Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Kodi kusankha Akhristu odzozedwa kunatha liti?

Baibulo silipereka yankho lachindunji la funso limeneli. Tikudziwa kuti kudzozedwa kwa otsatira a Yesu n’cholinga chokalandira moyo wakumwamba kunayamba mu 33 C.E. (Machitidwe 2:1-4) Tikudziwanso kuti pambuyo poti atumwi onse afa, mbewu za “tirigu,” zomwe ndi Akhristu oona odzozedwa, ‘zinkakulira pamodzi’ ndi “udzu,” womwe ndi Akhristu onyenga. (Mateyo 13:24-30) Kenaka kuyambira cha kumapeto kwa m’ma 1800, Akhristu odzozedwa anakhalanso achangu moonekera. Mu 1919 “zokolola za dziko lapansi,” zomwe zikuphatikizapo Akhristu otsalira odzozedwa, zinayamba kukololedwa.​—Chivumbulutso 14:15, 16.

Kuchokera cha kumapeto kwa m’ma 1800 mpaka mu 1931, cholinga chachikulu cha ntchito yolalikira chinali chosonkhanitsa otsalira a thupi la Khristu. Mu 1931, Ophunzira Baibulo anayamba kudziwika ndi dzina la m’Baibulo lakuti Mboni za Yehova. Ndipo Nsanja ya Olonda ya November 15, 1933, inafotokoza kuti dzina lapadera limeneli ndilo linali “ndalama ya dinari” imene Yesu anatchula m’fanizo lake la pa Mateyo 20:1-16. Inafotokozanso kuti maola 12 amene Yesu anawatchula mu fanizoli ankaimira zaka 12 kuchokera mu 1919 kufika mu 1931. Kwa zaka zambiri kuchoka pamene mfundoyi inalembedwa, Mboni za Yehova zinkakhulupirira kuti kusankha anthu okakhala mu Ufumu wa kumwamba kunatha mu 1931, ndiponso kuti anthu amene anasankhidwa mu 1930 ndi 1931 kuti akakhale olamulira anzake a Khristu anali “omaliza” kuitanidwa. (Mateyo 20:6-8) Komabe, mu 1966 anamveketsa bwino mfundoyi ponena kuti fanizoli silikukhudzana ndi nkhani ya kutha kwa ntchito yosankha odzozedwa.

Mu 1935 Mboni za Yehova zinamvetsa kuti “khamu lalikulu” lotchulidwa pa Chivumbulutso 7:9-15 ndi a “nkhosa zina,” omwe ndi Akhristu okhala ndi chiyembekezo chodzakhala padziko lapansi. Zinamvetsanso kuti Akhristu amenewa adzasonkhanitsidwa mu “masiku otsiriza” ndiponso kuti gulu la Akhristu amenewa lidzapulumuka pa Haramagedo. (Yohane 10:16; 2 Timoteyo 3:1; Chivumbulutso 21:3, 4) Pambuyo pa chaka chimenechi, cholinga chachikulu cha ntchito yolalikira chinali kusonkhanitsa khamu lalikulu. Motero, Mboni zinakhulupirira kuti kusankha anthu opita kumwamba kunatha mu 1935. Zinayamba kukhulupirira zimenezi makamaka pambuyo pa 1966. Zimenezi zinkaoneka kuti zili chonchodi makamaka chifukwa choti pafupifupi anthu onse amene anabatizidwa pambuyo pa chaka cha 1935 ankakhulupirira kuti anali ndi chiyembekezo chodzakhala padziko lapansi. Pambuyo pa chaka chimenechi, Mboni zinakhulupirira kuti anthu onse osankhidwa kukakhala kumwamba amalowa m’malo Akhristu odzozedwa amene sanakhulupirike.

Ndithudi, ngati wodzozedwa wina wasiya choonadi ndipo sakulapa, Yehova amasankha munthu wina kuti alowe m’malo mwake. (Aroma 11:17-22) Komabe, mwina odzozedwa amene akhala osakhulupirika si ambiri ayi. Komano, m’kupita kwa nthawi, mzimu woyera wakhala ukuchitira umboni Akhristu ena obatizidwa pambuyo pa 1935, kuti akakhala kumwamba. (Aroma 8:16, 17) Motero, zikuoneka kuti sitingatchule tsiku lenileni la kutha kwa ntchito yosankha Akhristu opita kumwamba.

Kodi munthu amene sakukayika ngakhale pang’ono kuti tsopano ndi wodzozedwa ndipo wayamba kudya zizindikiro pa Chikumbutso tiyenera kumuona bwanji? Sitiyenera kumuweruza chifukwa imeneyi ndi nkhani yapakati pa iyeyo ndi Yehova. (Aroma 14:12) Komabe, Akhristu odzozedwa enieni safuna ulemu wapadera. Sakhulupirira kuti kudzozedwa kwawoko kumawapatsa nzeru zinazake zapadera zimene ngakhale Akhristu ena okhwima mwauzimu a khamu lalikulu alibe. Sakhulupiriranso kuti kudzozedwako pakokha kumawachititsa kuti akhale ndi mzimu woyera wambiri kuposa anzawo a nkhosa zina, ndipo safunanso kuwachitira mautumiki ena apadera. Ndipo sanena kuti n’ngoposa akulu oikidwa mumpingo chifukwa choti amadya zizindikiro. Iwo amadzichepetsa pokumbukira kuti abale ena odzozedwa m’nthawi ya atumwi analibe ziyeneretso zotumikira monga akulu kapena atumiki othandiza. (1 Timoteyo 3:1-10, 12, 13; Tito 1:5-9; Yakobe 3:1) Ndipotu Akhristu ena odzozedwa anali ofooka mwauzimu. (1 Atesalonika 5:14) Komanso alongo, ngakhale kuti anali odzozedwa, sankaphunzitsa mumpingo.​—1 Timoteyo 2:11, 12.

Motero Akhristu odzozedwa, pamodzi ndi anzawo a nkhosa zina amayesetsa kukhala olimba mwauzimu, kukhala ndi zipatso za mzimu ndiponso kulimbikitsa mtendere mumpingo. Akhristu onse, odzozedwa ndi ankhosa zina, amachita khama pantchito yolalikira ndi kupanga ophunzira motsogozedwa ndi Bungwe Lolamulira. Akhristu odzozedwa amachita zimenezi mosangalala panthawi yonse imene Yehova wafuna kuti amutumikire ali padziko lapansi.