Kodi Ndingatani Kuti Ndiphunzitse Bwino Ana Anga?
Kodi Ndingatani Kuti Ndiphunzitse Bwino Ana Anga?
KUPHUNZITSA ana kumakhala ngati kuyenda ndi ana anu ulendo wosangalatsa koma umene uli ndi mavuto osiyanasiyana. Mumawalimbikitsa ndi kuwalangiza mwachikondi kuti muwathandize kuyenda bwino panjira ya moyo. Pamakhaladi zambiri zoti aphunzire.
Kuti ana akhale ndi moyo wabwino ndi wosangalala, ayenera kuona khalidwe labwino ndi zinthu zauzimu kuti n’zofunika kwambiri. Ayeneranso kuphunzira kusiyanitsa choyenera ndi cholakwika. Ana akaphunzitsidwa kudziwa ndi kukonda Yehova, ndiye kuti tikuwaphunzitsa maphunziro abwino ndi opindulitsadi ndipo adzawathandiza kwamuyaya. Zambiri zimene ana amaphunzira ndi mmene amaonera zimene akuphunzirazo, zimadalira makolo awo.
Kuphunzitsa ana, kumakhala ndi mavuto osiyanasiyana. Iwo sachedwa kutengeka ndipo angaphunzire zinthu zambiri zoipa zimene makolo sanawaphunzitse. Zili choncho chifukwa tikukhala m’dziko lolamuliridwa ndi Satana Mdyerekezi. (1 Yohane 5:19) Nayenso akufuna kuphunzitsa ana anu, koma cholinga chake ndi chosiyana kwambiri ndi chanu. Satana ndi mphunzitsi wodziwa ntchito yake amene wakhalapo zaka zambiri, koma ndi woipa zedi. Ngakhale kuti amadzionetsera ngati “mngelo wa kuwala,” kuwala kwake n’kwachinyengo ndi kotsutsana ndi Mawu a Yehova ndiponso chifuniro chake. (2 Akorinto 4:4; 11:14; Yeremiya 8:9) Mdyerekezi ndi ziwanda zake ndi akatswiri a chinyengo, amene amaphunzitsa anthu kudzikonda, kusaona mtima, ndi makhalidwe ena oipa.—1 Timoteyo 4:1.
Kodi mungateteze bwanji ana anu kuti asasocheretsedwe? Kodi mungawaphunzitse bwanji kukonda zinthu zabwino ndi zoyenera? Muyenera kudzifufuza nokha kaye kuti mukhale chitsanzo chabwino. Muyeneranso kudziwa kuti muli ndi udindo wophunzitsa ana anu ndipo muyenera kukhala ndi nthawi yochitira zimenezi. Koma tisanakambirane mfundo zimenezi, tiyeni tione kaye kuti kodi maziko a maphunziro abwino agona pati.
Maziko a Maphunziro Abwino
Tingaphunzire zambiri kuchokera kwa Mfumu Solomo ya Isiraeli, mmodzi wa anthu anzeru kwambiri. Baibulo limatiuza kuti: “Mulungu anam’patsa Solomo nzeru ndi luntha lambiri, ndi mtima wodziwa [zinthu] za mitundumitundu, zonga mchenga uli m’mbali mwa nyanja. Ndipo nzeru ya Solomo inaposa nzeru za anthu onse a kum’mawa, ndi nzeru zonse za ku Aigupto.” Solomo ‘ananena miyambi zikwi zitatu, ndipo nyimbo zake zinali chikwi chimodzi mphambu zisanu.’ Ankadziwanso kwambiri za zomera ndi zinyama. (1 Mafumu 4:29-34) Mfumu Solomo anayang’anira ntchito ya zomangamanga mu Isiraeli, kuphatikizapo ntchito yomangira Yehova kachisi wapamwamba kwambiri ku Yerusalemu.
