“Ha! Ndikondadi Chilamulo Chanu”
“Ha! Ndikondadi Chilamulo Chanu”
SALMO 119 ndi nyimbo yonena za mmene munthu amene analilemba ankamvera ponena za uthenga, kapena kuti mawu, ouziridwa a Mulungu. Wolemba salmoli anaimba kuti: ‘Ndinawabisa mawu anu mumtima mwanga.’ ‘Ndidzadzikondweretsa nawo malemba anu.’ ‘Mtima wanga wasweka ndi kukhumba maweruzo anu nyengo zonse.’ ‘Mboni zanu . . . ndizo zondikondwetsa.’ ‘Ndinalira malangizo anu.’ ‘Ndidzadzikondweretsa nawo malamulo anu, amene ndiwakonda.’ ‘Ndipo ndidzalingalira pa malemba anu.’ ‘Ha! Ndikondadi chilamulo chanu; ndilingiriramo ine tsiku lonse.’—Salmo 119:11, 16, 20, 24, 40, 47, 48, 97.
Wamasalmo ameneyu anayamikira kuchokera pansi pa mtima mawu omwe Mulungu anadziwitsa anthu. Kodi inu mumamvanso chimodzimodzi ndi uthenga wa m’Mawu a Mulungu, Baibulo? Kodi mumafuna kuti muziwakonda kwambiri choncho? Ngati n’choncho, choyamba mukufunikira kukhala ndi chizolowezi chowerenga Baibulo nthawi zonse, tsiku lililonse ngati kungakhale kotheka. Yesu Kristu anati: “Munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha, koma ndi mawu onse akutuluka m’kamwa mwa Mulungu.” (Mateyu 4:4) Chachiwiri, muyenera kusinkhasinkha zimene mwawerenga. Kuganizira za choonadi chonena za Mulungu, makhalidwe ake, chifuniro chake, ndiponso cholinga chake kungachititse kuti muzikonda kwambiri Baibulo. (Salmo 143:5) Ndipo chofunika kwambiri, muyenera kugwiritsa ntchito malangizo ake ogwira mtima m’moyo wanu wa tsiku ndi tsiku.—Luka 11:28; Yohane 13:17.
Kodi mungapindule motani ngati mumakonda kwambiri zimene Baibulo limanena? “Odala iwo akusunga mboni [za Mulungu],” limatero lemba la Salmo 119:2. Mboni, kapena kuti zikumbutso, zimene zimapezeka m’Baibulo zingakuthandizeni kupirira mavuto m’moyo. (Salmo 1:1-3) Mudzapeza nzeru, luntha, ndi kuzindikira, zimene zingakuthandizeni ‘kuletsa mapazi anu njira iliyonse yoipa.’ (Salmo 119:98-101) Kudziwa choonadi chonena za Mulungu ndi cholinga chake cha dziko lapansi, kudzachititsa moyo wanu kukhala watanthauzo kwambiri ndipo kudzalimbitsa chiyembekezo chanu cham’tsogolo.—Yesaya 45:18; Yohane 17:3; Chivumbulutso 21:3, 4.
Mboni za Yehova zimasangalala kwambiri kuthandiza ena kuti alidziwe bwino Baibulo ndiponso kuti azikonda uthenga wake. Tidzakhala osangalala ngati mutavomera pempho lathu lili m’munsimu.