Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ana Athu Ndi Cholowa Chamtengo Wapatali

Ana Athu Ndi Cholowa Chamtengo Wapatali

Ana Athu Ndi Cholowa Chamtengo Wapatali

“Taonani, ana ndiwo cholandira [“cholowa,” NW] cha kwa Yehova; chipatso cha m’mimba ndicho mphoto.”​—SALMO 127:3.

1. Kodi mwana woyamba wa munthu anakhalako motani?

TAGANIZIRANI zinthu zozizwitsa zimene Yehova Mulungu anachititsa kuti zizitheka malinga ndi mmene analengera mwamuna ndi mkazi woyamba. Adamu, yemwe anali bambo, ndiponso Hava, yemwe anali mayi, onse anapereka mbewu ya m’thupi mwawo imene inatheketsa kuti mluza uyambe kupangika m’mimba mwa Hava, ndipo mluzawu unakula n’kudzakhala mwana woyamba wa munthu. (Genesis 4:1) Mpaka panopo, timadabwa kwambiri ndi zimene zimachitika kuti mwana ayambe kupangika m’mimba ndiponso kuti abadwe.

2. Kodi n’chifukwa chiyani munganene kuti zimene zimachitika m’mimba mwa mayi wa pakati n’zodabwitsa?

2 Pakatha masiku 270 okha mayi atatenga pathupi, mluza uja, umene umayamba kupangika kuchokera pa selo imodzi yokha, imene inayamba mayi atakumana ndi bambo, umasanduka khanda ndipo khandalo limakhala ndi maselo osawerengeka. Selo yoyambirirayo imakhala ndi malangizo ofunika kuti papangike maselo a mitundu yokwana 200. Ndiyeno potsatira malangizo odabwitsawa, omwe palibe munthu amene angawamvetse, maselo opangidwa movuta kufotokozawa amakula m’njira yoyenerera mpaka kudzasanduka kakhanda.

3. N’chifukwa chiyani anthu ambiri oganiza bwino amavomereza mfundo yakuti Mulungu ndiye amachititsa kuti mwana akhaleko?

3 Kodi munganene kuti ndani kwenikweni amene amapanga mwana? N’zosachita kufunsa kuti ndi amene anapanga moyo weniweniwo. Munthu wina wolemba masalmo a m’Baibulo ananena kuti: “Dziwani kuti Yehova ndiye Mulungu; Iyeyu anatilenga, ndipo ife ndife ake.” (Salmo 100:3) Makolo, inuyo mukudziwa kuti mwana muli nayeyo sikuti munachita kumupanga nokha mwanzeru zanu zakuya. Amene akanatha kukonza mwana m’njira yodabwitsa yoteroyo, ndi Mulungu yekha basi, amene ali wanzeru zopanda malire. Kwa zaka masauzande ambiri, anthu oganiza bwino akhala akuona kuti amene amachititsa kuti mwana ayambe kupangika m’mimba mwa mayi ndi Mlengi Wamkulu. Kodi inunso mumaona chimodzimodzi?​—Salmo 139:13-16.

4. Kodi ndi khalidwe loipa lotani la anthu limene Yehova sangakhale nalo?

4 Koma kodi Yehova ndi Mlengi wosaganizira anthu, yemwe anangoyambitsa njira yoti amuna ndi akazi aziberekera ana, basi iyeyo n’kuiwalako? Ngakhale kuti anthu ena saganizira anzawo, Yehova si wotero ayi. (Salmo 78:38-40) Pa Salmo 127:3, Baibulo limati: “Taonani, ana ndiwo cholandira [“cholowa,” NW] cha kwa Yehova; chipatso cha m’mimba ndicho mphoto yake.” Tsopano tiyeni tione kuti kodi cholowa n’chiyani ndiponso kuti chimasonyeza chiyani?

