Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Njira za Yehova Zili Zoongoka”

“Njira za Yehova Zili Zoongoka”

“Njira za Yehova Zili Zoongoka”

“Njira za Yehova zili zoongoka; ndipo olungama adzayendamo.”​—HOSEYA 14:9.

1, 2. Kodi Yehova anawakonzera chiyambi chotani Aisrayeli, nanga kodi chinawachitikira n’chiyani?

YEHOVA anakonzera Aisrayeli chiyambi chabwino m’masiku a mneneri Mose. Podzafika kumayambiriro kwa zaka za m’ma 700 B.C.E., iwo anakhala oipa kwambiri moti Mulungu anawapeza ndi mlandu waukulu kwabasi. Machaputala 10 mpaka 14 a Hoseya akusonyeza zimenezi.

2 Mtima wa Israyeli unali utakhala wachinyengo. Anthu a ufumu wa mafuko khumiwo anali ‘atalima choipa’ ndipo anakolola chosalungama. (Hoseya 10:1, 13) Yehova anati: “Pamene Israyeli anali mwana, ndinam’konda, ndinaitana mwana wanga ali m’Aigupto.” (Hoseya 11:1) Ngakhale kuti Mulungu anali atalanditsa Aisrayeli kuwachotsa mu ukapolo ku Igupto, iwo anali atam’bwezera mabodza ndi chinyengo. (Hoseya 11:12) N’chifukwa chake Yehova anawapatsa uphungu uwu wakuti: “Utembenukire kwa Mulungu wako, sunga chifundo ndi chiweruzo.”​—Hoseya 12:6.

3. Kodi chinali kudzachitikira Samariya wopandukayo n’chiyani, nanga kuti Aisrayeli alandire chifundo anafunikira kuchita chiyani?

3 Samariya wopandukayo ndi mfumu yake anali kudzakumana ndi tsoka. (Hoseya 13:11, 16) Ngakhale zinali choncho, chaputala chomaliza cha ulosi wa Hoseya chimayamba ndi pempho lakuti: “Israyeli, bwerera kumka kwa Yehova Mulungu wako.” Inde, Aisrayeli akanayesetsa kupempha chikhululukiro, Mulungu akanawachitira chifundo. Ndipotu anafunika avomereze kuti “njira za Yehova zili zoongoka,” ndiyeno n’kumayendamo.​—Hoseya 14:1-6, 9.

4. Kodi tikambirana mfundo ziti za ulosi wa Hoseya?

4 Chigawo chimenechi cha ulosi wa Hoseya chili ndi mfundo zambiri zimene zingatithandize kuyenda ndi Mulungu. Tikambirana mfundo izi: (1) Yehova amafuna kum’pembedza mopanda chinyengo, (2) Mulungu amaonetsa chikondi chokhulupirika kwa anthu ake, (3) tifunikira kuyembekeza Yehova nthawi zonse, (4) njira za Yehova zili zoongoka nthawi zonse, ndi (5) ochimwa angabwerere kwa Yehova.

Yehova Amafuna Kum’pembedza Mopanda Chinyengo

5. Kodi Mulungu amafuna utumiki wotani kwa ife?

5 Yehova amafuna kuti ife tichite utumiki wopatulika kwa iye m’njira yoyera ndi yopanda chinyengo. Koma Israyeli anali atakhala “mpesa wotambalala” wosabereka. Anthu a mtunduwo anali ‘atachulukitsa maguwa a nsembe’ ogwiritsa ntchito pa kupembedza konyenga. Anthu ampatuko amenewa anali atakonza ngakhale zoimiritsa​—mwina zipilala zogwiritsa ntchito pa kupembedza konyansa. Yehova anali kudzapasula maguwa a nsembe amenewo ndi kuwononga zipilala zimenezo.​—Hoseya 10:1, 2.

6. Kuti tiziyenda ndi Mulungu, tiyenera kupewa khalidwe lotani?

6 Chinyengo n’chosaloleka pakati pa atumiki a Yehova. Nanga kodi n’chiyani chimene chinali chitachitika ndi Aisrayeli amenewo? Eya, ‘mtima wawo unagawikana,’ kapena kuti unakhala wachinyengo! Ngakhale kuti iwo poyamba analowa m’pangano ndi Yehova monga anthu ake odzipereka, iye anawapeza ndi mlandu wa chinyengo. Kodi tikuphunzirapo chiyani pamenepa? Ngati tinadzipereka kwa Mulungu, tisakhale achinyengo. Lemba la Miyambo 3:32 limachenjeza kuti: “Wamphulupulu [“munthu wachinyengo,” NW] anyansa Yehova; koma chinsinsi chake chili ndi oongoka.” Kuti tiyende ndi Mulungu, tiyenera kuonetsa chikondi “chochokera mu mtima woyera ndi m’chikumbumtima chokoma ndi chikhulupiriro chosanyenga.”​—1 Timoteo 1:5.

