Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Lolani Mawu a Mulungu Kutsogolera Mapazi Anu

Lolani Mawu a Mulungu Kutsogolera Mapazi Anu

Lolani Mawu a Mulungu Kutsogolera Mapazi Anu

“Mawu anu ndiwo nyali ya kumapazi anga, ndi kuunika kwa panjira panga.”​—SALMO 119:105.

1, 2. N’chifukwa chiyani anthu ambiri amalephera kupeza chimwemwe ndi mtendere?

KODI mungakumbukire nthawi imene munafunsirapo njira? Mwina munali mutatsala pang’ono kufika komwe munali kupita. Kapena munali mutasochera kwambiri moti munafunikira kusintha njira. Mulimonse mmene zinalili, kodi sizikanakhala bwino kufunsa munthu wodziwa bwino deralo kuti akuthandizeni? Munthu ameneyo akanakulozerani njira yolondola.

2 Kwa zaka zikwi zambiri, anthu akhala akuyesetsa kudzipezera njira yolondola pamoyo, popanda kupempha Mulungu kuti awathandize. Koma paokha, anthu amasochera kwambiri. Sangathe kupeza okha njira yotsogolera kumoyo wachimwemwe ndi mtendere. N’chifukwa chiyani amalephera kupeza njira yoteroyo? Zaka zoposa 2,500 zapitazo, mneneri Yeremiya ananena mawu akuti: “Sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.” (Yeremiya 10:23) Aliyense amene amayesa yekha kulongosola mapazi ake popanda kupempha thandizo, amagwira mwala. Anthu amafunikadi thandizo lowatsogolera pamoyo wawo!

3. N’chifukwa chiyani Yehova Mulungu ndiye amadziwadi kutitsogolera ndipo walonjeza chiyani?

3 Yehova Mulungu ndiye amadziwadi kutitsogolera. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa chakuti iyeyo amadziwa bwino mmene anthu alili. Amadziwanso bwino mmene anthu anasocherera. Ndipo amadziwanso zimene anthu ayenera kuchita kuti apezenso njira yolondola. Pokhala Mlengi wathu, Yehova nthawi zonse amadziwa zinthu zimene zingatithandize. (Yesaya 48:17) Choncho, tingakhulupirire zimene Mulungu analonjeza pa Salmo 32:8, kuti: “Ndidzakulangiza ndi kuphunzitsa iwe za njira ukayendayo; ndidzakupangira ndi diso langa lakuyang’ana iwe.” N’zosakayikitsa kuti Yehova ndi mtsogoleri wabwino kwambiri. Koma kodi amatitsogolera bwanji?

4, 5. Kodi Mawu a Mulungu angatitsogolere bwanji?

4 Popemphera kwa Yehova, wamasalmo anati: “Mawu anu ndiwo nyali ya kumapazi anga, ndi kuunika kwa panjira panga.” (Salmo 119:105) Mawu ndiponso zikumbutso za Mulungu zimene zimapezeka m’Baibulo, zingatithandize kuthana ndi mavuto pamoyo wathu. Tikamawerenga Baibulo ndi kulilola kutitsogolera, mawu a pa Yesaya 30:21 amagwira ntchito pa ife. Mawuwo amati: “Makutu ako adzamva mawu kumbuyo kwa iwe akuti, Njira ndi iyi, yendani inu m’menemo.”

5 Onani kuti lemba la Salmo 119:105 likutchula zinthu ziwiri zimene Mawu a Mulungu amachita. Choyamba, ali ngati nyali ya kumapazi athu. Tikamakumana ndi mavuto, mfundo za m’Baibulo ziyenera kutsogolera mapazi athu kuti tizisankha zinthu mwanzeru ndi kupewa misampha ndi mbuna za dzikoli. Chachiwiri, zikumbutso za Mulungu zimaunika pa njira pathu. Zimatithandiza kuchita zinthu zogwirizana ndi chiyembekezo chathu chodzakhala ndi moyo wosatha m’Paradaiso, amene Mulungu analonjeza. Timaoneratu zotsatira za zimene tikuchita, zabwino kapena zoipa, chifukwa chakuti kutsogolo kumene tikupita n’kowala bwino. (Aroma 14:21; 1 Timoteyo 6:9; Chivumbulutso 22:12) Tiyeni tione bwinobwino mmene Mawu a Mulungu alili nyali ya ku mapazi athu ndi kuunika kwa panjira pathu.

