Kuopa Yehova Ndiko Nzeru
Kuopa Yehova Ndiko Nzeru
“MAWU atha; zonse zamveka zatha; opa Mulungu, musunge malamulo ake; pakuti choyenera anthu onse ndi ichi.” (Mlaliki 12:13) Imeneyitu ndi mfundo yozama kwambiri imene Mfumu Solomo ya ku Israyeli wakale inafikapo mouziridwa ndi Mulungu. Kholo lakale Yobu anazindikiranso ubwino woopa Mulungu, chifukwa iye anati: “Tawonani, kuopa Ambuye ndiko nzeru; ndi kupatukana nacho choipa ndiko luntha.”—Yobu 28:28.
Baibulo limagogomezera kwambiri kufunika koopa Yehova. N’chifukwa chiyani kuyamba kuopa Mulungu kuli chinthu chanzeru? Kodi kuopa Mulungu kumatipindulitsa m’njira yotani patokhapatokha komanso monga gulu la olambira oona? Mavesi 26 mpaka 35 a chaputala 14 cha buku la Miyambo amayankha mafunso amenewa. *
Kumatipatsa ‘Chikhulupiriro Cholimba’
Solomo anati: “Wakuopa Yehova akhulupirira kolimba; ndipo ana ake adzakhala ndi pothawirapo.” (Miyambo 14:26) Munthu woopa Mulungu amakhulupirira Yehova yekha basi, yemwe ndi Mulungu wokhulupirika ndiponso wamphamvuyonse. Mpake kuti munthu wotere amakhala n’chikhulupiriro chonse akamaganizira za m’tsogolo. Tsogolo lake limakhala labwino ndiponso lodalitsika.
Komano, kodi tinganene chiyani za tsogolo la anthu amene amakhulupirira dzikoli, zolinga zake, mabungwe ake, mfundo zake, ndiponso chuma chake? Tsogolo lililonse limene anthu oterewa amalakalaka silikhalitsa, chifukwa Baibulo limati: “Dziko lapansi lipita, ndi chilakolako chake; koma iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala ku nthawi zonse.” (1 Yohane 2:17) Motero, kodi pali chifukwa chilichonse choti ifeyo ‘tikondere dziko lapansi, kapena za m’dziko lapansi’?—1 Yohane 2:15.
Kodi makolo oopa Mulungu angachitepo zotani kuti ana awo ‘adzakhale ndi pothawirapo.’ Wamasalmo ananena kuti: “Idzani ananu ndimvereni ine: ndidzakulangizani zakumuopa Yehova.” (Salmo 34:11) Makolo akamaphunzitsa ana awo kuopa Mulungu, mwa chitsanzo chawo ndiponso malangizo, m’posavuta kuti anawo akadzakula adzakhale anthu okhulupirira kwambiri Yehova.—Miyambo 22:6.
Solomo anapitiriza kuti: “Kuopa Yehova ndiko kasupe wa moyo, kupatutsa ku misampha ya imfa.” (Miyambo 14:27) Kuopa Yehova “ndiko kasupe wa moyo” chifukwa choti Mulungu woona ndiye “kasupe wa madzi amoyo.” (Yeremiya 2:13) Kudziwa Yehova ndi Yesu Kristu kungatipatse moyo wosatha. (Yohane 17:3) Kuopa Mulungu kumatithandizanso kupewa misampha ya imfa. Motani? Lemba la Miyambo 13:14 limati: “Malamulo a wanzeru ndiwo kasupe wa moyo, apatutsa ku misampha ya imfa.” Tikamaopa Yehova, kumvera malamulo ake, ndiponso kulola kuti Mawu ake azitsogolera mayendedwe athu, kodi sititetezeka ku makhalidwe ndiponso maganizo oipa amene angatiphetse msanga?
Kumapatsa “Ulemu wa Mfumu”
Kwa nthawi yambiri imene anali kulamulira, Solomo anali mfumu yoopa Mulungu, Miyambo 14:28 limayankha kuti: “Mu unyinji wa anthu muli ulemu wa mfumu; koma popanda anthu kalonga awonongeka.” Timadziwa kuti mfumu ikulamulira bwino poona mmene anthu ake akukhalira. Ngati anthu ambiri akufuna kumalamulidwa ndi mfumuyo, ndiye kuti ndi mfumu yolamulira bwino. Solomo ankalamulira anthu “kuchokera kunyanja [Yofiira] kufikira kunyanja [ya Mediterranean]. Ndi kuchokera ku Mtsinje [wa Firate] kufikira malekezero a dziko lapansi.” (Salmo 72:6-8) Ulamuliro wake unali wa mtendere ndiponso unabweretsa chitukuko chimene anthu anali asanaonepo n’kale lonse. (1 Mafumu 4:24, 25) Ulamuliro wa Solomo unali wabwino kwambiri. Komano anthu akamapanda kusangalala ndi ulamuliro, zimaonetsa kuti wolamulirayo n’ngwachabechabe.
