Kuthetsa Nzeru kwa Ntchito
Kuthetsa Nzeru kwa Ntchito
“Moyotu umakoma ndi ntchito! Kudziwa kuti ntchito idakalipo n’kosangalatsa zedi.”—Anatero Katherine Mansfield, wolemba mabuku (1888-1923).
KODI mukugwirizana ndi mawu ali pamwambawa ofotokoza ntchito kukhala chinthu chotamandika? Kodi inuyo ntchito mumaiona bwanji? Kodi masiku ogwira ntchito mumawaona kukhala chinthawi chachitali chovuta kupirira kuti mukafike ku mapeto a mlungu amene mumasangalala nawo? Kapena kodi ntchito yanu munafika poikondetsetsa kwambiri moti simuupeza mtima mukapanda kugwira ntchitoyo?
Kwa anthu ambiri, nthawi yawo yochuluka pamene sakugona imathera kuntchito. Ntchito ingalamule malo amene tingakhaleko ndi moyo umene tingakhale nawo. Anthu ambiri amaona kuti ntchito ndi chinthu chimodzi chimene chimatenga gawo lalikulu la moyo wawo, kuchokera paunyamata wawo kufikira nthawi yodzapuma pantchito. Enafe timasangalala kwambiri ndi ntchito yathu. Kwa ena, kuikonda ntchito kumadalira malipiro omwe angalandire kapena ulemerero umene ntchitoyo ingawapatse. Koma palinso ena amene ntchito amaiona ngati pongotayira nthawi, kapena ngati chinthu chongowadyera nthawi.
Pali ena amene amagwira ntchito kuti apeze zofunika pa moyo, komanso pali ena omwe cholinga chawo ndi kugwira ntchito basi. Ena amafa kumene chifukwa cha ntchito. Mwachitsanzo, malinga n’kunena kwa lipoti laposachedwa la bungwe la United Nations, ntchito zimavulaza ndi kupha anthu ambiri “kuposa nkhondo kapena mankhwala osokoneza bongo ndi mowa kuziphatikiza pamodzi.” Poikira ndemanga pa nkhani imeneyi, nyuzipepala ina ya ku London yotchedwa The Guardian inati: “Chaka chilichonse anthu oposa mamiliyoni awiri amamwalira ndi ngozi kapena matenda odza ndi ntchito yawo . . . Fumbi, mankhwala opangira zinthu, phokoso ndi cheza choopsa chotuluka m’zinthu zina zimadzetsa matenda a kansa, mtima ndi sitiroko.” Zochitika zina zokhumudwitsa kwambiri zokhudza ntchito za masiku ano ndi zinthu ngati kulemba ntchito ana ang’onoang’ono komanso kuumiriza anthu kugwira ntchito imene sakufuna.
Komanso, pali kutopa kotheratu chifukwa cha ntchito kumene katswiri wa maganizo, Steven Berglas anakufotokoza. Iye analongosola za munthu amene zinthu zamuyendera bwino kwambiri pantchito yake chifukwa chogwira ntchito molimbika. Kenako munthuyo “amayamba kukhala ndi mantha, nkhawa, kukanika kugwira ntchito kapena kudwala chifukwa cha maganizo. Zonsezo chifukwa choona kuti basi moyo wake wonse wamangika pantchito imene sangasiye ndipo sakusangalalanso nayo.”
Kugwira Ntchito Molimbika N’kosiyana ndi Kugwira Ntchito Mopitirira Muyeso
Popeza kuti anthu ambiri amagwira ntchito zolimba maola ochuluka, m’pofunika kusiyanitsa pakati
pa ogwira ntchito molimbika ndi ogwira ntchito mopitirira muyeso. Ogwira ntchito mopitirira muyeso ambiri amaona kuti akakhala kuntchito ali ku malo achitetezo m’dziko loopsa ndi losadalirikali. Koma ogwira ntchito mwakhama amaona ntchito ngati udindo wofunika ndipo nthawi zina wokhutiritsa. Ogwira ntchito mopitirira muyeso amalola ntchito kuphimba mbali zina zonse za moyo wawo. Koma ogwira ntchito molimbika amadziwa nthawi yoweruka, nthawi yoganizira zinthu zina, ndi nthawi yochita chisangalalo chokumbukira tsiku la ukwati wawo. Ogwira ntchito mopitirira muyeso amamva bwino ndipo zimawalimbikitsa akagwira ntchito mopitirira muyeso, koma ogwira ntchito molimbika satero.Malinga ndi moyo wa masiku ano, n’zovuta kusiyanitsa pakati pa kugwira ntchito molimbika ndi kugwira ntchito mopitirira muyeso. Zili choncho chifukwa kugwira ntchito mopitirira muyeso kumatamandidwa kwambiri. Zipangizo ngati mafoni a m’manja ndi zina zotero zimapangitsa kunyumba kukhala ngati kuntchito komwe. Pamene munthu amatha kugwira ntchito kulikonse kumene ali komanso nthawi iliyonse, ena amafika podzipweteka ndi ntchito.
Kodi ena amaziona bwanji zizolowezi zopweteka zimenezi? Akatswiri a maganizo aona kuti anthu ogwira ntchito modetsa nkhawa ndiponso otopa kwambiri ndi ntchito ayamba kulowetsa zinthu zauzimu pantchito. Magazini ina yotchedwa San Francisco Examiner inati: “Anthu ambiri tsopano amaphatikiza moyo wauzimu ndi ntchito.”
Ponena za malo otchedwa Silicon Valley, ku United States, amene ndiye kuchimake kwa makampani opanga zinthu za sayansi yotsogola kwambiri, lipoti laposachedwapa linati: “Pamene mabwana akuona kuti malo ambiri oimika magalimoto kumalo antchito akukhala opanda kanthu chifukwa cha kuchotsedwa kwa anthu kumene kukupitirirabe, malo oimika magalimoto akucheperachepera kumalo ophunzirira Baibulo madzulo.” Kaya zimenezo zidzakhala ndi zotsatira zotani, koma anthu ambiri padziko lonse akuona kuti Baibulo limawathandiza kuona ntchito kukhala yofunikira, zimene zimawathandizanso kukhala osangalala ndi moyo.
Kodi Baibulo lingatithandize motani kuona ntchito moyenerera? Kodi pali mfundo za m’Malemba zomwe zingatithandize kupirira mavuto a pantchito za masiku ano? Nkhani yotsatirayi iyankha mafunso amenewa.