Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Yense Adzasenza Katundu Wake wa Iye Mwini”

“Yense Adzasenza Katundu Wake wa Iye Mwini”

“Yense Adzasenza Katundu Wake wa Iye Mwini”

“Munthu aliyense wa ife adzadziwerengera mlandu wake kwa Mulungu.”​—AROMA 14:12.

1. Kodi Ahebri atatu anali ndi udindo wotani womwe anaukwaniritsa bwino?

AHEBRI atatu achinyamata omwe ankakhala ku Babulo anayenera kusankha moyo kapena imfa. Kodi agwadire fano mogwirizana ndi lamulo la dzikolo? Kapena akane kulambira fanolo n’kuponyedwa mng’anjo ya moto? Sadrake, Mesaki ndi Abedinego analibe nthawi yofunsa nzeru kwa wina aliyense; ndipo sanafunikire n’komwe kutero. Mosazengereza iwo anayankha kuti: “Dziwani, mfumu, kuti sitidzatumikira fano lagolidi mudaliimikalo.” (Danieli 3:1-18) Ahebri atatuwo anakwaniritsa udindo wawo wodziwa okha chochita.

2. Kodi ndani kwenikweni amene anamusankhira zochita Pilato pa mlandu wa Yesu Kristu, ndipo kodi potero kazembe wachiromayu anakhala wopanda mlandu?

2 Patatha zaka 600, kazembe wina anam’bweretsera munthu kuti amuzenge mlandu. Ataiona bwinobwino nkhaniyo anaona kuti munthu woimbidwa mlanduyo n’ngosalakwa. Koma chikhamu cha anthu chinkafuna kuti munthuyo aphedwe. Kazembeyo anayesa kutsutsana ndi anthuwo, koma sanachite khama kusenza udindo wake ndipo anagonjera zofuna za anthuwo. Iye anasamba m’manja n’kunena kuti: “Ine ndilibe kuchimwira mwazi wa munthu uyu wolungama.” Kenaka anapereka munthuyo kuti apachikidwe. M’malo mosenza udindo wake pankhani yoweruza Yesu Kristu, Pontiyo Pilato analola kuti anthu amuchitire udindo umenewu. Ngakhale adakasamba m’manja chotani sakanachotsa mlandu wake woweruza Yesu m’njira yolakwika yoteroyo.​—Mateyu 27:11-26; Luka 23:13-25.

3. N’chifukwa chiyani sibwino kulola anthu ena kutisankhira zochita?

3 Nanga inuyo bwanji? Kodi mukamaganiza zochita, mumachita zinthu monga Ahebri atatu aja, kapena mumalola kuti anthu ena achite kukusankhirani zochita? Kusankha zochita n’kovuta. Kuti munthu asankhe zochita zanzeru pamafunika uchikulire. Mwachitsanzo, makolo ayenera kuganizira bwino zinthu zoti ana awo aang’ono achite. Kusankha zochita kumavuta kwambiri ngati nkhani yake ili yovuta komanso yofunika kuganizira zinthu zosiyanasiyana. Komabe, udindo wosankha zochita sikuti ndi waukulu kwambiri moti n’kuuika m’gulu la “zothodwetsa” zimene anthu “auzimu” angatithandize kunyamula. (Agalatiya 6:1, 2) Koma udindo umenewu ndi katundu amene “munthu aliyense wa ife adzadziwerengera mlandu wake kwa Mulungu.” (Aroma 14:12) Baibulo limati “yense adzasenza katundu wake wa iye mwini.” (Agalatiya 6:5) Komano kodi tingasankhe bwanji zinthu mwanzeru pa moyo wathu? Choyamba tiyenera kudziwa kuti poti ndife anthu timaperewera mbali zina ndipo tiyenera kudziwa mmene tingakonzere mbali zoperewerazo.

