Kodi Melito wa ku Sarde Anatetezadi Choonadi cha M’Baibulo?
Kodi Melito wa ku Sarde Anatetezadi Choonadi cha M’Baibulo?
CHAKA ndi chaka Akristu oona amachita mwambo wa Mgonero wa Ambuye patsiku logwirizana ndi tsiku la Nisani 14 pa kalendala ya Ahebri. Pochita izi iwo amakhala akutsatira lamulo la Yesu lakuti: “Chitani ichi chikumbukiro changa.” Patsikuli, m’chaka cha 33 C.E. Yesu, atatha kuchita mwambo wa Paskha, anayambitsa Chikumbutso cha imfa yake yansembe. Iye anamwalira tsiku lomwelo.—Luka 22:19, 20; 1 Akorinto 11:23-28.
M’kati mwa zaka za m’ma 100 C.E. anthu ena anayamba kusintha nthawi ya mwambowu ndiponso kachitidwe kake. Ku Asia Minor anthu anapitiriza kugwiritsa ntchito deti limene Yesu anafa. Koma, mogwirizana ndi zomwe buku lina linanena, “ku Roma ndi ku Alesandriya anthu ankachita mwambo wokumbukira kuuka kwa akufa patsiku Lamlungu lotsatira deti la imfa ya Yesu,” ndipo ankatcha mwambowo kuti Paskha wa Kuuka kwa Akufa. Gulu lina lomwe linkadziwika ndi dzina loti Anthu Osunga Tsiku la Khumi ndi Chinayi linalimbikitsa zoti azikumbukira imfa ya Yesu Kristu pa Nisani 14. Naye Melito wa ku Sarde anali ndi maganizo amenewa. Kodi Melito anali ndani? Kodi anateteza motani choonadi cha m’Baibulo ndi mfundo zina?
‘Nyali Yowala Kwambiri’
Chakumapeto kwa zaka za m’ma 100 C.E., malinga ndi zimene analemba Eusebius wa ku Kaisareya m’buku lake lakuti Ecclesiastical History, Polycrates wa ku Efeso anatumiza kalata ku Roma pofuna kuteteza mwambo wa imfa ya Yesu wochitika “tsiku lakhumi ndi chinayi la Paskha mogwirizana ndi Uthenga Wabwino, osapatuka ngakhale pang’ono, koma kutsatira malamulo [achikristu].” Malinga ndi kalatayi, Melito, yemwe anali Bishopu wa ku Sarde, ku Lidiya, anali mmodzi wa anthu amene analimbikitsa kuti azichita mwambowu pa Nisani 14. Kalatayi inafotokoza kuti anthu a m’nthawi yake ankaona Melito kuti anali mmodzi wa ‘nyali zowala kwambiri zomwe zinamwalira.’ Polycrates ananena kuti Melito sanakwatire ndiponso “moyo wake wonse unali wogwirizana ndi Mzimu Woyera ndipo anaikidwa m’manda ku Sarde komwe anali kudikira kumva akumuitana kuchokera kumwamba Chivumbulutso 20:1-6.
pamene adzauke kwa akufa.” Izi zingathe kutanthauza kuti Melito anali mmodzi wa anthu amene ankakhulupirira kuti kuuka kwa akufa kudzachitika pokhapokha Kristu atabweranso.—Motero, zikuoneka kuti Melito anali munthu wolimba mtima komanso wakhama akafuna kuchita zinthu. Ndipotu, analemba buku la Apology pofuna kuteteza Akristu, ndipo limeneli ndi buku loyamba kutchulidwa kuti linapita kwa Marcus Aurelius, yemwe anali mfumu ya Roma kuyambira mu 161 mpaka 180 C.E. Melito analibe mantha poteteza Chikristu ndipo anadzudzula anthu oipa ndi adyera. Anthu amenewa ankapempha mfumu kuti ikhazikitse malamulo, kuti iwo apezerepo mwayi wozunza ndi kukhaulitsa Akristu, n’cholinga chowabera katundu.
Pa zimene analembera mfumu ija, Melito ananena molimba mtima kuti: “Tikungofuna kukupemphani kuti, inuyo muone bwino za anthu amene amayambitsa mavuto a [Akristu], ndi kugamulapo mosakondera ngati ndi oyenera kuphedwa ndi kulangidwa kapena ngati ndi oyenera kukhala mwabata ndi kutetezedwa. Koma ngati malangizo ndi lamulo latsopanoli, lomwe siloyenera kukhazikitsira ngakhale zigawenga, silochokera kwa inu, tikukuchondererani kuti musatinyalanyaze ife amene tikulandidwa katundu ndi anthu otizunza.”
Anagwiritsa Ntchito Malemba Poteteza Chikristu
Melito anali ndi chidwi chachikulu chophunzira Malemba Opatulika. Panopa palibe mndandanda wa mabuku onse amene iye analemba, komabe ina mwa mitu ya mabuku ake imasonyeza chidwi chomwe anali nacho pa nkhani za m’Baibulo. Ena mwa mabuku ake onena za chipembedzo ndi On Christian Life and the Prophets, On the Faith of Man, On Creation, On Baptism and Truth and Faith and Christ’s Birth, On Hospitality, The Key, ndi loti On the Devil and the Apocalypse of John.
