Sangalalani ndi Dziko Lapansi Lokongolali
Sangalalani ndi Dziko Lapansi Lokongolali
AKATSWIRI a sayansi ya zakuthambo aona kuti dziko lathu lapansi lili ngati kadontho kakang’ono chabe m’chilengedwe chonse. Kulibe kwina kulikonse m’chilengedwe chonsechi kumene kwapezeka moyo. Ndi padziko lapansi pokha pamene pali zonse zofunikira pamoyo.
Komanso, timatha kusangalala ndi moyo padziko lathu lokongolali. Inde, timasangalala kwabasi tikamaothera dzuwa kunja kukuzizira. Ndipo kodi ndani wa ife sasangalala akamaona kutuluka kapena kulowa kwa dzuwa kokongola? Koma dzuwa lathu limachita zambiri, osati kungotisangalatsa basi. N’lofunika kwambiri kuti tikhalebe ndi moyo.
Kwa zaka zosawerengeka, mphamvu yokoka ya dzuwa yapangitsa kuti dziko lapansi ndi mapulaneti ena zisamasinthe njira zawo zikamazungulira dzuwa. Ndipo, monga ana amaphunzirira ku sukulu, dzuwa ndi mapulaneti ake onse zimazungulira pakati pa mlalang’amba wathu wotchedwa Milky Way. Koma dzuwa, lomwe ndi nyenyezi, limayenda limodzi ndi nyenyezi zina zoposa 100 biliyoni pozungulira pakati pa mlalang’amba wathuwo.
Mphamvu yokoka imakoka mlalang’amba wa Milky Way ndi milalang’amba ina pafupifupi 34 kuti ipange gulu limodzi la milalang’amba. Magulu ena aakulu a milalang’amba, amakhala ndi milalang’amba yokwana masauzande angapo. Dzuwa lathu ndi mapulaneti olizungulira zikanakhala m’gulu lalikulu la milalang’amba yoyandikana kwambiri, zinthu zikanasokonekera. Koma, Guillermo Gonzalez ndi Jay W. Richards, m’buku lawo lakuti The Privileged Planet (Pulaneti Lapadera), ananena kuti m’chilengedwe chonse ndi malo ochepa chabe omwe “angayenerere moyo ngati wathuwu poyerekezera ndi malo amene pali dzuwa lathu ndi mapulaneti olizungulira.”
Kodi moyo unakhalapo pa dziko lapansili mwangozi kapena mwadzidzidzi? Kapena kodi moyo padziko lapansi lokongolali uli ndi cholinga chapadera?
Anthu ambiri afika pozindikira kuti dziko lathu linapangidwa mwapadera kuti pakhale moyo. * Zaka zambiri zapitazo, wolemba ndakatulo wachiheberi anatchula za dziko lapansi ndi kumwamba. Analemba kuti: “Pakuona ine thambo la kumwamba lanu, ntchito ya zala zanu, mwezi ndi nyenyezi, zimene munazikhazika, munthu ndani?” (Salmo 8:3, 4) Wolemba ndakatuloyu anakhulupirira kuti kuyenera kukhala Mlengi. Kodi m’nthawi yathu ya sayansi ino, ndi nzeru kukhulupirira zimenezi?
[Mawu a M’munsi]
[Bokosi/Chithunzi patsamba 3]
“Tikalionera patali, dziko lapansi limanyezimira ngati mwala wamtengo wapatali wokongola kwambiri m’thambo la mdima,” limatero buku la The Illustrated Science Encyclopedia—Amazing Planet Earth.
[Mawu a Chithunzi]
Globe: U.S. Fish & Wildlife Service, Washington, D.C./NASA