Chinthu Chofunika Kwambiri

4. Kodi kusamvera kwa anthu awiri oyambirira kungatiphunzitse mfundo yotani yofunika pa nkhani ya kusankha zochita?

4 Anthu awiri oyambirira anasankha zinthu zimene zinabweretsa mavuto adzaoneni. Iwo anasankha kudya chipatso cha mtengo wodziwitsa zabwino ndi zoipa. (Genesis 2:16, 17) Kodi anasankha choncho chifukwa chiyani? Baibulo limati: “Anaona mkaziyo kuti mtengo unali wabwino kudya, ndi kuti unali wokoma m’maso, mtengo wolakalakika . . . anatenga zipatso zake, nadya, napatsanso mwamuna wake amene ali naye, nadya nayenso.” (Genesis 3:6) Hava anasankha zimenezi chifukwa cha dyera. Zimene anachitazo zinachititsa kuti Adamu achite zomwezo. Motero, uchimo ndi imfa ‘zinafikira anthu onse.’ (Aroma 5:12) Kusamvera kwa Adamu ndi Hava kuyenera kutiphunzitsa mfundo yofunikira yokhudza kulephera kwa anthufe. Mfundo yake n’njakuti anthu akapanda kutsatira malangizo a Mulungu, amasankha kuchita zolakwika.

5. Kodi Yehova watipatsa malangizo otani, ndipo tingatani kuti tipindule nawo?

5 Tiyenera kusangalala kwambiri kuti Yehova anatipatsa malangizo oyenera kutsatira. Malemba amati: “Makutu ako adzamva mawu kumbuyo kwa iwe akuti, Njira ndi iyi, yendani inu m’menemo: potembenukira inu kulamanja, ndi potembenukira kulamanzere.” (Yesaya 30:21) Yehova amalankhula nafe kudzera m’Mawu ake ouziridwa, Baibulo. Tiyenera kuwerenga Malemba ndi kuwadziwa bwino. Kuti tisankhe zochita zolondola, tiyenera kudya ‘chakudya chotafuna cha anthu akulu msinkhu.’ ‘Mwa kuchita nawo’ timafika ‘pozoloweretsa maganizo athu kusiyanitsa chabwino ndi choipa.’ (Ahebri 5:14) Tingathe kuphunzitsa maganizo athu pogwiritsira ntchito zimene timawerenga m’Mawu a Mulungu.

6. Kodi m’pofunika chiyani kuti chikumbumtima chathu chizigwira ntchito yake bwino?

6 Chikumbumtima, chimene tonsefe timabadwa nacho, n’chofunika kwambiri posankha zochita. Chikumbumtima chimatha kuweruza, ndipo chingathe ‘kutitsutsa ngakhalenso kutivomereza.’ (Aroma 2:14, 15) Komabe, kuti chikumbumtima chathu chigwire ntchito bwinobwino, chiyenera kuunikiridwa ndi mfundo zolondola za m’Mawu a Mulungu ndipo chiyenera kulimbikitsidwa potsatira Mawuwo kuti chikhale champhamvu. Chikumbumtima chosaunikiridwa bwino chimatha kutengeka mosavuta ndi miyambo ndiponso zizolowezi za kudera limene munthu akukhala. Tingathenso kusokonezedwa ndi maganizo a anthu ena. Kodi n’chiyani chimachitika ngati chikumbumtima chathu timangochinyalanyaza n’kumaphwanya mfundo za Mulungu? Pamapeto pake chikumbumtimacho chimadzakhala ‘cholochedwa monga chitsulo chamoto,’ n’kukhala ngati khungu lokakala la chipsera cha moto, lomwe silimva kanthu mukalikhudza. (1 Timoteo 4:2) Komano, chikumbumtima chophunzitsidwa ndi Mawu a Mulungu chimakhala chodalirika.

7. Kodi chofunika kwambiri kuti munthu asankhe bwino zochita n’chiyani?

7 Motero, chinthu chofunika kwambiri kuti tikwaniritse udindo wathu wosankha bwino zochita, ndicho kudziwa bwino Malemba ndi kudziwa kuwagwiritsa ntchito. M’malo mochita zinthu mopupuluma, tiyenera kukhala kaye pansi n’kufunafuna mfundo za m’Baibulo, n’kuziganizira bwinobwino kuti tione mmene tingazigwiritsire ntchito. Ngati tikudziwa Mawu a Mulungu molondola ndiponso ngati chikumbumtima chathu chimatsatira Mawu a Mulungu, ngakhale titafunika kusankha zochita mwadzidzidzi, monga anachitira Sadrake, Mesaki ndi Abedinego, timakhala achikwanekwane. Kuti tione mmene kukhwima maganizo mwauzimu kungatithandizire kuti tizisankha bwino zinthu, tiyeni tione mbali ziwiri za moyo.