Melito anapanga ulendo wopita ku madera otchulidwa m’Baibulo pofuna kukafufuza chiwerengero chenicheni cha mabuku a Malemba Achihebri. Pankhaniyi iye analemba kuti: “Motero, nditapita Kum’mawa n’kufika kumalo
omwe ankalalikira ndi kuchita zinthu zimenezi, ndipo nditaphunzira bwino mabuku a Chipangano Chakale n’kulemba mfundo zake zenizeni, ndinakutumizirani.” Mndandandawu ulibe mabuku a Nehemiya ndi Estere, komabe ndi mndandanda wakale kwambiri wa mabuku ovomerezeka a Malemba Achihebri pa mabuku omwe anthu odzitcha Akristu analemba.Pakafukufuku wakeyo, Melito analemba pamodzi mavesi osiyanasiyana a m’Malemba Achihebri omwe anali ndi maulosi onena za Yesu. Buku lina la Melito, lakuti Extracts, limasonyeza kuti Yesu anali Mesiya yemwe anthu anamuyembekezera kwa nthawi yaitali ndiponso kuti Chilamulo cha Mose komanso Aneneri anali ataneneratu za Kristu.
Kuteteza Dipo
Mizinda ikuluikulu ya ku Asia Minor inali ndi Ayuda ambiri. Ayuda a ku Sarde, komwe Melito ankakhala, ankachita mwambo wa Paskha wa Ahebri pa Nisani 14. Melito analemba buku lakuti The Passover lomwe linasonyeza kufunika kochita Paskha m’Chilamulo ndiponso ananena kuti mwambo wa Mgonero wa Ambuye womwe Akristu amachita, uyenera kuchitika pa Nisani 14.
Atafotokoza maganizo ake pa chaputala 12 cha buku la Eksodo n’kusonyeza kuti Paskha anaimira nsembe ya Kristu, Melito anafotokoza chifukwa chake zinali zosamveka kuti Akristu azichita Paskha. Izi zinali choncho chifukwa chakuti Mulungu anali atathetsa Chilamulo cha Mose. Kenako anasonyeza chifukwa chake nsembe ya Kristu inali yofunika, kuti: Mulungu anaika Adamu m’paradaiso kuti azikhalamo mosangalala. Koma munthu woyambayu sanamvere lamulo lomuletsa kudya zipatso za mtengo wodziwitsa zabwino ndi zoipa. Apa m’pamene panayambira kufunika kwa dipo.
Melito anafotokozanso kuti Yesu anatumidwa ku dziko lapansi ndi kufa pamtengo kuti awombole ku uchimo ndi imfa anthu okhulupirira. N’zochititsa chidwi kuti Melito anagwiritsa ntchito mawu a Chigiriki akuti xylon, otanthauza “mtengo,” polemba za mtengo womwe Yesu anaferapo.—Machitidwe 5:30; 10:39; 13:29.
Melito sikuti anali kudziwika ku Asia Minor kokha. Tertullian, Clement wa ku Alesandriya, ndiponso Origen ankadziwa za mabuku ake. Komabe, katswiri wina wa mbiri yakale, dzina lake Raniero Cantalamessa, anati: “Kutha kwa Melito, komwe kunachititsa kuti mabuku ake ayambe kusowa pang’onopang’ono, kunayambika Paskha wa Lamlungu atakhazikika, ndipo panthawiyi anthu anayamba kuona Anthu Osunga Tsiku la Khumi ndi Chinayi ngati ampatuko.” M’kupita kwa nthawi, mabuku a Melito anasoweratu.
Kodi Anasokonezeka ndi Mpatuko?
Atumwi atatha kufa, mpatuko womwe unali utaloseredwa kale unalowa mu Chikristu choona. (Machitidwe 20:29, 30) N’zoonekeratu kuti zimenezi zinasokoneza Melito. Kalembedwe ka mabuku ake komwe kanali kovuta kumvetsa, kamagwirizana ndi mabuku a anthu okonda nzeru ya Agiriki ndi Aroma. Mwina ndi chifukwa chake Melito anatcha Chikristu kuti “nzeru yathu.” Komanso ankaona kuti kuphatikiza chipembedzo chotchedwa Chikristu ndi Ufumu wa Roma kunali “umboni wamphamvu . . . wakuti zinthu zikuyenda bwino.”
Mwachionekere Melito sanatsatire malangizo a mtumwi Paulo akuti: “Penyani kuti pasakhale wina wakulanda inu ngati chuma, mwa kukonda nzeru kwake, ndi chinyengo chopanda pake, potsata mwambo wa anthu, potsata zoyamba za dziko lapansi, osati potsata Kristu.” Motero, ngakhale kuti Melito anatetezako pang’ono mfundo za choonadi cha m’Baibulo, koma pa zinthu zambiri analephera kutsatira mfundozo.—Akolose 2:8.
[Chithunzi patsamba 18]
Yesu anayambitsa mwambo wa Mgonero wa Ambuye pa Nisani 14