Kuona Mtima N’kopindulitsa
Kuona Mtima N’kopindulitsa
KUSAONA mtima kwakhalapo kungoyambira m’munda wa Edene. Komabe, anthu ambiri ochokera m’madera osiyanasiyana padziko pano amaona kuti kuona mtima n’kofunika ndipo kuti kunama komanso chinyengo ndi zinthu zoipa ndi zosayenera. Kukhala munthu woti ena azikukhulupirira n’chinthu chonyaditsa. Koma masiku ano anthu ambiri amaona kuti pamafunika kuchita zinthu mosaona mtima kuti zawo ziwayendere. Inuyo mukuona bwanji? Kodi kuona mtima kungapindulitse munthu? Kodi inuyo mumatsatira mfundo zotani zodziwira kuti kuchita zakuti n’kuona mtima kapena n’kusaona mtima?
Kuti tim’sangalatse Mulungu, tiyenera kuchita zinthu moona mtima ndiponso kumalankhula zoona. Mtumwi Paulo analimbikitsa Akhristu anzake kuti: “Aliyense wa inu alankhule zoona kwa mnansi wake.” (Aefeso 4:25) Paulo analembanso kuti: “Timafuna kuchita zinthu zonse moona mtima.” (Aheberi 13:18) Cholinga chathu pokhala oona mtima si kufuna kutamidwa ndi anthu ena. Timachita zinthu moona mtima chifukwa cholemekeza Mlengi wathu ndiponso chifukwa chofuna kum’sangalatsa.
Musamadzibise
M’mayiko ambiri anthu amadzibisa kuti zinthu zinazake ziwayendere bwino. Amapeza ziphaso, masatifiketi, ndiponso zilolezo zabodza zolowera m’dziko kapena kupezera ntchito kapenanso udindo umene sali woyenera kukhala nawo. Makolo ena amapeza ziphaso zabodza zosonyeza kubadwa kwa ana awo n’cholinga choti anawo apitirize sukulu.
Komabe sitingasangalatse Mulungu ngati tili achinyengo. Baibulo limanena kuti Yehova ndi “Mulungu wa choonadi” ndiponso kuti amafuna kuti anthu amene amam’konda azinena zoona. (Salmo 31:5) Ngati tikufuna kugwirizana kwambiri ndi Yehova, tisatsanzire anthu abodza amene ali “anthu othyasika,” kapena kuti odzibisa.—Salmo 26:4.
Anthu ambiri amabisanso choonadi akaona kuti angathe kulangidwa pa zolakwa zawo zinazake. Ngakhale mumpingo wachikhristu, munthu angakhale pachiyeso chochita zimenezi. Mwachitsanzo, mumpingo winawake, mnyamata wina anavomereza kwa akulu kuti anachita machimo enaake. Koma sanavomere kuti anaba, ngakhale kuti panali umboni woti anabadi. Mapeto ake anam’tulukira ndipo anachotsedwa mumpingo. Kodi sichikanakhala chanzeru mnyamatayu akanangonena chilungamo n’kuthandizidwa kuti akhalenso ndi ubwenzi wamtengo wapatali womwe anali nawo ndi Yehova? Ndipotu Baibulo limanena kuti: “Usapeputse kulanga kwa Yehova, kapena kutaya Aheberi 12:5, 6.
mtima pokuwongolera iye. Pakuti amene Yehova am’konda am’langa.”—Nthawi zina mbale amene akukalamira maudindo mumpingo angayesetse kubisa zofooka zinazake zimene ali nazo kapena makhalidwe enaake oipa amene anachita m’mbuyomo. Mwachitsanzo, angabise zinthu zina poyankha mafunso pa fomu yofunsira utumiki winawake wapadera, mwina zokhudza thanzi lake ndi makhalidwe ake, poganiza kuti akanena zoona pa nkhani zimenezi ndiye kuti saitanidwa. Angamadzinamize kuti: ‘Sikuti ndanama kwenikweni ayi.’ Komano kodi pamenepa iyeyu wanenadi zoona? Taganizirani mfundo yotchulidwa pa Miyambo 3:32 yakuti: “Wamphulupulu [wachinyengo, NW] anyansa Yehova; koma chinsinsi chake chili ndi oongoka.”
Kuona mtima kumatanthauza kuti tisamadzinamize. Nthawi zambiri anthufe timakhulupirira zimene tikufuna kukhulupirira osati zimene zili zolondola ndiponso zoona. Sitichedwa kuloza chala munthu wina. Mwachitsanzo, Mfumu Sauli atachita zinthu zosamvera anayesa kupeza pobisalira poloza chala anthu ena. Motero, Yehova anam’chotsa kuti asakhale mfumu. (1 Samueli 15:20-23) Izitu n’zosiyana kwambiri ndi zimene anachita mfumu Davide, chifukwa anapemphera kwa Yehova kuti: “Ndinavomera choipa changa kwa Inu; ndipo mphulupulu yanga sindinaibisa. Ndinati, ndidzaululira Yehova machimo anga; ndipo munakhululukira choipa cha kulakwa kwanga.”—Salmo 32:5.
