Akhala Okhulupirika Ndiponso Osasunthika Mpaka Pano
Akhala Okhulupirika Ndiponso Osasunthika Mpaka Pano
Kum’mwera kwa dziko la Poland, kufupi ndi komwe linachita malire ndi dziko la Slovakia ndiponso Czech Republic, kuli katauni kotchedwa Wisła. Kataunika mwina inuyo simunakamvepo, koma kali ndi mbiri imene mosakayika, Akristu oona angachite nayo chidwi kwambiri. Ndi mbiri yokhudza kulambira Yehova mokhulupirika ndiponso mwakhama. Kodi chinachitika n’chiyani kuti kataunika kakhale ndi mbiri imeneyi?
TAUNI ya Wisła ili m’dera lokongola kwambiri lamapiri ochititsa kaso. Ili ndi timitsinje tothamanga kwambiri tomwe timakathira mumtsinje wa Vistula, umene umayenda mozungulira mapiri ndiponso umadutsa m’zigwa zoŵirira kwambiri. Chifukwa cha anthu ake ansangala ndiponso chifukwa cha nyengo yabwino ya m’derali, tauniyi ndi yotchuka pankhani ya zachipatala ndiponso kuchitirako tchuthi nyengo ya chilimwe ngakhalenso yachisanu.
Zikuoneka kuti dera loyamba kukhala ndi dzina la tauniyi linakhazikitsidwa m’zaka za m’ma 1590. M’derali anakhazikitsamo fakitale yocheka matabwa, ndipo posakhalitsa m’mapiri a m’derali amene anali opanda mitengo munayamba kukhala anthu omwe ankalima ndiponso kuŵeta nkhosa ndi ng’ombe. Koma moyo wa anthu osaukaŵa unakhudzidwa ndi kusintha kwakukulu kwa zachipembedzo. Derali linakhudzidwa kwambiri pamene Martin Luther anayamba zosintha Chikatolika, zimene zinapangitsa kuti chipembedzo chotchedwa Lutheran chikhale “chipembedzo cha dziko lonselo mu 1545,” malingana ndi zimene ananena wofufuza wina dzina lake Andrzej Otczyk. Komano, zinthu zinatembenuka kwambiri chifukwa cha nkhondo ya zaka 30 ndiponso ntchito yolimbana ndi zakuti Chikatolika chisasinthe. Otczyk ananenanso kuti: “M’chaka cha 1654 matchalitchi onse a zipembedzo zimene zinachoka m’Chikatolika analandidwa, kupemphereramo kunaletsedwa, ndipo matchalitchiwo anawalanda mabaibulo komanso mabuku awo ena achipembedzo.” Ngakhale zinali choncho, anthu ambiri a kumeneku sanasiye chipembedzo cha Lutheran.
Mbewu Zoyambirira za Choonadi cha Baibulo
Mwayi wake, zinthu zofunika kwambiri pankhani yachipembedzo zinadzasintha m’tsogolo. M’chaka cha 1928, mbewu zoyambirira za choonadi cha Baibulo zinabzalidwa ndi anthu aŵiri a gulu la Ophunzira Baibulo, lomwe linali dzina la gulu la Mboni za Yehova panthaŵiyo. Chaka chotsatira, Jan Gomola anafika ku tauni ya Wisła ali ndi galamafoni imene anthu ankamvetserapo malekodi a nkhani za m’Malemba. Kenaka anapitiriza ulendo wake n’kupita ku chigwa chinachake chapafupi ndithu kumene anakapeza munthu wachidwi dzina lake Andrzej Raszka, yemwe anali mwamuna wamfupi, wadzitho ndiponso wamtima wofunadi kuphunzira. Nthaŵi yomweyo Raszka anatulutsa Baibulo kuti aone ngati mfundo zotchulidwa mu nkhani za pa galamafonizo zinali zoonadi. Atatsimikizira ananena mosangalala kuti: “Mbale wanga, choonadi chija ndachipeza tsopano. Ndakhala ndikudzifunsa mafunso osiyanasiyana kuchokera panthaŵi imene ndinkamenya nawo nkhondo yoyamba ya padziko lonse.”
