Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
• Kodi tingamvetse chisoni motani mzimu woyera wa Mulungu popeza mzimuwo si munthu?
Mtumwi Paulo ndi amene analemba kuti: “Musamvetse chisoni Mzimu Woyera wa Mulungu.” (Aefeso 4:30) Ena amatenga mawu ameneŵa monga chizindikiro chakuti mzimu woyera ndi munthu. Koma mabuku ofalitsidwa ndi “mdindo wokhulupirika” akhala akupereka mobwerezabwereza umboni wa m’Malemba ndiponso wa m’mbiri wosonyeza kuti Akristu oyambirira sankaona mzimu woyera monga munthu kapenanso monga mulungu wofanana ndi Wam’mwambamwamba amene ali mbali ya chimene amati Utatu. * (Luka 12:42) Motero Paulo sankanena za mzimu woyera wa Mulungu ngati kuti ndi munthu.
Mzimu woyera wa Mulungu ndi mphamvu yosaoneka yomwe iye amagwiritsa ntchito. (Genesis 1:2) Yesu anali kudzabatiza “ndi Mzimu Woyera,” monga momwe Yohane ankabatizira ndi madzi. (Luka 3:16) Pa Pentekoste m’chaka cha 33 Kristu Atabwera, ophunzira pafupifupi 120 “anadzazidwa . . . ndi Mzimu Woyera.” Mwachionekere iwo sanadzazidwe ndi munthu. (Machitidwe 1:5, 8; 2:4, 33) Odzozedwa amenewo anayamba kuyembekezera kupita kumwamba, ndipo mzimu wa Mulungu unawatsogolera kukhala okhulupirika. (Aroma 8:14-17; 2 Akorinto 1:22) Mzimuwo unawapatsa makhalidwe okondweretsa Mulungu ndi kuwathandiza kupeŵa “ntchito za thupi” zauchimo zimene zikanawapangitsa kuti asayanjidwe ndi Mulungu.—Agalatiya 5:19-25.
Ngati ndife atumiki a Mulungu omwe akuyembekezera kudzakhala padziko lapansi, ndiye kuti sitinadzozedwe ndi mzimu woyera. Komabe, tingathe kukhala ndi mzimu wa Mulungu wosasiyana kuchuluka kwake ndi mzimu umene anthu oyembekezera kupita kumwamba ali nawo. Motero nafenso tingathe kumvetsa chisoni mzimu. Komano, kodi tingachite zimenezi motani?
Ngati tinyalanyaza malangizo a m’Malemba omwe analembedwa motsogozedwa ndi mzimu woyera, tingathe kuyamba kukhala ndi makhalidwe omwe angatichititse kuti tichimwire mzimu mwadala, kuti tisayanjidwenso ndi Yehova, ndi kuti tidzawonongedwe m’tsogolo. (Mateyu 12:31, 32) Mwina sitinayambe kuchita machimo akuluakulu panopa, koma zingatheke kuti tayamba kuchita zinthu zinazake, zomwe mapeto ake zingatichititse zinthu zosemphana ndi zomwe mzimu umatsogolera. Tingamvetse chisoni mzimu woyera ngati zinthu zafika pamenepo.
Choncho, kodi tingatani kuti tisamvetse chisoni mzimu wa Mulungu? Tifunika kusamala ndi maganizo athu ndi zochita zathu. M’chaputala 4
cha kalata yomwe mtumwi Paulo analembera Aefeso, iye analankhula za kupeŵa chizoloŵezi cholankhula zabodza, chosunga mkwiyo, chokhala waulesi, ndi cholankhula zosayenera. Ngati tavala “munthu watsopano” koma n’kulola kubwerera ku makhalidwe ameneŵa, kodi tingakhale tikuchita chiyani? Tingakhale tikuchita zinthu zotsutsana ndi malangizo a m’Mawu a Mulungu, Baibulo, omwe ndi ouziridwa ndi mzimu. Mwa kuchita zimenezi, tingakhale tikumvetsa chisoni mzimu woyera.Mu Aefeso chaputala 5, timaŵerenga malangizo a Paulo olimbikitsa kupeŵa chilakolako chochita dama. Mtumwiyu analimbikitsanso okhulupirira anzake kuti apeŵe makhalidwe onyansa ndiponso nthabwala zotukwana. Ngati sitikufuna kumvetsa chisoni mzimu woyera wa Mulungu, tifunika kumakumbukira malangizo ameneŵa pamene tikusankha zinthu zosangalatsa. Kodi pali chifukwa chochitira chidwi ndi zinthu zimenezi mwa kuzitchula, kuziŵerenga, ndiponso kuzionera pa wailesi ya kanema kapena m’njira ina iliyonse?
