Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mudzawalitsa Ulemerero wa Mulungu?

Kodi Mudzawalitsa Ulemerero wa Mulungu?

Kodi Mudzawalitsa Ulemerero wa Mulungu?

‘Timawalitsa . . . ulemerero wa Yehova.’​2 AKORINTO 3:18, NW.

1. Kodi Mose anaona chiyani, kenako panachitika zotani?

ANALITU masomphenya ochititsa nthumanzi imene palibe munthu wina aliyense amene anagwidwapo nayo. Mose ali yekhayekha m’mwambamo m’phiri la Sinai, anapatsidwa mwayi wapadera kwambiri. Analoledwa kuona zimene munthu aliyense anali asanaonepo​—ulemerero wa Yehova. Koma sikuti Mose anaona Yehova mwachindunji ayi. Maonekedwe a Mulungu ndi aulemerero woopsa moti palibe munthu angamuone ndi kukhalabe ndi moyo. M’malo mwake, Yehova anaphimba Mose ndi “dzanja” lake pomuteteza kufikira Iye atadutsa, mwachionekere moimiridwa ndi mngelo. Ndiyeno Yehova analola Mose kuona kuwala kotsalira m’mbuyo kwa ulemerero wake. Yehova analankhulanso ndi Mose kupyolera mwa mngelo. Baibulo limafotokoza zimene zinatsatirapo motere: “Ndipo kunali pakutsika Mose pa phiri la Sinai, . . . khungu la nkhope yake linanyezimira popeza iye [Yehova] adalankhula naye.”​—Eksodo 33:18–34:7, 29.

2. Kodi mtumwi Paulo analembanji za ulemerero umene Akristu amawalitsa?

2 Tayerekezani kuti munali limodzi ndi Mose pamwamba m’phirimo. Ha! Mukanachitatu nthumanzi kwambiri poona ulemerero wothobwa m’maso wa Wamphamvuyonseyo, ndi pakumva mawu ake! Ukanakhala mwayi bwanji, kutsikira limodzi ndi Mose m’phiri la Sinai! Inde, kuyenda limodzi ndi nkhoswe yeniyeniyo ya chipangano cha Chilamulo! Koma kodi mukudziwa kuti Akristu oona amawalitsa ulemelero wa Mulungu kuposa mmene Mose anachitira? Mfundo yochititsa chidwi imeneyi ikupezeka m’kalata imene mtumwi Paulo analemba. Iye analemba kuti Akristu odzozedwa amawalitsa “monga mwa kalilore ulemerero wa Ambuye [Yehova].” (2 Akorinto 3:7, 8, 18) M’lingaliro linanso, ngakhale Akristu omwe ali ndi chiyembekezo chodzakhala padziko lapansi, nawonso amawalitsa ulemerero wa Mulungu.

Mmene Akristu Amawalitsira Ulemerero wa Mulungu

3. Kodi Yehova tam’dziwa motani kuposa mmene Mose anam’dziwira?

3 Kodi tingawalitse motani ulemerero wa Mulungu? N’zoona kuti ife sitinamuonepo Yehova kapena kumva mawu ake mmene Mose anachitira. Komabe, ife tadziwa zambiri za Yehova kuposa mmene Mose anam’dziwira. Yesu anadzaonekera monga Mesiya patapita zaka zambirimbiri kuchokera pamene Mose anamwalira, zaka pafupifupi 1,500. Kuwonjezera pamenepo, Mose sakanatha kudziwa mmene Chilamulo chinali kudzakwaniritsidwira mwa Yesu, amene anamwalira kuti awombole anthu ku ukapolo woipitsitsa wa uchimo ndi imfa. (Aroma 5:20, 21; Agalatiya 3:19) Ndiponso, Mose analibe chithunzi chokwanira cha ulemerero wonse wa cholinga cha Yehova. Inde, cholinga chokhudza Ufumu wa Mesiya, ndi Paradaiso amene Ufumuwo udzabweretsa. Choncho ifeyo timaona ulemerero wa Yehova ndi maso a chikhulupiriro chozikidwa pa ziphunzitso za m’Baibulo, osati ndi maso athu enieni. Komanso, sitinamve mawu a Yehova kudzera mwa mngelo ayi, koma kupyolera m’Baibulo. Inde, makamaka Mauthenga Abwino, amene amafotokoza mochititsa chidwi zimene Yesu anaphunzitsa ndi utumiki wake.