yomveradi Yehova. Choncho ulamuliro wake unali kuyenda bwino. Kodi n’chiyani chimasonyeza kuti mfumu ikulamulira bwino? Lemba laKodi pankhaniyi, tinganenepo chiyani za ulemerero wa Solomo Wamkulu, Mfumu ya Umesiya, yemwe ndi Yesu Kristu? Taganizirani anthu amene iye akulamulira ngakhale panopo. Padziko lonse lapansi, amuna ndi akazi oopa Mulungu opitirira sikisi miliyoni asankha kale kukhala muulamuliro wa Kristu. Iwo amakhulupirira Yesu ndipo amagwirizana polambira Mulungu wamoyo m’choonadi. (Yohane 14:1) Pamapeto pa Ulamuliro wa Zaka 1,000, anthu onse amene Yehova akuwakumbukira adzakhala ataukitsidwa. Motero dziko lapansi laparadaiso lidzakhala ndi anthu osangalala komanso olungama, amene anasonyeza kuyamikira Mfumuyi. Uwutu udzakhala umboni wosatsutsika wakuti ulamuliro wa Kristu wayenda bwino. Tiyeni tiyesetse kugwira mwamphamvu chiyembekezo cha Ufumu chosangalatsachi.
Kumatithandiza Kukhala Auzimu ndi Athanzi
Kuopa Mulungu kungatikhazike mtima pansi ndiponso kutipatsa mtendere m’maganizo. Ichi n’chifukwa chakuti nzeru zimam’pangitsanso munthu kuona njira yabwino kwambiri yoyendetsera zinthu ndiponso kutha kumvetsa bwinobwino zinthu. Lemba la Miyambo 14:29 limati: “Wosakwiya msanga apambana kumvetsa; koma wansontho akuza utsiru.” Kukhala womvetsa kumatithandiza kuzindikira kuti kukwiya mosadziletsa kumasokoneza moyo wathu wauzimu. Zina mwa ntchito zimene zinatchulidwa kuti zingatikanikitse ‘kudzalowa Ufumu wa Mulungu’ ndi “madano, ndewu, kaduka, zopsa mtima, zotetana.” (Agalatiya 5:19-21) Baibulo limatilangiza kuti ngakhale titakwiya pa zifukwa zomveka, tisamasunge chakukhosi. (Aefeso 4:26, 27) Ndipotu mtima wapachala ungatilankhulitse pambali n’kutichititsa zinthu zoduka mutu, zomwe mapeto ake tinganong’oneze nazo bondo.
Potchulapo za mmene mkwiyo umawonongera thupi la munthu, mfumu ya Israyeli ija inati: “Mtima wabwino ndi moyo wa thupi; koma nsanje ivunditsa mafupa.” (Miyambo 14:30) Pali matenda ena amene amayamba chifukwa cha mkwiyo ndiponso kukalipa, monga matenda ovutika kupuma, kuthamanga magazi, matenda a chiwindi ndi a kapamba. Madokotala amanenanso kuti mkwiyo ndiponso kukalipa kumawonjezera ngakhalenso kuyambitsa matenda ngati zilonda zam’mimba, zidzolo kapena kuti anabiri, chifuwa cha mphumu, matenda a pakhungu, ndiponso kusagayika bwino kwa chakudya m’thupi. Komano “mtima wabwino ndi moyo wa thupi.” (Miyambo 14:30) Motero, monga anthu anzeru, tiyeni “tilondole zinthu za mtendere, ndi zinthu zakulimbikitsana wina ndi mnzake.”—Aroma 14:19.
Kuopa Mulungu Kumatithandiza Kusakhala a Tsankho
Solomo anati: “Wotsendereza aumphawi atonza Mlengi wake; koma wochitira wosauka chifundo am’lemekeza.” (Miyambo 14:31) Munthu woopa Mulungu amazindikira kuti anthu onse anapangidwa ndi Yehova Mulungu. Motero, ngakhale munthu wonyozeka ndi munthube basi, ndipo Mlengi wa anthu amakhudzidwa ndi zimene timam’chitira munthuyo. Kuti tipatse Mulungu ulemerero, tiyenera kuchita zinthu mosakondera ndiponso mopanda tsankho. Mkristu wosauka ayenera kuthandizidwa mwauzimu popanda kum’sankha. Tiyenera kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu kwa olemera ndi osauka omwe.