Mulungu Amaonetsa Chikondi Chokhulupirika kwa Anthu Ake

7, 8. (a) Kodi tingalandire chikondi chokhulupirika cha Mulungu tikamachita chiyani? (b) Kodi tiyenera kuchita chiyani tikachita tchimo lalikulu?

7 Ngati tipembedza Yehova mopanda chinyengo ndiponso moongoka, timalandira kukoma mtima kwake, kapena kuti chikondi chake chokhulupirika. Aisrayeli amphulupulu aja anawauza kuti: “Mudzibzalire m’chilungamo mukolole monga mwa chifundo; limani masala anu, pakuti yafika nthawi ya kufuna Yehova, mpaka afika Iye, navumbitsira inu chilungamo.”​—Hoseya 10:12.

8 Aisrayeli akanakhala kuti anafuna Yehova ndi kulapa, iye mosangalala ‘akanawavumbitsira [malangizo, NW] m’chilungamo.’ Tikachita tchimo lalikulu, tizifuna Yehova, kupemphera kwa iye kuti atikhululukire ndi kupempha thandizo lauzimu kwa akulu achikristu. (Yakobo 5:13-16) Tizifunanso chitsogozo cha mzimu woyera, pakuti “wakufesera kwa thupi la iye yekha, chochokera m’thupi adzatuta chivundi; koma wakufesera kwa Mzimu, chochokera mu Mzimu adzatuta moyo wosatha.” (Agalatiya 6:8) ‘Tikafesera kwa mzimu,’ tidzapitiriza kulandira chikondi chokhulupirika cha Mulungu.

9, 10. Kodi lemba la Hoseya 11:1-4 limagwira ntchito motani pa Israyeli?

9 Tili ndi chidaliro chakuti Yehova nthawi zonse amasonyeza chikondi pochita zinthu ndi anthu ake. Umboni wa zimenezi ukupezeka pa Hoseya 11:1-4, pamene pamati: “Pamene Israyeli anali mwana, ndinam’konda, ndinaitana mwana wanga ali m’Aigupto. . . . Anaphera nsembe Abaala, nafukizira mafano osema. Koma Ine ndinaphunzitsa Efraimu [Aisrayeli] kuyenda, ndinawafungata m’manja mwanga; koma sanadziwa kuti ndinawachiritsa. Ndinawakoka ndi zingwe za munthu, ndi zomangira za chikondi; ndinakhala nawo ngati iwo akukweza goli pampuno pawo, ndipo ndinawaikira chakudya.”

10 Pano Israyeli anamuyerekeza ndi mwana wamng’ono. Yehova mwachikondi anaphunzitsa Aisrayeli kuyenda, ndipo anawafungata m’manja mwake. Iye sanasiye kuwakoka ndi “zomangira za chikondi.” Zimenezi n’zokhudzatu mtima kwambiri! Tayerekezani kuti ndinu kholo ndipo mukuphunzitsa mwana wanu wamng’ono kuti ayambe kuyenda. Mumatambasula manja anu. N’kuthekanso kuti mungagwiritse ntchito zingwe zoti mwana wanuyo agwire kuti asagwe. Eya, ndi mmenenso chikondi cha Yehova pa inuyo chilili. Iye amakonda kukutsogolerani ndi “zomangira za chikondi.”

11. Kodi Mulungu anakhala bwanji ngati ‘wokweza goli’?

11 Pochita zinthu ndi Aisrayeli, Yehova ‘anakweza goli pampuno pawo, ndi kuwaikira chakudya.’ Mulungu anakhala ngati wokweza goli kapena wolikankhira kumbuyo kwambiri kuti nyama ithe kudya bwinobwino. Pamene Aisrayeli anasiya kugonjera Yehova m’pamene anakhala pansi pa goli lopondereza la adani awo. (Deuteronomo 28:45, 48; Yeremiya 28:14) Tisalole kukhala pansi pa mdani wathu wamkulu, Satana, n’kumavutika ndi goli lake lopondereza komanso lopweteka. M’malo mwake, tiyeni tipitirize kuyenda mokhulupirika ndi Mulungu wathu wachikondi.

