N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuchita Zabwino?
N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuchita Zabwino?
MWAMUNA wina wophunzira kwambiri anati: “Ndimafuna kuchita zabwino, koma sinditha kuzichita. Pakuti chinthu chabwino chimene ndimafuna kuchita sindichita, koma choipa chimene sindifuna kuchita ndi chimene ndimachita.” N’chifukwa chiyani mwamunayu zinkamuvuta kuchita zinthu zabwino zimene ankafuna? Iye analongosola kuti: “Chotero kwa ine, ndimapeza lamulo ili lakuti: pamene ndikufuna kuchita chinthu chabwino, choipa chimakhala chili nane. Mu mtima mwanga ndimasangalala kwambiri ndi chilamulo cha Mulungu, koma ndimaona chilamulo china m’ziwalo zanga chikumenyana ndi chilamulo cha m’maganizo mwanga ndi kundipanga kapolo wa chilamulo cha uchimo chimene chili m’ziwalo zanga.”—Aroma 7:18, 19, 21-23.
Mawu a mtumwi Paulo amenewa, analembedwa zaka pafupifupi 2,000 zapitazo, ndipo akulongosola mmene zimawavutira anthu opanda ungwiro kuchita zinthu zabwino. Kupitiriza kutsatira mfundo za makhalidwe abwino, makamaka panthawi za chiyeso, kumafuna kulimba mtima. Choncho tingachite bwino kufunsa kuti, Kodi pali chifukwa chilichonse chofunika kwambiri chochitira zinthu zabwino?
Taonani zimene Malemba amanena za tsogolo la munthu amene akuchita zabwino. Pa Salmo 37:37, 38, timawerenga kuti: “Tapenya wangwiro, ndipo taona woongoka mtima! Pakuti kumatsiriziro ake a munthuyo kuli mtendere. Koma olakwa adzawonongeka pamodzi: matsiriziro a oipa adzadulidwa.” Lemba la Miyambo 2:21, 22 limatiuza kuti: “Pakuti oongoka mtima adzakhala m’dziko, angwiro nadzatsalamo. Koma oipa adzalikhidwa m’dziko, achiwembu adzazulidwamo.”
Ngakhale kuti malonjezo amenewa ndiponso ena opezeka m’Baibulo amatilimbikitsa kuchita zinthu zimene zimakondweretsa Mulungu, sindiwo chifukwa chachikulu chimene timachitira zinthu zabwino. Chifukwa chake chenicheni chikugwirizana ndi nkhani yokhudza zolengedwa zonse zanzeru, chilichonse pachokhapachokha. Nkhani yotsatirayi ilongosola za chifukwa chimenecho ndiponso mmene chimatikhudzira.