Khulupirirani Mawu a Yehova
Khulupirirani Mawu a Yehova
“Ndikhulupirira mawu anu.”—SALMO 119:42.
1. Kodi mukudziwa chiyani za munthu amene analemba Salmo 119, nanga anali ndi maganizo otani?
WOLEMBA Salmo 119 ankakonda kwambiri mawu a Yehova. N’kutheka kuti amene analemba Salmo limeneli ndi Hezekiya, panthawi imene anali Kalonga wa Yuda. Maganizo omwe ali m’nyimbo youziridwayi akugwirizanadi ndi maganizo amene Hezekiya anali nawo. Pamene anali mfumu ya Yuda, iye “anaumirira Yehova.” (2 Mafumu 18:3-7) Choncho n’zoonekeratu kuti wolemba Salmo limeneli ankadziwa kusowa kwake kwauzimu.—Mateyu 5:3.
2. Kodi nkhani yaikulu mu Salmo 119 ndi yotani, nanga nyimboyi inalembedwa motani?
2 Nkhani yaikulu mu Salmo 119 yagona pa phindu la mawu, kapena kuti uthenga wa Mulungu. * Mwinamwake pofuna kuti azikumbukira mosavuta, mlembi ameneyu analemba nyimboyi motsatira ndondomeko ya zilembo za alifabeti. Mavesi ake onse okwana 176 anawalemba motsatira ndondomeko ya zilembo za alifabeti yachihebri. M’chihebri choyambirira, salmo limeneli lili ndi zigawo 22 ndipo chilichonse mwa zigawo zimenezi chili ndi mizera 8 yomwe ikuyamba ndi chilembo chofanana. Salmo limeneli likutchula mawu, chilamulo, zikumbutso, njira, malangizo, malemba, malamulo ndi maweruzo a Mulungu. M’nkhani ino komanso mu nkhani yotsatira tikambirana Salmo 119 malinga ndi mmene analimasulira m’Baibulo kuchokera ku Chihebri. Kusinkhasinkha zochitika pa moyo wa atumiki a Yehova akale ndi amakono omwe, kutithandiza kumvetsa bwino nyimbo youziridwa ndi Mulungu imeneyi, ndiponso kukulitsa mtima wathu woyamikira Baibulo, Mawu olembedwa a Mulungu.
Mverani Mawu a Mulungu Kuti Mukhale Achimwemwe
3. Fotokozani zimene kukhala opanda cholakwa kumatanthauza, ndipo perekani chitsanzo.
3 Kuyenda m’chilamulo cha Mulungu n’kumene kumatipatsa chimwemwe chenicheni. (Salmo 119:1-8) Ngati tikuyenda m’chilamulo cha Mulungu, kwa Yehova tidzakhala ‘opanda cholakwa m’mayendedwe athu.’ (Salmo 119:1, NW) Kukhala opanda cholakwa sikutanthauza kuti ndife angwiro, koma zimangosonyeza kuti tikuyesetsa kuchita chifuniro cha Yehova Mulungu. “Nowa anali munthu wolungama ndi [wopanda cholakwa] m’mibadwo yake” chifukwa chakuti “anayendabe ndi Mulungu.” Kholo lakale lokhulupirikali, limodzi ndi banja lake linapulumuka Chigumula chifukwa chakuti kholo limeneli linali kutsatira malangizo a Yehova pa moyo wake. (Genesis 6:9; 1 Petro 3:20) Mofanana ndi zimenezo, kuti nafenso tidzapulumuke mapeto a dziko lino tifunika ‘kusamalira malangizo a Mulungu mwachangu,’ kapena kuti kuchita chifuniro chake.—Salmo 119:4.
4. Kodi chofunika n’chiyani kuti tikhale achimwemwe komanso kuti zinthu zitiyendere bwino pamoyo wathu?
4 Yehova sadzatisiya konse ngati ‘tikumuyamika Salmo 119:7, 8) Mulungu sanamusiye Yoswa, mtsogoleri wa Aisrayeli amene anamvera malangizo akuti azilingirira ‘buku la chilamulo usana ndi usiku, kuti achite zonse zolembedwamo.’ Chifukwa chotsatira malangizo amenewa, zinthu zinamuyendera bwino ndipo anatha kuchita zinthu mwanzeru. (Yoswa 1:8) Cha kumapeto kwa moyo wake, Yoswa anali akuyamikabe Mulungu ndipo analimbikitsa Aisrayeli kuti: “Mudziwa m’mitima yanu yonse, ndi m’moyo mwa inu nonse, kuti pa mawu okoma onse Yehova Mulungu wanu anawanena za inu sanagwa padera mawu amodzi.” (Yoswa 23:14) Monga momwe zinalili kwa Yoswa ndiponso kwa amene analemba Salmo 119, ifenso tingakhale achimwemwe ndiponso zinthu zingatiyendere bwino pamoyo wathu tikamatamanda Yehova ndi kukhulupirira mawu ake.
