Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kufalikira kwa Chikristu Pakati pa Ayuda M’nthawi ya Atumwi

Kufalikira kwa Chikristu Pakati pa Ayuda M’nthawi ya Atumwi

Kufalikira kwa Chikristu Pakati pa Ayuda M’nthawi ya Atumwi

CHA m’ma 49 C.E., ku Yerusalemu kunachitika msonkhano wofunika kwambiri. Pamsonkhanopo panali Yohane, Petro, ndi Yakobo, mng’ono wake wa Yesu. Anthu amenewa ndiwo “amene anayesedwa mizati” ya mpingo wa Chikristu nthawi imeneyo. Anthu enanso awiri amene anatchulidwa kuti anali nawo pamsonkhanowu anali mtumwi Paulo ndi mnzake Barnaba. Nkhani imene ankafuna kukambirana inali ya kugawa gawo lawo lalikulu limene ankafunika kulalikiramo. Paulo analongosola kuti: “Anapatsa ine ndi Barnaba dzanja lamanja la chiyanjano, kuti ife tipite kwa amitundu, ndi iwo kwa mdulidwe.”​—Agalatiya 2:1, 9. *

Kodi zimene anagwirizanazi tiyenera kuzimva motani? Kodi gawo lolalikiramo uthenga wabwino analigawa motengera kuti madera ena anali a Ayuda ndi anthu otembenukira ku Chiyuda pamene ena anali a Akunja? Kapena kodi anagawa gawolo mogwirizana ndi kumene maderawo anali, osati za mtundu wa anthu okhalako? Kuti tipeze yankho logwira mtima la mafunsowa, tiyenera kudziwa kaye mbiri ya Ayuda okhala kunja kwa Palestina.

Ayuda a M’nthawi ya Atumwi

Kodi m’nthawi ya atumwi panali Ayuda angati okhala kunja kwa Palestina? Zikuoneka kuti akatswiri ambiri amavomereza mfundo yotchulidwa m’buku la Atlas of the Jewish World, yoti: “N’zovuta kudziwa chiwerengero chenicheni cha anthuwa, koma ena amati n’zotheka kuti chaka cha 70 chitangotsala pang’ono kukwana, ku Yudeya kunali Ayuda mamiliyoni awiri ndi theka ndipo m’madera ena onse a kunja kwa Palestina a mu Ufumu wa Roma, munali Ayuda oposa 4 miliyoni. . . . N’zotheka kuti pa anthu khumi aliwonse mu Ufumu wa Roma mmodzi anali Myuda, ndipo m’madera okhala ndi Ayuda ambiri, omwe anali m’mizinda ya m’zigawo za kummawa, pa anthu 100 aliwonse a m’maderawo anthu 25 kapena kuposa anali Ayuda.”

Madera a kummawa omwe kunali Ayuda ambiri anali Suriya, Asiyamina, Babulo, ndi Aigupto, ndipo ku Ulaya kunkapezekanso Ayuda mwa apo ndi apo. Ena mwa Akristu akale odziwika bwino omwe anali Ayuda, anali ochokera m’madera a kunja kwa Palestina. Mwachitsanzo, Barnaba anali wa ku Kupro, Priska ndi Akula anali a ku Ponto koma kenaka anasamukira ku Roma, Apolo anali wa ku Alesandreya, ndipo Paulo anali wa ku Tariso.​—Machitidwe 4:36; 18:2, 24; 22:3.

Ayuda okhala kunja kwa Palestina ankagwirizana ndi Ayuda a kwawo ku Palestina m’njira zambiri. Njira imodzi inali yakuti nawonso ankakhoma msonkho wa pachaka ndipo ndalama zake ankatumiza ku kachisi ku Yerusalemu, pofuna kugwirizana nawo pa zochitika ndiponso kupembedza kwa m’kachisi. Pankhani imeneyi, katswiri wina, John Barclay analongosola kuti: “Pali umboni wokwanira wosonyeza kuti Ayuda a kunja kwa Palestina sankalephera kutolera ndalama zamsonkho zimenezi, ndipo ankawonjezaponso zopereka za anthu olemera.”

