N’chifukwa Chiyani Sitiyenera Kuchita Zinthu Monyanyira?
N’chifukwa Chiyani Sitiyenera Kuchita Zinthu Monyanyira?
YEHOVA n’chitsanzo chabwino kwambiri cha kusachita zinthu monyanyira. “Ntchito yake ndi yangwiro,” ndipo chilungamo chake chilibe nkhanza chifukwa nthawi zonse chimaphatikizapo chifundo. (Deuteronomo 32:4) Chikondi chake si chongotengeka maganizo, chifukwa amatsatira malamulo angwiro. (Salmo 89:14; 103:13, 14) Makolo anthu oyambirira analengedwa bwino kwambiri. Sanali ochita zinthu monyanyira. Komabe, uchimo unayambitsa “chilema” cha kupanda ungwiro, chimene chinachititsa kuti anthu ayambe kuchita zinthu monyanyira.—Deuteronomo 32:5.
Mwachitsanzo, kodi munayamba mwakwerapo galimoto kapena njinga imene inali ndi tayala lofufuma kwambiri mbali imodzi? N’zosakayikitsa kuti chilema chimenecho chinapangitsa ulendo wanu kukhala wosakoma ndi woopsa. Tayala lotere liyenera kukonzedwa mwamsanga lisanaphwe. N’chimodzimodzi ifeyo, kupanda ungwiro kwathu nthawi zambiri kumatichititsa kuti tizipanga zinthu monyanyira. Ngati titalola chilema chimenechi kukula, ulendo wathu pamoyo ungakhale wovuta kwambiri ndi woopsa.
Nthawi zina ngakhale zinthu zimene timazichita bwino kwambiri, tikhoza kuzichita monyanyira. Mwachitsanzo, n’zoona kuti Chilamulo cha Mose chinati zovala za Aisiraeli zizikhala ndi mphonje, koma Afarisi a m’nthawi ya Yesu pofuna kuoneka osiyana ndi anthu ena, ‘ankakulitsa mphonje za zovala zawo’ monyanyira. Ankachita zimenezi kuti azioneka olungama kwambiri kuposa anthu ena.—Mateyo 23:5; Numeri 15:38-40.
Masiku anonso anthu ena amayesetsa kuchita china chilichonse kuti anthu awadziwe, mpaka kufika podabwitsa ena. Kumeneku kumakhala ngati kulira kuti: “Ndioneni! Inenso ndine munthu!” Koma kuvala, kuganiza, ndi kuchita zinthu monyanyira sikungachititse Mkhristu kupeza zinthu zimene amafunikiradi pamoyo wake.
Kuona Ntchito Moyenerera
Kaya ndife ndani, kaya timakhala kuti, ntchito yabwino n’chinthu chimodzi chimene chimapangitsa moyo wathu kukhala waphindu. Tinalengedwa kuti tizisangalala ndi ntchito yotero. (Genesis 2:15) Mogwirizana ndi zimenezi, Baibulo limaletsa ulesi. Mtumwi Paulo ananena momveka bwino kuti: “Ngati wina safuna kugwira ntchito, asadyenso.” (2 Atesalonika 3:10) Zoonadi, ulesi ungam’bweretsere munthu umphawi ndi kusakhutira, komanso Mulungu sangasangalale naye.
Koma anthu ena amagwira ntchito monyanyira mpaka kufika pokhala kapolo wa ntchito yawo yomwe. Amachoka pa nyumba m’mamawa n’kubwera usiku, n’kumati akuchita zimenezo chifukwa chakuti akufunira banja lawo zabwino. Koma zoona zake n’zakuti banja lawo likhoza kuvutika chifukwa cha kugwira ntchito kotere. Mkazi wina amene mwamuna wake nthawi zambiri amagwira ntchito yowonjezera nthawi yowerukira itakwana, ananena kuti: “Ndingasangalale kusinthanitsa chilichonse m’nyumba yapamwambayi kuti mwamuna wanga azikhala nane panyumba pamodzi ndi ana athu.” Anthu amene amagwira ntchito monyanyira ayenera kuganizira mozama moyo wa Mfumu Solomo, yomwe inati: “Ndinayang’ana zonse manja anga Mlaliki 2:11.
anazipanga, ndi ntchito zonse ndinasauka pozigwira; ndipo taona, zonse zinali zachabechabe ndi kungosautsa mtima, ndipo kunalibe phindu kunja kuno.”—Nkhani apa n’njakuti tiyenera kupewa ulesi komanso kugwira ntchito monyanyira. Tingathe kugwira ntchito molimbika, tikudziwanso kuti kukhala kapolo wa ntchito kungatimanitse chimwemwe ndi zinthu zinanso zambiri.—Mlaliki 4:5, 6.