ndi mtima woongoka ndi kusamalira malemba ake.’ (Mawu a Yehova Amatithandiza Kukhala Oyera
5. (a) Fotokozani zomwe zimachititsa kuti tithe kukhala oyera mwauzimu. (b) Kodi wachinyamata amene wachita tchimo lalikulu angathandizidwe motani?
5 Tingathe kukhala oyera mwauzimu mwa kusamalira mayendedwe athu monga mwa mawu a Mulungu. (Salmo 119:9-16) Izi zingatheke ngakhale pamene makolo athu sanatipatse chitsanzo chabwino. Ngakhale kuti bambo ake a Hezekiya anali olambira mafano, Hezekiya ‘anayeretsa mayendedwe ake,’ mwina posiya kutsatira njira zachikunja. Tiyerekezere kuti wachinyamata amene akutumikira Mulungu masiku ano wachita tchimo lalikulu. Kulapa, kupemphera, thandizo la makolo ake, ndiponso thandizo lachikondi la akulu achikristu zingamuthandize ‘kuyeretsa mayendedwe ake ndi kuwasamalira’ monga mmene Hezekiya anachitira.—Yakobo 5:13-15.
6. Kodi ndi akazi ati amene ‘anayeretsa mayendedwe awo ndi kuwasamalira monga mwa mawu a Mulungu’?
6 Ngakhale kuti Rahabi ndi Rute anakhalako zaka zambirimbiri Salmo 119 lisanalembedwe, iwo ‘anayeretsa mayendedwe awo.’ Rahabi anali mkazi wadama wachikanani, koma anadziwika chifukwa cha chikhulupiriro chake monga wolambira Yehova. (Ahebri 11:30, 31) Rute, yemwe anali mkazi wachimoabu anasiya milungu yake, nayamba kutumikira Yehova ndi kutsatira Chilamulo chimene Mulungu anapatsa mtundu wa Israyeli. (Rute 1:14-17; 4:9-13) Akazi onsewa, omwe sanali Aisrayeli ‘anasamalira mayendedwe awo monga mwa mawu a Mulungu’ ndipo analandira ulemu waukulu wokhala makolo achikazi a Yesu Kristu.—Mateyu 1:1, 4-6.
7. Kodi Danieli ndi anyamata ena atatu achihebri anasonyeza motani chitsanzo chabwino cha kukhalabe oyera mwauzimu?
7 “Ndingaliro ya mtima wa munthu ili yoipa kuyambira pa unyamata wake,” komabe achinyamata angayende m’njira yoyera m’dziko loipa lolamulidwa ndi Satana lino. (Genesis 8:21; 1 Yohane 5:19) Pamene Danieli limodzi ndi anyamata ena atatu achihebri anali akapolo ku Babulo, ‘anasamalira mayendedwe awo monga mwa mawu a Mulungu.’ Mwachitsanzo, iwo sanafune kudzidetsa “ndi chakudya cha mfumu.” (Danieli 1:6-10) Ababulo ankadya nyama zodetsedwa, zoletsedwa m’Chilamulo cha Mose. (Levitiko 11:1-31; 20:24-26) Kawirikawiri sanali kukhetsa magazi nyama zimene anali kupha, choncho mwa kudya nyama zosakhetsa magazizo ankaswa chilamulo cha Mulungu pankhani ya magazi. (Genesis 9:3, 4) Choncho n’zosadabwitsa kuti Ahebri anayiwo sanalole kudya chakudya cha mfumu. Anyamata oopa Mulungu amenewo anakhalabe oyera mwauzimu ndipo mwa kuchita zimenezi anapereka chitsanzo chabwino zedi kwa ife.