Cholowa Ndiponso Mphoto

5. Kodi n’chifukwa chiyani ana ali cholowa?

5 Cholowa chili ngati mphatso. Nthawi zambiri makolo amagwira ntchito mwakhama kwambiri kuti adzasiyire ana awo cholowa. Cholowa chake chingakhale ndalama, katundu, kapena zinthu zina zamtengo wapatali. Mulimonsemo, cholowacho chimasonyeza chikondi cha makolowo. Baibulo limanena kuti ana ndi cholowa chimene Mulungu amapereka kwa makolo. Ana ndi mphatso imene Mulungu anapereka mwachikondi chake. Ngati inuyo muli kholo, kodi munganene kuti zochita zanu zimasonyeza kuti ana anu mumawaona ngati mphatso imene Mlengi wa chilengedwe chonse wakuikizani?

6. Kodi cholinga cha Mulungu pochititsa kuti anthu azitha kukhala ndi ana chinali chotani?

6 Cholinga cha Yehova popereka mphatso imeneyi chinali chakuti dziko lapansi lidzaze ndi mbadwa za Adamu ndi Hava. (Genesis 1:27, 28; Yesaya 45:18) Yehova sikuti analenga munthu aliyense payekhapayekha, ngati mmene analengera angelo, amene alipo ambirimbiri. (Salmo 104:4; Chivumbulutso 4:11) M’malomwake, Mulungu anaganiza zolenga anthu m’njira yakuti azibereka ana okhala ngati iwowo. Kwa mayi ndiponso bambo, ndi mwayi waukulu kwabasi kubereka ndiponso kusamalira munthu wongobadwa kumeneyo. Kodi inuyo makolo, mumayamikira Yehova pochititsa kuti muthe kukhala ndi cholowa chamtengo wapatali chonchi?

Tengerani Chitsanzo cha Yesu

7. Mosiyana ndi zimene makolo ena amachita, kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti amaganizira “ana a anthu”?

7 N’zomvetsa chisoni kuti si makolo onse amene amaona kuti ana awo ndi mphoto. Pali makolo ambiri amene saganizira kwenikweni za ana awo. Makolo oterewa satsanzira mtima wa Yehova ndiponso Mwana wake. (Salmo 27:10; Yesaya 49:15) Komano, taonani mtima woganizira ana umene Yesu anali nawo. Ngakhale pamene Yesu anali munthu wauzimu wamphamvu kumwamba, asanabwere padziko lapansi kudzakhala munthu, Baibulo limanena kuti iye anali “kusekerera ndi ana a anthu.” (Miyambo 8:31) Yesu ankakonda kwambiri anthu moti mpaka anapereka moyo wake kuti ukhale dipo pofuna kuti anthufe tidzathe kukhala ndi moyo wosatha.​—Mateyu 20:28; Yohane 10:18.

8. Kodi Yesu anapereka bwanji chitsanzo chabwino kwa makolo?

8 Ali padziko pano, Yesu anapereka chitsanzo china chabwino kwambiri, makamaka kwa makolo. Taganizirani zimene anachita. Iye anadzipatsa nthawi yocheza ndi ana, ngakhale pamene anali wotanganidwa kwambiri ndiponso wotopa. Ankawaonerera akusewera pamsika ndipo anatchulapo zochitika zawo pophunzitsa anthu. (Mateyu 11:16, 17) Paulendo wake womaliza wopita ku Yerusalemu, Yesu ankadziwa kuti akazunzidwa ndiponso akaphedwa. Motero, anthu atam’bweretsera ana, ophunzira ake anayesa kuthamangitsa anawo, mwina pofuna kumupepuza Yesuyo. Koma Yesu anadzudzula ophunzira akewo. Posonyeza “kusekerera” kapena kuti kukondwera ndi ana, iye anati: “Lolani tiana tidze kwa Ine; musatiletse.”​—Marko 10:13, 14.