Njira inanso yowagwirizanitsa inali maulendo a chaka n’chaka omwe Ayuda ambirimbiri ankayenda kupita ku Yerusalemu kukachita nawo zikondwerero zokhudza kupembedza Mulungu. Nkhani ya pa Machitidwe 2:9-11 yonena za chikondwerero cha Pentekoste m’chaka cha 33 C.E., imasonyeza zimenezi. Pachikondwerero chimenechi panali Ayuda ochokera ku Parti, Mediya, Elamu, Mesopotamiya, Kapadokiya, Ponto, Asiya, Frugiya, Pamfuliya, Aigupto, Libiya, Roma, Krete, ndi Arabiya.

Akuluakulu oyendetsa ntchito za pakachisi ku Yerusalemu ankalemberana makalata ndi Ayuda okhala kunja kwa Palestina. N’zodziwika bwino kuti Gamaliyeli, mphunzitsi wa chilamulo wotchulidwa pa Machitidwe 5:34, anatumiza makalata ku Babulo ndi m’madera ena a padziko lapansi. Cha m’ma 59 C.E., mtumwi Paulo atafika ku Roma ali mkaidi, “akulu a Ayuda” anamuuza kuti “sitinalandira akalata onena za inu ochokera ku Yudeya, kapena sanadza kuno wina wa abale ndi kutiuza kapena kulankhula kanthu koipa ka inu.” Zimenezi zikusonyeza kuti nthawi zambiri, Ayuda a ku Palestina ankatumiza makalata ndiponso malipoti ku Roma.​—Machitidwe 28:17, 21.

Baibulo limene Ayuda okhala kunja kwa Palestina ankagwiritsira ntchito linali Baibulo lomasuliridwa mu Chigiriki la Malemba Achihebri lotchedwa Septuagint. Buku lina limati: “N’zotheka ndithu kuti m’madera onse a kunja kwa Palestina, Ayuda ankawerenga Baibulo la LXX [kapena kuti Septuagint] ndipo ankaliona monga Baibulo la Ayuda akumeneko kapena kuti ‘malemba oyera.’” Akristu a m’nthawi ya atumwi ankagwiritsiranso ntchito kwambiri Baibuloli pophunzitsa.

Anthu a m’bungwe lolamulira lachikristu ku Yerusalemu ankadziwa bwino kuti umu ndi mmene zinthu zinalili. Uthenga wabwino unali utafika kale kwa Ayuda okhala ku Suriya ndiponso m’madera ena akutali kwambiri, kuphatikizapo Damasiko ndi Antiokeya. (Machitidwe 9:19, 20; 11:19; 15:23, 41; Agalatiya 1:21) Pa msonkhano umene unachitika mu 49 C.E., zikuoneka kuti anthu amene anali pamsonkhanopo anali kukonzekera ntchito ya m’tsogolo. Tiyeni tione zimene Baibulo limatchulapo zokhudza kufalikira kwa Chikristu pakati pa Ayuda ndi anthu otembenukira ku Chiyuda.

Paulo Anakumana ndi Ayuda a Kunja kwa Palestina M’maulendo Ake

Ntchito yoyamba imene mtumwi Paulo anapatsidwa inali ‘yotengera dzina la Yesu Kristu pamaso pa amitundu ndi mafumu ndi ana a Israyeli.’ * (Machitidwe 9:15) Msonkhano wa ku Yerusalemu uja utatha, Paulo anapitiriza kulalikira kwa Ayuda okhala kunja kwa Palestina m’madera onse amene iyeyo anafikako. (Onani bokosi patsamba 14.) Zimenezi zimasonyeza kuti nkhani ya gawo ija inali yokhudza madera olalikiramo osati mitundu ya anthu okhala m’maderawo. Paulo ndi Barnaba anafutukula ntchito yawo yaumishonale mpaka kumadzulo kwa Ufumu wa Roma, ndipo atumwi ena anachita ntchito yawo kwawo kwa Ayuda ku Palestina, ndiponso m’madera ena a kummawa okhala ndi Ayuda ambiri.

