Kodi Mwachimwira Mzimu Woyera?
Kodi Mwachimwira Mzimu Woyera?
“Pali tchimo lobweretsa imfa.”—1 YOHANE 5:16.
1, 2. Kodi tikudziwa bwanji kuti ndi zotheka kuchimwira mzimu woyera wa Mulungu?
“NDAKHALA ndikuvutika ndi maganizo akuti ndachimwira mzimu woyera.” Mawu amenewa analembedwa ndi mayi wina ku Germany ngakhale kuti anali kutumikira Mulungu. Kodi ndi zotheka Mkhristu kuchimwira mzimu woyera, kapena kuti mphamvu ya Mulungu yogwira ntchito?
2 Inde, ndi zotheka kuchimwira mzimu woyera wa Yehova. Yesu Khristu anati: “Anthu adzakhululukidwa tchimo la mtundu uliwonse ndi mnyozo uliwonse, koma wonyoza mzimu sadzakhululukidwa.” (Mateyo 12:31) Tikuchenjezedwanso kuti: “Ngati timachita uchimo dala pambuyo podziwa choonadi molondola, sipatsalanso nsembe ina ya machimo athu. Koma pamakhala chiyembekezo china choopsa cha chiweruzo.” (Aheberi 10:26, 27) Nayenso mtumwi Yohane analemba kuti: “Pali tchimo lobweretsa imfa.” (1 Yohane 5:16) Koma kodi zili kwa munthu amene wachimwa kwambiriyo kudziwa ngati wachita “tchimo lobweretsa imfa” kapena ayi?
Munthu Akalapa Amakhululukidwa
3. Kodi kukhala ndi chisoni chachikulu chifukwa cha tchimo limene tachita, kungatanthauze chiyani?
3 Yehova ndiye Woweruza wamkulu wa anthu ochimwa. Zimenezi ndi zoona chifukwa tonsefe tidzayankha mlandu kwa iye, ndipo iye amachita chilungamo nthawi zonse. (Genesis 18:25; Aroma 14:12) Yehova ndiye amadziwa ngati tachita tchimo losakhululukidwa, ndipo angatichotsere mzimu wake. (Salmo 51:11) Koma ngati tili ndi chisoni chachikulu chifukwa cha tchimo limene tachita, n’kutheka kuti ndife olapadi. Nanga kodi kulapa kwenikweni n’kutani?
4. (a) Kodi kulapa kumatanthauza chiyani? (b) Kodi ndi chifukwa chiyani lemba la Salmo 103:10-14 lili lotonthoza mtima kwambiri?
4 Kulapa kumatanthauza kusintha maganizo athu ndi kuyamba kuipidwa ndi tchimo limene tachita kapena limene tinafuna kuchita. Kumatanthauza kumva chisoni ndi tchimolo ndi kulisiya. Tikachita tchimo lalikulu kenako ndi kutsatira njira zosonyeza kuti talapadi, mawu a wamasalmo angatonthoze mtima wathu. Iye anati: “[Yehova] sanatichitira monga mwa zolakwa zathu, kapena kutibwezera monga mwa mphulupulu zathu. Pakuti monga m’mwamba mutalikira ndi dziko lapansi, motero chifundo chake chikulira iwo akumuopa Iye. Monga kum’mawa kutanimpha ndi kumadzulo, momwemo anatisiyanitsira kutali zolakwa zathu. Monga atate achitira ana ake chifundo, Yehova achitira chifundo iwo akumuopa Iye. Popeza adziwa mapangidwe athu; akumbukira kuti ife ndife fumbi.”—Salmo 103:10-14.
5, 6. Tchulani mfundo yaikulu pa lemba la 1 Yohane 3:19-22, ndipo fotokozani zimene mawu a mtumwiyo akutanthauza.