Mawu a Mulungu Amatithandiza Kukhala Okhulupirika
8. Kodi tifunika kukhala ndi mtima wotani ndiponso kudziwa chiyani kuti tithe kumvetsa bwino chilamulo cha Mulungu ndi kuchigwiritsa ntchito?
8 Kukonda mawu a Mulungu ndi chinthu chofunika kwambiri chomwe chingatithandize kukhalabe okhulupirika kwa Yehova. (Salmo 119:17-24) Ngati ndife ofanana ndi wamasalmo wouziridwayu, tidzakhala ofunitsitsa kumvetsetsa “zodabwitsa” za m’chilamulo cha Mulungu. Nthawi zonse ‘tidzakhumba maweruzo a Yehova’ ndi kusonyeza kuti tikukondwera ndi zikumbutso zake. (Salmo 119:18, 20, 24) Ngati tangodzipereka kumene kwa Yehova, kodi ‘takulitsa chilakolako cha mkaka wosasukuluka wa mawu’? (1 Petro 2:1, 2, NW) Tifunika kumvetsetsa ziphunzitso zikuluzikulu zoyambirira za m’Baibulo kuti tithe kumvetsa bwino chilamulo cha Mulungu ndi kuchigwiritsa ntchito.
9. Kodi tiyenera kuchita chiyani ngati zofuna za anthu zikutsutsana ndi malamulo a Mulungu?
9 N’kutheka kuti timakonda zikumbutso za Mulungu, koma bwanji ngati “nduna” zikutsutsana nafe pa zifukwa zina? (Salmo 119:23, 24) Masiku ano, anthu aulamuliro kawirikawiri amayesa kutikakamiza kuti tinyalanyaze malamulo a Mulungu n’kutsatira malamulo a anthu. Kodi tidzachita chiyani ngati zofuna za anthu zikutsutsana ndi chifuniro cha Mulungu? Kukonda kwathu mawu a Mulungu kudzatithandiza kukhalabe okhulupirika kwa Yehova. Mofanana ndi atumwi a Yesu Kristu omwe anali kuzunzidwa, tidzanena kuti: “Tiyenera kumvera Mulungu koposa anthu.”—Machitidwe 5:29.
10, 11. Fotokozani mmene tingakhalirebe okhulupirika kwa Yehova pamene tikukumana ndi ziyeso zovuta kwambiri.
10 N’zotheka kukhalabe okhulupirika kwa Yehova ngakhale pamene tikukumana ndi ziyeso zovuta kwambiri. (Salmo 119:25-32) Kuti tithe kukhalabe okhulupirika kwa Mulungu, tiyenera kukhala ofunitsitsa kuphunzira ndi kupemphera moona mtima kuti atipatse malangizo ake. Tiyeneranso kusankha “njira yokhulupirika.”—Salmo 119:26, 30.
11 Hezekiya, amene n’kutheka kuti ndiye analemba Salmo 119, anasankha “njira yokhulupirika.” Iye anachita zimenezi ngakhale kuti anali pakati pa olambira onyenga komanso mwina anali kunyozedwa ndi anthu okhala m’nyumba yachifumu. Mosakayikira, ‘moyo wake unasungunuka ndi chisoni’ chifukwa cha zochitika zoterezi. (Salmo 119:28) Komabe Hezekiya anakhulupirira Mulungu, anali mfumu yabwino, ndipo anachita “zowongoka pamaso pa Yehova.” (2 Mafumu 18:1-5) Tikadalira Mulungu, nafenso tidzapirira ziyeso ndi kukhalabe okhulupirika kwa Mulungu.—Yakobo 1:5-8.