“Nyali ya Kumapazi Anga”

6. Kodi Mawu a Mulungu angakhale bwanji nyali ya kumapazi athu?

6 Tsiku lililonse timafunika kusankha zochita pamoyo wathu. Zosankha zina zingaoneke zazing’ono. Koma nthawi zina tingafunike kusankha zochita pazinthu zimene zingayese kudzisunga kwathu, kuona mtima kwathu, kapena kusalowerera kwathu nkhani zandale. Kuti tigonjetse mayesero oterowo, tiyenera ‘kuphunzitsa luntha lathu la kuzindikira kuti lisiyanitse choyenera ndi cholakwika.’ (Aheberi 5:14) Tikamaphunzira ndi kumvetsa bwino Mawu a Mulungu ndi mfundo zake, timaphunzitsanso chikumbumtima chathu kuchita zinthu zokondweretsa Yehova.​—Miyambo 3:21.

7. Fotokozani zimene zingachititse Mkhristu kukopeka ndi kuyamba kucheza kwambiri ndi anzake osakhulupirira a kuntchito.

7 Tiyeni tione chitsanzo. Kodi ndinu munthu wamkulu ndithu, amene akuyesetsa kukondweretsa mtima wa Yehova? (Miyambo 27:11) Ngati zili choncho, mukuchita bwino. Koma tayerekezani kuti anzanu ena kuntchito akugulirani tikiti kuti mukalowe nawo limodzi kubwalo la zamasewera. Iwo amasangalala kugwira nanu ntchito ndipo akufuna kuti mukacheze nawo kumalo ena. Mwina mumaona kuti anthuwa si oipa ayi. Ndipo n’kutheka kuti ali ndi makhalidwe ena abwino. Kodi mungatani? Kodi pangakhale vuto kupita nawo? Kodi Mawu a Mulungu angakuthandizeni bwanji kusankha mwanzeru?

8. Kodi ndi mfundo za m’Malemba ziti zimene zingatithandize pa nkhani ya mayanjano?

8 Tiyeni tione mfundo zingapo za m’Malemba. Mfundo yoyamba ili pa lemba la 1 Akorinto 15:33, limene limati: “Mayanjano oipa amawononga makhalidwe abwino.” Kodi lemba limeneli likunena kuti tizipeweratu osakhulupirira? Ayi, si zimene Malemba amanena. Ndipotu, ngakhale mtumwi Paulo ankakonda “anthu osiyanasiyana,” ndi osakhulupirira omwe. (1 Akorinto 9:22) Chikhristu chenicheni chimafuna kuti tizikonda anthu ena, ngakhale osakhulupirira. (Aroma 10:13-15) N’zovuta kutsatira uphungu wakuti “tichitire onse zabwino” ngati timadzipatula kwa anthu amene akufunikira thandizo lathu.​—Agalatiya 6:10.

9. Kodi ndi uphungu wa m’Baibulo uti umene ungatithandize kuti tizisamala ndi anzathu a kuntchito?

9 Komabe, kungocheza ndi mnzanu wa kuntchito n’kosiyana kwambiri ndi kukhala bwenzi lake lapamtima. Lemba linanso lingathandize pa mfundo imeneyi. Mtumwi Paulo anachenjeza Akhristu kuti: “Musamangidwe m’goli ndi osakhulupirira.” (2 Akorinto 6:14) Kodi mawu oti “musamangidwe m’goli” akutanthauza chiyani? Mabaibulo ena amamasulira mawuwa kuti “musamayendere limodzi,” “musayese kuchita zofanana nawo,” kapena “siyani kupanga ubwenzi wosayenera.” Kodi ndi ubwenzi wotani ndi anzanu a kuntchito umene ndi wosayenera? Kodi ubwenziwo umapitirira muyezo ukafika pati? Kodi umakhala bwanji kumangidwa m’goli ndi osakhulupirira? Mawu a Mulungu, Baibulo, angatsogolere mapazi anu pankhani imeneyi.

10. (a) Kodi Yesu ankasankha anthu otani kukhala anzake apamtima? (b) Kodi ndi mafunso ati amene angatithandize kusankha bwino anzathu?

10 Taganizirani chitsanzo cha Yesu, amene wakhala akukonda anthu kuyambira pamene iwo analengedwa. (Miyambo 8:31) Ali pa dziko lapansi, ankakonda kwambiri ophunzira ake. (Yohane 13:1) ‘Anakondanso’ ngakhale munthu amene anali wosocheretsedwa pankhani ya kupembedza. (Maliko 10:17-22) Komabe, Yesu anali ndi malire posankha anzake apamtima. Sanasankhe munthu aliyense amene sanafune kuchita chifuniro cha Atate wake kukhala bwenzi lake lapamtima. Nthawi ina Yesu anati: “Mukhalabe mabwenzi anga mukamachita zimene ndikukulamulani.” (Yohane 15:14) Mwina mumagwirizana bwino ndi mnzanu wina wa kuntchito. Koma dzifunseni kuti: ‘Kodi munthu ameneyu akufuna kuchita zimene Yesu analamula? Kodi iyeyu akufuna kuphunzira za Yehova, amene Yesu anati tizimulambira? Kodi ali ndi makhalidwe abwino ngati makhalidwe anga achikhristu?’ (Mateyo 4:10) Mukamacheza ndi anzanu a kuntchito ndi kuyesetsa kuchita zimene Baibulo limanena, mudzapeza mayankho a mafunso amenewa.

