Musaope Yehova Ali Nanu
Musaope Yehova Ali Nanu
ZAKA zoposa 50 zapitazo, bomba loyamba la nyukiliya litangophulitsidwa chakumene, Harold C. Urey, wasayansi yemwe analandira mphoto yapamwamba ya Nobel Prize, analongosola tsogolo la anthu motere: “Tidzadya mwamantha, kugona mwamantha, kukhala mwamantha ndiponso kufa mwamantha.” Masiku ano, dziko lathuli ladzazadi ndi zinthu zambiri zochititsa mantha, ndipotu m’pake. Tsiku lililonse, manyuzipepala amafalitsa nkhani zoopsa zofotokoza za uchigawenga, ziwawa, ndi za matenda oopsa osadziwika bwinobwino.
Akristufe timadziwa tanthauzo la zinthu zimenezi. Zimasonyeza kuti tikukhala m’nthawi imene Baibulo limati “masiku otsiriza” a dongosolo loipa lino. Baibulo linati nthawiyi idzadziwika ndi “nthawi zowawitsa.” (2 Timoteo 3:1) Motero zimenezi zimatilimbitsa mtima kuti Yehova Mulungu watsala pang’ono kubweretsa dziko latsopano limene mudzakhale chilungamo. (2 Petro 3:13) Komabe, kodi pakali pano sitikhudzidwa ndi zinthu zochititsa mantha?
Mmene Atumiki a Mulungu Amaonera Mantha
Yakobo, Davide, ndi Eliya anali ena mwa atumiki a Yehova amene anachita mantha atakumana ndi zoopsa. (Genesis 32:6, 7; 1 Samueli 21:11, 12; 1 Mafumu 19:2, 3) Komatu iwowa sikuti analibe chikhulupiriro ayi. Anasonyeza kuti amadalira Yehova ndi mtima wonse. Komabe, Yakobo, Davide, ndi Eliya anali anthu basi, moti nawonso ankachita mantha. Wophunzira Yakobo analemba kuti: “Eliya anali munthu wakumva zomwezi tizimva ife.”—Yakobo 5:17.
Ifenso tingachite mantha tikamaganizira vuto linalake limene tili nalo kapena limene tidzakhale nalo patsogolo. M’pomveka kukhala ndi mantha oterowo. Pajatu Baibulo limati Satana Mdyerekezi watsimikiza “kuchita nkhondo” ndi anthu “amene asunga malamulo a Mulungu, nakhala nawo umboni wa Yesu.” (Chivumbulutso 12:17) Ngakhale kuti mawu amenewa amanena makamaka za Akristu odzozedwa, Paulo analemba kuti: ‘Onse akufuna kukhala opembedza m’moyo mwa Kristu Yesu, adzamva mazunzo.’ (2 Timoteo 3:12) Komabe, tikakhala pa mavuto sitiyenera kuchita mantha mopitirira muyezo. Chifukwa chiyani?
“Mulungu wa Chipulumutso”
Wamasalmo Davide analemba kuti: “Mulungu akhala kwa ife Mulungu wa chipulumutso.” (Salmo 68:20) Yehova anasonyeza mobwerezabwereza kuti iye amatha kupulumutsa anthu ake, mwina powachotsa m’zovuta kapena powapatsa mphamvu kuti athe kupirira. (Salmo 34:17; Danieli 6:22; 1 Akorinto 10:13) Kodi ndi nkhani zingati za “chipulumutso” zimene mukukumbukira m’nkhani zimene mwakhala mukuwerenga m’Baibulo?
Pogwiritsira ntchito Watch Tower Publications Index, * bwanji osafufuza kuti mudziwe bwino nkhani monga za Chigumula chadziko lonse cha m’masiku a Nowa, za kupulumutsidwa kwa Loti ndi ana ake ku Sodomu ndi Gomora, za ulendo wa Aisrayeli wochoka ku Aigupto n’kudutsa ku Nyanja Yofiira, kapena za chiwembu cha Hamani chofuna kupha Ayuda, chomwe chinalephereka? Kuwerenga ndi kusinkhasinkha nkhani zochititsa chidwi zoterezi kungalimbikitse chikhulupiriro chanu kuti musamakayike zoti Yehova ndi Mulungu wa chipulumutso. Ndipo zimenezi zingakuthandizeni kuthana ndi ziyeso za chikhulupiriro chanu mopanda mantha.
Zitsanzo za Masiku Ano
Kodi mukudziwapo munthu aliyense kwanuko amene ali chitsanzo chamakono cha kupirira?
