Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Chisoni Chachikulu Ndiponso Chosatherapo

Chisoni Chachikulu Ndiponso Chosatherapo

Chisoni Chachikulu Ndiponso Chosatherapo

CHAPOSACHEDWAPA, wofufuza wina anafuna kudziwa kuti kodi anthu amene ana awo anamwalira amamva bwanji m’kupita kwa nthawi. Iye anatumiza chikalata cha mafunso kwa makolo angapo amene ana awo anamwalira zaka zingapo zapitazo. Si makolo onse amene anam’yankha. Bambo wina dzina lake Vladimir, mwana wake anali atamwalira zaka zisanu zapitazo, ndipo anati mpaka pano amavutika kwambiri akakumbutsidwa za mwana wakeyu. *

Makolo ambiri amakhala ndi chisoni choterechi ana awo akamwalira. Zaka 10 zapitazo, bambo wina dzina lake William, mwana wake anamwalira ali ndi zaka 18. Bamboyu analemba kuti: “Imfa ya mwana wangayu imandiwawabe mpaka pano ndipo sindidzaiiwala mpaka kalekale.” Patatha zaka zisanu kuchokera pamene mwana wamkazi wa Lucy anamwalira atangodwala mwadzidzidzi, Lucy analemba kuti: “Mwanayo atamwalira, kwa masiku angapo mumtima mwanga ndinkangoti, ‘Zimenezi n’zosatheka ayi.’ Ndinkangoona ngati kuti ndi maloto basi. Patapita kanthawi ndinazindikira kuti n’zoonadi, mwana uja wapita. Ngakhale kuti patha zaka zisanu, nthawi zina ndimati ndikakhala phee ndimangolira.”

N’chifukwa chiyani makolo amene ana awo anamwalira, monga Vladimir, William, ndi Lucy, amakhala ndi chisoni chachikulu komanso chosatherapo? Tiyeni tione zifukwa zina.

N’chifukwa Chiyani Chisoni Chawo Sichitherapo?

M’banja mukabadwa mwana makolo amam’konda mwapadera kwambiri. Kungom’nyamula m’manja, kumuona akugona, kapena akumwetulira kumawasangalatsa mosaneneka. Makolo achikondi amanyadira kwambiri ana awo. Amawaphunzitsa khalidwe labwino ndiponso ulemu. (1 Atesalonika 2:7, 11) Anawo akamamvera zimenezi, makolowo amasangalala ndipo amaona kuti anawo akadzakula adzachita zazikulu.

Makolo otere amachita khama zedi kusamalira ana awo. Nthawi zambiri amasunga ndalama kapena katundu winawake kuti zidzathandize ana awo akamadzalowa m’banja. (2 Akorinto 12:14) Tikaganizira za chikondi, nthawi, khama ndiponso ndalama zochuluka zimene makolo amawonongera pa ana awo timaona kuti makolo amafuna kuti ana awo adzakule bwinobwino osati kuti adzamwalire. Mwana akamwalira, ndiye kuti zonsezi zalowa m’madzi. Imfa ili ngati khoma lotsekereza chikondi chachikulu chimene makolo amakhala nacho pa ana awo. Imfa ya mwana wawo imawapweteka mosaneneka. Kulira kwawo kumakhala kosatherapo.

Baibulo limasonyeza kuti imfa ya mwana imakhala yowawa kwambiri kwa makolo ndipo saiiwala. Baibulo limanena mawu otsatirawa pofotokoza zimene zinachitika pamene Yakobo anamva kuti mwana wake Yosefe wamwalira. Limati: “Yakobo ndipo anang’amba malaya ake, navala chiguduli m’chuuno mwake nam’lirira mwana wake masiku ambiri. Ndipo ana aamuna ake onse ndi ana aakazi onse anauka kuti am’tonthoze: koma anakana kutonthozedwa; ndipo anati, Pakuti ndidzatsikira kumanda kwa mwana wanga, ndilinkulirabe.” Patadutsa zaka zambiri, Yakobo ankalirabe mwana wakeyo, chifukwa ankaganiza kuti anamwaliradi. (Genesis 37:34, 35; 42:36-38) Chitsanzo china cha m’Baibulo n’cha mkazi wina wokhulupirika, dzina lake Naomi, amene ana ake aamuna awiri anamwalira iye ali moyo. Chifukwa choti chisoni chinam’kulira, iye anafuna kusintha dzina lake kuti lisakhalenso Naomi, kutanthauza kuti “Wosangalala,” koma kuti likhale Mara, kutanthauza kuti “Wokhumudwa.”​—Rute 1:3-5, 20, 21.

Sikuti Baibulo limangovomereza kuti makolo amakhala ndi chisoni chachikulu ana awo akamwalira. Koma limasonyezanso kuti Yehova amalimbikitsa anthu amene akulira. M’nkhani yotsatirayi tikambirana njira zimene Mulungu amalimbikitsira anthuwa.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Mayina ena tawasintha.