9. N’chifukwa chiyani tinganene kuti zochita zathu zimaposa zonena zathu?

9 Chitsanzo cha Yesu chingatiphunzitse kanthu kena. Kodi ana akatipeza timatani, ngakhale pamene tili otanganidwa? Kodi timachita zimene Yesu anachita? Zimene ana amafuna, makamaka kwa makolo awo, ndi zimene Yesu anawapatsa mofunitsitsa. Zinthu zake ndizo kukhala ndi nthawi yocheza nawo ndiponso kuchita nawo chidwi. N’zoona kuti ana amafunika kuwauza kuti mumawakonda. Komatu zimene mumawachitira zimaposa mawu chabe. Chikondi chanu sikuti chimaonekera pa zimene mumanena zokha ayi komanso makamaka pa zimene mumachita. Chimaonekera mukamakhala nawo nthawi yaitali, kuchita nawo chidwi ndiponso kuwasamalira. Komabe, n’kutheka kuti kuchita zinthu zonsezi sikungaphule kanthu. Kapena mwina zingatenge nthawi ndithu. Choncho m’pofunika kuleza mtima. Tingaphunzire kuleza mtima potsanzira mmene Yesu ankachitira zinthu ndi ophunzira ake.

Yesu Anali Woleza Mtima Ndiponso Wachikondi

10. Kodi Yesu anaphunzitsa bwanji ophunzira ake kudzichepetsa, ndipo kodi anakwanitsa kuwaphunzitsa zimenezi poyambirira penipeni?

10 Yesu ankadziwa kuti ophunzira ake anali kupikisana pankhani yakuti wamkulu ndani. Tsiku lina, atafika ku Kapernao ndi ophunzira ake, iye anawafunsa kuti: “Munalikutsutsana ninji panjira? Koma iwo anakhala chete; pakuti anatsutsana wina ndi mnzake panjira, kuti, wamkulu ndani?” M’malo mowakalipira, Yesu analeza mtima n’kuwapatsa chitsanzo chooneka ndi maso pofuna kuwaphunzitsa kudzichepetsa. (Marko 9:33-37) Kodi chitsanzo chimenechi chinawathandizadi? Inde, koma osati nthawi yomweyo ayi. Patatha miyezi sikisi, Yakobo ndi Yohane anatuma amayi awo kuti akam’pemphe Yesu kuti adzawapatse maudindo apamwamba mu Ufumu. Apanso, Yesu analeza mtima n’kuwathandiza maganizo.​—Mateyu 20:20-28.

11. (a) Kodi atumwi ali m’chipinda chapamwamba ndi Yesu, analephera kuchita ntchito yotani yogwirizana ndi chikhalidwe cha kumeneko? (b) Kodi Yesu anachitapo chiyani ndipo kodi zimene anachitazo zinaphula kanthu panthawiyo?

11 Posakhalitsa, chikondwerero cha Paskha cha mu 33 C.E. chinafika, ndipo Yesu anakumana ndi atumwi ake pawokha kuti achite chikondwererochi. Atafika m’chipinda chapamwamba, palibe aliyense wa atumwi 12 aja amene anafuna kuti achite ntchito yosambitsa mapazi otuwa a anzakewo, malingana ndi mmene anthu ankachitira pa chikhalidwe cha kumeneko. Imeneyi inali ntchito yonyozeka yomwe panyumba ankaichita ndi antchito kapena akazi. (1 Samueli 25:41; 1 Timoteo 5:10) Yesu ayenera kuti anamva chisoni kwambiri kuona ophunzira ake akupitirizabe kulimbana pankhani ya maudindo. Motero Yesu anasambitsa aliyense wa ophunzirawo kenaka anawalimbikitsa mwamphamvu kuti atsatire chitsanzo chake chotumikira ena. (Yohane 13:4-17) Koma kodi iwo anatero? Baibulo limanena kuti pa nthawi ina madzulo omwewo “kunakhala kutsutsana mwa iwo, ndani wa iwo ayesedwe wamkulu.”​—Luka 22:24.