Yembekezani Yehova Nthawi Zonse

12. Malinga ndi Hoseya 12:6, kodi chofunika n’chiyani kuti tipitirize kuyenda ndi Mulungu?

12 Kuti tipitirize kuyenda ndi Mulungu, tiyenera kuyembekeza iye nthawi zonse. Aisrayeli anawauza kuti: “M’mwemo utembenukire kwa Mulungu wako, sunga chifundo ndi chiweruzo, nuyembekezere Mulungu wako kosalekeza.” (Hoseya 12:6) Mwa kusonyeza chifundo, kapena kuti kukoma mtima, mwa kuchita chiweruzo kapena kuti cholungama, ndi ‘kuyembekeza Mulungu mosaleka,’ Aisrayeli akanapereka umboni wakuti akubwerera kwa Yehova chifukwa cha kulapa kwawo. Ngakhale ngati takhala tikuyenda ndi Mulungu mokhulupirika mpaka pano, tikufunikabe kusonyeza kukoma mtima, kuchita zinthu mwachilungamo, ndi kuyembekeza Mulungu nthawi zonse.​—Salmo 27:14.

13, 14. Kodi Paulo akugwiritsa ntchito motani lemba la Hoseya 13:14, ndipo akutipatsa chifukwa chotani choyembekezera Yehova?

13 Ulosi wa Hoseya wokhudza Aisrayeli umatipatsa chifukwa chapadera choyembekezera Mulungu. Yehova anati: “Ndidzawaombola ku mphamvu ya kumanda, ndidzawaombola ku imfa; imfa, miliri yako ili kuti? Manda, chiwonongeko chako chili kuti?” (Hoseya 13:14) Yehova sanali kufuna kuombola Aisrayeli osamvera ku imfa panthawi imeneyo, koma pomaliza pake anali kudzameza imfa kosatha ndi kuthetsa mphamvu ya imfayo.

14 Polembera Akristu anzake odzozedwa, Paulo anagwira mawu a ulosi wa Hoseya ndipo analemba kuti: “Pamene chovunda ichi chikadzavala chisavundi ndi cha imfa ichi chikadzavala chosafa, pamenepo padzachitika mawu olembedwa, Imfayo yamezedwa m’chigonjetso. Imfawe, chigonjetso chako chili kuti? Imfawe, mbola yako ili kuti? Koma mbola ya imfa ndiyo uchimo; koma mphamvu ya uchimo ndiyo chilamulo: koma ayamikike Mulungu, amene atipatsa ife chigonjetso mwa Ambuye wathu Yesu Kristu.” (1 Akorinto 15:54-57) Yehova anaukitsa Yesu kwa akufa, ndipo anapereka chitsimikizo chotonthoza mtima chakuti anthu amene Mulungu amawakumbukira adzaukitsidwa. (Yohane 5:28, 29) Ndiyetu tili ndi chifukwa chosangalatsa kwambiri choyembekezera Yehova! Koma pali chinanso kuwonjezera pa chiyembekezo chakuti akufa adzauka chimene chikutilimbikitsa kuyenda ndi Mulungu.

Njira za Yehova Zili Zoongoka Nthawi Zonse

15, 16. Kodi ulosi unati chiyani za Samariya, ndipo unakwaniritsidwa motani?

15 Kukhulupirira ndi mtima wonse kuti “njira za Yehova zili zoongoka” kumatithandiza kuyendabe ndi Mulungu. Anthu a ku Samariya sanayende m’njira zolungama za Mulungu. N’kuona anakumana ndi mavuto chifukwa cha kulakwa kwawo ndi kupanda chikhulupiriro kwawo mwa Yehova. Ulosiwo unati: “Samariya adzasanduka wabwinja, pakuti anapandukana ndi Mulungu wake; iwo adzagwa ndi lupanga, ana awo amakanda adzaphwanyika, ndi akazi awo okhala ndi pakati adzatumbulidwa.” (Hoseya 13:16) Mbiri yakale imasonyeza kuti Asuri, amene anagonjetsa Samariya, anali kuchita nkhanza ngati zimenezi.