5 Nawonso mawu a mtumwi Yohane ndi otonthoza kwambiri. Iye anati: “Umu ndi mmene tidzadziwira kuti ndife ochokera m’choonadi, ndipo tidzatsimikizira mitima yathu pamaso pake za chilichonse chimene mitima yathu ingatitsutse, chifukwa Mulungu ndi wamkulu kuposa mitima yathu ndipo amadziwa zonse. Okondedwa, ngati mitima yathu sititsutsa, tili ndi ufulu wa kulankhula kwa Mulungu; ndipo chilichonse chimene tipempha, iye adzatipatsa, chifukwa tikusunga malamulo ake ndi kuchita zomukondweretsa.”—1 Yohane 3:19-23.
Salmo 119:11) Ngati pazifukwa zina mtima wathu ukutitsutsa, tizikumbukira kuti “Mulungu ndi wamkulu kuposa mitima yathu ndipo amadziwa zonse.” Yehova amatichitira chifundo chifukwa chakuti amadziwa kuti tili ndi “chikondi chaubale chopanda chinyengo,” tikulimbana ndi uchimo, ndiponso tikuyesetsa kuchita chifuniro chake. (1 Petulo 1:22) Mtima wathu ‘sungatitsutse’ ngati timakhulupirira Yehova, timakonda abale athu, ndiponso ngati tilibe chizolowezi chochita dala tchimo. Zikatere, timakhala ndi “ufulu wa kulankhula kwa Mulungu” m’pemphero, ndipo amatiyankha chifukwa chakuti tikusunga malamulo ake.
6 ‘Tikudziwa kuti ndife ochokera m’choonadi’ chifukwa chakuti timakonda abale athu ndipo tilibe chizolowezi chochita tchimo. (Anachimwira Mzimu
7. Kodi ndi chiyani chimene chimachititsa kuti tchimo likhululukidwe kapena lisakhululukidwe?
7 Kodi ndi machimo otani amene sakhululukidwa? Kuti tiyankhe funso limeneli, tiyeni tikambirane zitsanzo za m’Baibulo. Zimenezi ziyenera kutitonthoza ngati tikuvutikabe mtima ndi tchimo lalikulu limene tinachita ngakhale kuti tinalapa. Tiona kuti chimene chimachititsa kuti tchimo likhululukidwe kapena lisakhululukidwe ndi zolinga za munthu, mtima wake, ndiponso ngati anachita dala kapena sanachite dala tchimolo, osati mtundu wa tchimo limene anachita.
8. Kodi atsogoleri ena a Chiyuda m’nthawi ya Yesu anachimwira mzimu woyera m’njira yotani?
8 Atsogoleri a Chiyuda amene mwaliuma Mateyo 12:22-32.
anatsutsa Yesu Khristu anali kuchimwira mzimu woyera. Iwo anaona mmene mzimu wa Mulungu unagwirira ntchito pa Yesu pamene ankachita zozizwitsa zimene zinalemekeza Yehova. Koma adani a Khristu amenewa anati mphamvuyo inachokera kwa Satana Mdyerekezi. Yesu ananena kuti anthu onyoza mzimu woyera wa Mulungu mwanjira imeneyi anali kuchita tchimo losakhululukidwa “m’dongosolo lino la zinthu kapena likubweralo.”—9. Kodi mnyozo ndi chiyani, ndipo Yesu anati chiyani za mnyozowo?
9 Mnyozo ndiwo mawu oipa ndi achipongwe opeputsa munthu. Popeza kuti mzimu woyera umachokera kwa Mulungu, munthu akamalankhula zonyoza mzimuwo amakhala akunyoza Yehova. Ngati munthu amakonda kulankhula zoterezi ndipo salapa, sangakhululukidwe. Nkhani imene inachititsa kuti Yesu anene za tchimo limeneli imasonyeza kuti iye anali kunena za anthu amene mwadala amatsutsa mzimu woyera wa Mulungu. Afarisiwo anachimwa ponyoza mzimuwo chifukwa chakuti ataona mphamvu ya mzimu wa Yehova pa Yesu, anati mphamvuyo inachokera kwa Mdyerekezi. Ndiye chifukwa chake Yesu anati: “Aliyense amene anyoza mzimu woyera sadzakhululukidwa mpaka kalekale, koma akhala ndi mlandu wa tchimo losatha.”—Maliko 3:20-29.