4. (a) Kodi Akristu odzozedwa amawalitsa motani ulemerero wa Mulungu? (b) Kodi amene ali ndi chiyembekezo cha moyo wosatha padziko lapansi, nawonso angawalitse ulemerero wa Mulungu m’njira zotani?

4 Ngakhale kuti Akristu sawalitsa ulemerero wa Mulungu mwa kunyezimira kwenikweni kwa nkhope zawo, nkhope zawo zimawalabe pamene auza ena za makhalidwe aulemerero a Yehova ndi zolinga zake. Ponena za masiku athu ano, mneneri Yesaya analosera kuti anthu a Mulungu “adzabukitsa ulemerero [wa Yehova] pakati pa amitundu.” (Yesaya 66:19) Ndiponso, pa 2 Akorinto 4:1, 2, timawerenga kuti: “Popeza tili nawo utumiki . . .  takaniza zobisika za manyazi, osayendayenda mochenjerera, kapena kuchita nawo mawu a Mulungu konyenga; koma ndi maonekedwe a choonadi tidzivomeretsa tokha ku chikumbumtima cha anthu onse pamaso pa Mulungu.” Paulo anali kunena kwenikweni za Akristu odzozedwa, amene ndi “atumiki a pangano latsopano.” (2 Akorinto 3:6) Koma utumiki wawo wakhudzanso anthu osawerengeka omwe apeza chiyembekezo cha moyo wosatha padziko lapansi. Mwa utumiki wawo, magulu onse awiriwa amawalitsa ulemerero wa Yehova. Amatero mwa zimene amaphunzitsa komanso mwa makhalidwe awo. Ndithudi, ndi udindo wathu, komanso mwayi wathu kuwalitsa ulemerero wa Mulungu Wam’mwambamwambayo!

5. Kodi kupita patsogolo kwathu kwauzimu ndi umboni wa chiyani?

5 Masiku ano, ulemerero wa uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulugu ukulalikidwa m’madera onse a dziko lapansi kumene kuli anthu, ngati mmene Yesu ananenera. (Mateyu 24:14) Anthu ochokera m’mayiko, mitundu, mafuko, ndi malilime osiyanasiyana alabadira uthenga wabwino mosangalala, ndipo asintha miyoyo yawo kuti achite chifuniro cha Mulungu. (Aroma 12:2; Chivumbulutso 7:9) Mofanana ndi Akristu oyambirirawo, iwo sangaleke kulankhula zinthu zimene aona ndi kumva. (Machitidwe 4:20) Anthu opitirira sikisi miliyoni, chiwerengero choposa cha panthawi ina iliyonse m’mbuyomu, akuwalitsa ulemerero wa Mulungu lerolino. Kodi ndinu mmodzi wa iwo? Kupita patsogolo kwa anthu a Mulungu kukupereka umboni wokhutiritsa wakuti Yehova akuwadalitsa ndi kuwateteza. Tikaona magulu amphamvu omwe akulimbana nafe, zikuonekeratu kuti mzimu wa Yehova uli pa ife. Tiyeni tsopano tione chifukwa chake mzimu wa Yehova uli pa ife.

