Kufalitsa Uthenga Wabwino M’dziko Lokongola la Haiti
Kufalitsa Uthenga Wabwino M’dziko Lokongola la Haiti
MAYIKO a Haiti ndi Dominican Republic ali pachilumba chimodzi chotchedwa Hispaniola, chomwe chili ndi mapiri aatali kwambiri kuposa mapiri onse omwe ali pazilumba za m’nyanja ya Caribbean. Ena a mapiriwo n’ngotalika mamita oposa 2,400. M’miyezi imene amati ndi yozizira, madzi a m’maiwe omwe ali kumapiri amaundana pamwamba, ndiponso mame amene amachita kumeneko amakhala oundana.
Mapiri ndi zigwa zomwe zili kumwera kwa dziko la Haiti n’zokutidwa ndi nkhalango zobiriwira kwambiri. Koma kumadera ena, mapiri anayera ndipo amaoneka osakongola ndi osongoka kwambiri chifukwa chodula mitengo. Ngati mungayende kumpoto kapena kum’mwera, mungaone kuti dziko la Haiti n’lokongola kwambiri. Mukamayenda m’njira zina za m’mapiri, zomwe zili zokhotakhota, mungasangalale kuona madera osiyanasiyana ochititsa kaso a kumtunda ndiponso a panyanja. Paliponse mungaonenso maluwa owala a mitundumitundu.
Ambiri mwa anthu 8.3 miliyoni omwe ali m’dziko lokongolali amakhala kumidzi ndipo anachokera ku Africa. Ambiri a iwo ndi osauka, komabe ndi okoma mtima ndiponso okonda kuchereza alendo. Kwa zaka pafupifupi 60, Mboni za Yehova zasangalala kuuza anthu amenewa uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu ndipo anthuwo akhala akuzilandira ndi manja awiri.—Mateyo 24:14.
Kulalikira M’dera la Kumudzi
Panthawi yoyamba imene mmishonale wina anakalalikira m’dera la kumudzi, anakumana ndi zimene zimachitika nthawi zonse mukapita kukalalikira m’dera lotere. Mlongoyu analemba kuti:
“Tsiku lina mu March 2003, tinakalalikira m’tawuni yaing’ono yochedwa Casale. Kuti mufike kumeneko, mumayenda mphindi 30 pagalimoto kuchokera ku tawuni ya Cabaret. Tawuni ya Cabaret imeneyi n’kumene kuli nyumba yathu ya amishonale, ndipo ili pamtunda wa makilomita 30 kumpoto kwa likulu la Haiti lotchedwa Port-auPrince. Nthawi yotsiriza imene Mboni zinalalikira ku Casale inali mu 1999, choncho tinanyamuka mofunitsitsa nthawi ya 7 koloko m’mawa. Tinalipo anthu okwana 22, womwe unali pafupifupi mpingo wathu wonse, ndipo tinakwera galimoto ziwiri zikuluzikulu. Onse anali kucheza ndi kuseka mosangalala pamene tinali kutsika misewu yafumbi yotsetsereka n’kufika ku chigwa chomwe chili ndi mitengo ikuluikulu yambiri. Mtsinje wina umayenda m’chigwacho ndipo umadutsanso mkati mwa tawuni ya Casale.
“Mbiri ya tawuni yabatayi inayamba kumayambiriro a zaka za m’ma 1800 pamene asilikali a Chipolishi, omwe anabwera ku Haiti kudzathandiza amene kale anali akapolo kuti apeze ufulu, anakhazikika m’chigwa chachondechi ndi akazi awo a Chihaiti. Iwo anayambitsa mtundu wa anthu okongola. Inde n’zosangalatsa kuona anthu a kumidzi omwe ali ndi khungu loyera, loderapo, lakuda, a maso obiriwira, odera kwambiri, ndi zina zotero.
“Pakhomo loyamba, munthu amene tinamupeza sanachite chidwi. Titanyamuka kuti tizipita, munthu wina anali kubwera mumsewu kuti akumane nafe. Iyeyo anafuna kudziwa ngati timakhulupirira kuti Yesu ndi Mulungu ndi anthu osiyana. Titamupempha, anakatenga Baibulo lake ndipo Yohane 17:3) Anthu ambiri anatipempha kuti tikhale pansi n’kukambirana nawo. Ena anafunsa kuti, ‘Kodi mudzabweranso liti kudzaphunzira nafe Baibulo?’