Kodi Tizicheza ndi Anthu Otani?

8, 9. (a) Kodi ndi mfundo ziti zimene zimasonyeza kufunika kopewa mayanjano oipa? (b) Kodi mayanjano oipa amangotanthauza kucheza pamaso m’pamaso ndi anthu opanda khalidwe? Longosolani.

8 Mtumwi Paulo analemba kuti: “Musanyengedwe; mayanjano oipa aipsa makhalidwe okoma.” (1 Akorinto 15:33) Yesu Kristu anauza ophunzira ake kuti: “Simuli a dziko lapansi.” (Yohane 15:19) Tikadziwa mfundo zimenezi, nthawi yomweyo timazindikira kuti ndibwino kupewa kucheza ndi adama, achigololo, akuba, oledzera, ndi anthu ena otero. (1 Akorinto 6:9, 10) Komabe tikamadziwa zambiri zokhudza choonadi cha m’Baibulo, timazindikira kuti ngakhale kuonerera mafilimu, mapulogalamu a pa TV, kapena zinthu zina za pakompyuta kapenanso kuwerenga mabuku okhala ndi anthu oterewa, kungatisokonezenso chimodzimodzi. N’chimodzimodzinso kucheza pa Intaneti ndi “anthu otyasika” kapena kuti odzibisa.​—Salmo 26:4.

9 Nanga bwanji kucheza ndi anthu amene mwina ali ndi makhalidwe abwino koma sakhulupirira Mulungu woona? Malemba amatiuza kuti: “Dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19) Timafika pozindikira kuti akati mayanjano oipa satanthauza anthu olowerera okhaokha kapena anthu akhalidwe loipa okha. Motero n’chinthu chanzeru kuonetsetsa kuti anzathu apamtima azikhala amene amakonda Yehova basi.

10. Kodi n’chiyani chimatithandiza kuganiza mwauchikulire pa nkhani ya kucheza ndi anthu akudziko?

10 N’zosatheka kupeweratu anthu akudziko ndipo palibe lamulo loti tizipeweratu anthu otere. (Yohane 17:15) Timakumana ndi anthu akudziko mu utumiki wachikristu, kusukulu, ndiponso kuntchito. Mkristu amene anakwatirana ndi munthu wosakhulupirira amakhala ndi anthu akunja nthawi zambiri kuyerekezera ndi Akristu ena. Komabe, tikaganizira mwanzeru tingathe kuona kuti kucheza ndi anthu akunja kwa kanthawi chabe pa nkhani zofunika n’kosiyana ndi kukhala nawo pa ubwenzi wa ponda apa m’pondepo. (Yakobo 4:4) Motero timatha kuganiza mwauchikulire pa nkhani zokhudza kuchita zinthu zinazake kusukulu, monga zamasewera ndi zovina, kapena kupita ku maphwando akuntchito kwathu.

Kusankha Ntchito

11. Kodi chinthu choyamba chimene tiyenera kuchiganizira pankhani yopeza ntchito n’chiyani?

11 Kutsatira mfundo za m’Baibulo mwauchikulire kumatithandiza kuganiza bwino zochita pa nkhani ya mmene tingakwaniritsire udindo ‘wosunga mbumba yathu.’ (1 Timoteo 5:8) Chinthu choyamba kuchiganizira ndicho mtundu wa ntchitoyo, kapena kuti zimene tizifunikira kuchita pantchitoyo. N’zachidziwikire kuti n’kulakwa kusankha ntchito imene imalimbikitsa kuchita zinthu zimene Baibulo limaletseratu. Motero Akristu oona salola ntchito zokhudzana ndi kulambira mafano, kuba, kugwiritsa ntchito magazi molakwa, kapena zinthu zina zoletsedwa m’Malemba. Chinanso, sitingalolere kunama kapena kuba, ngakhale ngati bwana wathu atafuna kuti titero.​—Machitidwe 15:29; Chivumbulutso 21:8.

12, 13. Kodi poganizira ntchito yoyenera kugwira pali zinthu zinanso ziti kuphatikizapo ntchito yeniyeniyo zimene tiyenera kuziganizira bwino?

