Kodi Mukukumbukira?
Kodi Mukukumbukira?
Kodi mwapindula powerenga magazini aposachedwapa a mu Nsanja ya Olonda? Tayesani kuyankha mafunso otsatirawa:
• Kodi tingaphunzire chiyani pa fanizo la Yesu lonena za wolandira mlendo wolimbikira? (Luka 11:5-10)
Fanizo limeneli limasonyeza zimene tiyenera kuchita popemphera. Tiyenera kupemphera mwankhakamira, kapena kuti mosaleka, makamaka tikamapempha mzimu woyera wa Mulungu. (Luka 11:11-13)—12/15, masamba 20-22.
• Kodi fanizo la Yesu la mkazi wamasiye ndi woweruza limatiphunzitsa chiyani? (Luka 18:1-8)
Fanizoli limagogomezera kufunika kopemphera. Mosiyana ndi woweruza uja Yehova ndi wolungama ndipo amafuna kutithandiza. Komanso tiyenera kukhala ndi chikhulupiriro changati cha mayi wamasiye wa m’fanizoli.—12/15, masamba 26-28.
• N’chifukwa chiyani mtumwi Paulo anauza Akhristu a ku Korinto kuti “futukulani mtima wanu.” (2 Akorinto 6:11-13)
Zikuoneka kuti Akhristu ena ku Korinto anayamba kusawerengera Akhristu anzawo, motero anayamba kuchita zinthu mowasala. Tiyenera kuyesetsa kukhala ndi mtima woona Akhristu anzathu kuti n’ngofunikiradi, mpaka kufika poyesetsa kuti tiyambe kukhala ndi anzathu ambiri.—1/1, masamba 9-11.
• Kodi n’kuika chisindikizo kotani kumene kunatchulidwa pa Chivumbulutso 7:3?
Mulungu akadzoza Akhristu ndi mzimu woyera, Akhristuwo amaikidwa chisindikizo koyamba. Koma lemba la Chivumbulutso 7:3 likunena za kuika chisindikizo kotsiriza, panthawi imene Mulungu amatsimikizira kuti odzozedwawa asonyeza kukhulupirika kwawo mosakayikitsa ngakhale pang’ono.—1/1, masamba 30-31.
• Makolo angaphunzire chiyani pankhani ya m’Baibulo ya Samueli?
N’zosakayikitsa kuti makolo a Samueli ankam’phunzitsa mwana wawoyo Mawu a Mulungu. Motero makolo masiku ano azichita chimodzimodzi ndi ana awo. Komanso azilimbikitsa ana awo kukhala ndi cholinga chogwira ntchito yotumikira Yehova.—1/15, masamba 16.
• Kodi tingasonyeze bwanji kuti tikusangalala podikirira Yehova?
Tikudikirira “tsiku la Yehova” ndipo tikuyembekeza nthawi imene adzachotse anthu onse osaopa Mulungu. (2 Petulo 3:7, 12) Koma ngakhale Yehova akufunitsitsa kuchotsa zoipa zonse, akuleza mtima n’cholinga choti adzapulumutse Akhristu m’njira yotamanditsa dzina lake. Tisamakayike ngakhale pang’ono kuti Yehova akudziwa nthawi yoyenerera kuchita kanthu, ndipo pakali pano tiziyesetsa kuchita zinthu zomutamanda. (Salmo 71:14, 15)—3/1, masamba 17-18.
• Kodi Nowa analowetsa nyama zingati zodyedwa m’chingalawa? Kodi pamtundu uliwonse analowetsapo nyama seveni zokha kapena analowetsa seveni zamphongo ndi seveni zazikazi?
Nowa anauzidwa kuti nyama zonse zodyedwa ‘adzitengereko yekha zisanu ndi ziwiri, zisanu ndi ziwiri.’ (Genesis 7:1, 2) Malemba ena m’Baibulo amasonyeza kuti Mawu Chiheberi omasuliridwa kuti “zisanu ndi ziwiri, zisanu ndi ziwiri” satanthauza kuti panali zisanu ndi ziwiri zamphongo komanso zisanu ndi ziwiri zazikazi. Motero zikuoneka kuti Nowa anatenga nyama zisanu ndi ziwiri pamtundu uliwonse wa nyama zodyedwa. Zitatu zazikazi ndi zitatu zamphongo ndipo yachisanu ndi chiwiriyo inali yoti adzapereke nsembe patsogolo. (Genesis 8:20)—3/15, masamba 31.
• N’chifukwa chiyani Akhristu ayenera ‘kuonetsetsa’ chikhulupiriro cha akulu amene akutsogolera?
Mtumwi Paulo akutiuza kuti ‘tionetsetse’ madalitso a khalidwe lokhulupirika la akulu ndi kutsanzira chitsanzo chawo cha chikhulupiriro. (Aheberi 13:7) Timatero chifukwa choti Mawu a Mulungu amatilangiza kuti tizitero. Komanso sitikayikira ngakhale pang’ono kuti akulu amaganizira kwambiri za Ufumu komanso za ifeyo.—4/1, tsamba 28.