Zolemba za Solomo, ngati zimene zili m’buku la Mlaliki, zimasonyeza kuti ankamvetsa bwino chibadwa cha anthu. Anauziridwa ndi Mulungu kuti afotokoze maziko a maphunziro abwino. Solomo anati: “Kuopa Yehova ndiko chiyambi cha kudziwa.” Mfumu yanzeru imeneyi inatinso: “Chiyambi cha nzeru ndicho kuopa Yehova; kudziwa Woyerayo ndiko luntha.”—Miyambo 1:7; 9:10.
Ngati timaopa Mulungu, timamulemekeza 1 Akorinto 3:19) Ana anu amafunikira maphunziro amene maziko ake ndi “nzeru yochokera kumwamba.”—Yakobe 3:15, 17.
ndipo timapewa kumukhumudwitsa. Timazindikira kuti iye ndi Wam’mwambamwamba ndi wofunika kumugonjera. Anthu amene sawerengera Mulungu yemwe anatipatsa moyo, angaonedwe ngati anzeru, koma nzeru imeneyi ndi ‘yopusa’ kwa Mulungu. (Munthu amene amakonda Yehova amaopa kumukhumudwitsa. Yehova amafuna kuti atumiki ake azimuopa ndi kumukonda. Mose anati: “Tsopano, Israyeli, Yehova Mulungu wanu afunanji nanu, koma kuti muziopa Yehova Mulungu wanu, kuyenda m’njira zake zonse, ndi kukonda, ndi kutumikira Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse, kusunga malamulo a Yehova, ndi malemba ake, amene ndikuuzani lero kuti kukukomereni inu?”—Deuteronomo 10:12, 13.
Tikamaphunzitsa ana athu kuopa Yehova, timakhala tikuyala maziko a maphunziro amene angawathandize kukhaladi anzeru. Anawo akapitiriza kumanga pa maziko amenewo, adzayamba kulemekeza kwambiri Mlengi wawo, Gwero la nzeru yeniyeni. Zimenezi zingawathandize kumvetsa ndi kugwiritsa ntchito bwino zimene akuphunzira. Potero adzatha “kusiyanitsa choyenera ndi cholakwika.” (Aheberi 5:14) Maziko otere angawathandizenso kukhala odzichepetsa ndi kupewa kuchita zoipa.—Miyambo 8:13; 16:6.
Ana Anu Amaona Zimene Mumachita
Koma kodi tingathandize bwanji ana athu kukonda ndi kuopa Yehova? Tingapeze yankho la funso limeneli m’Chilamulo chimene Yehova anapatsa Aisiraeli kudzera mwa mneneri Mose. Aisiraeli amene anali ndi ana anauzidwa kuti: “Muzikonda Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse, ndi mphamvu yanu yonse. Ndipo mawu awa ndikuuzani lero, azikhala pamtima panu; ndipo muziwaphunzitsa mwachangu kwa ana anu, ndi kuwalankhula awa pokhala pansi m’nyumba zanu, ndi poyenda inu panjira, ndi pogona inu pansi, ndi pouka inu.”—Deuteronomo 6:5-7.
Lemba limeneli limaphunzitsa makolo mfundo zofunika kwambiri. Mfundo yoyamba ndi yakuti: Kholo liyenera kukhala chitsanzo chabwino. Kuti muphunzitse ana anu kukonda Yehova, nanunso muyenera kukonda Mulungu ndipo mawu ake ayenera kukhala pa mtima panu. N’chifukwa chiyani zimenezi n’zofunika? Chifukwa chakuti ana amaphunzira zambiri kwa makolo awo. Zinthu zimene ana anu amaona mukuchita n’zimene zimakhudza kwambiri moyo wawo. Palibenso china chimene ana amatsanzira kwambiri kuposa chitsanzo cha makolo awo.