12 Nanga tingatani ngati ntchitoyo payokha siyophwanya lamulo lililonse la Mulungu? Tikamawonjezera zimene tikudziwa pa choonadi ndiponso tikayamba kuganiza mwauchikulire, timafika pozindikira kuti pali zinthu zinanso zimene tiyenera kuziganizira. Bwanji ngati ntchitoyo ili yokhudzana ndi zinthu zosemphana ndi Malemba, monga kuyankha mafoni pa malo otchovera njuga? Tiyeneranso kuganizira za kumene ndalama zotilipirira zikuchokera komanso tiyenera kuganizira za malo amene timagwirira ntchitoyo. Mwachitsanzo, kodi Mkristu amene ali ndi bizinesi yakeyake yopenta nyumba angafune kugwira ntchito yopenta matchalitchi pamene akudziwiratu kuti kutero n’kulimbikitsa nawo chipembedzo chonyenga?​—2 Akorinto 6:14-16.

13 Koma bwanji ngati kuntchito kwathu bwana wapeza ntchito yopenta malo a chipembedzo chonyenga? Pamenepa m’pofunika kuona bwino nkhani yonseyo. Tingadzifunse mafunso ngati akuti, ‘Kodi ineyo ndikakhala ndi udindo waukulu motani pa ntchitoyo?’ ‘Kodi ndikachita nawo ntchitoyo mpaka kufika pati?’ Nanga bwanji kugwira ntchito zina zosatsutsana ndi Baibulo, monga ntchito yofuna kuti muzikapereka makalata pena paliponse m’dera linalake, kuphatikizapo malo amene amachitako zinthu zosayenera? Kodi mfundo yotchulidwa pa Mateyu 5:45 sitingaigwiritse ntchito pamenepa? Sitiyeneranso kunyalanyaza mmene kugwira ntchitoyo tsiku ndi tsiku kungakhudzire chikumbumtima chathu. (Ahebri 13:18) N’zoona kuti kusenza udindo wosankha zochita mwauchikulire pankhani ya ntchito kumafunika kuti tinole nzeru zathu ndi kuphunzitsa chikumbumtima chimene Mulungu anatipatsa.

“Um’lemekeze M’njira Zako Zonse”

14. Kodi tikamasankha zochita pankhani inayake tiyenera kuganizira chiyani nthawi zonse?

14 Nanga bwanji zinthu zina zimene timasankha kuchita, monga za maphunziro ndiponso zovomera kapena kukana chithandizo chinachake cha mankhwala? Tikamasankha chochita pa nkhani iliyonse, tiyenera kuona bwinobwino mfundo zonse za m’Baibulo zogwirizana ndi nkhani imeneyo kenaka n’kuganizira mofatsa mfundozo kuti tione mmene tingazigwiritsire ntchito pankhaniyo. Solomo, mfumu ya nzeru ya ku Israyeli inati: “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako; um’lemekeze m’njira zako zonse, ndipo Iye adzaongola mayendedwe ako.”​—Miyambo 3:5, 6.

15. Kodi tikuphunzirapo chiyani kwa Akristu oyambirira pankhani ya kusankha zochita?

15 Nthawi zambiri zimene timachita zimakhudzanso anthu ena, motero mfundo imeneyi tiyenera kuiganizira. Mwachitsanzo, Akristu oyambirira sanalinso pansi pa malamulo ambiri a m’Chilamulo cha Mose oletsa zakudya zinazake. Akanatha kusankha kudya zakudya zinazake zimene m’Chilamulo zinali zodetsedwa koma zimene zinalibe vuto lina lililonse. Komabe, mtumwi Paulo anatchulapo za nyama imene inakafika pa kachisi wa milungu ya mafano. Iye anati: “Ngati chakudya chikhumudwitsa mbale wanga, sindidzadya nyama ku nthawi yonse, kuti ndingakhumudwitse mbale wanga.” (1 Akorinto 8:11-13) Akristu oyambirira ankalimbikitsidwa kuti aziganizira chikumbumtima cha anthu ena kuti asawakhumudwitse. Zimene timasankha kuchita ‘zisamakhumudwitse’ ena.​—1 Akorinto 10:29, 32.