Angathe kukhala munthu amene anamangidwa chifukwa cha kukhulupirika kwake. Mungathe kudziwa Mkristu wachikulire amene akutumikira Yehova ngakhale kuti n’ngodwaladwala. Kapena ganizirani achinyamata amene amayesetsa kusatengera zinthu zakudziko zimene anzawo ambirimbiri akusukulu amachita. Ndiye palinso makolo olera okha ana popanda mwamuna kapena mkazi. Palinso anthu amene ali mbeta omwe akutumikira Yehova ngakhale kuti nthawi zina amakhala osungulumwa. Kodi mungaphunzire chiyani kwa anthu amenewa? Kuganizira kukhulupirika kwawo kungakuthandizeni kupirira ndi kusachita mantha ngakhale mutakumana ndi ziyeso zotani.Timafunika kusachita mantha osati kokha tikamatsutsidwa kapena kuzunzidwa komanso tikayamba kukayikira zoti Yehova amatikonda. M’pofunika kuti tisamakayike kuti nsembe ya dipo ya Kristu imagwira ntchito kwa ifeyo patokha. (Agalatiya 2:20) Motero tingathe kupemphera kwa Yehova popanda kuchita mantha osayenera. Ngati timaona kuti sindife munthu woti Yehova angam’konde, tiganizire mawu awa omwe Yesu anauza anthu omutsatira: ‘Kodi mpheta ziwiri sizigulidwa kakobiri? Ndipo imodzi ya izo siigwa pansi popanda Atate wanu: komatu inu, tsitsi lonse la m’mutu mwanu liwerengedwa. Chifukwa chake musamaopa; inu mupambana mpheta zambiri.’—Mateyu 10:29-31.
Nthawi zambiri magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! amafalitsa nkhani za Mboni za Yehova za masiku ano zimene zathana kapena zikupirira mavuto osiyanasiyana molimba mtima. Koma sikuti anthuwa panthawi ina sanachitepo mantha ndi mavuto awowo. Anachita mantha, koma sanalole kuti achite kufika posiya kutumikira Yehova. Nkhani zawo zomwe zinafalitsidwazo zingakuthandizeni nanunso kupirira molimba mtima. Taganizirani zitsanzo ziwiri izi.
Ngozi Inasintha Moyo Wake
Mu Galamukani! ya May 8, 2003, muli nkhani yakuti “Mmene Moyo Wanga Unasinthira N’tachita Ngozi.” M’nkhaniyi, Mbale Stanley Ombeva, wa Mboni za Yehova wa ku Kenya, akunenamo za mavuto amene anakumana nawo chifukwa chogundidwa ndi galimoto. Thanzi lake litalowa pansi, anam’chotsa ntchito ndipo akuntchito kwake anasiya kumuthandiza m’njira ina iliyonse. M’nkhaniyo Mbale Ombeva akuti: “Nditaonadi kuti apa zinthu zavuta basi, palibenso chilichonse chimene ndinachiona kuti n’chabwino, sindinkafunanso kumva za wina, ndiponso ndinkangonyanyala msanga. Nthawi zina ndinkangokhala wolunda, ndinkatsutsa china chilichonse.” Ngakhale kuti anali ndi vutoli Mkristuyu analimbabe mtima. Sanalole kuti akhumudwe mpaka n’kungotayiratu mtima. M’malo mwake anadalira Yehova. Mbale Ombeva akuti: “Iye wakhala akundilimbikitsabe kwambiri m’mavuto anga onsewa, moti nthawi zina ndinkaona kuti penapake sindimam’chitira bwino ayi. Ndinakonza zoti ndionetsetse kuti ndawerenga ndi kusinkhasinkha malemba omwe ndinkaona kuti angandilimbikitse pavutoli.”
Mawu oona mtima a Mbale Ombeva anathandiza anthu ena ambiri kupirira ziyeso mosaopa. Mlongo wina wachikristu anati: “Nkhaniyi inandiliritsa nditaiwerenga. Ndinkaona kuti Yehova wagwiritsa ntchito nkhani imeneyi kuti andisonyeze kuti amandikonda, kundisamalira ndiponso kuti amandilimbikitsa.” Mboni inanso inalemba kuti: “Nkhani zoterezi zimalimbitsa mtima kwambiri anthu ngati ifeyo amene timavutika popanda kudandaulira ena.”
