Yefita Anasunga Chowinda Chake kwa Yehova
Yefita Anasunga Chowinda Chake kwa Yehova
MSILIKALI akubwerera ku nyumba atapambana nkhondo ndi kulanditsa mtundu wake kwa adani. Mwana wake wamkazi akutuluka m’nyumba ndi kuthamanga kukamuchingamira, akuimba lingaka ndi kuvina mokondwera. Atangomuona, m’malo mosangalala, msilikaliyo akung’amba zovala zake. N’chifukwa chiyani akutero? Kodi nayenso sakusangalala kuti wabwerako mwamtendere? Kodi nkhondo imene wapambanayo anali kumenyana ndi ndani? Nanga msilikaliyo ndani?
Msilikali ameneyu ndi Yefita, woweruza m’Isiraeli wakale nthawi imeneyo. Koma kuti tiyankhe mafunso enawo ndi kuona kufunika kwa nkhani imeneyi, dikirani tifotokoze zimene zinachitika anthu awiriwa asanakumane.
Nthawi Yovuta mu Isiraeli
Nthawi ya Yefita inali yovuta kwambiri. Aisiraeli anzake anali atasiya kulambira koona ndi kuyamba kulambira milungu ya Sidoni, Moabu, Amoni, ndi ya Afilisti. Choncho, Yehova anapereka anthu ake m’manja mwa Aamoni ndi Afilisti, amene anawapondereza zaka 18. Anthu a ku Gileadi, kum’mawa kwa mtsinje wa Yordano, ndi amene anavutika kwambiri. * Patapita nthawi, Aisiraeli anazindikira kulakwa kwawo, analapa ndi kutembenukira kwa Yehova, nayamba kumutumikira, ndipo anachotsa milungu yachikunja pakati pawo.—Oweruza 10:6-16.
Aamoni anamanga misasa ku Gileadi ndipo Aisiraeli anamemezana kuti akamenyane nawo. Koma Aisiraeliwo analibe mkulu wa nkhondo. (Oweruza 10:17, 18) Izi zili choncho, Yefita nayenso anali ndi mavuto ake. Abale ake a mayi wina anam’thamangitsa kuti amulande cholowa chake. N’chifukwa chake Yefita anathawira ku Tobu, dera la kum’mawa kwa Gileadi losatetezeka kwa adani a Aisiraeli. “Anyamata opanda pake,” amene mwina anachotsedwa ntchito ndi adani a Aisiraeli kapena amene anapandukira adaniwo, anapita kwa Yefita. Iwo ‘anatuluka naye pamodzi,’ mwina kutanthauza kuti anatsagana ndi Yefita pokaukira adani awo. Malemba amati Yefita anali “ngwazi yamphamvu,” mwina chifukwa chakuti anali wodziwa kumenya nkhondo. (Oweruza 11:1-3) Ndani tsopano angatsogolere Aisiraeli pomenyana ndi Aamoni?
“Tiye Ukhale Kazembe Wathu”
Akulu a Gileadi anapempha Yefita kuti: “Tiye ukhale kazembe wathu.” Ngati iwo anaganiza kuti iye atangomva zimenezo, basi anyamuka kubwerera kwawo, analemba m’madzi. Iye anawayankha Oweruza 11:4-7.
kuti: “Simunandida kodi, ndi kundichotsa m’nyumba ya atate wanga? Ndipo mundidzeranji tsopano pokhala muli m’kusauka?” Ati kupanda chilungamo kwake! Poyamba, anam’thamangitsa koma tsopano akufuna thandizo lake.—Yefita ananena kuti awatsogolera ku Gileadi ngati iwo atamvera pempho lake. Anati, ‘Yehova akapereka ana a Amoni pamaso panga, ndidzakhala mkulu wanu.’ Apa Yefita anatanthauza kuti akapambana nkhondo imeneyi, ndiye kuti Mulungu ali naye. Komanso, anafuna kutsimikiza kuti iwo sadzakana ulamuliro wa Mulungu vutoli likangotha.—Oweruza 11:8-11.
Analimbana ndi Aamoni
Yefita anayesa kukambirana ndi Aamoni. Anatumiza amithenga kwa mfumu yawo kuti adziwe chifukwa chake iwo anali kulimbana ndi Aisiraeli. Poyankha, mfumuyo inawaimba mlandu wakuti: Aisiraeli atachoka ku Iguputo, analanda dziko la Aamoni, choncho alibweze.—Oweruza 11:12, 13.