12. Kodi makolo angatsanzire bwanji Yesu poyesetsa kuphunzitsa ana awo?

12 Kodi makolonu, ana anu akamalephera kumvera malangizo anu, mumatha kuona mmene Yesu ayenera kuti ankamvera? Komatu musaiwale kuti Yesu sanatope nawo atumwi akewo, ngakhale kuti sankasintha mwamsanga zofooka zawo. Komabe patsogolo pake, zinthu zinayamba kuyenda bwino chifukwa cha kuleza mtima kwake. (1 Yohane 3:14, 18) Makolonu, muzitsanzira chikondi ndiponso kuleza mtima kwa Yesu, ndipo musamatope kuphunzitsa ana anu.

13. N’chifukwa chiyani makolo sayenera kumukalipira mwana akamafunsa mafunso?

13 Ana ayenera kumadziwa kuti makolo awo amawakonda ndiponso kuti amawaganizira. Yesu ankafuna kuti azidziwa zimene ophunzira ake akuganiza, motero ankamvetsera iwowo akamafunsa zinthu. Ankawafunsanso zimene iwowo akuganiza pa nkhani zina. (Mateyu 17:25-27) Inde, njira yabwino yophunzitsira zinthu ndiyo kukhala womvetsera bwino ndiponso kuchita chidwi. Makolo ayenera kuyesetsa kuthetsa khalidwe loti mwana akafunsa chinthu, iwo azingomuuza kuti: “Tachoka apa! Sukuona kuti ndatanganidwa?” Ngati alidi otanganidwa, ayenera kumuuza bwinobwino mwanayo kuti nkhaniyo akambirana nthawi ina. Kenaka, makolowo azionetsetsa kuti akambirana nayedi mwanayo nkhaniyo. Potero, mwanayo angathe kuona kuti makolowo amamuganiziradi, moti angakhale womasuka nawo kumawauza zakukhosi.

14. Kodi makolo angaphunzire chiyani kwa Yesu pa nkhani yosonyeza ana awo chikondi?

14 Kodi n’zoyenera kuti makolo aziika manja awo m’mapewa mwa ana awo ndiponso kuwakumbatira powasonyeza chikondi? Apanso makolo angathe kuphunzirapo kanthu pa chitsanzo cha Yesu. Baibulo limanena kuti Yesu ‘anayangata tiana, natidalitsa, ndi kuika manja ake pa ito.’ (Marko 10:16) Kodi mukuganiza kuti anawo anamva bwanji? N’zosakayikitsa kuti anamva bwino kwambiri mumtima mwawo ndipo anayamba kumukonda kwambiri Yesu. Ngati makolonu mumakondana kwambiri ndi ana anu, anawo angamakumvereni mosavuta mukamafuna kuwalanga ndi kuwaphunzitsa.

Kodi Ana Muzikhala Nawo Nthawi Yaitali Motani?

15, 16. Kodi ndi mfundo yotani ya kaleredwe ka ana imene yatchuka, ndipo kodi zikuoneka kuti inayamba chifukwa chiyani?

15 Anthu ena amakayikira zoti ana amafunikira kuti makolo awo azikhala nawo kwa nthawi yaitali ndiponso kuti aziwasonyeza chikondi. Mfundo imene anthu ena aitchukitsa mochenjera ndi mfundo yakuti ana amafunika kukhala nawo kwa nthawi yochepa koma yopindulitsa. Anthu amene amalimbikitsa mfundo imeneyi amanena kuti ana safunika kukhala ndi makolo awo kwa nthawi yaitali, koma amangofunika kuti pa nthawi yochepa imene mungakhale nawoyo muzichita zinthu zopindulitsa ndiponso zoti mwazikonzekera bwino. Kodi mfundo imeneyi ndi mfundo yothandiza, yomwe anaiganizira mowafuniradi zabwino ana?