Mawu a Yehova Amatilimbitsa Mtima
12. Kodi ifeyo patokha tingagwiritse ntchito motani lemba la Salmo 119:36, 37?
12 Kutsatira mawu a Mulungu kumatilimbitsa mtima. Kulimba mtima kumeneku n’kofunika kuti tipirire ziyeso pa moyo wathu. (Salmo 119:33-40) Modzichepetsa timafunafuna malangizo a Yehova kuti tithe kusunga malamulo ake ‘ndi mtima wonse.’ (Salmo 119:33, 34) Mofanana ndi wamasalmoyu, timapempha Mulungu kuti: “Lingitsani mtima wanga ku [zikumbutso] zanu, si ku chisiriro ayi” kapena kuti, ku mapindu achinyengo. (Salmo 119:36) Monga momwe mtumwi Paulo anachitira, ife “tili nacho chikumbumtima chokoma m’zonse,” kapena kuti, timachita zinthu zonse moona mtima. (Ahebri 13:18) Ngati bwana wathu kuntchito akufuna kuti tichite zinthu zachinyengo, timalimba mtima ndi kumamatira malangizo a Mulungu, ndipo nthawi zonse Yehova amadalitsa kulimba mtima koteroko. Ndipotu amatithandiza kupewa zilakolako zonse zoipa. Chotero pemphero lathu likhale lakuti: “Muchititse mlubza maso anga ndisapenye zachabe.” (Salmo 119:37) Chilichonse chimene Mulungu amadana nacho, sitingafune n’komwe kuchiona ngati chabwino. (Salmo 97:10) Mwa zina, pemphero limeneli lingatithandize kupewa zinthu zolaula ndi zinthu zokhudzana ndi kukhulupirira mizimu.—1 Akorinto 6:9, 10; Chivumbulutso 21:8.
13. Kodi atumwi a Yesu omwe anali kuzunzidwa chinawalimbitsa mtima n’chiyani kuti apitirize kulalikira mopanda mantha?
13 Kudziwa molondola mawu a Mulungu kumatithandiza kuti tithe kulalikira molimba mtima. (Salmo 119:41-48) Ndipotu timafunikadi kulimba mtima kuti ‘tikhale nawo mawu akuyankha wotitonza.’ (Salmo 119:42) Nthawi zina, tingafanane ndi ophunzira a Yesu omwe anali kuzunzidwa. Iwo anapemphera kuti: “Ambuye, . . . patsani kwa akapolo anu alankhule mawu anu ndi kulimbika mtima konse.” Kodi zotsatira zake zinali zotani? “Anadzazidwa onse ndi Mzimu Woyera, nalankhula mawu a Mulungu molimbika mtima.” Ambuye Mfumu yemweyo amatilimbitsa mtima nafenso kuti tilankhule mawu ake mopanda mantha.—Machitidwe 4:24-31.
14. N’chiyani chimene chimatithandiza kulalikira molimba mtima monga mmene Paulo anachitira?
14 Ngati timakonda “mawu a choonadi” ndi ‘kusamalira malamulo a Mulungu chisamalire,’ tidzatha kulimba mtima ndi kulalikira mopanda manyazi. (Salmo 119:43, 44) Tikamaphunzira Mawu olembedwa a Mulungu mwakhama, timakhala okonzekera ‘kulankhulanso za [zikumbutso] zake pamaso pa mafumu.’ (Salmo 119:46) Pemphero komanso mzimu wa Yehova zidzatithandizanso kulankhula zinthu zoyenera m’njira yoyenera. (Mateyu 10:16-20; Akolose 4:6) Molimba mtima Paulo analankhula za zikumbutso za Mulungu kwa mafumu a m’zaka 100 zoyambirira. Mwachitsanzo, anachitira umboni kwa kazembe wachiroma Felike, amene ‘anamvetsera kwa iye za chikhulupiriro cha Kristu Yesu.’ (Machitidwe 24:24, 25) Paulo anachitiranso umboni pamaso pa kazembe Festo ndi mfumu Agripa. (Machitidwe 25:22–26:32) Ndi thandizo la Yehova, nafenso tingakhale mboni zolimba mtima, zosachita manyazi ndi “uthenga wabwino.”—Aroma 1:16.
Mawu a Mulungu Amatitonthoza
15. Kodi Mawu a Mulungu angatitonthoze bwanji pamene ena akutinyoza?
15 Mawu a Yehova amatitonthoza nthawi zonse. (Salmo 119:49-56) Nthawi zina timafunikiradi kwambiri kutonthozedwa. Ngakhale kuti timalankhula molimba mtima monga Mboni za Yehova, nthawi zina “odzikuza,” kapena kuti anthu omwe amachita zinthu modzitukumula pamaso pa Mulungu, ‘amatinyoza kwambiri.’ (Salmo 119:51) Komabe, pamene tikupemphera tingakumbukire zinthu zabwino zopezeka m’Mawu a Mulungu, ndipo zimenezi ‘tingadzitonthoze’ nazo. (Salmo 119:52) Popemphera tingakumbukire lamulo kapena mfundo ya m’Malemba yomwe ingatitonthoze ndi kutithandiza kukhala olimba mtima m’nthawi yovuta.