Mukavutika Maganizo
Nkhani ina yokhudza mtima kwambiri ndi ya Herbert Jennings, yomwe inalongosoledwa * Mbale Jennings ali ndi matenda a maganizo ochititsa munthu kusinthasintha zochitika. Poganizira za masiku oyambirira a matenda ake, iye anati: “Kunali kovuta kwambiri kuti ndifike pa misonkhano yachikristu. Komabe, ndinkadziwa bwino kwabasi za kufunika kwa mayanjano auzimu. Kuti ndithane ndi zimenezo, nthawi zambiri ndinkalowa m’Nyumba ya Ufumu khamu lonse la anthu litakhala pansi ndipo ndinkatuluka khamulo lisanayambe kuyendayenda pamapeto pa pulogalamu.”
m’nkhani yakuti “Simudziwa Chimene Chidzagwa Mawa.”Kulalikiranso kunkamuvuta. Mbale Jennings anati: “Nthawi zina, ngakhale tikafika panyumba, sindinkatha kulimba mtima mpaka kufika poliza belu la pakhomo. Komabe, sindikanatha kusiya chifukwa ndinkadziwa kuti utumiki umatanthauza chipulumutso kwa ife eni ndiponso kwa aliyense amene amamvetsera ndi kuchitapo kanthu. (1 Timoteo 4:16) Pakapita kanthawi pang’ono, ndimatha kuthetsa nkhawa zanga, n’kupita pakhomo lina, ndi kuyesanso. Mwa kupitiriza kuchita nawo utumiki, ndapitirizabe kukhala wathanzi mwauzimu, ndipo zimenezi zawonjezera kupirira kwanga.”
Nkhani yosabisa kanthu ya Mbale Jennings inathandiza owerenga ambiri kuti nawonso alimbane ndi mavuto awo mosaopa. Mwachitsanzo, mlongo wina wachikristu analemba kuti: “Pa zaka 28 zimene ndakhala ndikuwerenga magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! sindinakhudzidwepo mtima kwambiri ngati mmene ndinakhudzidwira nditawerenga nkhani imeneyi. Ndinasiya kuchita utumiki wa nthawi zonse, koma ndinkadziimba mlandu kwambiri poganiza kuti n’kadakhala ndi chikhulupiriro chokwanira sindikanasiya utumikiwu. Motero nditawerenga nkhaniyi n’kuona kuti Mbale Jennings naye anasiya utumiki kuti adzisamalire pa matenda ake, mtima wanga unakhala m’malo. Ndithu, nkhani imeneyi inali yankho la mapemphero anga.”
Palinso mbale wina wachikristu amene analemba kuti: “Ndinali mkulu kwa zaka 10 koma ndinatula pansi utumiki wamtengo pataliwu chifukwa cha matenda a maganizo. Ndinkadziona kuti ndine munthu wokanika kwambiri moti nthawi zambiri ndinkalefuka kwambiri ndikawerenga nkhani zosimba zinthu zogometsa zosiyanasiyana zomwe anthu a Yehova akumana nazo pamoyo wawo. Koma ndinatsitsimulidwa kwambiri ndi khama la Mbale Jennings. Nkhani imeneyi ndaiwerenga nthawi zambirimbiri.”
Pitirizani Kutumikira Molimba Mtima
Ngakhale kuti Mboni za Yehova zina zili m’mavuto adzaoneni, zambiri zikupitirizabe kulambira Yehova Mulungu molimba mtima, mofanana ndi Mbale Ombeva ndi Mbale Jennings. Ngati inuyo muli m’gulu limeneli dziwani kuti mukuchita bwino kwambiri. Musakayikire kuti: “Mulungu sali wosalungama kuti adzaiwala ntchito yanu, ndi chikondicho mudachionetsera ku dzina lake, umo mudatumikira oyera mtima ndi kuwatumikirabe.”—Ahebri 6:10.
Yehova anathandiza anthu akale okhulupirika kugonjetsa adani awo, ndipo angakuthandizeni inunso kugonjetsa vuto lililonse limene mungakumane nalo. Motero, khulupirirani mawu amene Yehova ananena kudzera mwa mneneri Yesaya, akuti: “Usaope, pakuti Ine ndili pamodzi ndi iwe; usaopsedwe, pakuti Ine ndine Mulungu wako; ndidzakulimbitsa; inde, ndidzakuthangata; inde, ndidzakuchirikiza ndi dzanja langa lamanja la chilungamo.”—Yesaya 41:10.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 9 Yofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
[Zithunzi patsamba 16]
Monga Stanley Ombeva (ali pamwambayu) ndi Herbert Jennings (ali kudzanja lamanjayu), ambiri akutumikira Yehova mosaopa
[Mawu a Chithunzi patsamba 14]
USAF photo