16 Samariya linali likulu la ufumu wa Israyeli wa mafuko khumi. Komabe, dzina lakuti Samariya panopa liyenera kuti lagwiritsidwa ntchito kunena dera lonse la ufumuwo. (1 Mafumu 21:1) Mfumu Salimanezere Wachisanu wa Asuri anazinga mzinda wa Samariya m’chaka cha 742 B.C.E. Pamene Samariya anagwa m’chaka cha 740 B.C.E., ambiri mwa anthu ake otchuka anatengedwa ukapolo kupita ku Mesopotamiya ndi Mediya. Sitikudziwa ngati amene analanda Samariya anali Salimanezere Wachisanu kapena Sarigoni Wachiwiri amene anam’lowa m’malo. (2 Mafumu 17:1-6, 22, 23; 18:9-12) Mulimonsemo, zolemba za Sarigoni zimatchula kuti anagwira Aisrayeli 27,290 kupita nawo kudera la kumtunda kwa Firate ndi ku Mediya.

17. M’malo monyoza miyezo ya Mulungu, kodi tiyenera kuchita chiyani?

17 Nzika za Samariya zinalangidwa chifukwa chosamvera Yehova ndiponso chifukwa chosayenda m’njira zake zoongoka. Ifenso monga Akristu odzipereka, tingakumane ndi tsoka ngati tingakhale ndi chizolowezi chochita tchimo, n’kumanyoza miyezo ya Mulungu yolungama. Tiyeni tisatsate njira yoipa ngati imeneyo. M’malo mwake, tiyeni yense wa ife titsatire uphungu wa Petro wakuti: “Asamve zowawa wina wa inu ngati wambanda, kapena mbala, kapena wochita zoipa, kapena ngati wodudukira; koma akamva zowawa ngati Mkristu asachite manyazi; koma alemekeze Mulungu m’dzina ili.”​—1 Petro 4:15, 16.

18. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti ‘tizilemekezabe Mulungu’?

18 ‘Timalemekeza Mulungu’ mwa kuyenda m’njira zake zoongoka m’malo mochita zinthu modalira nzeru zathuzathu. Kaini anachita mbanda chifukwa chakuti anayendera nzeru zakezake ndipo analephera kumvera chenjezo la Yehova lakuti uchimo unali utatsala pang’ono kum’likwira. (Genesis 4:1-8) Balamu analandira malipiro kwa mfumu ya Moabu koma anayesetsa mosaphula kanthu kutemberera Israyeli. (Numeri 24:10) Ndipo Mulungu anapha Kora, Mlevi, ndi ena chifukwa chopandukira ulamuliro wa Mose ndi Aroni. (Numeri 16:1-3, 31-33) Kunena zoona, ifeyo sitikufuna ‘kuyenda m’njira yambanda ya Kaini,’ ‘kudziwononga m’chisokero cha Balamu,’ kapena kutayika ‘m’chitsutsano cha Kora.’ (Yuda 11) Koma ngati tingalakwe, ulosi wa Hoseya umatitonthoza.

Ochimwa Angabwerere kwa Yehova

19, 20. Kodi Aisrayeli olapa anatha kupereka nsembe zotani?

19 Ngakhale amene agwa mwa kuchita tchimo lalikulu atha kubwerera kwa Yehova. Pa Hoseya 14:1, 2, timapezapo mawu ochonderera awa: “Israyeli, bwerera kumka kwa Yehova Mulungu wako; pakuti wagwa mwa mphulupulu yako. Mukani nawo mawu, nimubwerere kwa Yehova; nenani kwa Iye, Chotsani mphulupulu zonse, nimulandire chokoma; ndipo tidzapereka mawu milomo yathu ngati ng’ombe.”

20 Aisrayeli olapa, anatha kupereka kwa Mulungu ‘milomo yawo ngati ng’ombe.’ Zimenezi zinali nsembe zachitamando zochokera pansi pa mtima. Paulo ananena za ulosi umenewu pamene analimbikitsa Akristu ‘kupereka nsembe ya kuyamika Mulungu, ndiyo chipatso cha milomo yovomereza dzina lake.’ (Ahebri 13:15) Tili ndi mwayi waukulu woyenda ndi Mulungu ndi kupereka nsembe zotero masiku ano!

21, 22. Kodi Aisrayeli olapa anali kudzaona kuchira kotani?