Anthu a Mulungu Sadzatsekedwa Pakamwa

6. N’chifukwa chiyani chikhulupiriro ndi kulimba mtima zili zofunika kuti munthu aime kumbali ya Yehova?

6 Tayerekezani kuti mukufunika kukhoti kuti mukapereke umboni pa mlandu wa munthu wina amene ndi chigawenga choopsa. Mukudziwa kuti munthuyo ali ndi gulu lamphamvu kwambiri, ndipo adzachita chilichonse chotheka kuti mlandu usam’gwere. Kuti mukapereke umboni wotsutsana ndi chigawenga choterocho, mufunikira kulimba mtima komanso chitsimikiziro chakuti boma lidzakutetezani. Mmenemo ndi mmene zilili kwa ife. Pochitira umboni za Yehova ndi zolinga zake, timapereka umboni wotsutsa Satana Mdyerekezi. Timakhala tikumuulula kuti ndi waumbanda ndiponso wabodza, amene akusocheretsa anthu onse okhala padziko lapansi. (Yohane 8:44; Chivumbulutso 12:9) Kuti munthu aime kumbali ya Yehova ndi kutsutsana ndi Mdyerekezi, afunika kukhala ndi chikhulupiriro komanso kulimba mtima.

7. Kodi Satana ali ndi mphamvu zotani, ndipo amayesa kuchita chiyani?

7 Inde, Yehova ndiye Wamkulu Koposa. Mphamvu za Satana si kanthu poziyerekeza ndi za Yehova. Tikhale otsimikiza kuti Yehova siwokhoza chabe kutiteteza pamene tikum’tumikira mokhulupirika, koma alinso wofunitsitsa kutero. (2 Mbiri 16:9) Komabe, Satana ndiye wolamulira wa ziwanda ndi dziko lonse la anthu otalikirana ndi Mulungu. (Mateyu 12:24, 26; Yohane 14:30) Popeza kuti Satana ali kuno kudziko lapansi ndipo ali ndi “udani waukulu,” iye amalimbana koopsa ndi atumiki a Yehova. Amagwiritsanso ntchito dziko limene akulilamulira poyesa kuwatseka pakamwa onse amene amalalikira uthenga wabwino. (Chivumbulutso 12:7-9, 12, 17) Kodi amachita motani zimenezo? Amatero makamaka m’njira zitatu.

8, 9. Kodi Satana amagwiritsa ntchito motani chikondi cholakwika, ndipo n’chifukwa chiyani tiyenera kusamala posankha anthu ocheza nawo?

8 Njira imodzi imene dziko la Satana limayesera kutisokoneza ndiyo mwa zinthu zofunika pa moyo. Anthu masiku otsiriza ano ndi okonda ndalama, odzikonda okha, ndi okonda zosangalatsa. Sakonda Mulungu. (2 Timoteo 3:1-4) Pokhala otanganidwa ndi zochitika za tsiku ndi tsiku, anthu ochuluka amakhala ‘osadziwa kanthu’ za uthenga wabwino umene timawalalikira. Alibiretu chidwi m’pang’ono pomwe chophunzira choonadi cha Baibulo. (Mateyu 24:37-39) Maganizo oterowo akhoza kutiyambukira ndi kutipatsa mphwayi pa zinthu zauzimu. Ngati tiyamba kukonda kwambiri zinthu zakuthupi ndi zosangalatsa za moyo, chikondi chathu kwa Mulungu chidzazilala.​—Mateyu 24:12.

9 Pachifukwa chimenechi, Akristu amakhala osamala posankha anthu ocheza nawo. “Ukayenda ndi anzeru udzakhala wanzeru,” analemba motero Mfumu Solomo. “Koma mnzawo wa opusa adzaphwetekedwa.” (Miyambo 13:20) Tiyenitu ‘tiziyenda’ ndi aja amene amawalitsa ulemerero wa Mulungu. Kunena zoona, zimakhala zosangalatsa kwambiri! Pamene tisonkhana pamodzi ndi abale ndi alongo athu auzimu pamisonkhano ndi panthawi zina, timalimbikitsidwa ndi chikondi chawo, chikhulupiriro chawo, chisangalalo chawo, ndi nzeru zawo. Mayanjano abwino oterowo amatilimbitsa mtima kuti tilimbikirebe mu utumiki wathu.

