ya ulaliki wake inali Ufumu wa Mulungu. (Luka 4:43) M’pemphero lake lachitsanzo, lomwe nthaŵi zina limatchedwanso Pemphero la Ambuye, Yesu anaphunzitsa otsatira ake kupempherera kuti Ufumu umenewo udze ndi kuti chifuno cha Mulungu chichitike padziko lapansi pano. (Mateyu 6:9, 10) Ufumuwu ndi boma lomwe lidzalamulire dziko lonse, osati kuchokera ku likulu linalake la padziko lapansi, koma kuchokera kumwamba. Motero, Yesu anautcha kuti “Ufumu wa Kumwamba.”—Mateyu 11:12.
Kodi ndani ali woyenereradi kukhala Mfumu ya Ufumu umenewu kuposa Yesu Kristu, munthu amene anafera anthu ake a m’tsogolo? (Yesaya 9:6, 7; Yohane 3:16) Posachedwapa Wolamulira wangwiro ameneyu, yemwe tsopano ndi munthu wamphamvu wauzimu, adzaponya chilombo, mafumu ake, ndiponso asilikali ake “m’nyanja yamoto yakutentha ndi sulfure,” chizindikiro chakuti adzawonongedweratu. Komatu si zokhazi. Yesu adzawononganso Satana, ntchito imene palibe munthu angachite.—Chivumbulutso 11:15; 19:16, 19-21; 20:2, 10.
Ufumu wa Mulungu udzabweretsa mtendere kwa anthu ake onse omvera. (Salmo 37:11, 29; 46:8, 9) Ngakhale chisoni, zopweteka, ndi imfa sizidzakhalaponso. Ndi chiyembekezo chabwino kwambiritu chimenechi chomwe anthu okana chizindikiro cha chilombo ali nacho!—Chivumbulutso 21:3, 4.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 9 Kuti mumve kufotokoza kwatsatanetsatane kwa mavesi ameneŵa, onani chaputala 28 cha buku lakuti Revelation—Its Grand Climax At Hand!, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
^ ndime 11 Ngakhale kuti Akristu oona amadziŵa kuti ulamuliro wa anthu nthaŵi zambiri umakhala ngati chilombo, iwo amagonjera “maulamuliro aakulu” a maboma malinga ndi malangizo a m’Baibulo. (Aroma 13:1) Koma maulamuliro ameneŵa akalamula Akristuwo kuchita zinthu zotsutsana ndi lamulo la Mulungu, iwo ‘amamvera Mulungu koposa anthu.’—Machitidwe 5:29.
[Bokosi patsamba 5]
Njira Zodziŵira Tanthauzo la 666
1. Nthaŵi zambiri mayina a m’Baibulo amasonyeza kenakake kokhudza khalidwe kapena moyo wa mwinidzinalo, ngati momwe zilili ndi mayina monga Abrahamu, Yesu, ndiponso anthu ena ambiri. N’chimodzimodzinso ndi dzina la chilombo, nalo likuimira makhalidwe a chilombochi.
2. M’buku la m’Baibulo la Danieli, zilombo zosiyanasiyana zimaimira maufumu a anthu oloŵana m’malo. Chilombo cha pa Chivumbulutso 13:1, 2, chomwe chili ndi makhalidwe a zilombo zosiyanasiyana, chikuimira dongosolo landale lapadziko lonse, lomwe limapatsidwa mphamvu ndi Satana ndipo ndi iye akuliyendetsa.
3. Chilombochi chili ndi ‘chiŵerengero cha munthu,’ zomwe zikusonyeza kuti chikuimira anthu osati ziwanda. Motero chimasonyeza kulephera kwa anthu chifukwa cha uchimo ndi kupanda ungwiro.
4. M’maso mwa Mulungu, nambala ya sikisi imasonyeza kupanda ungwiro popeza kuti imapereŵera pa nambala ya seveni, yomwe m’Baibulo imasonyeza kukwanira, kapena ungwiro. Chilembo cha 666 chikutsindika kupereŵera kumeneko mwa kubwereza nambalayo katatu.
[Zithunzi patsamba 6]
Ulamuliro wa anthu walephera, ndipo ukuimiridwa bwino ndi nambala ya 666
[Mawu a Chithunzi]
Starving child: UNITED NATIONS/Photo by F. GRIFFING
[Zithunzi patsamba 7]
Yesu Kristu adzabweretsa ulamuliro wangwiro padziko lapansi