Zioneni Bwino Zosangalatsa
Potchula za nthawi yathu, Baibulo linaneneratu kuti: “Anthu adzakhala . . . okonda zosangalatsa, m’malo mokonda Mulungu.” (2 Timoteyo 3:2, 4) Kukonda zosangalatsa ndi chida chachikulu kwambiri chimene Satana akugwiritsa ntchito masiku ano posocheretsa anthu kuti asatumikire Mulungu. Kukonda kwambiri zinthu zosangalatsa, monga masewera oopsa zikuwonjezereka masiku ano. Pamene zosangalatsa ndi masewera otere akuwonjezereka, anthu amene akuchita nawo zinthu zimenezi akuwonjezerekanso. Kodi zinthu zimenezi zikufala chifukwa chiyani? N’chifukwa chakuti anthu ambiri sasangalala ndi moyo wawo wa tsiku ndi tsiku, choncho amayamba kufunafuna zinthu zimene zingawasangalatse. Koma kuti apitirize kusangalala ndi zinthu zimenezi, amaika moyo wawo pachiswe. Akhristu amene amayesetsa kusangalatsa Mulungu amapewa masewera oika moyo pachiswe chifukwa chakuti amalemekeza moyo komanso Wopereka moyo.—Salmo 36:9.
Mulungu atalenga anthu awiri oyamba, kodi anawaika kuti? Anawaika m’munda wa Edene, dzina limene m’chilankhulo choyambirira limatanthauza ‘Chisangalalo.’ (Genesis 2:8) Apa n’zachionekere kuti Yehova anafuna kuti anthu azikhala mosangalala.
Yesu anatisiyira chitsanzo chabwino kwambiri pankhani yoona zosangalatsa moyenerera. Iye anadzipereka kotheratu kukwaniritsa chifuniro cha Yehova, ndipo sanaleke kutsatira malamulo ndi mfundo za Mulungu ngakhale tsiku limodzi. Anapatula nthawi yake kusamalira anthu osowa ngakhale atatopa. (Mateyo 14:13, 14) Koma Yesu ankaitanidwa ku chakudya ndipo ankapatula nthawi yopuma ndi yosangalala. Ankadziwanso kuti adani ake ankamuyang’ana ndi diso loipa chifukwa chochita zimenezi. Ankamunena kuti: “Taonani! Munthu wosusuka ndi wokondetsa vinyo.” (Luka 7:34; 10:38; 11:37) Koma Yesu sankaganiza kuti kudzipereka kumatanthauza kupeweratu zinthu zonse zokondweretsa.
Mungaone kuti ndi bwino kwambiri kupewa kuchita zinthu monyanyira pankhani ya zosangalatsa. Kuona zosangalatsa ngati chinthu chofunika kwambiri pamoyo wathu sikungatibweretsere chimwemwe chenicheni. Kungangotichitsa kuti tiiwale zinthu zofunikira kwambiri, kuphatikizapo ubwenzi wathu ndi Mulungu. Ngakhale zili choncho, sikuti tichite kudzimaniratu kusangalala kulikonse kapena kuyamba kudzudzula ena amene akusangalala ndi moyo moyenerera.—Mlaliki 2:24; 3:1-4.
Pezani Chimwemwe Pochita Zinthu Mosanyanyira
Wophunzira Yakobe analemba kuti: “Tonsefe timapunthwa nthawi zambiri.” (Yakobe 3:2) Mwina zimenezi zingatichitikire ifeyo pamene tikuyesetsa kupewa kuchita zinthu monyanyira. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tizichita zinthu mosanyanyira? Tiyenera kudziwa bwino zofooka zathu komanso zinthu zimene timachita bwino. Kudziwa zimenezi sikophweka. N’zotheka kuyamba kuchita zinthu monyanyira tisakudziwa. Choncho, ndi bwino kugwirizana ndi Akhristu okhwima mwauzimu ndi kuyesetsa kumvera malangizo awo abwino. (Agalatiya 6:1) Tingathe kupempha malangizo otere kwa mnzathu wapamtima kapena akulu odziwa bwino zinthu. Kuphatikiza pa Malemba, malangizo a m’Baibulo amene anthu amenewa angatipatse amakhala ngati “kalilole” woti tionerepo mmene tikuonekera pamaso pa Yehova.—Yakobe 1:22-25.
N’zosangalatsa kuti tikhoza kupewa kuchita zinthu monyanyira. Ndi khama lathu komanso ndi thandizo la Yehova, titha kupewa kuchita zinthu monyanyira n’kukhala anthu osangalala. Potero, ubwenzi wathu ndi abale ndi alongo auzimu umalimba, ndipo titha kukhala zitsanzo zabwino kwambiri kwa anthu amene timawalalikira. Koposa zonse, tidzakhala tikutsanzira kwambiri Mulungu wathu wachikondi ndi wosanyanyira pochita zinthu, Yehova.—Aefeso 5:1.
[Mawu a Chithunzi patsamba 28]
©Greg Epperson/age fotostock