Popeza kuti Yefita ankaidziwa bwino mbiri ya Isiraeli, sizinamuvute kuwatsutsa Aamoni. Anawauza kuti Aisiraeli atachoka ku Iguputo, sanamenyane ndi Amoni, Moabu, kapena Edomu. Anawauzanso kuti Aisiraeli pochoka ku Iguputo, sanapeze Aamoni m’dziko limene akuti ndi lawo. Dziko limenelo linali la Aamori, ndipo Mulungu anapereka Sihoni, mfumu yawo, m’manja mwa Aisiraeli. Chinanso, Aisiraeli anali atakhala m’dziko limenelo zaka 300. Choncho, ndi zosamveka kuti pano Aamoni aziti ndi dziko lawo.—Oweruza 11:14-22, 26.
Yefita akutchulanso mfundo yaikulu imene yalowetsa Aisiraeli m’mavuto. Mfundo yakeyo ndi yakuti: Kodi Mulungu woona ndani? Ndi Yehova kapena milungu ya dziko limene Aisiraeli analanda? Kodi Kemosi akanakhala mulungu wamphamvu, sakanateteza dziko la anthu ake kuti ena asalilande? Pano, mkanganowu kwenikweni uli pakati pa kulambira konyenga kwa Aamoni, ndi kulambira koona. N’chifukwa chake Yefita akuti: “Yehova, Woweruzayo, aweruze lerolino pakati pa ana a Israyeli ndi ana a Amoni.”—Oweruza 11:23-27.
Mfumu ya Aamoni sinamvere uthenga wosanyengerera wa Yefita. Choncho, “mzimu wa Yehova unam’dzera Yefita, napitira iye ku Gileadi, ndi Manase,” mwina kukamemeza amuna amphamvu kuti akamenyane ndi Aamoni.—Oweruza 11:28, 29.
Chowinda cha Yefita
Yefita ankafunitsitsa kuti Mulungu am’tsogolere, n’chifukwa chake anawinda kuti: “Mukaperekatu ana a Amoni m’dzanja langa, ndipo kudzali kuti chilichonse chakutuluka pakhomo pa nyumba yanga kudzakomana nane pakubweranso ine ndi mtendere kuchokera kwa ana a Amoni, chidzakhala cha Yehova, ndipo ndidzachipereka nsembe yopsereza.” Mulungu atamva zimenezo, anadalitsa Yefita pomuthandiza kuwononga midzi 20 ya Aamoni ndi “makanthidwe aakulu ndithu,” n’kugonjetseratu adani a Isiraeli.—Oweruza 11:30-33.
Yefita atabwerako ku nkhondo, kodi anakumana ndi ndani? Sanakumane ndi wina koma mwana wake yekha wamkazi wokondedwa. “Pakumuona anang’amba zovala zake, nati, Tsoka ine, mwana wanga, wandiweramitsa kwakukulu, ndiwe wa iwo akundisaukitsa ine; pakuti ndam’tsegulira Yehova pakamwa panga ine, ndipo sinditha kubwerera.”—Oweruza 11:34, 35.
Kodi Yefita akanaperekadi nsembe mwana wake? Ayi sakanatero. Iye sakanaganiza zimenezo n’komwe. Yehova amadana ndi kupereka anthu nsembe. Akanani ndiwo anali ndi makhalidwe onyansa amenewa opereka anthu nsembe. (Levitiko 18:21; Deuteronomo 12:31) Pamene Yefita anawinda, mzimu wa Mulungu unali naye komanso Yehova anadalitsa khama lake. Malemba amatamanda Yefita chifukwa cha chikhulupiriro chake ndiponso chifukwa cha ntchito imene anagwira pokwaniritsa chifuniro cha Mulungu. (1 Samueli 12:11; Aheberi 11:32-34) Choncho sakanaganiza m’pang’ono pomwe kupereka munthu nsembe chifukwa kutero ndi kupha. Kodi nanga Yefita ankaganiza chiyani pamene analumbira kupereka munthu nsembe kwa Yehova?
Zikuoneka kuti cholinga cha Yefita chinali Eksodo 38:8; 1 Samueli 2:22) Sitidziwa zambiri za ntchito imeneyi, sitidziwanso ngati inali ya moyo wonse. Yefita ayenera kuti powinda anali kuganizira za utumiki wapadera umenewu, ndipo zikuoneka kuti anawinda kuti munthuyo akatumikire Mulungu moyo wake wonse.
kupereka munthu amene adzakumane naye kuti azitumikira Mulungu nthawi zonse. Chilamulo cha Mose chinkalola makolo kuti aziwinda kupereka ana awo kwa Yehova. Mwachitsanzo, akazi ankatumikira ku chihema, mwina kutunga madzi. (Mwana wa Yefita ndiponso Samueli, ali mwana, anagwirizana ndi makolo awo oopa Mulungu kuti akwaniritse zowinda zawo. (1 Samueli 1:11) Mwana wa Yefita ankalambira Yehova mokhulupirika ndipo nayenso, ngati bambo ake, anafuna kuti chowindacho chikwaniritsidwe. Chimenechi chinali chowinda chachikulu kwa mwana wa Yefita, chifukwa sakanadzakwatiwa moyo wake wonse. Analirira unamwali wake chifukwa Mwisiraeli aliyense ankafuna kukhala ndi ana kuti dzina la banja lawo lipitirire ndi kuti adzawasiyire cholowa. Kuti Yefita nayenso akwaniritse chowinda chake, anafunika kusiyana ndi mwana wake mmodzi yekhayo wokondedwa.—Oweruza 11:36-39.
