Kufunafuna Utsogoleri Wabwino
Kufunafuna Utsogoleri Wabwino
“Ndikuti uchoke, tatopa nawe. Tikunenetsa pali Mulungu kuti choka!” Izi ananena ndi Leopold Amery, phungu wa Nyumba ya Malamulo ya ku Britain, pobwereza mawu a Oliver Cromwell.
Nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse inali itavutitsa anthu kwa miyezi isanu ndi itatu, ndipo dziko la Britain komanso mayiko ogwirizana nalo zinthu sizinali kuwayendera bwino pankhondoyo. Leopold Amery ndi akuluakulu ena a boma ankaona kuti m’pofunika kusintha utsogoleri. Motero, pa May 7, 1940, m’nyumba ya malamulo ya ku Britain, bambo Amery ananena mawu apamwambawo kwa nduna yaikulu ya dzikolo a Neville Chamberlain. Patangotha masiku atatu, nduna yaikuluyo inatula pansi udindo wake, ndipo m’malo mwake munaloŵa a Winston Churchill.
ANTHU amafunikira utsogoleri, koma sikuti mtsogoleri aliyense angathe kutsogolera anthu bwinobwino. Ngakhale m’banja, kuti mayi ndi ana azikhala mosangalala, bambo amayenera kudziŵa kuwatsogolera bwino. Motero, ingoganizirani mmene mtsogoleri wadziko linalake kapenanso dziko lonse lapansi ayenera kukhalira. M’pake kuti atsogoleri abwino akusoŵa kwambiri.
N’chifukwa chake kungoyambira kalekale, anthu akhala akulonga atsogoleri atsopano, kusintha maboma, kulanda maboma mwaupandu, kuika pampando anthu atsopano, kuchita zisankho, kupha atsogoleri, ndiponso kusintha zipani zolamulira. Mafumu, nduna zazikulu, akalonga, mapulezidenti, alembi aakulu, ndiponso atsogoleri ankhanza akhala akuikidwa ndi kuchotsedwa pampando. Ngakhale atsogoleri amphamvu atula pansi maudindo awo zinthu zitasintha mwadzidzidzi. (Onani bokosi lakuti “Kuchoka Pampando Mosayembekezeka,” lomwe lili patsamba 5.) Komabe, zaoneka kuti m’povuta kupeza utsogoleri wabwino ndiponso wokhalitsa.
“Tingosankha Omweŵa Basi” Kapena Kodi Tingachitire Mwina?
Motero, n’zosadabwitsa kuti anthu ambiri ataya chikhulupiriro pankhani yopeza utsogoleri wabwino. M’mayiko ena, panthaŵi yachisankho m’pamene pamaonekera kwambiri kuti anthu ataya mtima ndipo akuchita mphwayi kusankha atsogoleri. Geoff Hill, yemwe ndi mtolankhani ku Africa kuno anati: “Anthu akamaona kuti palibenso chimene angachite kuti adzichotse m’mavuto awo, ambiri amachita mphwayi [kukavota] mwinanso savota n’komwe . . . Ku Africa kuno anthu akapanda kuvota sizitanthauza kuti ndi osangalala ndi bomalo ayi. Nthaŵi zambiri amatero chifukwa chosoŵa pogwira ndiponso chifukwa choona kuti palibe aliyense akuwaganizira
pa mavuto awo.” Munthu wina wolemba nkhani m’nyuzipepala ina ku United States ananenanso chimodzimodzi chisankho chitayandikira. Iye anati: “Ndikulakalaka pachisankhochi pakanakhala munthu wangwiro woti timuvotere.” Ndiye anapitiriza kunena kuti: “Tsoka ilo, palibe munthu wotere. Ndipotu munthu wotere sangapezeke kwina kulikonse. Choncho, tingosankha omweŵa basi.”Kodi anthu alibedi atsogoleri ena oti n’kuwasankha kuposa ‘kungosankha omweŵa,’ opanda ungwiroŵa? Kodi pakuti anthu amene akhala akutsogolera alephera kukwaniritsa zofuna za anthu awo ndiye kuti basi sitidzakhalanso ndi utsogoleri wabwino? Ayi sichoncho. Utsogoleri wabwino kwambiri ulipo. Nkhani yotsatirayi inena za mtsogoleri wabwino koposa ndiponso mmene utsogoleri wake ungapindulitsire anthu ambirimbiri osiyanasiyana, kuphatikizapo inuyo.
[Mawu a Chithunzi patsamba 3]
Pamwamba chakumanzere: Neville Chamberlain
Pamwamba chakumanja: Leopold Amery
Pamunsi: Winston Churchill
[Mawu a Chithunzi]
Chamberlain: Photo by Jimmy Sime/Central Press/Getty Images; Amery: Photo by Kurt Hutton/Picture Post/Getty Images; Churchill: The Trustees of the Imperial War Museum (MH 26392)