Kodi Ndi Maphunziro Otani Amene Angakuthandizeni Kukhala ndi Moyo Wabwino?
Kodi Ndi Maphunziro Otani Amene Angakuthandizeni Kukhala ndi Moyo Wabwino?
KODI munayamba mwakumanapo ndi mavuto ochuluka zedi moti munkangoona kuti mulibiretu pogwira? Tangoganizirani mmene mavuto angakusautsireni ngati mutalephera kuthana nawo bwinobwino. Palibe munthu amene amabadwa akudziwa kuthana ndi mavuto onse bwinobwino, moti n’kumachita zinthu zonse mwanzeru. N’chifukwa chake pamafunika maphunziro. Komano kodi n’kuti kumene mungapeze maphunziro okukonzekeretsani kuthana bwinobwino ndi mavuto a m’moyo?
Anthu ambiri, ana ndi achikulire omwe, amaona kuti kukhala munthu wophunzira kwambiri ndiko kuli kofunika zedi. Pali akatswiri ena amene anafika ponena kuti iwowo “sakayika ngakhale pang’ono kuti munthu sangapeze ntchito [yabwino] popanda kukhala ndi digiri inayake ya ku koleji.” Komatu anthu amafunikira zinthu zinanso zimene maphunziro oterewa sangabweretse. Mwachitsanzo, kodi kuphunzira kwambiri kungakuthandizeni kukhala kholo labwino, mkazi kapena mwamuna wabwino, kapenanso bwenzi labwino? Ngakhaletu anthu amene amawatayira kamtengo chifukwa cha kuphunzira kwawo amatha kuyamba makhalidwe oipa, kulephera kuyendetsa bwino banja lawo, ndipo mwinanso amadzipha kumene.
Anthu ena amaona kuti kupembedza n’kumene kungawathandize ndi kuwaphunzitsa zinthu, koma amakhumudwa chifukwa sikuwathandiza m’njira yeniyeni pankhani ya kuthana ndi mavuto a m’moyo. Chitsanzo cha zimenezi ndi Emilia * wa ku Mexico, yemwe anati: “Zaka 15 zapitazo ndinaona kuti n’zosatheka kuti ine ndi mwamuna wanga tipitirize kukhalira limodzi. Tinkangokhalira kukangana. Ndinakanika kumusiyitsa mowa. Nthawi zambiri ndinkasiya ana athu aang’ono ali okhaokha, n’kumakafunafuna mwamuna wanga. Kenaka ndinafika potopa nazo. Ndinapita kutchalitchi nthawi zingapo kukafuna thandizo. Ngakhale kuti kutchalitchiko ankawerenga Baibulo mwa apo ndi apo, sindinamvepo malangizo aliwonse okhudza vuto langalo; ndipo palibe aliyense kumeneko amene anandilankhulapo n’kundithandiza maganizo. Kukhala m’tchalitchimo kwa kanthawi n’kumanena mapemphero omangobwerezabwereza, sikunathandize.” Anthu ena amasokonezeka akaona kuti atsogoleri awo enieniwo sakupereka chitsanzo chabwino. Chifukwa cha izi, ambiri sakhulupiriranso kuti kupembedza ndiko kungawaphunzitse kukhala ndi moyo wabwino.
Motero, mwina mukudzifunsa kuti, ‘Ndiyenera kuphunzira zotani kuti ndikhale ndi moyo wabwino?’ Kodi Chikristu choona chimayankha funso lofunikali? Zimenezi tizilongosola m’nkhani yotsatirayi.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 4 Dzinali talisintha.