Chimwemwe chili tsaya, Raszka anam’tenga Gomola kuti akakumane ndi anzake aŵiri, Jerzy ndi Andrzej Pilch, amenenso anakondwera kwambiri ndi uthenga wa Ufumuwu. Andrzej Tyrna, amene anaphunzira choonadi cha Baibulo ku France, anathandiza anthu ameneŵa kuti adziŵe mozama uthenga wa Mulungu. Pasanapite nthaŵi, iwo anabatizidwa. Pofuna kuthandiza kagulu ka Ophunzira Baibulo a ku Wisła, cha m’ma 1930 abale a m’matauni oyandikana nayo anayamba kumayendera anthu m’kataunika. Motero zinthu zinayamba kuyenda bwino kwabasi.
Anthu ambirimbiri ochita chidwi anayamba kuloŵa gululo. Mabanja a kumeneku a chipembedzo cha Lutheran anali ndi chizoloŵezi chomaŵerenga Baibulo kunyumba kwawo. Motero ambiri akangowasonyeza mfundo zokhutiritsa za m’Malemba zokhudza chiphunzitso cha moto wa helo ndiponso Utatu, sizinkawavuta kuona kuti zoona n’ziti ndiponso kuti zabodza n’ziti. Mabanja ambiri anaganiza zosiya kukhulupirira ziphunzitso zabodza. Motero mpingo wa ku Wisła unakula, ndipo pofika mu 1939 unali ndi anthu pafupifupi 140. Komabe, n’zodabwitsa kuti anthu akuluakulu ambiri mumpingowu anali osabatizidwa. Helena, mmodzi wa Mboni zoyambirirazi anati: “Sikuti zimenezi zinachitika chifukwa chakuti ofalitsa osabatizidwaŵa sankafuna kulambira Yehova ndi mtima wonse.” Ndiye anapitiriza kunena kuti: “Pamayesero amene anadzakumana nawo, anatsimikizira kuti anali okhulupirika.”
Nanga ana awo bwanji? Anawo anazindikira kuti makolo awo apeza choonadi. Franciszek Branc analongosola kuti: “Bambo anga atazindikira kuti apeza choonadi, anayamba kundiphunzitsa ineyo pamodzi ndi mchimwene wanga. Ndinali ndi zaka eyiti ndipo iyeyo anali ndi zaka teni. Bambowo ankatifunsa mafunso ophweka monga akuti: ‘Kodi Mulungu ndani, ndipo dzina lake ndani? Kodi mukudziŵapo chiyani za Yesu Kristu?’ Ndiye tinkalemba mayankho ake n’kulembanso mavesi otsimikizira mayankhowo.” Wa Mboni winanso anati: “Chifukwa chakuti makolo anga anamvera uthenga wa Ufumu mofunitsitsa n’kusiya tchalitchi cha Lutheran mu 1940, ndinkavutitsidwa ndiponso kumenyedwa
kusukulu. Ndikuthokoza kwambiri makolo anga pondiphunzitsa mfundo za m’Baibulo. Mfundo zimenezi zinandithandiza kwambiri panthaŵi yovutayo.”Chikhulupiriro Chawo Chiyesedwa
Nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse itayamba, deralo n’kulandidwa ndi anthu a chipani cha Nazi, anthu a chipanichi ankafuna kuti a Mboni za Yehova onse m’deralo atheretu. Poyamba, anthu achikulire, makamaka azibambo a ana analimbikitsidwa kuti asayine chikalata chosonyeza kuti ndi nzika za ku Germany pofuna kuti awapatse ufulu wotha kuchita zina n’zina. Koma a Mboni anakana kugwirizana ndi anthu a chipani cha Nazi. Abale ndiponso anthu ambiri ochita chidwi ndi uthenga wabwino amene anali a msinkhu wakuti angapite kunkhondo anayenera kusankha pakati pa zinthu ziŵiri izi: Kuvomera kuloŵa usilikali kapena kukaniratu kwamtuwagalu ndipo akakana ankapatsidwa chilango cholapitsa. Andrzej Szalbot amene anamangidwa ndi apolisi otchedwa Gestapo m’chaka cha 1943 analongosola kuti: “Ukakana usilikali ankakutumiza ku ndende zozunzirako anthu, makamaka ndende ya ku Auschwitz. Panthaŵiyi n’kuti ndisanabatizidwe, koma mawu olimbikitsa amene Yesu ananena pa Mateyu 10:28, 29 ndinkawadziŵa. Ndinkadziŵa kuti ndikafa chifukwa chokhulupirira Yehova, iye angathe kudzandiukitsa.”