10. Kodi Satana waugwiritsa ntchito motani msampha wonyoza anthu owalitsa ulemerero wa Mulungu?

10 Njira yachiwiri imene Satana amayesera kulepheretsa Akristu kuwalitsa ulemerero wa Mulungu ndiyo mwa kuchititsa kuti azinyozedwa. Msampha umenewu suyenera kutidabwitsa. Pamene Yesu Kristu anali padziko lapansi, anthu anamunyoza, anamuseka, anamunyogodola, anamutonza, anamuchitira chipongwe, ngakhalenso kumuthira malovu. (Marko 5:40; Luka 16:14; 18:32) Akristu oyambirira nawonso anaseleulidwa. (Machitidwe 2:13; 17:32) Atumiki a Yehova amakono amanyozedwanso mofananamo. Zikugwirizana ndi zimene mtumwi Petro ananena, kuti atumikiwo adzatchedwa “aneneri onama.” Petro anatero kuti, “masiku otsiriza adzafika onyoza ndi kuchita zonyoza, oyenda monga mwa zilakolako za iwo eni, ndi kunena, Lili kuti lonjezano la kudza kwake? Pakuti . . . zonse zikhala monga chiyambire chilengedwe.” (2 Petro 3:3, 4) Anthu a Mulungu amasekedwa kuti amakhwimitsa kwambiri moyo. Anthu amaona makhalidwe olimbikitsidwa m’Baibulo kukhala achikalekale. Ambiri amaona uthenga umene timalalikira kukhala chinthu chopusa. (1 Akorinto 1:18, 19) Akristu amanyozedwa kusukulu, kuntchito, ndipo nthawi zina ngakhale ndi achibale awo. Koma ifeyo sitisunthika m’pang’ono pomwe. M’malo mwake, timapitiriza kuwalitsa ulemerero wa Mulungu mwa kulalikira. Timatero chifukwa timadziwa, ngati mmene Yesu anadziwira, kuti Mawu a Mulungu ndiwo choonadi.​—Yohane 17:17.

11. Kodi Satana wagwiritsa ntchito motani chizunzo poyesa kuwatseka pakamwa Akristu?

11 Msampha wachitatu umene Mdyerekezi amagwiritsa ntchito poyesa kutitseka pakamwa ndiwo kupangitsa anthu kudana nafe kapena kutizunza. Yesu anauza otsatira ake kuti: “Adzakuperekani kunsautso, nadzakuphani; ndipo anthu a mitundu yonse adzadana nanu, chifukwa cha dzina langa.” (Mateyu 24:9) Ndithudi, chifukwa chokhala Mboni za Yehova, takumana ndi mazunzo oopsa m’madera ambiri a dziko lapansi. Tikudziwa kuti kalekalelo, Yehova ananeneratu kuti padzakhala chidani pakati pa anthu otumikira Mulungu ndi aja otumikira Satana Mdyerekezi. (Genesis 3:15) Timadziwanso kuti mwa kukhalabe okhulupirika pamene tikuyesedwa, timapereka umboni wakuti Yehova ndiye Mfumu yoyenerera ya chilengedwe chonse. Kudziwa zimenezi kungatilimbitse ngakhale pokumana ndi mayesero oopsa chotani. Palibe chizunzo chimene chingatitsekeretu pakamwa mtima wathu ukakhala wosasunthika pa kuwalitsa ulemerero wa Mulungu.