zimene tinakambirana naye mogwiritsa ntchito Malemba, zinamutsimikizira kuti Yesu ndi mwana wa Mulungu ndipo Yehova ndiye ‘Mulungu yekha woona.’ (“Panthawi ya masana, tinapeza malo abwino a pamthunzi kuti tidyerepo. Alongo awiri anali ataphika nsomba zambiri. Ndipo zinali zokoma kwabasi! Pamene tinali kudya ndi kucheza, tinkalalikiranso anthu omwe anali kudutsa. Kenako, tinawoloka mtsinjewo n’kupita ku mbali ya tawuni yomwe ili kutsidya linalo. Tinasangalala kucheza ndi anthu okoma mtima amenewa omwe anali kukhala pansi pamitengo yomwe ili pafupi ndi nyumba zawo zing’onozing’ono. N’zosangalatsa kwambiri kumva phokoso la ana akusewera, azimayi akuchapa zovala mumtsinje, ndi agogo akupera nthanga za khofi.
“Posakhalitsa, 4 koloko inakwana, ndipo gulu lathu losangalala linakakwera galimoto zija kuti tibwerere ku Cabaret. Ine ndi mwamuna wanga tinasangalala kwambiri pa ulendo wathu woyamba wopita ku tawuni ya Casale, yomwe anthu ake n’ngokoma mtima ndi okonda kulandira alendo.”
Kuchokera pamene amishonale oyamba a Mboni anafika ku Haiti mu 1945, chiwerengero cha olengeza Ufumu m’dzikoli chakhala chikukwera moti tsopano kuli anthu okwana 14,000 omwe amalalikira ndi kuchititsa maphunziro a Baibulo oposa 22,000. Iwo akhudza miyoyo ya anthu okwana 59,372 omwe anafika pa Chikumbutso mu March 2005 ndipo akhala akulengeza poyera Ufumu wa Mulungu. Taonani mmene ntchito ya Mboni za Yehova yakhudzira anthu m’njira zosiyanasiyana.
Uthenga Wabwino mu Zojambulajambula
Anthu ambiri a ku Haiti amakonda zinthu zowala kwambiri. Amaonetsa zimenezi ndi zovala zawo, nyumba zawo zopenta, maluwa osiyanasiyana amene amadzala pakhomo pawo, ndi zojambulajambula zawo. Nsalu zojambulidwa m’njira ya kwawo yotchedwa L’Art Haitien, zimapezeka paliponse m’misewu ya ku Port-au-Prince. Anthu obwera kudzagula nsaluzo amachokera ku madera ambiri a dziko lapansi.
Zojambulajambula zowala sizingopezeka pa nsalu zokha ayi. Misewu ya ku Port-au-Prince n’njodzala ndi galimoto zonyamula anthu zomwe n’zojambulidwa ndi zithunzi zambiri zochititsa chidwi. Nthawi zambiri munthu angaone nkhani za m’Baibulo zojambulidwa m’zithunzizi.
Mukamayenda mumsewu, mosayembekezera mukhoza kuona nkhani imene mumaidziwa bwino kwambiri, monga ngati ya Adamu ndi Hava m’munda wa Edene. Inde, mungaione itajambulidwa pawindo la kumbuyo la galimoto yonyamula anthu yomwe yangokudutsani. Kawirikawiri, pa galimoto zimenezi kapena m’mayina a mabizinesi, amalembamo malemba kapena mawu ena okhala ndi dzina lakuti Yehova.
Kulalikira Uthenga Wabwino ku Sukulu
Achinyamata a Mboni ku Haiti ali ndi mipata yabwino yothandizira anzawo a kusukulu kuphunzira Baibulo. Lipoti lotsatirali lochokera kwa mtsikana wa Mboni wa zaka 17 ndi chitsanzo cha zimenezi.
“Tsiku lina mnyamata wina wa m’kalasi yathu anandifunsa kuti ‘dama’ n’chiyani. Ndinamunyalanyaza poganiza kuti akufuna kundizolowera. Koma atafunsa mnyamata mnzake funso lomwelo, anthu onse m’kalasi anachita chidwi. Chotero mlungu wotsatira, nditafufuza za nkhani imeneyi, ndinawafotokozera achinyamata m’kalasimo chifukwa chimene Mboni za Yehova zimayesetsa kukhala zoyera m’makhalidwe, mwauzimu, ndi mwakuthupi.