11. Kodi Mawu a Mulungu ayenera kutsogolera mapazi athu pazinthu ngati ziti?

11 Mawu a Mulungu angakhale ngati nyali ya kumapazi athu pazinthu zinanso zambiri. Mwachitsanzo, mwina Mkhristu yemwe sali pa ntchito angapeze ntchito imene akuifuna kwambiri. Komabe, ntchitoyo ingakhale yopanikiza ndipo ngati ataiyamba, azidzaphonya misonkhano yambiri ndi zinthu zinanso zokhudza kulambira koona. (Salmo 37:25) Mkhristu wina mwina angakopeke kuti aonere zinthu zotsutsana ndi mfundo za m’Baibulo. (Aefeso 4:17-19) Winanso mwina sachedwa kukhumudwa Akhristu anzake akalakwitsa zinthu. (Akolose 3:13) Pazinthu zonsezi, tiyenera kulola Mawu a Mulungu kukhala nyali ya kumapazi athu. Tikamatsatira mfundo za m’Baibulo, tingathanedi ndi vuto lina lililonse. Mawu a Mulungu ndi “opindulitsa pa kuphunzitsa, kudzudzula, kuwongola zinthu, [ndi] kulangiza m’chilungamo.”​—2 Timoteyo 3:16.

“Kuunika kwa Panjira Panga”

12. Kodi Mawu a Mulungu amakhala bwanji kuunika kwa panjira pathu?

12 Lemba la Salmo 119:105 limanenanso kuti Mawu a Mulungu angaunike panjira pathu kuti tione kumene tikupita. Baibulo limatiuza chifukwa chake padzikoli pali mavuto ambiri ndipo limafotokoza zimene zidzachitike m’tsogolo. M’pake kuti sitili mu mdima. Ndithudi, tikudziwa kuti tikukhala “m’masiku otsiriza” a dongosolo loipali la zinthu. (2 Timoteyo 3:1-5) Kudziwa zimene zidzachitike m’tsogolo kuyenera kukhudza zimene tikuchita panopa. Mtumwi Petulo analemba kuti: “Popeza zinthu zonsezi zidzasungunuka, lingalirani za mtundu wa munthu amene muyenera kukhala pa khalidwe loyera ndi pa ntchito za kudzipereka kwanu kwa Mulungu. Teroni poyembekezera ndi kukumbukira nthawi zonse kukhalapo kwa tsiku la Yehova.”​—2 Petulo 3:11, 12.

13. Kodi kudziwa kuti nthawi yatha kuyenera kukhudza bwanji zimene timaganiza ndi kuchita pa moyo wathu?

13 Zimene timaganiza ndi kuchita pa moyo wathu ziyenera kusonyeza kuti timakhulupirira ndi mtima wonse kuti “dziko likupita limodzi ndi chilakolako chake.” (1 Yohane 2:17) Kugwiritsa ntchito malangizo a m’Baibulo kungatithandize kusankha mwanzeru zimene tikufuna kudzachita m’tsogolo. Mwachitsanzo, Yesu anati: “Pitirizani kufuna ufumu choyamba ndi chilungamo chake, ndipo zina zonsezi zidzawonjezedwa kwa inu.” (Mateyo 6:33) Timayamikira achinyamata ambiri amene akukhulupirira mawu a Yesu amenewa ndipo akuchita utumiki wa nthawi zonse. Anthu ena, ngakhale mabanja amene, adzipereka ndipo asamukira ku madera kumene kulibe ofalitsa Ufumu ambiri.

14. Kodi banja lina linatani kuti lichite zambiri muutumiki?

14 Banja lina lachikhristu la ana awiri la ku United States linasamukira ku dziko la Dominican Republic kukatumikira mu mpingo wa ofalitsa pafupifupi 130 m’tawuni ya anthu 50,000. Pa April 12, 2006, anthu pafupifupi 1,300 anapezeka pa Chikumbutso cha imfa ya Khristu. Munda kumeneko ‘wayera kale ndipo ndi wofunika kukolola.’ Patapita miyezi isanu yokha, banjalo linali kuchititsa maphunziro a Baibulo 30. (Yohane 4:35) Bambowo anati: “Mpingo umenewu uli ndi abale ndi alongo 30 ochokera ku mayiko ena amene anabwera kuno kudzathandiza. Pafupifupi 20 ndi ochokera ku United States, enawo amachokera ku Bahamas, Canada, Italy, New Zealand, ndi Spain. Onsewo ndi achangu muutumiki ndipo alimbikitsa kwambiri abale a kuno.”