12. N’chifukwa chiyani tiyenera kusangalala pamene tikukhalabe okhulupirika poyang’anizana ndi chidani cha Satana?

12 Kodi mumatha kukana zonyengerera za dzikoli ndi kukhalabe wokhulupirika pamene anthu akukunyozani ndi kudana nanu? Ngati mumatero muli ndi chifukwa chabwino chokhalira wosangalala. Yesu anawatsimikizira amene anafuna kum’tsatira kuti: “Odala muli inu mmene adzanyazitsa inu, nadzazunza inu, nadzakunenerani monama zoipa zilizonse chifukwa cha Ine. Sekerani, sangalalani: chifukwa mphoto yanu ndi yaikulu m’Mwamba: pakuti potero anazunza aneneri anakhalawo musanabadwe inu.” (Mateyu 5:11, 12) Kukhulupirika kwanu kumapereka umboni wakuti mzimu woyera wamphamvu wa Yehova uli pa inu, ndipo umakupatsani mphamvu kuti muwalitse ulemerero wake.​—2 Akorinto 12:9.

Yehova Amatithandiza Kupirira

13. Kodi timapirira mu utumiki wathu wachikristu makamaka chifukwa chiyani?

13 Chifukwa chachikulu chimene timapiririra mu utumiki n’chakuti timakonda Yehova, ndipo timasangalala kuwalitsa ulemerero wake. Mwachibadwa anthu amakonda kutsanzira anthu amene amawakonda ndi amene amawalemekeza, ndipo palibe amene tingayenere kumutsanzira kuposa Yehova Mulungu. Chifukwa cha chikondi chake chachikulu, anatumiza Mwana wake padziko lapansi kuti adzaikire umboni choonadi ndi kudzawombola anthu omvera. (Yohane 3:16; 18:37) Mofanana ndi Mulungu, ifenso timakhumba kuti anthu onse, kaya akhale otani, alape kuti adzapulumuke. Ndiye chifukwa chake timalalikira kwa iwo. (2 Petro 3:9) Chikhumbo chathu chimenechi, limodzi ndi mtima umene tili nawo wofuna kutsanzira Mulungu, zimatithandiza kulimbikirabe kuwalitsa ulemerero wake mu utumiki wathu.

14. Kodi Yehova amatilimbikitsa motani kuti tipirire mu utumiki wathu?

14 Komabe, nyonga imene imatithandiza kupirira mu utumiki wathu wachikristu kwenikweni imachokera kwa Yehova. Ndi amene amatichirikiza ndi kutilimbikitsa mwa mzimu wake, gulu lake, ndi Mawu ake, Baibulo. Yehova amapereka “chipiriro” kwa amene akufuna kuwalitsa ulemerero wake. Amayankha mapemphero athu ndipo amatipatsa nzeru zothanira ndi mayesero. (Aroma 15:5; Yakobo 1:5) Komanso, Yehova salola kuti tigwere m’mayesero alionse amene sitingathe kuwapirira. Ngati tidalira Yehova, adzatiikira populumukira kuti tipitirize kuwalitsa ulemerero wake.​—1 Akorinto 10:13.

15. Kodi n’chiyani chimatithandiza kupirira?

15 Kupirira mu utumiki wathu kumapereka umboni wakuti mzimu wa Mulungu uli nafe. Tifanizire chonchi: Yerekezani kuti munthu wina wakupemphani kuti muzikagawira buledi wake waulere khomo ndi khomo. Akukuuzani kuti ndalama zoyendera ndi zofunikira zina mukonza nokha, komanso ntchito imeneyi muziigwira m’nthawi yanu. Koma kungoyamba ntchitoyo mukuona kuti anthu ambiri sakumufuna bulediyo; mpaka ena akulimbana nanu kuti musiye kumugawira. Kodi mukuganiza kuti mungapitirize kugwira ntchito imeneyo mwezi ndi mwezi, chaka ndi chaka? N’zokayikitsa. Komabe, mwina inuyo mwakhala mukudzipereka pa kulengeza uthenga wabwino m’nthawi yanu ndi kuwonongerapo ndalama zanu, kwa zaka zambirimbiri. Chifukwa chiyani? Kodi si chifukwa chakuti mumakonda Yehova, ndi kuti kudzera mwa mzimu wake iye wadalitsa khama lanu pokuthandizani kupirira? Mosakayika konse!