“Achinyamatawo anafunsa mafunso ambiri ndipo anavomereza mayankho ochokera m’Baibulo omwe ndinapereka. Ngakhale mphunzitsi wamkulu pa sukuluyo, yemwe poyamba sanafune, anafunsa mafunso ambiri ndipo anakonza zoti ndilankhule ndi anthu a m’makalasi enanso. Ndinawasonyeza buku lakuti Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza, * ndipo ambiri anachita nalo chidwi. Tsiku lotsatira, ndinagawira ana a sukulu anzanga mabuku 45. Ambiri a iwo anamaliza msanga kuwerenga buku lawolo, ndipo ena tsopano akuphunzira Baibulo ndi Mboni za kufupi ndi kwawo. Mwana wa sukulu wina, yemwe amakhala m’dera la kwathu, tsopano amapita kumisonkhano yonse.”
Kugwiritsa Ntchito Chinenero cha Chikiliyo
Dzikoli ndi anthu ake n’ngokongola ndi osangalatsa, chimodzimodzinso ndi chinenero chake cha Chikiliyo cha ku Haiti, chomwe chili ndi mawu a Chifalansa koma chimatsatira malamulo a zinenero za ku West Africa. Chikiliyo ndi chinenero cha anthu a ku Haiti ndipo n’chimene chimawafika pamtima. Mboni za Yehova zimagwiritsa ntchito kwambiri chinenerochi mu utumiki wawo, ndipo pali makonzedwe oti mabuku owonjezeka ofotokoza Baibulo apangidwe mu Chikiliyo chimenechi.
Mu 1987 kabuku ka Sangalalani ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha! kanasindikizidwa mu Chikiliyo cha ku Haiti, kenako buku la Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha, ndipo pambuyo pake kabuku ka Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? Mabukuwa athandiza kwambiri anthu amene ayamba kumene kuphunzira Baibulo, omwe akufuna kudziwa mfundo zikuluzikulu za m’Mawu a Mulungu. Kuyambira pa September 1, 2002, magazini ya Nsanja ya Olonda inayamba kusindikizidwa mu chinenero cha Chikiliyo. Mabuku a chinenero cha Chifalansa amagwiritsidwabe ntchito, koma anthu ambiri amakonda kuwerenga mabuku omwe ali mu chinenero chawo.
Kulalikira Uthenga Wabwino kwa Akaidi
Posachedwapa, Mboni za Yehova zayamba kulalikira uthenga wabwino kwa amuna ndi akazi omwe ali m’ndende. Mboni zomwe zikuchita zimenezi zimakondwera kuti zimauza anthu omvetsa chisoni amenewa uthenga wotonthoza. Mbale wina anafotokoza kuti:
“Pa ulendo wathu woyamba ku ndende ina, akaidi anawasonkhanitsa m’chipinda chachikulu kuti aonane nafe. Ndipo sitinkadziwa kuti mawu athu awalandira bwanji. Koma, titafotokoza kuti tabwera kudzawathandiza kumvetsa Baibulo, anthu onsewo okwana 50 anasangalala nafe. Tinawagawira timabuku ta Dziperekeni pa Kuŵerenga ndi Kulemba ndi Sangalalani ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha! mu chinenero cha Chikiliyo ndipo tinayambitsa maphunziro a Baibulo ndi anthu 26 mwa iwo. Analipo anthu 10 omwe anali osadziwa kuwerenga, koma titawasonyeza mmene angagwiritsire
ntchito zithunzi zomwe zili mu timabukuto kuti amvetse mawu ake, anachita chidwi.”Mboni zitapitakonso, mwamuna wina anati: “Ndawerenga mobwerezabwereza kabuku kaja. Ndimangokhalira kuganiza za zimene kabukuko kamanena, ndipo ndakhala ndikukudikirani mwachidwi.” Mwamuna wina yemwe anamangidwa chifukwa choba ndi mfuti ananena kuti iyeyo akufuna kusintha, ndipo anapempha kuti munthu wina azikaphunzira Baibulo ndi mkazi wake. Bambo wina wa ana awiri anapemphanso zomwezo n’cholinga choti mkazi wake aone kusiyana pakati pa zikhulupiriro zoona ndi zonama. Mtsogoleri wachipembedzo cha Chipolotesitanti yemwe anali ndi mlandu wobera anthu a m’tchalitchi chake ndalama zambiri, ananena kuti tsopano wapeza choonadi ndipo akadzamaliza zaka zimene ayenera kukhala m’ndende, adzathandiza anthu a m’tchalitchi chake kukhala Mboni za Yehova.