Chakumayambiriro kwa chaka cha 1942, a chipani cha Nazi anamanga abale 17 a ku Wisła. M’miyezi itatu yokha, abale 15 pagululi anamwalira ali kundende ya Auschwitz. Kodi zimenezi zinawakhudza bwanji a Mboni omwe anatsala ku Wisła? Iwo sanasiye chikhulupiriro chawo chifukwa cha zimenezo, m’malo mwake zinawalimbikitsa kuti akhalebe nganganga pambuyo pa Yehova. Pamiyezi isanu ndi umodzi yotsatira, ku Wisła ofalitsa anawonjezeka moŵirikiza. Posakhalitsa anayambanso kuwamanga. Onse amene anakhudzidwa ndi nkhanza za Hitler analipo abale 83, anthu ochita chidwi, komanso ana. Anthu 53 mwa anthuŵa anawatumiza ku ndende zozunzirako anthu (makamaka ku Auschwitz) kapena ku ndende kokagwira ntchito yakalavulagaga ya kumigodi ndi koswa miyala ku Poland, Germany, ndi Bohemia.
Kukhulupirika ndi Kusasunthika
Ku Auschwitz, a chipani cha Nazi anayesa kukopa a Mboni powauza kuti angathe kuwapatsa ufulu nthaŵi yomweyo. Msilikali wa gulu la SS anauza mbale wina kuti: “Ukangosayina pepala lonena kuti wachoka m’gulu la Ophunzira Baibulo, tikutulutsa ndipo tikulola kupita kwanu.” Anamuuza zimenezi nthaŵi zambiri, koma mbaleyo sanagonje n’kusiya kutsatira Yehova. Motero anamumenya, kumunena, ndiponso kumugwiritsa ntchito yakalavulagaga ku Auschwitz ndi ku Mittelbau-Dora, ku Germany. Mbaleyu atatsala pang’ono kumasulidwa, imfa anasemphana nayo pang’onong’ono ataphulitsa mabomba pa ndende imene anali kukhala.
Wamboni amene wamwalira posachedwapa, dzina lake Paweł Szalbot, panthaŵi ina ananena kuti: “Ndili m’manja mwa asilikali a Gestapo, ankandifunsa nthaŵi zambirimbiri kuti n’chifukwa chiyani ndinkakana kuloŵa gulu la asilikali a ku Germany ndiponso kunena mawu otamanda Hitler.” Iyeyu atawalongosolera zimene Baibulo limanena pankhani yakuti Akristu asamaloŵelere m’ndale, anamupatsa chilango chakuti akagwire ntchito pa fakitale yopanga zida. Iye akuti: “N’zachidziŵikire kuti chifukwa cha chikumbumtima changa sindikanalola kuchita ntchito yotereyi, motero ananditumiza ku ntchito ya kumigodi.” Koma iyeyu anakhalabe wokhulupirika.
Azimayi ndi ana, omwe sanamangidwe, ankatumiza chakudya kwa anthu amene anatsekeredwa ku Auschwitz. Mbale wina amene panthaŵiyi anali kamnyamata anati: “M’nyengo ya chilimwe tinkapita
kutchire kuthyola mtundu winawake wa mabulosi n’kukawagulitsa mosinthanitsa ndi tirigu. Kenaka alongo ankaphika buledi n’kumupaka zinthu monga majalini. Ndiyeno tinkamutumiza pang’onopang’ono kwa a Mboni anzathu amene anali m’ndende.”Amboni onse a ku Wisła amene anatumizidwa ku ndende zozunzirako anthu ndiponso omwe anatumizidwa kokagwira ntchito yakalavulagaga analipo 53. Pagululi 38 anamwalira.
Mmene Zinakhudzira Achinyamata
Ana a Mboni za Yehova anakhudzidwanso ndi nkhanza za anthu a chipani cha Nazi. Ana ena anatumizidwa ku ndende zongogwirizira za ku Bohemia pamodzi ndi amayi awo. Ena ankatengedwa m’manja mwa makolo awo n’kutumizidwa ku ndende yoopsa ya ana ku Lodz.
Ana atatu otereŵa anati: “M’galimoto yoyamba yopita ku Lodz, Ajeremani anatenga ana teni pagulu lathu, a zaka zoyambira pa 5 mpaka 9.” Tinkalimbikitsana popemphera ndi kukambirana za m’Baibulo. Tinafunika kulimba nazo kwambiri.” M’chaka cha 1945 ana onsewo anabwerera m’makwawo. Palibe anafapo koma onse anali atawonda ndiponso atasokonezeka kwambiri maganizo. Koma chikhulupiriro chawo sichinasunthe m’njira ina iliyonse.