10. Kodi ndi chifukwa chiyani Yesu anati Yudasi ndi “mwana wa chiwonongeko”?
10 Taganiziraninso za Yudasi Isikarioti. Iye anali ndi khalidwe losaona mtima, ndipo anali kuba ndalama m’bokosi limene ankasunga. (Yohane 12:5, 6) Kenako Yudasi anapita kwa atsogoleri a Chiyuda ndi kupangana nawo zopereka Yesu ndi ndalama 30 zasiliva. N’zoona kuti atapereka Yesu, Yudasi anazindikira kuti walakwa koma sanalape tchimo lake ladalalo. Choncho, Yudasi ndi wosayenera kuukitsidwa. N’chifukwa chake Yesu anati Yudasiyo ndi “mwana wa chiwonongeko.”—Yohane 17:12; Mateyo 26:14-16.
Anachimwa Koma Sanachimwire Mzimu
11-13. Kodi Mfumu Davide inachita tchimo lotani ndi Bateseba, ndipo kodi njira imene Mulungu anaweruzira mlandu wawo ingatonthoze bwanji mtima wathu?
11 Nthawi zina, Akhristu amene aulula machimo awo aakulu ndi kulandira thandizo lauzimu kwa akulu mumpingo, angakhalebe ndi nkhawa chifukwa cholakwira malamulo a Mulungu. (Yakobe 5:14) Ngati ifeyo tikuvutika mwanjira imeneyi, mosakayikira zitithandiza kuona zimene Malemba amanena za anthu amene machimo awo anakhululukidwa.
12 Mfumu Davide inachimwa kwambiri ndi Bateseba, mkazi wa Uriya. Davide ali pa tsindwi la nyumba yake, anaona mkazi wokongola ameneyu akusamba. Kenako analamula kuti amubweretse ku nyumba yake yachifumu ndipo anagona naye. Atauzidwa kuti mkaziyo ali ndi pathupi, anakonza zoti Uriya mwamuna wake, agone naye kuti zisadziwike kuti anachita naye chigololo. Zitakanika, mfumu inakonza zoti Uriya aphedwe ku nkhondo. Ndiyeno, Bateseba anakhala mkazi wa Davide ndipo anamuberekera mwana yemwe kenako anamwalira.—2 Samueli 11:1-27.
13 Yehova anaweruza mlandu wa Davide ndi Bateseba. Iye anakhululukira Davide. Ayenera kuti anatero chifukwa chakuti Davideyo analapa ndiponso anachita naye pangano la Ufumu. (2 Samueli 7:11-16; 12:7-14) Bateseba nayenso ayenera kuti anali ndi mtima wolapa, chifukwa chakuti anadzapatsidwa mwayi wokhala mayi a Mfumu Solomo ndiponso kholo la Yesu Khristu. (Mateyo 1:1, 6, 16) Tikalakwa, ndi bwino kukumbukira kuti Yehova amaona mtima wathu wolapa.
14. Kodi nkhani ya Mfumu Manase imasonyeza bwanji kuti Mulungu amakhululuka kwambiri?
14 Nkhani ya Mfumu Manase ya ku Yuda imasonyezanso kuti Yehova amakhululuka kwambiri. Manase anachita zinthu zoipa pamaso pa Yehova. Anamangira Baala maguwa a nsembe, analambira “khamu lonse la kuthambo,” ndipo anamangiranso milungu yonama maguwa a nsembe m’mabwalo awiri a m’kachisi. Anapititsa ana ake pamoto, analimbikitsa zamizimu, ndipo analakwitsa anthu a ku Yuda ndi Yerusalemu kuti ‘achite choipa koposa amitundu, amene Yehova anawawononga pamaso pa ana a Israyeli.’ Sanamvere machenjezo a aneneri a Mulungu. Mapeto ake, mfumu ya Asuri inamugwira ndi kupita naye kuukapolo. Ali ku ukapolo, Manase analapa ndipo ankapemphera modzichepetsa kwa Mulungu. Mulungu anamukhululukira ndipo anamubwezeretsa pa ufumu wake ku Yerusalemu, kumene analimbikitsa kulambira koona.—2 Mbiri 33:2-17.
