Kodi Zidzatheka Kukhaladi Mosatekeseka?
Kodi Zidzatheka Kukhaladi Mosatekeseka?
NDANI sasangalala kuona ana akuseŵera mokondwa ndi makolo awo achikondi? Ana satekeseka ndi chilichonse akakhala ndi makolo awo amene amawasamala. Komatu, ana ambiri kaŵirikaŵiri sakhala ndi nthaŵi zosangalala ngati zimenezi. M’malo mwake, ana ena tsiku ndi tsiku amakhala ndi nkhaŵa yoti n’kuti kumene angapeze malo ogona. Kodi pali chiyembekezo chilichonse choti ana ameneŵa komanso anthu ena amene ali m’mavuto osiyanasiyana adzakhala mosatekeseka?
Mukamaganiza za m’tsogolo mwina mungaone kuti palibe chilichonse cholimbitsa mtima, koma Mawu a Mulungu amatipatsa chiyembekezo. Mneneri Yesaya analosera kuti lidzakwana tsiku loti anthu onse adzakhala mosatekeseka. Analemba kuti: “Adzamanga nyumba ndi kukhalamo; ndipo iwo adzawoka minda yamphesa, ndi kudya zipatso zake. Iwo sadzamanga, ndi wina kukhalamo; iwo sadzawoka, ndi wina kudya.”—Yesaya 65:21, 22.
Koma kodi pali zifukwa zomvekadi zoyembekezera zinthu zimenezi? Tikufunsa choncho chifukwa choti ngakhale mawu akuti “chiyembekezo” enieniwo si nthaŵi zonse pamene amasonyeza kuti zinthu ndi zotsimikizika kuti zichitika. Mwachitsanzo, ku Brazil, mawu akuti, “A esperança é a última que morre,” ndi ofala kwambiri. Mawu ameneŵa amatanthauza kuti, “Chiyembekezo ndiye chinthu chimene chimamalizira kufa.” Izi zikutanthauza kuti anthu ambiri amakhalabe ndi chiyembekezo ngakhale panthaŵi yomwe palibe zifukwa zomveka zokhalira ndi chiyembekezocho. Koma chiyembekezo chomwe Mulungu wamoyo amatipatsa ndi chosiyana ndi zimenezi. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Amene aliyense akhulupirira [Mulungu], sadzachita manyazi.” (Aroma 10:11) Maulosi a m’Baibulo amene anakwaniritsidwa kale amatipatsa chikhulupiriro chakuti malonjezo ena onse amene Yehova Mulungu anapanga adzakwaniritsidwanso. Malonjezo amenewo akadzakwaniritsidwa, sikudzakhalanso zinthu zimene zimachititsa kuti ana azingoyendayenda m’misewu.
Ngakhale panopo, malangizo othandiza kwambiri omwe ali m’Baibulo angathandize anthu omwe alibe chiyembekezo kusintha miyoyo yawo ndi kuyamba kukhala mosatekeseka. Kodi zimenezi zingatheke motani? Mboni za Yehova m’dera lanulo zingasangalale kukuthandizani kupeza yankho la funso limeneli.