N’chiyani Chinadzachitika Pambuyo Pake?
Nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse itatsala pang’ono kutha, chikhulupiriro cha a Mboni a ku Wisła chinali cholimbabe ndipo anali okonzekabe kuyambiranso ntchito yawo yolalikira mwakhama ndiponso ndi mtima wonse. Magulu a abale ankayendera anthu akutali ndi Wisła, mwina okhala mtunda wautali makilomita okwana 40 ndipo ankakawalalikira ndi kuwagaŵira mabuku ofotokoza za m’Baibulo. Jan Krzok anati: “Posakhalitsa m’tauni yathu munakhazikitsidwa mipingo itatu yamphamvu. Komabe, ufulu wachipembedzowu sunakhalitse.
Mu 1950, boma la chikomyunizimu limene linaloŵa m’malo mwa boma la chipani cha Nazi, linaletsa ntchito ya Mboni za Yehova ku Poland. Motero abale a kumeneku anayenera kuchita utumiki wawo mochenjera. Nthaŵi zina ankayendera anthu m’nyumba zawo ponamizira kuti akufuna kugula ziŵeto kapena mbewu. Nthaŵi zambiri ankachita misonkhano yachikristu usiku m’timagulu ting’onoting’ono. Komabe, asilikali aboma anamanga anthu ambiri olambira Yehova, n’kuwaimba mlandu wopanda umboni ngakhale pang’ono, wakuti anali akazitape a bungwe linalake lakunja. Akuluakulu ena a asilikali anaopseza Paweł Pilch pomuuza mwachipongwe kuti: “Hitler analephera kukusintha, koma ifeyo tikusintha, uona.” Koma iyeyu anapitiriza kukhala wokhulupirika kwa Yehova n’kukhala m’ndende kwa zaka zisanu. Achinyamata ena a Mboni atakana kusayina chikalata cha ndale, anathamangitsidwa kusukulu ndipo ena anachotsedwa ntchito.
Yehova Anapitiriza Kuwathandiza
M’chaka cha 1989, zinthu zinasintha pankhani zandale ndipo gulu la Mboni za Yehova linavomerezedwa ndi boma ku Poland. Ku Wisła, anthu olambira Yehova mosasunthika anachita ntchito yawo mwachangu, monga mmene kuchuluka kwa apainiya, kapena kuti atumiki a nthaŵi zonse, kukusonyezera. Abale ndi alongo pafupifupi 100 a m’dera limeneli akuchita utumiki waupainiya. Motero, n’zosadabwitsa kuti tauniyi imatchedwa kuti Fakitale Yopangirako Apainiya.
Ponena za mmene Yehova anathandizira atumiki ake kale, Baibulo limati: “Akadapanda kukhala nafe Yehova, pakutiukira anthu: akadatimeza amoyo.” (Salmo 124:2, 3) Panthaŵi ino, ngakhale kuti anthu ambiri saganizako za Mulungu ndiponso ali ndi makhalidwe oipa, olambira Yehova ku Wisła akuyesetsa kukhalabe okhulupirika ndipo akudalitsidwa kwambiri. Amboni a mibadwo yosiyanasiyana a m’dera limeneli angathe kuchitira umboni kuti mawu otsatiraŵa amene Paulo ananena n’ngoonadi: “Ngati Mulungu ali ndi ife, adzatikaniza ndani?”—Aroma 8:31.
[Chithunzi patsamba 26]
Emilia Krzok pamodzi ndi ana ake, mayina awo Helena, Emilia ndi Jan, anatumizidwa ku ndende yongogwirizira ya ku Bohemia
[Chithunzi patsamba 26]
Atakana kuloŵa usilikali, Paweł Szalbot anatumizidwa ku ntchito ya kumigodi
[Chithunzi patsamba 27]
Abale atatumizidwa ku ndende ya Auschwitz, ena n’kufera konko, ntchito yolalikira sinasiye kuyenda bwino ku Wisła
[Chithunzi patsamba 28]
Paweł Pilch ndi Jan Polok anatengedwa kupita ku ndende ya achinyamata ku Lodz
[Mawu a Chithunzi patsamba 25]
Berries and flowers: © R.M. Kosinscy/www.kosinscy.pl