21 Aisrayeli amene anasiya njira yawo yamphulupulu ndi kubwerera kwa Mulungu anapereka kwa iye ‘milomo yawo ngati ng’ombe.’ Chifukwa cha zimenezo, anachira mwauzimu, ngati mmenedi Mulungu anali atalonjezera. Pa Hoseya 14:4-7 pamati: “[Ine Yehova] ndidzachiritsa kubwerera kwawo, ndidzawakonda mwaufulu; pakuti mkwiyo wanga wam’chokera. Ndidzakhala kwa Israyeli ngati mame; adzachita maluwa ngati kakombo, ndi kutambalalitsa mizu yake ngati Lebano. Nthambi zake zidzatambalala, ndi kukoma kwake kudzanga kwa mtengo wa azitona, ndi fungo lake ngati Lebano. Iwo okhala pansi pa mthunzi wake adzabwera, nadzatsitsimuka ngati tirigu, nadzaphuka ngati mpesa, chikumbukiro chake chidzanga vinyo wa Lebano.”

22 Aisrayeli olapa anali kudzachiritsidwa mwauzimu ndi kukondedwanso ndi Mulungu. Yehova anali kudzakhala ngati mame otsitsimula kwa iwo mwa kuwadalitsa kwambiri. Anthu ake obwezeretsedwawo anali kudzakhala ‘okoma ngati mtengo wa azitona,’ ndipo anali kudzayenda m’njira za Mulungu. Popeza kuti ife tikutsimikiza kuti tidzayenda ndi Yehova Mulungu, kodi tikufunika kuchita chiyani?

Yendanibe M’njira Zoongoka za Yehova

23, 24. Kodi buku la Hoseya likumaliza ndi ulosi wolimbikitsa uti, ndipo umatikhudza motani?

23 Kuti tipitirize kuyenda ndi Mulungu, tiyenera kukhala ndi “nzeru yochokera kumwamba” ndi kuchita zinthu zogwirizana ndi njira zake zoongoka. (Yakobo 3:17, 18) Vesi lomaliza la ulosi wa Hoseya likunena kuti: “Wanzeru ndani, kuti azindikire izi? Waluntha, kuti adziwe izi? Pakuti njira za Yehova zili zoongoka; ndipo olungama adzayendamo, koma olakwa adzagwamo.”​—Hoseya 14:9.

24 M’malo motsogozedwa ndi nzeru ndi mfundo za dzikoli, titsimikize kuyenda m’njira zoongoka za Mulungu. (Deuteronomo 32:4) Hoseya anachita zimenezo kwa zaka 59 kapena kuposapo. Iye anapereka mauthenga a Mulungu mokhulupirika, podziwa kuti anzeru ndi aluntha akazindikira mawuwo. Nanga ifeyo bwanji? Kaya Yehova adzatilola kuchitira umboni mpaka liti, tidzapitirizabe kufunafuna anthu amene mwanzeru adzalandira kukoma mtima kwake. Ndipo tikusangalala kuchita zimenezi mogwirizana kotheratu ndi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.”​—Mateyu 24:45-47.

25. Kodi zimene takambirana zokhudza ulosi wa Hoseya ziyenera kutithandiza kuchita chiyani?

25 Zimene takambirana zokhudza ulosi wa Hoseya ziyenera kutithandiza kuyendabe ndi Mulungu, tikuyembekeza moyo wosatha m’dziko lake latsopano limene analonjeza. (2 Petro 3:13; Yuda 20, 21) Koma ndiye chiyembekezo chimene tili nacho n’chabwino kwambiri! Ndipotu chiyembekezo chimenecho chidzakwaniritsidwa kwa ife aliyense payekha ngati tipitiriza kusonyeza mwa mawu ndi zochita zathu kuti tikamanena kuti, “njira za Yehova zili zoongoka,” timakhala tikunenadi zochokera pansi pa mtima.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Ngati tipembedza Mulungu m’njira yoyera, kodi iye adzachita nafe motani?

• N’chifukwa chiyani tiyenera kuyembekeza Yehova nthawi zonse?

• N’chifukwa chiyani muli otsimikiza kuti njira za Yehova zili zoongoka?

• Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tiziyendabe m’njira za Yehova zoongoka?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 28]

Landirani thandizo lauzimu kwa akulu achikristu

[Chithunzi patsamba 29]

Ulosi wa Hoseya umatipatsa chifukwa choyembekezera malonjezo a Yehova oti akufa adzauka

[Zithunzi patsamba 31]

Yendanibe ndi Mulungu mukumayembekeza moyo wosatha