16 Wolemba nkhani wina amene analankhula ndi ana ambiri ananena kuti chinthu chimene ana “amafunikira kwambiri kwa makolo awo ndicho kukhala nawo nthawi yaitali,” ndiponso “kuwasonyeza kuti akuchita nawo chidwi kwambiri.” N’zochititsa chidwi kuti pulofesa wa pa koleji ina ananena kuti: “Mfundo yakuti [ana amafunika nthawi yochepa koma yopindulitsa] inayamba chifukwa chakuti makolo anayamba kuona kuti sakukwanitsa udindo wawo. Iwo anayamba kudzipezera tizifukwa todziikira kumbuyo pofuna kuti asamakhale ndi ana awo kwa nthawi yaitali.” Koma kodi makolo ayenera kukhala ndi ana awo kwa nthawi yaitali motani?

17. Kodi ana amafunikira chiyani kwa makolo awo?

17 Baibulo silitchula kuti makolo azikhala ndi ana awo kwa nthawi yaitali motani. Komabe, makolo achiisrayeli analimbikitsidwa kuti ayenera kumalankhula ndi ana awo akakhala m’nyumba, akamayenda pamsewu, akakhala pansi, ndiponso akadzuka. (Deuteronomo 6:7) Zimenezi zikusonyezeratu kuti makolo ayenera kumacheza ndi ana awo ndiponso kumawaphunzitsa tsiku lililonse.

18. Kodi Yesu anagwiritsira ntchito motani mipata yomwe ankaipeza pophunzitsa atumwi ake, ndipo kodi makolo angaphunzirepo chiyani pamenepa?

18 Yesu anaphunzitsa bwinobwino ophunzira ake pamene ankadya nawo, kuyenda nawo ndiponso ngakhale pocheza nawo. Motero anagwiritsira ntchito mpata uliwonse kuwaphunzitsa. (Marko 6:31, 32; Luka 8:1; 22:14) Makolo achikristu nawonso ayenera kuyesetsa kugwiritsira ntchito mpata uliwonse kuti ayambe kapena apitirize kumalankhula bwino ndi ana awo ndiponso kuwaphunzitsa kuyenda m’njira za Yehova.

Zoyenera Kuwaphunzitsa Ndiponso Mmene Mungaphunzitsire

19. (a) Kodi kuphatikiza pa kukhala ndi nthawi yocheza ndi ana palinso chiyani chofunikira? Kodi n’chiyani chimene makolo amafunikira kwambiri kuti athe kuphunzitsa ana?

19 Kuti ana muwalere bwino, sikuti mumangofunika kuchezanawo ndi kuwaphunzitsa kokha ayi. Pamafunikanso kuganizira bwino zowaphunzitsazo. Taonani mmene Baibulo limagogomezerera zinthu zimene ziyenera kuphunzitsidwa. Baibulo limati: “Mawu awa ndikuuzani lero . . . muziwaphunzitsa mwachangu kwa ana anu.” Kodi “mawu awa” amene ana ayenera kuphunzitsidwa ndi mawu ati? Zikuoneka kuti awa ndi mawu amene anali atangotchulidwa kumene, akuti: “Muzikonda Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse, ndi mphamvu yanu yonse.” (Deuteronomo 6:5-7) Yesu anati lamulo limeneli ndilo lofunika kwambiri pa malamulo onse a Mulungu. (Marko 12:28-30) Chinthu chachikulu chimene makolo ayenera kuphunzitsa ana ndicho zinthu zokhudza Yehova, ndipo ayenera kuwalongosolera chifukwa chimene Yehova yekha ndiye ali woyenerera kuti tizimukonda ndiponso kumulambira ndi moyo wathu wonse.

20. Kodi makolo akale, Mulungu anawalamula kuti aziphunzitsa chiyani ana awo?

20 Komabe, “mawu awa” amene makolo akulimbikitsidwa kuti aziphunzitsa ana awo sakutanthauza kungokonda chabe Mulungu ndi moyo wonse. Mukawerenga chaputala cham’mbuyo cha buku la Deuteronomo, muona kuti Mose ankabwereza malamulo amene Mulungu analemba pa magome a miyala. Malamulowa amatchedwa kuti Malamulo Khumi. Ena mwa malamulowa ndi malamulo akuti osanama, osaba, osapha, ndiponso osachita chigololo. (Deuteronomo 5:11-22) Motero, panthawiyo makolo anasonyezedwa kufunika kophunzitsa ana awo makhalidwe abwino. Makolo achikristu masiku ano ayenera kuwaphunzitsa ana awo malangizo oterewa powathandiza kuti adzakhale ndi tsogolo labwino ndiponso losangalatsa.