Paulo ndi anzake atayamba ulendo wachiwiri waumishonale kuchokera ku Antiokeya wa ku Suriya, analowera kumadzulo podzera ku Asiyamina mpaka kukafika ku Trowa. Atachoka kumeneku anapita ku Makedoniya chifukwa anaganiza kuti ‘Mulungu anawaitanira iwo kulalikira Uthenga Wabwino kwa [anthu a ku Makedoniya].’ Pambuyo pake, anayambitsa mipingo yachikristu m’mizinda ina ya ku Ulaya, kuphatikizapo Atene ndi Korinto.​—Machitidwe 15:40, 41; 16:6-10; 17:1–18:18.

Cha m’ma 56 C.E., pamapeto a ulendo wake wachitatu waumishonale, Paulo anakonza zopitiriza ulendo wake kulowera cha kumadzulo kwambiri n’kuwonjezera gawo limene anapatsidwa pa msonkhano wa ku Yerusalemu uja. Iye analemba kuti: ‘Ndili kufuna kulalikira uthenga wabwino kwa inunso a ku Roma,’ ndipo ananenanso kuti ‘ndidzapyola kwanu kupita ku Spanya.’ (Aroma 1:15; 15:24, 28) Koma nanga bwanji za Ayuda ambirimbiri a kunja kwa Palestina omwe ankakhala kummawa?

Ayuda a Kummawa

M’nthawi ya atumwi, dziko la Aigupto ndilo linali ndi Ayuda ambiri koposa, makamaka mumzinda wa Alesandreya, womwe unali likulu la dzikolo. Mzindawu, womwenso unali likulu la zamalonda ndi chikhalidwe, unali ndi Ayuda masauzande ambirimbiri, ndipo mumzinda wonsewo munali masunagoge ochuluka. Philo, yemwe anali Myuda wokhala ku Alesandreya, ananena kuti panthawiyo ku Aigupto konse kunali Ayuda osachepera wani miliyoni. Ayuda ochuluka ndithu ankakhalanso mumzinda wa Kurene komanso m’madera ozungulira mzindawu ku Libiya, komwe kunali kufupi ndi ku Aigupto.

Ayuda ena amene anakhala Akristu anali a m’madera amenewa. M’Baibulo amatchulamo za “Apolo, fuko lake la ku Alesandreya,” za “amuna a ku Kupro, ndi Kurene,” ndi za “Lukiya wa ku Kurene” omwe anathandiza mpingo wa ku Antiokeya ku Suriya. (Machitidwe 2:10; 11:19, 20; 13:1; 18:24) Kupatulapo pa nkhani za anthu tatchulawa, komanso nkhani ya Filipo amene analalikira uthenga wabwino kwa mdindo wa ku Aitiopiya, Baibulo silinenapo chilichonse pa za ntchito ya Akristu ku Aigupto ndi m’madera ena ozungulira dzikoli.​—Machitidwe 8:26-39.

Ayuda ambiri ankakhalanso ku Babulo, ndipo ena anafalikira mpaka ku Parti, Mediya ndi Elamu. Munthu wina wolemba mbiri ananena kuti: “Ayuda ankapezeka m’chigawo chilichonse cha m’chigwa chamtsinje wa Tigirisi ndi Firate, kungochokera ku Armenia mpaka kukafika ku gombe la Persia, ndiponso kulowera kumpoto cha kummawa kukafika ku nyanja ya Caspian, ndiponso kulowera kummawa mpaka kukafika ku Mediya.” Buku la Encyclopaedia Judaica limati mwina m’chigawochi munali Ayuda 800,000 kapena kuposa. Josephus, yemwe anali Myuda wolemba mbiri wa m’nthawi ya atumwi anati Ayuda masauzande angapo a ku Babulo ankapita ku Yerusalemu kukachita nawo zikondwerero za pachaka.