Inde, pali njira zinanso zomwe tingamvetsere chisoni mzimu. Mzimu wa Yehova umalimbikitsa umodzi mu mpingo. Koma tiyerekeze kuti ife tikufalitsa miseche kapena kulimbikitsa magaŵano mu mpingo. Kodi sitingakhale tikuchita zotsutsana ndi zomwe mzimu umalimbikitsa, zoti pakhale umodzi? Tinganene kuti, tingakhale tikumvetsa chisoni mzimu woyera, mofanana ndi anthu omwe anachititsa magaŵano mu mpingo wa ku Korinto. (1 Akorinto 1:10; 3:1-4, 16, 17) Tingakhalenso tikumvetsa chisoni mzimu ngati tipeputsa mwadala amuna oikidwa ndi mzimu mu mpingo.—Machitidwe 20:28; Yuda 8.
Motero, n’zoonekeratu kuti n’chinthu chanzeru kupenda maganizo ndi zochita zathu kuti tione ngati zikugwirizana ndi zimene timadziŵa kuti n’zimene mzimu woyera umalimbikitsa monga momwe zinalembedwera m’Baibulo ndiponso zimasonyezedwera mu mpingo wachikristu. Komanso, tiyeni ‘tizipemphera mu Mzimu Woyera’ nthaŵi zonse, tizitsatira zomwe umalimbikitsa ndiponso nthaŵi zonse tizichita zinthu mogwirizana ndi zomwe zinanenedwa m’Mawu ouziridwa a Mulungu. (Yuda 20) Tiyeni titsimikize mtima kusamvetsa chisoni mzimu, koma uzititsogolera nthaŵi zonse kuti dzina loyera la Yehova lilemekezedwe.
• Yesu Kristu anayerekezera kuvutika kwa munthu wolemera poloŵa Ufumu ndi ngamila imene ikuyesa kuloŵa m’diso la singano. Kodi Yesu anali kunena za ngamila yeniyeni ndiponso singano yeniyeni?
Malemba atatu omwe anagwira mawu a Yesu ameneŵa n’ngosasiyana kwenikweni. Malinga ndi zimene Mateyu analemba, Yesu anati: “N’kwapafupi kuti ngamila ipyole diso la singano, koposa mwini chuma kuloŵa Ufumu wa Kumwamba.” (Mateyu 19:24) Mofanana ndi lembali, timaŵerenga pa Marko 10:25 kuti: “N’kwapafupi kuti ngamila ipyole diso la singano koposa kuti mwini chuma aloŵe mu Ufumu wa Mulungu.” Ndipo Luka 18:25 amagwira mawu a Yesu kuti: “N’kwapafupi kwa ngamila apyole diso la singano koma kwa munthu mwinichuma, kuloŵa Ufumu wa Mulungu n’kwapatali.”
Mabuku ena amati “diso la singano” limene anatchulali linali geti laling’ono pa limodzi mwa mageti akuluakulu a Yerusalemu. Geti lalikululo likatsekedwa usiku, anthu ankatha kutsegula geti laling’onolo. Anthu ena amakhulupirira kuti ngamila inkatha kudutsa pa geti limenelo. Kodi izi ndi zomwe Yesu anali kutanthauza?
