Mafunso Ochokera kwa Owerenga
Mafunso Ochokera kwa Owerenga
Kodi Yesu anali kuchenjeza za zinthu zoopsa zitatu ziti pa Mateyu 5:22?
Pa ulaliki wake wa pa phiri, Yesu Kristu anachenjeza otsatira ake kuti: “Ndinena kwa inu, kuti yense wokwiyira mbale wake wopanda chifukwa adzakhala wopalamula mlandu; ndipo amene adzanena ndi mbale wake, Wopanda pake iwe, adzakhala wopalamula mlandu wa akulu: koma amene adzati, Chitsiru iwe: adzakhala wopalamula gehena wamoto.”—Mateyu 5:22.
Yesu anagwiritsa ntchito zinthu zodziwika kwa Ayuda, zomwe ndi wopalamula mlandu, mlandu wa akulu, ndi Gehena wamoto, kuwasonyeza bwino za kusiyana kwa zilango za machimo owopsa.
Choyamba, Yesu ananena kuti yense wokwiyira mbale wake wopanda chifukwa adzakhala “wopalamula mlandu,” kapena kuti mlandu wa kukhoti. Malinga ndi mwambo wa nthawi imeneyo, makhoti amenewa ankaikidwa mu mzinda womwe uli ndi amuna akuluakulu okwana 120 kapena kuposerapo. (Mateyu 10:17; Marko 13:9) Oweruza m’makhoti amenewa anali ndi udindo wopereka chiweruzo, ngakhale pa milandu yakupha. (Deuteronomo 16:18; 19:12; 21:1, 2) Choncho, Yesu anasonyeza kuti munthu amene amadana ndi mbale wake ndiye kuti akuchita tchimo lalikulu.
Kenako Yesu ananena kuti munthu amene “adzanena ndi mbale wake, Wopanda pake iwe, adzakhala wopalamula mlandu wa akulu.” Liwu la Chigiriki lakuti rha·kaʹ limene analimasulira kuti “wopanda pake” limatanthauza “wachabechabe” kapena kuti “wopanda nzeru.” Malinga ndi The New Thayer’s Greek-English Lexicon of the New Testament, liwu limenelo “ndi liwu lonyoza limene Ayuda ankagwiritsa ntchito m’nthawi ya Kristu.” Choncho Yesu anali kuchenjeza za kuwopsa kosonyeza chidani kwa mbale wako pomulankhula mawu onyoza. Yesu ankatanthauza kuti munthu amene amagwiritsa ntchito mawu amenewo adzaweruzidwa osati chabe ndi khoti laling’ono koma ndi khoti lapamwamba, Sanihedirini yonse. Limeneli linali bungwe loweruza milandu ku Yerusalemu lomwe linkakhala ndi mkulu wa ansembe, kuphatikizapo amuna akulu ndi alembi okwanira 70.—Marko 15:1.
Pomaliza, Yesu analongosola kuti ngati munthu adzati, “Chitsiru iwe,” adzakhala wopalamula Gehena wamoto. Liwu lakuti “Gehena” limachokera ku mawu a Chihebri akuti geh hin·nomʹ, kutanthauza “chigwa cha Hinomu,” chimene chinali kumadzulo mpaka kum’mwera kwa mzinda wakale wa Yerusalemu. M’tsiku la Yesu, chigwachi chinali malo owotcherako zinyalala, kuphatikizapo mitembo ya anthu opalamula milandu amene sankayenerera kuikidwa m’manda. Choncho dzina lakuti “Gehena” linali chizindikiro choyenerera cha chiwonongeko chotheratu.
Kodi nanga liwu lakuti “chitsiru” limatanthauzanji? Liwu limene anagwiritsa ntchito pamenepa limamveka lofanana ndi mawu a Chihebri amene amatanthauza “wopanduka” kapena “wogalukira.” Limasonyeza kuti munthuyo ndi wamakhalidwe opanda pake, wampatuko ndiponso woukira Mulungu. Choncho munthu wonena mnzake kuti “Chitsiru” amatanthauza kuti mbale wakeyo akuyenera kulandira chilango chimene munthu woukira Mulungu angalandire, chimene ndi chiwonongeko chotheratu. Malinga ndi mmene Mulungu amaonera, munthu amene amaweruza mnzake motere, ayenera kulangidwa iyeyo ndi chilango chomwecho, cha chiwonongeko chotheratu.—Deuteronomo 19:17-19.
Motero, Yesu anakhazikitsira otsatira ake khalidwe lapamwamba kuposa limene mfundo za m’Chilamulo cha Mose zinakhazikitsa. Ngakhale kuti anthu ankakhulupirira kuti munthu wakupha mnzake ‘amapalamula mlandu’ wa kukhoti, Yesu anatsindika mfundo ina. Anaphunzitsa otsatira ake kuti ayenera kupewa ngakhale kudana ndi abale awo.—Mateyu 5:21, 22.