Kodi n’zotheka kuti ena mwa Ayuda a ku Babulowa anabatizidwa nawo pa Pentekoste mu 33 C.E.? Sitikudziwa, koma pa anthu amene anamva mtumwi Petro akulankhula pa tsikuli panali ena ochokera ku Mesopotamiya. (Machitidwe 2:9) Ndipo tikudziwa kuti mtumwi Petro anali ku Babulo cha m’ma 62 mpaka 64 C.E. Kumeneku n’kumene iye analembera kalata yake yoyamba ndiponso mwina kalata yake yachiwiri. (1 Petro 5:13) N’zosachita kufunsa kuti chigawo cha Babulo, chomwe chinali ndi Ayuda ambiri, chinali mbali ya gawo limene anapatsa Petro, Yohane, ndi Yakobo pa msonkhano umene unatchulidwa mu kalata yopita kwa Agalatiya.

Kugwirizana kwa Mpingo wa ku Yerusalemu ndi Ayuda a Kunja kwa Palestina

Yakobo, yemwenso analipo pa msonkhano umene anakambirana za magawo uja, anali woyang’anira mu mpingo wa ku Yerusalemu. (Machitidwe 12:12, 17; 15:13; Agalatiya 1:18, 19) Iyeyo anaona ndi maso zochitika za pa Pentekoste mu 33 C.E. pamene Ayuda ambirimbiri ochokera kunja kwa Palestina anakhulupirira uthenga wabwino n’kubatizidwa.​—Machitidwe 1:14; 2:1, 41.

Panthawiyi ndiponso panthawi zotsatira, Ayuda ambirimbiri anabwera kudzachita nawo zikondwerero za pachaka. Anthu anadzadza mzinda wonsewo ndipo alendo ankakhala m’midzi ya pafupi ndi mzindawo kapena ankagona m’mahema. Buku la Encyclopaedia Judaica limalongosola kuti anthuwa ankabwerera kudzaonana ndi anzawo, ndiponso kukapembedza m’kachisi, kupereka nsembe, ndi kuphunzira Tora, omwe ali mabuku asanu oyambirira a m’Baibulo.

N’zosakayikitsa kuti Yakobo ndi anthu ena mumpingo wa ku Yerusalemu anagwiritsira ntchito mwayi umenewu kulalikira kwa Ayuda ochokera kunja kwa Palestina. N’kutheka kuti panthawi imene “kunayamba kuzunza kwakukulu pa Mpingo unali m’Yerusalemu” chifukwa cha imfa ya Stefano, atumwiwo ankalalikira mosamala kwambiri kwa Ayudawa. (Machitidwe 8:1) Nkhaniyi imaonetsa kuti izi zisanachitike ndiponso pambuyo pake, okhulupirira anapitirira kuwonjezeka chifukwa cha khama la Akristu amenewa polalikira.​—Machitidwe 5:42; 8:4; 9:31.

Kodi Tingaphunzirepo Chiyani?

Inde, Akristu a m’nthawi ya atumwi anayesetsa kwambiri kupeza Ayuda kulikonse kumene Ayudawo ankakhala. Panthawi yomweyo, Paulo ndi Akristu ena anayesetsa kupeza anthu Akunja okhala ku Ulaya. Iwo anamvera lamulo limene Yesu anapereka potsanzikana ndi otsatira ake lakuti apange ophunzira mwa “anthu a mitundu yonse.”​—Mateyu 28:19, 20.

