Kutamanda Yehova ku Sukulu
Kutamanda Yehova ku Sukulu
PA DZIKO lonse lapansi, ana omwe ndi Mboni za Yehova akupeza njira zotamandira Mulungu ku sukulu. Ndipo akuchita zimenezi mwa zolankhula zawo ndi zochita zawo. Taonani zina zimene zinachitika zosonyeza changu chawo pamene ali achinyamata.
Mboni ina yachinyamata ku Greece inauzidwa kuti ilembe lipoti lonena za kuwononga mpweya wa dziko lapansi. Atafufuza mu Watch Tower Publications Index, anapeza mfundo zofunika m’magazini ya Galamukani! Ndipo pamapeto pa lipoti lake anasonyeza kuti mfundo zimene analembazo anazitenga m’magazini ya Galamukani! Mphunzitsi wake anamuuza kuti lipoti lake linali limodzi la malipoti abwino kwambiri amene anawawerengapo. Mphunzitsiyo panthawi ina anagwiritsa ntchito mfundozo pamsonkhano wa aphunzitsi ndipo zinali zothandiza. Mlongo wachinyamatayo anagawira mphunzitsiyo magazini ena a Galamukani! kuphatikizapo yomwe inali ndi nkhani yoti, “Kodi Tidakatani Padakapanda Aphunzitsi?” Panthawi ina m’kalasi, mphunzitsiyo anayamikira magazini ya Galamukani! moti ophunzira ena anayamba kupempha magaziniwo. Zimenezi zinachititsa mlongoyo kubweretsa magazini ena ku sukulu kuti ophunzirawo awawerenge.
Ku Benin mu Africa muno, Mkristu wina wachinyamata anakumana ndi vuto la mtundu wina. Malinga ndi mmene anali kuchitira pasukulupo, makolo a ophunzira a pa sukulupo anagwirizana zolipira aphunzitsi ena apadera kuti aziphunzitsa anawo maphunziro omwe anali ovuta n’cholinga choti akonzekere mayeso. Koma aphunzitsi apaderawo anasankha kumaphunzitsa Loweruka m’mawa. Mboni yachinyamata ija inakana, ndipo inati: “Loweruka m’mawa ndi nthawi imene mpingo wathu wonse umalalikira pamodzi. Pa masiku onse a pamlungu ndi nthawi yokhayo imene ndimasangalala kwambiri ndipo sindingaisinthanitse ndi chilichonse.” Bambo ake, amene anali kholo lopanda mkazi komanso Mboni, anavomereza ndipo anayesa kupempha gulu limodzi la makolo ndi aphunzitsi apadera kuti asinthe nthawiyo. Koma onse anakana. Msungwanayu anasankha kusachita nawo maphunziro apaderawo. M’malo mwake iye anali kulalikira limodzi ndi mpingo. Anzake a m’kalasi anali kumunyoza ndi kumuuza kuti asiye zolalalikira ndiponso zolambira Mulungu wakeyo. Iwo anali otsimikiza kuti adzalephera mayeso. Koma zomwe zinachitika n’zoti, ophunzira omwe anali ndi aphunzitsi apadera analephera mayeso, pamene mlongo wathu wachinyamata anakhoza. Ndipo kunyoza konse kunathera pomwepo. Ophunzira aja tsopano anayamba kumuuza kuti, “Upitirize kutumikira Mulungu wako.”
Ku Czech Republic, mtsikana wa zaka 12 anafunika kulemba lipoti lofotokoza buku lina lililonse. Amayi ake anamulimbikitsa kuti agwiritse ntchito buku lakuti Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako. Anayamba lipoti lake ndi mafunso akuti: “Kodi mukuona bwanji? Ndani angakhale munthu wamkulu woposa onse amene anakhalako?” Iye anafotokoza za Yesu, moyo wake ali padziko lapansi, ndiponso zimene anaphunzitsa. Kenako, anafotokoza mutu wakuti, “Phunziro la Kukhululukira.” Mphunzitsi wake mosangalala anati: “Limeneli ndi lipoti labwino kwambiri poliyerekeza ndi ena onse omwe ndamva kwa iwe!” Mphunzitsiyo analandira bukulo moyamikira kwambiri. Ndipo ophunzira anzake ena nawonso anafuna bukulo. Tsiku lotsatira, mtsikanayu anasangalala kwambiri kugawira mabuku 18.
Achinyamata oterowa akupeza chimwemwe chachikulu potamanda Yehova ku sukulu. Ife tonse tiyenera kutsanzira changu cha anyamata amenewa.