Mwachionekere ayi. N’zoonekeratu kuti Yesu anali kunena za singano yeniyeni. Popeza kuti m’derali apezamo singano zachikale za mafupa ndi za zitsulo, ziyenera kuti zimenezi zinali ziwiya zapakhomo zogwiritsidwa ntchito kwambiri.
Anthu osiyanasiyana olemba mabuku otanthauzira mawu amagwirizana ndi kunena kuti ankanena Mateyu 19:24 ndi pa Marko 10:25 (rha·phisʹ) amachokera ku mawu otanthauza “kusoka.” Ndipo mawu achigiriki a pa Luka 18:25 (be·loʹne) amagwiritsidwa ntchito ponena za singano yosokera mabala pa opaleshoni. Buku lotanthauzira mawu lakuti Vine’s Expository Dictionary of Old and New Testament Words limati: “Zikuoneka kuti malingaliro ogwiritsa ntchito mawu akuti ‘diso la singano’ kutanthauza mageti ang’onoang’ono n’ngatsopano; palibe umboni uliwonse wosonyeza kuti kalelo ankawagwiritsa ntchito motero mawu ameneŵa. Mfundo ya Ambuye m’chiganizochi inali kusonyeza kulephera kwa anthu ndipo palibe chifukwa chofeŵetsera kulephera kumeneko mwa kunena kuti mawu akuti singano akutanthauza chinthu china osati singano yeniyeni.”—1981, Voliyumu 3, tsamba 106.
za “singano” yeniyeni. Mawu achigiriki otembenuzidwa kuti “singano” paEna amati m’mavesiŵa mawu akuti “ngamila” afunika kumasuliridwa kuti “chingwe.” Mawu achigiriki a chingwe (kaʹmi·los) ndi a ngamila (kaʹme·los) ndi osasiyana kwenikweni. Komabe, mawu achigiriki a “ngamila” osati mawu a “chingwe” ndi omwe ali pa Mateyu 19:24 m’zolemba zakale kwambiri zapamanja zachigiriki zomwe zilipo panopo za Uthenga Wabwino wa Mateyu (zolemba zotchedwa Sinaitic, Vatican No. 1209, ndi Alexandrine). Zikuoneka kuti poyambirira Mateyu analemba Uthenga wake Wabwino m’Chihebri ndipo mwina iye mwini anautembenuzira m’Chigiriki. Ankadziŵa bwino zomwe Yesu ananena ndipo motero anagwiritsa ntchito mawu oyenera.
Motero, Yesu anatanthauza singano yeniyeni ndiponso ngamila yeniyeni. Iye anagwiritsa ntchito zinthu zimenezi pofuna kutsindika kuti chinthu chinachake chinali chosatheka. Koma kodi Yesu anatanthauza kuti palibe munthu wolemera amene adzaloŵe Ufumu? Ayi, chifukwa chakuti Yesu sananene izi pofotokoza zinthu zenizenidi. Anagwiritsa ntchito mawu okokomeza pofuna kusonyeza kuti monga momwe zilili zosatheka kuti ngamila iloŵe m’diso la singano yeniyeni, n’zosathekanso kuti munthu wolemera aloŵe Ufumu ngati apitiriza kukakamira chuma chakecho, osaika Yehova poyamba m’moyo wake.—Luka 13:24; 1 Timoteo 6:17-19.
Yesu ananena izi wolamulira wina wachinyamata wolemera kwambiri atakana mwayi waukulu woti akhale wotsatira wa Yesu. (Luka 18:18-24) Munthu wolemera wokonda kwambiri chuma chake kuposa zinthu zauzimu sangayembekezere kupeza moyo wosatha m’makonzedwe a Ufumu. Komabe, anthu ena olemera anakhalapo ophunzira a Yesu. (Mateyu 27:57; Luka 19:2, 9) Motero munthu wolemera amene akudziŵa zosoŵa zake zauzimu ndipo amafunafuna thandizo la Mulungu angapulumutsidwe.—Mateyu 5:3; 19:16-26.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 3 Onani kabuku kakuti Kodi Muyenera Kukhulupirira Utatu? kofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.