Potchula phindu lina la kuopa Mulungu, mfumu yanzeruyi inati: “Wochimwa adzakankhidwa m’kuipa kwake; koma wolungama akhulupirirabe pomwalira.” (Miyambo 14:32) Kodi woipa amakankhidwa motani? Akatswiri ena ofufuza za m’Baibulo amanena kuti mawuwa amatanthauza kuti woipayo sathanso kubwerera mwakale akakumana ndi mavuto enaake. Koma munthu woopa Mulungu akakumana ndi mavuto amakhulupirira kuti Mulungu ali naye chifukwa choti iye ndi wokhulupirika kwa Mulungu. Chifukwa chokhala wokhulupirika kwambiri kwa Yehova ngakhale kulolera kufa, munthuyu amatsimikiza mtima monga anachitira Yobu, yemwe anati: “Mpaka kufa ine sinditaya ungwiro wanga.”—Yobu 27:5.
Kuti tikhalebe okhulupirika tiyenera kuopa Mulungu ndiponso kukhala ndi nzeru. Ndipo kodi nzeru zimenezi tingazipeze kuti? Lemba la Miyambo 14:33 limayankha kuti: “Nzeru ikhalabe m’mtima wa wozindikira, nidziwika pakati pa opusa.” Inde tingapeze nzeru mumtima wa munthu wozindikira. Komano kodi nzeru imadziwika bwanji pakati pa opusa? Buku lina linati “wopusa, poyesetsa kuti aoneke ngati wanzeru, amapupuluma kunena zinthu zimene iye amaona ngati n’zanzeru koma potero zinthuzo zimasanduka zopusa.”
‘Kumakuza Mtundu wa Anthu’
Mfumu ya Israyeliyi itamaliza kufotokoza mmene kuopa Yehova kumakhudzira munthu inayamba kufotokoza mmene kumakhudzira mtundu wonse. Iyo inati: “Chilungamo chikuza mtundu wa anthu; koma tchimo lichititsa fuko manyazi.” (Miyambo 14:34) Mfundo imeneyi inaonekera bwino kwambiri pa mtundu wa Israyeli. Kutsatira malamulo a Mulungu kunakwezetsa kwambiri mtunduwu poyerekezera ndi mitundu yoyandikana nayo. Komano kusamvera Yehova mobwerezabwereza kunaubweretsera zamanyazi ndipo mapeto ake Yehova anausiya. Mfundo imeneyi imakhudzanso anthu a Mulungu masiku ano. Gulu la Yehova limasiyana ndi dziko chifukwa choti limayesetsa kutsatira mfundo zolungama za Mulungu. Koma kuti likhalebe lokwezeka choncho, tonsefe patokhapatokha tiyenera kukhala ndi moyo wopanda chodetsa. Kuchita uchimo nthawi zambiri kumangom’bweretsera munthu manyazi, komanso kumanyozetsa mpingo ndiponso Mulungu.
Polongosola chimene chimachititsa mfumu kusangalala, Solomo anati: “Mfumu ikomera mtima kapolo wochita mwanzeru; koma idzakwiyira wochititsa manyazi.” (Miyambo 14:35) Ndipo lemba la Miyambo 16:13 limati: “Milomo yolungama ikondweretsa mafumu; wonena zoongoka am’konda.” Inde, Mtsogoleri wathu, yemwenso ali Mfumu yathu, Yesu Kristu, amasangalala tikamachita zinthu zolungama ndiponso zanzeru n’kumagwiritsira ntchito milomo yathu pa ntchito ya Ufumu yolalikira ndi kupanga ophunzira. Motero tiyeni tichite zonse zomwe tingathe pogwira ntchito imeneyi kwinaku tikusangalala ndi madalitso obwera chifukwa choopa Mulungu woona.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 3 Nkhani yofotokoza Miyambo 14:1-25, mungaipeze mu Nsanja ya Olonda ya November 15, 2004, masamba 26 mpaka 29, ndi ya July 15, 2005, masamba 17 mpaka 20.
[Chithunzi patsamba 15]
Munthu angathe kuphunzitsidwa kuopa Mulungu