Kuona Mtima Kumabweretsa Madalitso
Anthu amakuonani m’njira inayake malingana n’kuona mtima kapena kusaona mtima kwanu. Anthu akadziwa kuti munawanamiza nthawi inayake, ngakhale kamodzi kokha, amasiya kukukhulupirirani, ndipo m’povuta kuti adzayambirenso kutero. Komano ngati muli munthu wonena chilungamo ndiponso woona mtima, mudzakhala ndi mbiri yoti ndinu munthu wodalirika, woti n’kumukhulupirira. Chifukwa cha zochita zawo, Mboni za Yehova zili ndi mbiri yotereyi. Taganizirani zitsanzo zina izi.
Bwana wamkulu pa kampani ina anazindikira kuti antchito ake ambiri akubera kampaniyo, motero anaitana apolisi kuti afufuze nkhaniyo. Atazindikira kuti mmodzi wa antchito ake amene anamangidwa ndi apolisiwo anali wa Mboni za Yehova, anapita kupolisiko kuti akamasulitse Wamboniyo nthawi yomweyo. N’chifukwa chiyani anatero? N’chifukwa chakuti bwanayo ankadziwa kuti munthuyo ankagwira ntchito moona mtima ndiponso kuti anali wosalakwa. Motero, Wamboniyo anapitiriza ntchito pamene enawo anachotsedwa. Amboni anzake anasangalala podziwa kuti khalidwe lake linachititsa kuti dzina la Yehova lilemekezeke.
Anthu salephera kuona ngati munthu ali ndi khalidwe labwino. M’dera linalake la ku Africa kuno, mlatho wa pa ngalande inayake yaikulu unkafunika kukonzedwa chifukwa choti matabwa ake ena anali atabedwa. Anthu a m’deralo anaganiza zosonkhetsa ndalama kuti agule matabwa ena, komano kodi ndani akanayang’anira ndalamazo? Onse anavomerezana kuti anayenera kukhala Wamboni za Yehova.
Panthawi imene m’dziko lina ku Africa kuno munali mavuto a zandale ndi a kusamvana pakati pa mitundu, Wamboni wina amene ankagwira ntchito yowerengetsera ndalama pa kampani inayake ya m’mayiko osiyanasiyana anasamutsidwa ndi kampani yakeyo, chifukwa choti moyo wake unali pangozi. Ndiye kampaniyo inakonza zoti akagwire ntchito kwa miyezi yambiri kunja ndi kuti imulipirira zonse zofunikira mpaka zinthu zidzasinthe m’dziko mwake. N’chifukwa chiyani kampaniyo inatero? N’chifukwa choti m’mbuyomo iye anakana kuchita nawo upo pofuna kubera kampaniyo. Mabwana a pakampaniyo ankadziwa kuti iyeyu anali ndi mbiri yabwino, yoti anali munthu woona mtima zedi. Kodi mukuganiza kuti mabwanawa akanalolera kuthandiza Wamboniyu m’njira imeneyi akanakhala kuti anali munthu wotchuka n’kusaona mtima?
Lemba la Miyambo 20:7 limati: ‘Wolungama ayenda mwangwiro.’ Munthu woona mtima amakhala wokhulupirika. Sanamiza kapena kunyenga anthu anzake. Kodi izi si zimene inuyo mumafuna kuti anthu ena azikuchitirani? Kukhala oona mtima n’kofunika kwambiri pa kulambira koona. Kumasonyeza chikondi chimene tili nacho pa Mulungu ndiponso pa anansi athu. Pochita zinthu moona mtima, timaonetsa kuti tikufuna kutsatira mfundo ya makhalidwe abwino imene Yesu ananena, yakuti: “Zinthu zonse zimene mukufuna kuti anthu akuchitireni, inunso muwachitire zimenezo.”—Mateyo 7:12; 22:36-39.
Kukhala oona mtima nthawi zonse kuli n’zovuta zake, koma zovuta zimenezi n’zazing’ono zedi mukaganizira za chikumbumtima choyera chimene mungakhale nacho, chomwe n’chamtengo wapatali kwambiri. Kukhala oona mtima ndi owongoka mtima kumapindulitsa kwambiri patsogolo pake. Ndipotu kunena zoona, palibe chinthu chamtengo wapatali koposa ubwenzi wabwino ndi Yehova. Ndiyetu si zoona kuti munthu angasokoneze dala ubwenzi wotere chifukwa chongofuna kuti asachite manyazi, kapena chifukwa chongofuna kupeza phindu mwachinyengo? Kaya tikumane ndi mavuto otani, tisakayikire mawu a wamasalmo akuti: “Wodala munthuyo wakuyesa Yehova wokhulupirika; wosasamala odzikuza, ndi opatukira kubodza.”—Salmo 40:4.
[Zithunzi patsamba 18]
Akhristu oona sagula kapena kugwiritsira ntchito ziphaso kapenanso zikalata zabodza.