Pachitsanzo chawochi, tikuphunzirapo kuti m’pofunika kulalikira mwadongosolo kuti tithandizidwe ndi mzimu wa Yehova. Tikuthanso kuona ubwino wolankhula ndi anthu amene amalemekeza Mawu a Mulungu, makamaka m’magawo okhala ndi Mboni za Yehova zochepa. Kodi madera ena a gawo la mpingo wanu ali ndi anthu ambiri achidwi kuyerekezera ndi madera ena? Ngati n’choncho ndiye kuti ndi bwino kulalikira m’madera amenewa kawirikawiri. Kodi cha kumene mukukhalako kukuchitika misonkhano inayake imene ingakupatseni mwayi wochita ntchito yapadera ya ulaliki wamwamwayi ndiponso ulaliki wa mumsewu?

Timapindula tikamawerenga m’Baibulo za Akristu oyambirirawa komanso tikamaphunzira zina n’zina zokhudza mbiri yawo ndiponso madera amene ankakhala. Chinthu chimodzi chomwe chingatithandize pophunzira zimenezi ndi kabuku kotchedwa ‘Onani Dziko Lokoma,’ komwe kali ndi mapu ndiponso zithunzi zambirimbiri.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 N’kutheka kuti msonkhanowu unachitikira pamodzi ndi msonkhano umene bungwe lolamulira panthawiyo linakambiranapo za nkhani ya mdulidwe, apo ayi unali msonkhano wina umene anakhala nawo panthawi imene ankakambirana za mdulidwezo.​—Machitidwe 15:6-29.

^ ndime 13 Nkhani ino ikulongosola makamaka za kulalikira kwa Paulo pakati pa Ayuda, osati za ntchito yake monga “mtumwi wa anthu amitundu.”​—Aroma 11:13.

[Tchati patsamba 14]

PAULO ANALI KUGANIZIRA AYUDA OKHALA KUNJA KWA PALESTINA

ASANACHITE MSONKHANO KU YERUSALEMU MU 49 C.E.

Machitidwe 9:19, 20 Damasiko — “m’masunagoge analalikira”

Machitidwe 9:29 Yerusalemu — “analankhula . . . ndi Aheleniste,” kapena

kuti Ayuda olankhula Chigiriki

Machitidwe 13:5 Salami, Kupro — “analalikira mawu a Mulungu

m’masunagoge a Ayuda”

Machitidwe 13:14 Antiokeya ku Pisidiya — “analowa m’sunagoge”

Machitidwe 14:1 Ikoniyamu — “analowa . . . m’sunagoge wa

Ayuda”

ATACHITA MSONKHANO KU YERUSALEMU MU 49 C.E.

Machitidwe 16:14 Filipi — “Lidiya, . . . amene anapembedza Mulungu”

Machitidwe 17:1 Tesalonika — “sunagoge wa Ayuda”

Machitidwe 17:10 Bereya — “sunagoge wa Ayuda”

Machitidwe 17:17 Atene — “anatsutsana ndi Ayuda m’sunagoge”

Machitidwe 18:4 Korinto — “anafotokozera m’sunagoge”

Machitidwe 18:19 Efeso — “analowa m’sunagoge, natsutsana ndi

Ayuda”

Machitidwe 19:8 Efeso — “analowa m’sunagoge, nanena molimba

mtima, miyezi itatu”

Machitidwe 28:17 Roma — “anaitana akulu a Ayuda

asonkhane”

[Mapu patsamba 15]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Anthu amene anamva uthenga wabwino pa Pentekoste mu 33 C.E. anachokera m’madera akutali

ILURIKO

ITALIYA

Roma

MAKEDONIYA

GIRISI

Atene

KRETE

Kurene

LIBIYA

BITUNIYA

GALATIYA

ASIYA

FRUGIYA

PAMFULIYA

KUPRO

AIGUPTO

AITIOPIYA

PONTO

KAPADOKIYA

KILIKIYA

MESOPOTAMIYA

SURIYA

SAMARIYA

Yerusalemu

YUDEYA

MEDIYA

Babulo

ELAMU

ARABIYA

PARTI

[Nyanja]

Nyanja ya Mediterranean

Nyanja Yakuda

Nyanja Yofiira

Gombe la Perisiya