Funafunani Nzeru za Mulungu

16. Kodi pemphero limatithandiza bwanji tikamasankha zochita?

16 Chinthu chofunika kwambiri tikasankha zochita ndicho pemphero. Wophunzira Yakobo anati: “Wina wa inu ikam’sowa nzeru, apemphe kwa Mulungu, amene apatsa kwa onse modzala manja, niwosatonza; ndipo adzam’patsa iye.” (Yakobo 1:5) Mosakayika, tizipemphera kwa Yehova n’kumufunsa kuti atipatse nzeru zimene tikufunikira kuti tiganizire moyenerera zinthu zoyenera kuchitazo. Tikamamuuza Mulungu woona nkhawa zathu ndi kupempha kuti atitsogolere, mzimu woyera ungatithandize kumvetsa bwino malemba amene tikuwaganizira n’kutikumbutsa ena amene mwina sitinawaganizire.

17. Kodi ena angatithandize bwanji tikamasankha zochita?

17 Kodi anthu ena angatithandize kusankha zochita? Inde, Yehova watipatsa anthu okhwima maganizo mumpingo. (Aefeso 4:11, 12) Tingathe kufunsa anthu amenewa, makamaka ngati zimene tikufuna kuchitazo zili zazikulu. Anthu amene ali ndi nzeru zozama ndiponso amene aona zambiri pamoyo angathe kutikumbutsa mfundo zina za m’Baibulo zimene zingatithandize kuganizira bwino nkhaniyo n’kutithandiza ‘kutsimikizira zinthu zofunika kwambiri.’ (Afilipi 1:9, 10, NW) Komabe apa m’pofunika chenjezo: Tisamale kusalola ena kutisankhira zochita. Tiyenera kusenza tokha udindo umenewu.

Kodi Zimathandiza Nthawi Zonse?

18. Kodi tinganene chiyani pankhani ya zimene zingachitike tikasankha kuchita zinthu zolondola?

18 Kodi tikasankha zinthu mogwirizana ndendende ndi mfundo za m’Baibulo ndiponso chikumbumtima chathu nthawi zonse zinthuzo zimayenda bwino? Inde, zimayenda bwino pamapeto pake. Komabe nthawi zina mwina zimaoneka kuti sizinayende bwino panthawi imeneyoyo. Sadrake, Mesaki, ndi Abedinego ankadziwa kuti akakana kulambira fano lija akhoza kuphedwa. (Danieli 3:16-19) Chimodzimodzinso, atumwi atauza Sanihedirini kuti ayenera kulambira Mulungu koposa anthu, anawakwapula kaye asanawamasule. (Machitidwe 5:27-29, 40) Ndiponsotu zinthu ‘zongotigwera’ zingathe kusokoneza zinthu zimene tasankha kuchitazo. (Mlaliki 9:11) Ngati zimene tasankha kuchita zatiika m’mavuto m’njira inayake ngakhale kuti zinali zolondola, tisakayike kuti Yehova atithandiza kupirira ndipo pamapeto pake atidalitsa.​—2 Akorinto 4:7.

19. Kodi tingasenze bwanji molimba mtima udindo wathu pankhani ya kusankha zochita?

19 Motero, tikamasankha zochita, tiyenera kufunafuna mfundo za m’Malemba ndi kuziganizira mozama kuti tizigwiritse ntchito moyenerera. Tiyenera kuyamikira kwambiri kuti Yehova watipatsa mzimu wake woyera ndiponso anthu okhwima maganizo mumpingo! Popeza tili ndi thandizo limeneli, tiyeni tisenze udindo wathuwu molimba mtima posankha bwino zinthu zoyenera kuchita.

Kodi Mwaphunzirapo Chiyani?

• Kodi n’chiyani chimene chili chofunika kwambiri posankha zochita?

• Kodi kukula mwauzimu kumakhudza bwanji nkhani ya anzathu amene timasankha?

• Kodi pali mfundo zina ziti zofunikira zimene tiyenera kuziganizira pankhani ya ntchito?

• Kodi pali thandizo lanji pa nkhani yosankha zochita?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 22]

Kusamvera kwa Adamu ndi Hava kumatipatsa phunziro lofunikira kwambiri

[Chithunzi patsamba 24]

Tisanasankhe kuchita zinazake zofunikira, tizifufuza kaye mfundo za m’Baibulo zogwirizana ndi nkhaniyo