21. Kodi malangizo akuti ana “muziwaphunzitsa mwachangu” mawu a Mulungu, amatanthauza chiyani?

21 Onani kuti makolo anauzidwa njira imene ayenera kuphunzitsira “mawu awa,” kapena kuti malamulowo kwa ana awo. Njira yake inali yakuti: “Muziwaphunzitsa mwachangu kwa ana anu.” Mawu akuti ‘kuphunzitsa mwachangu’ amatanthauza “kuphunzitsa ndi kugogomezera zinthu mobwerezabwereza. Amatanthauzanso kulimbikitsa kapena kuchinyiza zinthuzo m’maganizo.” Motero, pamenepa kwenikweni Mulungu akuuza makolo kuti akhazikitse ndondomeko yokonzedwa bwino yophunzitsira ana awo Baibulo, yomwe cholinga chake chizikhala makamaka chochinyiza kapena kuti kutsendereza zinthu zauzimu m’maganizo a ana awo.

22. Kodi makolo achiisrayeli anauzidwa kuti azitani pophunzitsa ana awo, ndipo kodi zimenezo zinkatanthauza chiyani?

22 Ntchito imeneyi imafunika kukhala ndi ndondomeko yabwino. Motero kuti itheke pamafunika kuti makolo achite khama kwambiri. Baibulo limati: “Muziwamanga [“mawu awa,” kapena kuti malamulo a Mulungu] padzanja panu ngati chizindikiro, ndipo akhale ngati chapamphumi pakati pa maso anu. Ndipo muziwalembera pa mphuthu za nyumba zanu, ndi pa zipata zanu.” (Deuteronomo 6:8, 9) Zimenezi sizikutanthauza kuti makolo azilembadi malamulo a Mulungu pamwamba pa zitseko ndiponso pa geti la kunyumba kwawo, kapenanso kuwamanga pa manja kayanso pa mphumi za ana awo. Koma mfundo ya apa n’njakuti nthawi zonse makolo azikumbutsa ana zimene Mulungu amaphunzitsa. Ayenera kumaphunzitsa ana awo nthawi zonse, moti zizingokhala ngati kuti nthawi ina iliyonse anawo akuona malamulo a Mulungu.

23. Kodi m’phunziro la mlungu wamawa tidzakambirana chiyani?

23 Kodi ndi zinthu zina ziti zofunika kwambiri zimene makolo ayenera kuphunzitsa ana awo? Kodi n’chifukwa chiyani kuli kofunikira masiku ano kuti ana aziphunzitsidwa ndiponso kusonyezedwa mmene angadzitetezere? Kodi pali thandizo lotani limene makolo angagwiritsire ntchito kuti aphunzitse bwino ana awo? Mafunso amenewa pamodzinso ndi ena amene amakhudza makolo ambiri ayankhidwa m’nkhani yotsatirayi.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• N’chifukwa chiyani makolo ayenera kuona kuti ana awo n’ngamtengo wapatali?

• Kodi makolo ndiponso anthu ena angaphunzire chiyani kwa Yesu?

• Kodi makolo ayenera kukhala ndi nthawi yaitali motani ndi ana awo?

• Kodi ana ayenera kuphunzitsidwa chiyani ndiponso motani?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 10]

Kodi makolo angaphunzire chiyani pa kaphunzitsidwe ka Yesu?

[Zithunzi patsamba 11]

Kodi makolo achiisrayeli ankafunika kuphunzitsa bwanji ana awo ndiponso pa nthawi yotani?

[Zithunzi patsamba 12]

Makolo ayenera kuthandiza ana awo kukumbukira malamulo a Mulungu nthawi zonse