Moyo wa namwali wokhulupirika ameneyu sunali wopanda pake. Moyo wake wotumikira pa nyumba ya Yehova unali njira yabwino, yosangalatsa, ndi yotamandika yolemekezera Mulungu. N’chifukwa chake ‘ana aakazi a Israyeli ankamuka chaka ndi chaka kum’lirira [kukayamikira, NW] mwana wa Yefita wa ku Gileadi.’ (Oweruza 11:40) Ndipo n’zosakayikitsa kuti Yefita ankasangalala kuona mwana wake akutumikira Yehova.
Masiku anonso, anthu a Mulungu ambiri amasankha utumiki wa nthawi zonse. Ena ndi apainiya, amishonale, atumiki oyendayenda, kapena ali pa Beteli. Anthu amenewa mwina saonana kawirikawiri ndi achibale awo monga mmene angafunire. Ngakhale zili choncho, iwo ndi achibale awo amasangalala ndi utumiki wopatulika woperekedwa kwa Yehova.—Salmo 110:3; Aheberi 13:15, 16.
Anakana Kutsogoleredwa ndi Mulungu
Nthawi ya Yefita, Aisiraeli ambiri anakana kutsogoleredwa ndi Yehova. Ngakhale kuti anali ndi umboni wonse wakuti Mulungu anadalitsa Yefita, Aefraimu anakangana naye. Anafuna kudziwa chifukwa chake sanawaitane ku nkhondo, mpaka anafuna kutentha nyumba yake iye ali momwemo.—Oweruza 12:1.
Yefita anayankha kuti anawaitana Aefraimuwo, koma anakana. Ngakhale anakana, Mulungu anamenya nkhondoyo ndi kupambana. Kodi mwina anakwiya chifukwa chakuti Agileadi sanawafunse posankha Yefita kukhala kazembe? Kunena zoona, Aefraimu sanadziwe kuti polimbana ndi Yefita, anali kulimbana ndi Yehova ndipo palibenso kuchitira mwina koma kumenyana nawo. Pankhondo imeneyi, Aefraimu anangoti balala. Pothawapo, amuna a Efraimu sanavute kuwazindikira chifukwa sankatha kunena bwinobwino kuti “Shiboleti.” Pamapeto pake, Aefraimu 42,000 anathera pa nkhondo imeneyo.—Oweruza 12:2-6.
Imeneyi inalidi nthawi yachisoni m’mbiri ya Aisiraeli. Nkhondo zimene oweruza ena monga Otiniyeli, Ehudi, Baraki, ndi Gidiyoni anapambana zinabweretsa mtendere. Koma pankhondoyi sipakutchulidwa za mtendere. Nkhaniyo imangomaliza ndi mawu akuti: “Yefita anaweruza Israyeli zaka zisanu ndi chimodzi; nafa Yefita Mgileadi, naikidwa m’mudzi wina wa Gileadi.”—Oweruza 3:11, 30; 5:31; 8:28; 12:7.
Kodi tikuphunzirapo chiyani pamenepa? Tikuphunzira kuti ngakhale kuti moyo wa Yefita unali wamavuto okhaokha, iye anali wokhulupirika kwa Mulungu. Ngwazi imeneyi inatchula dzina la Yehova polankhula ndi akulu a Gileadi, Aamoni, mwana wake, Aefraimu, ndiponso pamene imawinda. (Oweruza 11:9, 23, 27, 30, 31, 35; 12:3) Mulungu anadalitsa Yefita chifukwa cha kudzipereka kwake, ndipo anagwiritsa ntchito iye ndi mwana wake kutukula kulambira koona. Pamene ena anatayira ku nkhongo mfundo za Mulungu, Yefita anamamatirabe mfundozo. Kodi inuyo mudzapitirizabe kumvera Yehova ngati Yefita?
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 5 Aamoni anali anthu ankhanza kwambiri. Patapita zaka pafupifupi 60 kuchokera nthawi imeneyi, anaopseza kukolowola diso lakumanja la munthu wina aliyense wokhala m’mudzi wina wa ku Gileadi. Mneneri Amosi ananenaponso kuti anthu amenewa nthawi ina anatumbula akazi apakati a ku Gileadi.—1 Samueli 11:2; Amosi 1:13.