Kodi Mumalakalaka Dziko Limene Anthu Azidzakhala Opanda Mantha?
Kodi Mumalakalaka Dziko Limene Anthu Azidzakhala Opanda Mantha?
“Tikukhala ‘atcheru nthawi zonse ndiponso . . . othedwa nzeru’ chifukwa cha ‘zoopsa . . zosadziwika bwinobwino zomwe zingatigwere pa nthawi iliyonse, mwa mtundu uliwonse, ndiponso popanda chenjezo.’”
MAWU amenewa, amene analembedwa chaka chatha mu magazini ya Newsweek, akusonyeza mmene anthu ambiri akumvera masiku ano chifukwa chokhala m’dziko lachisokonezoli. Yesu Kristu anasonyeza kuti chisokonezo chimenechi chidzawonjezeka m’tsogolo mukubweramu. Iye ananena za nthawi imene mitundu ya anthu idzasautsidwa koopsa moti idzathedwa nzeru, ndipo anthu adzakomoka ndi mantha ndiponso chifukwa choganizira zinthu zomwe zikubwera pa dziko lapansili. Koma ife sitidzafunikira kuchita mantha kapena kusowa chochita, chifukwa Yesu anapitiriza kuti: “Poyamba kuchitika izi weramukani, tukulani mitu yanu; chifukwa chiwomboledwe chanu chayandikira.”—Luka 21:25-28.
Pofotokoza mmene anthu ake adzakhalire padziko lapansi akadzawomboledwa, Yehova Mulungu anati: “Anthu anga adzakhala m’malo a mtendere, ndi mokhala mokhulupirika ndi mopuma mwa phe.” (Yesaya 32:18) Kudzera mwa mneneri wake Mika, Yehova ananena kuti: “Adzakhala munthu yense patsinde pa mpesa wake, ndi patsinde pa mkuyu wake; ndipo sipadzakhala wakuwaopsa.”—Mika 4:4.
Zimenezo n’zosiyana kwambiri ndi mmene moyo ulili masiku ano! Anthu sadzaopanso zoopsa zosadziwika. M’malo mokhala tcheru ndiponso kuthedwa nzeru nthawi zonse, adzakhala ndi mtendere ndi chimwemwe chosatha.