Ntchito Imene Siidzaiwalika

16. Kodi chidzachitika n’chiyani kwa ife ndi amene amatimvetsera ngati tipirira mu utumiki wathu?

16 Utumiki wa pangano latsopano ndi mphatso yosayerekezeka. (2 Akorinto 4:7) Mofananamo, utumiki wachikristu umene nkhosa zina zimachita padziko lonse ndi chuma cha mtengo wapatali. Monga analembera Paulo kwa Timoteo, inunso ngati mupirirabe mu utumiki wanu, ‘mudzadzipulumutsa inu nokha ndi iwo akumva inu.’ (1 Timoteo 4:16) Taganizani tanthauzo la zimenezo. Uthenga wabwino umene mumalalikira umapatsa ena mwayi wodzakhala ndi moyo wosatha. Mukhoza kupalana ubwenzi wolimba ndi anthu amene mumawathandiza mwauzimu. Tangoganizani kusangalatsa kwake, kudzakhala ndi moyo kosatha m’Paradaiso limodzi ndi anthu amene munawathandiza kuphunzira za Mulungu! Kunena zoona, iwo sangadzaiwale zonse zimene munachita powathandiza. Zosangalatsa kwabasi!

17. N’chifukwa chiyani nthawi imene tikukhalamo ili yapadera kwambiri m’mbiri ya anthu?

17 Ife tikukhala m’nthawi yapadera kwambiri m’mbiri ya anthu. Sikudzakhalanso nthawi ina pamene uthenga wabwino udzalalikidwa m’dziko la anthu otalikirana ndi Mulungu. Nowa anakhala m’dziko loterolo, ndipo analiona likuchoka. Ayenera kuti anasangalala kwambiri podziwa kuti anachita chifuniro cha Mulungu mokhulupirika mwa kumanga chingalawa, chimene iye limodzi ndi banja lake anapulumukiramo. (Ahebri 11:7) Inunso mukhoza kukhala ndi chisangalalo choterocho. Taganizani mmene mudzamvere m’dziko latsopano podzayang’ana m’mbuyo ndi kuona ntchito zimene mukuchita m’masiku ano otsiriza. Inde, mudzasangalala podziwa kuti munachita zimene mukanatha zokhudza Ufumuwo.

18. Kodi ndi chitsimikizo ndi chilimbikitso chotani chimene Yehova akupatsa atumiki ake?

18 Choncho, tiyeni tipitirizebe kuwalitsa ulemerero wa Mulungu. Ndi chinthu chimene tidzakumbukira kwamuyaya. Yehova amakumbukiranso ntchito zathu. Baibulo limapereka chilimbikitso ichi: “Mulungu sali wosalungama kuti adzaiwala ntchito yanu, ndi chikondicho mudachionetsera ku dzina lake, umo mudatumikira oyera mtima ndi kuwatumikirabe. Koma tikhumba kuti yense wa inu aonetsere changu chomwechi cholinga ku chiyembekezo chokwanira kufikira chitsiriziro; kuti musakhale aulesi, koma akuwatsanza iwo amene alikulowa malonjezano mwa chikhulupiriro ndi kuleza mtima.”​—Ahebri 6:10-12.

Kodi Mungafotokoze?

• Kodi Akristu amawalitsa motani ulemerero wa Mulungu?

• Kodi ndi misampha yotani imene Satana amagwiritsa ntchito poyesa kutseka pakamwa anthu a Mulungu?

• Kodi pali umboni wotani wosonyeza kuti mzimu wa Mulungu uli nafe?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 15]

Nkhope ya Mose inawalitsa ulemerero

[Zithunzi pamasamba 16, 17]

Timawalitsa ulemerero wa Mulungu mu utumiki wathu