Mkaidi wina yemwe analibe kabuku kakekake ka Mulungu Amafunanji m’Chikiliyo, anakopera mawu onse a m’kabuku ka mnzake ndipo anawaloweza pamtima. Mkaidi wina wamkazi anayamba kuuza akaidi anzake 9 zimene anali kuphunzira, mpaka anafika poyamba kuwaphunzitsa. Mkaidi wina wamwamuna anamaliza kuphunzira kabukuko n’kuyamba kuphunzira buku la Chidziŵitso ndipo anayambanso kulalikira kwa akaidi ena. Posapita nthawi, anali kuchititsa maphunziro a Baibulo ndi anthu anayi mwa iwo.
Mercony * kale ankaphunzira Baibulo ndipo ali ndi achibale ake omwe ndi Mboni za Yehova. Iye analimbikitsa akaidi ena kuwerenga mabuku ofotokoza za m’Baibulo omwe achibale akewo anamubweretsera. Iye anati: “Ndikamagawira mabukuwo kwa akaidi, amanditcha Mboni ya Yehova. Koma ndimawauza kuti ayi sindine wa Mboni popeza ndikudziwa zimene kukhala mmodzi wa iwo kumatanthauza. Ndikufuna tsopano kuyesetsa kwambiri kuphunzira Baibulo ndiponso kuti ndibatizidwe. Ndikanatsatira zimene anachita achimwene anga pamene ndinali mnyamata, si bwenzi pano ndili m’ndende muno.”
Mmodzi wa akaidi amene analandira magazini kuchokera kwa Mercony anauza wa Mboni wina amene anadzamuchezera kuti: “Musanabwere Lolemba mlungu watha, ndinali wovutika maganizo kwambiri moti ndinkafuna kudzipha. Koma nditawerenga magaziniwa, ndinapemphera kwa Mulungu kuti andikhululukire zoipa zomwe ndachita ndipo anditumizire munthu woti andisonyeze zimene ndiyenera kuchita. Ndinakondwera kwabasi pamene munabwera tsiku lotsatira kudzaona ngati akaidi akufuna kuphunzira nanu Baibulo. Ndingakonde kuti mundiphunzitse mmene ndingatumikirire Yehova.”
Galamukani! Ikufalitsa Uthenga Wabwino kwa Anthu Ambiri
Magazini ya Galamukani! ya November 8, 2000, inali ndi nkhani zokhudza ntchito ya unamwino. Mkazi wina analandira magazini okwana 2,000, ndipo anagawira magaziniwo kwa manesi omwe anapezeka pamsonkhano ku Port-au-Prince. Galamukani! ya July 8, 2002, yomwe inali ndi nkhani zofotokoza za apolisi ndi ntchito yawo, inafalitsidwa kwa apolisi ambiri ku Port-au-Prince. Iwo anayamikira kwambiri magaziniyi, ndipo ngakhale tsopano, anthu ena akakumana ndi Mboni pa msewu amaziimitsa kuti apemphe ena a magazini amenewo.
Posachedwapa, wogwira ntchito m’bungwe loona za umoyo pa dziko lonse la WHO anakonza pulogalamu yophunzitsa anthu za vuto la Edzi. Iyeyo anaitanidwa ku ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova, kumene anasonyezedwa zomwe zinalembedwa mu Galamukani! pankhani imeneyi. Anachita chidwi kuona nkhani zimene, mochokera m’Baibulo, zikufotokoza njira yabwino yopewera Edzi, komanso mmene mungathandizire munthu wodwala matenda amenewa kuti athe kulimbana ndi zimene akukumana nazo. Iyeyo ananena kuti magazini ya Galamukani! ili patsogolo kudziwitsa anthu zankhaniyi.
Inde, m’njira zambiri Mboni za Yehova zikufalitsa uthenga wabwino wa Ufumu m’dziko lokongola la Haiti, monga momwe zikuchitira m’mayiko ena okwana 234 padziko lonse lapansi. Ambiri akulabadira uthenga wa chiyembekezo umenewu ndipo akuthandizidwa kusaganiza kwambiri za mavuto a moyo panopa, koma kuganiza za m’tsogolo, pa nthawi imene kudzakhale dziko latsopano, limene onse olambira Mulungu woona, Yehova, adzakondwera ndi moyo wangwiro wochuluka.—Chivumbulutso 21:4.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 20 Mabuku amene mitu yake taitchula m’nkhaniyi amafalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
^ ndime 29 Dzinali talisintha.
[Mawu a Chithunzi patsamba 9]
Background: ©Adalberto Rios Szalay/photodisc/age fotostock