15. Kodi mwalandira madalitso otani chifukwa chofuna Ufumu choyamba pamoyo wanu?

15 N’zomveka kuti ambiri sangakwanitse kusamukira ndi kukathandiza ku dziko limene kulibe ofalitsa ambiri. Koma amene angakwanitse kutero kapena angasinthe zinthu m’moyo wawo kuti akwanitse, adzalandira madalitso ambiri pochita zimenezi. Kulikonse kumene muli, mungapeze chimwemwe ngati mukutumikira Yehova ndi mphamvu yanu yonse. Ngati mufuna Ufumu choyamba pamoyo wanu, Yehova akulonjeza ‘kukutsegulirani mazenera a kumwamba, ndi kukutsanulirani mdalitso wakuti adzasoweka malo akuulandira.’​—Malaki 3:10.

Yehova Akamatitsogolera, Timapindula

16. Kodi tingapindule bwanji tikalola Mawu a Mulungu kutitsogolera?

16 Taona kuti mawu a Yehova amatitsogolera m’njira ziwiri. Mawuwo amakhala ngati nyali ya kumapazi athu potithandiza kuyenda pa njira yabwino ndi kutitsogolera posankha zochita. Ndipo amaunika pa njira pathu kuti tiziona bwinobwino kutsogolo kumene tikupita. Zimenezi zimatithandiza kumvera malangizo a Petulo akuti: “Valani zilimbe m’maganizo mwanu kukonzekera kugwira ntchito, sungani maganizo anu bwino lomwe; ikani chiyembekezo chanu pa kukoma mtima kwa m’chisomo kumene mudzaonetsedwa pa vumbulutso la Yesu Khristu.”​—1 Petulo 1:13.

17. Kodi kuphunzira Baibulo kungatithandize bwanji kutsogoleredwa ndi Mulungu?

17 Sitikayikira kuti Yehova amatitsogolera. Koma funso n’lakuti, Kodi mumagonjera akamakutsogolerani? Kuti mumvetse mmene Yehova amatitsogolerera, yesetsani kuwerenga Baibulo tsiku ndi tsiku. Sinkhasinkhani zimene mukuwerenga, yesani kumvetsa zimene Yehova akufuna, ndipo ganizirani mmene mungagwiritsire ntchito zimene mukuwerengazo pamoyo wanu. (1 Timoteyo 4:15) Komanso posankha zochita, muzigwiritsa ntchito “luntha la kulingalira.”​—Aroma 12:1.

18. Kodi timalandira madalitso otani tikalola Mawu a Mulungu kutitsogolera?

18 Ngati titazilola, mfundo za m’Mawu a Mulungu zingatiunikire ndi kutitsogolera kuti tisankhe mwanzeru njira yolondola pamoyo wathu. Tingakhale ndi chikhulupiriro chonse kuti mawu olembedwa a Yehova ‘amapatsa opusa nzeru.’ (Salmo 19:7) Tikalola Baibulo kutitsogolera, timakhala ndi chikumbumtima chabwino ndipo timasangalala kudziwa kuti tikukondweretsa Yehova. (1 Timoteyo 1:18, 19) Tikalola Mawu a Mulungu kutsogolera mapazi athu tsiku lililonse, Yehova adzatipatsa mphoto yaikulu kwambiri ya moyo wosatha.​—Yohane 17:3.

Kodi Mukukumbukira?

• N’chifukwa chiyani kulola Yehova Mulungu kutsogolera mapazi athu n’kofunika?

• Kodi Mawu a Mulungu angakhale bwanji nyali ya kumapazi athu?

• Kodi Mawu a Mulungu angakhale bwanji kuunika kwa panjira pathu?

• Kodi kuphunzira Baibulo kungatithandize bwanji kutsogoleredwa ndi Mulungu?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 15]

Kodi kuyanjana kwanu ndi munthu wosakhulupirira kumakhala kosayenera kukafika pati?

[Chithunzi patsamba 16]

Mabwenzi apamtima a Yesu anali anthu amene ankachita chifuniro cha Yehova

[Zithunzi patsamba 17]

Kodi moyo wathu umasonyeza kuti timafuna Ufumu choyamba?