16. Kodi n’chiyani chimene atumiki a Mulungu sanachite ngakhale anali kuzunzidwa?
16 Anthu odzikuza amene ankanyoza wamasalmoyu anali Aisrayeli, anthu a mtundu wodzipereka kwa Mulungu. Zinali zomvetsa chisoni kwabasi! Salmo 119:51) Pamene anali kuzunzidwa ndi Anazi kapena kuzunzidwa m’njira zina pa zaka zambiri zapitazi, atumiki a Mulungu ambirimbiri anakana kupatuka pa malamulo ndi mfundo zamakhalidwe abwino zopezeka m’Mawu a Mulungu. (Yohane 15:18-21) Ndipotu kumvera Yehova sikolemetsa, chifukwa kwa ife malemba ake ali ngati nyimbo zolimbikitsa.—Salmo 119:54; 1 Yohane 5:3.
Koma mosiyana ndi iwowo, tiyeni tikhale otsimikiza mtima kusapatuka pa chilamulo cha Mulungu. (Muziyamikira Mawu a Yehova
17. Kodi kuyamikira mawu a Mulungu kumatilimbikitsa kuchita chiyani?
17 Timasonyeza kuyamikira mawu a Mulungu mwa kutsatira mawuwo. (Salmo 119:57-64) Wamasalmo analonjeza kuti ‘adzasunga mawu a Yehova,’ ndipo ngakhale ‘pakati pa usiku ankadzuka ndi kuyamika Mulungu chifukwa cha maweruzo Ake olungama.’ Ngati titadzuka usiku, umenewutu ungakhale mpata wabwino kwabasi woyamika Mulungu m’pemphero. (Salmo 119:57, 62) Kuyamikira kwambiri mawu a Mulungu kumatilimbikitsa kufunafuna ziphunzitso za Mulungu ndipo kumatithandiza ‘kuyanjana nawo akuopa Yehova,’ anthu amene amaopa ndi kulemekeza Mulungu. (Salmo 119:63, 64) Kodi padziko lapansi pangakhale mabwenzi abwino kuposa amenewa?
18. Kodi Yehova amayankha motani mapemphero athu pamene ‘takulungidwa nazo zingwe za oipa’?
18 Tikamapemphera ndi mtima wathu wonse ndi kupempha Yehova modzichepetsa kuti atiphunzitse, ndiye kuti ‘tikupembedzera pankhope pake’ kuti atichitire chifundo. Timafunika kupemphera makamaka pamene ‘takulungidwa nazo zingwe za oipa.’ (Salmo 119:58, 61) Yehova angadule zingwe za adani zoletsa ntchito yathu ndi kutimasula kuti tipitirize ntchito yolalikira Ufumu ndi kupanga ophunzira. (Mateyu 24:14; 28:19, 20) Izi zachitika mobwerezabwereza m’mayiko omwe ntchito yathu inali yoletsedwa.
Khulupirirani Mawu a Mulungu
19, 20. Kodi kuzunzidwa kungatikomere motani?
19 Kukhulupirira Mulungu ndi mawu ake kumatithandiza kupirira chizunzo ndi kupitiriza kuchita chifuniro chake. (Salmo 119:65-72) Ngakhale kuti anthu odzikuza ‘anam’pangira bodza,’ wamasalmoyu anaimba kuti: “Kundikomera kuti ndinazunzidwa.” (Salmo 119:66, 69, 71) Kodi kuzunzidwa kungamukomere motani mtumiki aliyense wa Yehova?
20 Pamene tikuzunzidwa, mosakayikira timapemphera kwa Yehova moona mtima, ndipo zimenezi zimatithandiza kuti tiyandikire kwambiri kwa iye. Tingathe nthawi yochuluka tikuphunzira Mawu olembedwa a Mulungu ndipo tingayesetse mwakhama kuwagwiritsa ntchito. Izi zimatithandiza kukhala ndi moyo wachimwemwe kwambiri kuposa kale. Koma bwanji ngati kuzunzidwako kwatichititsa kuti tisonyeze makhalidwe oipa, monga kusaleza mtima ndi kudzikuza? Pemphero loona mtima komanso thandizo la Mawu a Mulungu ndi mzimu wake, zingatithandize kuthetsa mavuto amenewa ndi ‘kuvala umunthu watsopano’ mokwanira. (Akolose 3:9-14) Komanso, tikamapirira chizunzo chikhulupiriro chathu chimalimba. (1 Petro 1:6, 7) Paulo anapindula ndi masautso amene anakumana nawo chifukwa chakuti anam’thandiza kudalira kwambiri Yehova. (2 Akorinto 1:8-10) Kodi timalola kuti masautso amene tikukumana nawo atipindulitse?