Zinthu zimene mumalakalaka, kukonda, ndi kusangalala nazo, zimaonekera m’zochita zanu osati m’zonena zanu zokha. (Aroma 2:21, 22) Kuyambira ali khanda, ana amaphunzira zinthu mwa kuonerera makolo awo. Amatha kuzindikira zinthu zimene makolo awo amaziona kukhala zofunika, ndipo zinthu zimenezi ndi zimene zimakhalanso zofunika kwa iwo. Mukamakonda kwambiri Yehova, ana anunso amaona zimenezi. Mwachitsanzo, angaone kuti mumaona kuwerenga ndi kuphunzira Baibulo kuti n’zofunika. M’kupita kwa nthawi amazindikira kuti mumaika Ufumu poyamba pamoyo wanu. (Mateyo 6:33) Mukamapezeka pa misonkhano yachikhristu ndi kulalikira Ufumu nthawi zonse, ana anu amazindikira kuti kutumikira Yehova n’kofunika kwambiri kwa inu.—Mateyo 28:19, 20; Aheberi 10:24, 25.
Musazembe Udindo Wanu
Mfundo ina imene makolo mungaphunzire m’lemba la Deuteronomo 6:5-7 ndi yakuti: Makolo ali ndi udindo wophunzitsa ana awo. Kale pakati pa anthu a Yehova, makolo ndiwo anali ndi udindo wonse wophunzitsa ana awo. M’nthawi ya atumwi, makolo achikhristu analinso ndi udindo waukulu wophunzitsa ana awo. (2 Timoteyo 1:5; 3:14, 15) Polembera kalata Akhristu anzake, mtumwi Paulo anasonyeza kuti abambo makamaka ndiwo ayenera ‘kulera [ana awo] m’malango a Yehova ndi kuwaphunzitsa kalingaliridwe kake.’—Aefeso 6:4.
Masiku ano, anthu ndi otanganidwa kwambiri ndi ntchito kapena zinthu zina, choncho mwina makolo angafune kungosiyira aphunzitsi kapena anthu ena udindo wawo wophunzitsa ana. Koma palibe munthu wina amene angalowe m’malo mwa kholo lachikondi. Musadziderere, ndinu wofunika kwambiri pamoyo wa mwana wanu. Mukafuna thandizo sankhani mwanzeru, koma musasiyire wina udindo wanu wopatulikawu.
Khalani ndi Nthawi Yophunzitsa Ana Anu
Mfundo inanso imene makolo angaphunzire m’lemba la Deuteronomo 6:5-7 ndi yakuti: Kuphunzitsa ana kumafuna nthawi ndi khama. Kale ku Isiraeli, makolo anauzidwa ‘kuphunzitsa’ ana awo choonadi cha Mulungu. Mawu oyambirira a Chiheberi amene amamasuliridwa kuti ‘kuphunzitsa’ amatanthauza “kubwereza” kapena “kunena zinthu kambirimbiri.” Makolo anayenera kuphunzitsa motere tsiku lonse, kuyambira mbandakucha mpaka kuda, ‘m’nyumba zawo’ kapena “panjira.” Zimafunadi nthawi ndi khama kuti makolo aphunzitse ana awo kukhala ndi maganizo ndiponso makhalidwe okondweretsa Mulungu.
Choncho, kodi mungatani kuti muphunzitse bwino ana anu? Mungachite zambiri. Aphunzitseni kukonda ndi kuopa Yehova. Khalani chitsanzo chabwino. Musazembe udindo wanu, koma khalani ndi nthawi yabwino yowaphunzitsa. Sindinu wangwiro, ndipo simungalephere kulakwitsa pena ndi pena. Mukamayesetsa ndi mtima wonse kuchita chifuniro cha Mulungu, ana anu angayamikire zimene mumachita ndipo angapindule nazo. Angapinduledi chifukwa lemba la Miyambo 22:6 limati: “Phunzitsa mwana poyamba njira yake; ndipo angakhale atakalamba sadzachokamo.”
Kuphunzira kuli ngati ulendo umene munthu amayenda moyo wake wonse. Ngati inu ndi ana anu mumakonda Mulungu, mudzasangalala kuyenda ulendowu kwamuyaya. Izi zili choncho chifukwa pali zambirimbiri zoti tiphunzire zokhudza Yehova ndi zimene tingachite kuti tizimukondweretsa.—Mlaliki 3:10, 11.
[Chithunzi patsamba 15]
Kodi mumawerengera Baibulo ana anu?
[Chithunzi patsamba 16]
Khalani ndi nthawi yophunzitsa ana anu za Mlengi