Khulupirirani Yehova Nthawi Zonse
21. Kodi chimachitika n’chiyani Mulungu akachititsa manyazi anthu odzikuza?
21 Mawu a Mulungu amatipatsa zifukwa zomveka zokhulupirira Yehova. (Salmo 119:73-80) Ngati timakhulupiriradi Mlengi wathu moona mtima, sitidzachita manyazi. Koma chifukwa cha zimene ena amatichitira, timafunika kulimbikitsidwa ndipo tingafune kupemphera kuti: “Odzikuza achite manyazi.” (Salmo 119:76-78) Yehova akachititsa manyazi anthu oterewa, njira zawo zoipa zimaonekera poyera ndipo dzina lake loyera limayeretsedwa. Ndife otsimikiza kuti ozunza anthu a Mulungu sangapinduledi kalikonse. Mwachitsanzo, sangathe ndipo sadzatha kufafaniza Mboni za Yehova, zomwe zimakhulupirira Mulungu ndi mtima wawo wonse.—Miyambo 3:5, 6.
22. Kodi wamasalmo anafanana motani ndi “thumba lofukirira”?
22 Mawu a Mulungu amalimbitsa chikhulupiriro chathu mwa iye pamene tikuzunzidwa. (Salmo 119:81-88) Chifukwa chozunzidwa ndi anthu odzikuza, wamasalmo anadzifanizira ndi “thumba lofukirira.” (Salmo 119:83, 86) M’nthawi za m’Baibulo, ankagwiritsa ntchito matumba a zikopa zanyama akafuna kusunga madzi, vinyo ndi zinthu zina zamadzimadzi. Matumba amenewa akakhala kuti sakugwiritsidwa ntchito ankatha kukhwinyata chifukwa cha utsi ngati awapachika m’khitchini. Kodi nthawi zina mumamva ngati ndinu “thumba lofukirira,” chifukwa chokumana ndi mavuto kapena chizunzo? Ngati ndi choncho, khulupirirani Yehova ndipo muzipemphera kuti: “Mundipatse moyo monga mwa chifundo chanu; ndipo ndidzasamalira mboni ya pakamwa panu.”—Salmo 119:88.
23. Kodi mu Salmo 119:1-88 taphunziramo chiyani, nanga tidzifunse chiyani pamene tikukonzekera kuphunzira Salmo 119:89-176?
23 Zomwe taphunzira m’chigawo choyambachi cha Salmo 119 zikusonyeza kuti Yehova amachitira chifundo atumiki ake chifukwa chakuti iwo amakhulupirira mawu ake ndipo amakonda malemba, zikumbutso, ndi malamulo ake. (Salmo 119:16, 47, 64, 70, 77, 88) Mulungu amasangalala akaona anthu odzipereka kwa iye akusamala mayendedwe awo monga mwa mawu ake. (Salmo 119:9, 17, 41, 42) Pamene mukukonzekera kuphunzira mbali yotsala ya salmo lolimbikitsali, mudzifunse kuti, ‘Kodi ndimaloladi kuti mawu a Yehova aunike njira yanga?’
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 2 Apa tikungonena za uthenga wa Yehova, osati zonse zopezeka m’Mawu a Mulungu, Baibulo.
Kodi Mungayankhe Bwanji?
• Kodi n’chiyani chimene chimatipatsa chimwemwe chenicheni?
• Kodi mawu a Yehova amatithandiza bwanji kukhala oyera mwauzimu?
• Kodi mawu a Mulungu amatilimbitsa mtima ndi kutitonthoza motani?
• N’chifukwa chiyani tiyenera kukhulupirira Yehova ndi mawu ake?
[Mafunso]
[Zithunzi patsamba 11]
Rute, Rahabi, ndi anyamata achihebri omwe anali ku ukapolo ku Babulo anachita ‘mosamala monga mwa mawu a Mulungu’
[Chithunzi patsamba 12]
Molimba mtima Paulo ‘analankhula za zikumbutso za Mulungu pamaso pa mafumu’