15. Kodi ndi nkhani iti pamoyo wa mtumwi Petulo imene imasonyeza kuti Yehova amakhululuka “koposa”?
15 Patapita zaka mazana ambiri, mtumwi Petulo anachimwa kwambiri pokana Yesu. (Maliko 14:30, 66-72) Komabe, Yehova anakhululukira Petulo “koposa.” (Yesaya 55:7) Anatero chifukwa chakuti Petulo analapa ndi mtima wonse. (Luka 22:62) Umboni wosatsutsika wakuti Mulungu anamukhululukira unaoneka patadutsa masiku 50, patsiku la Pentekoste, pamene Petulo anapatsidwa mwayi wolalikira za Yesu molimba mtima. (Machitidwe 2:14-36) Kodi pali chifukwa chilichonse chokayikirira kuti Mulungu angakhululukire Akhristu amene alapadi masiku ano? Wamasalmo anaimba kuti: “Mukasunga mphulupulu, Yehova, adzakhala chilili ndani, Ambuye? Koma kwa Inu kuli chikhululukiro.”—Salmo 130:3, 4.
Kuchotsa Nkhawa Yakuti Tachimwira Mzimu
16. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti Mulungu atikhululukire?
16 Zitsanzo zimene tatchulazi ziyenera kutithandiza kuchotsa nkhawa yakuti tachimwira mzimu woyera. Zikusonyeza kuti Yehova amakhululukiradi anthu olapa. Chofunika kwambiri ndi pemphero lochokera pansi pa mtima. Tikachimwa, tingapemphe kuti Mulungu atikhululukire pa maziko a nsembe ya dipo la Yesu, chifundo cha Yehova, kupanda ungwiro Aefeso 1:7.
kwathu, ndi mbiri yathu ya kukhulupirika. Podziwa kukoma mtima ndi chisomo cha Yehova, timapempha kuti atikhululukire, tikudziwa kuti atiyankha.—17. Kodi tiyenera kuchita chiyani ngati tachimwa ndipo tikufunika thandizo lauzimu?
17 Nanga bwanji ngati tikulephera kupemphera chifukwa chakuti tafooka mwauzimu ndi tchimo lathu? Pankhani imeneyi, wophunzira Yakobe analemba kuti: “[Munthu wotero] aitane akulu a mpingo, ndipo iwo am’pempherere, am’pake mafuta m’dzina la Yehova. Ndipo pemphero la chikhulupiriro lidzachiritsa wodwalayo, ndipo Yehova adzamuutsa. Ndiponso ngati anachita machimo, iye adzakhululukidwa.”—Yakobe 5:14, 15.
18. Kodi n’chifukwa chiyani munthu akachimwa sindiye kuti tchimo lakelo ndi losakhululukidwa ngakhale ngati atachotsedwa mu mpingo?
18 Ngakhale ngati munthu wochimwa ali wosalapa panthawi imene akumuthandiza ndipo wachotsedwa mu mpingo, sindiye kuti tchimo lakelo ndi losakhululukidwa. Ponena za munthu wodzozedwa amene anachotsedwa mu mpingo wa ku Korinto, Paulo analemba kuti: “Chidzudzulo choperekedwa ndi anthu ambiri chimenechi n’chokwanira kwa munthu ameneyu. M’malo mwake tsopano, m’khululukireni ndi mtima wonse ndi kum’tonthoza, kuopera kuti mwina wotereyu angamezedwe kotheratu ndi chisoni chake chopitirira malire.” (2 Akorinto 2:6-8; 1 Akorinto 5:1-5) Komabe, kuti achire mwauzimu, anthu ochimwa afunikira kulandira thandizo la m’Baibulo loperekedwa ndi akulu mumpingo ndipo afunikira kusonyeza kuti alapadi. Ayenera ‘kubala zipatso zosonyeza kulapa.’—Luka 3:8.
19. Kodi ndi chiyani chingatithandize kukhala “olimba m’chikhulupiriro”?
19 Kodi ndi chiyani chingachititse munthu kuganiza kuti wachimwira mzimu woyera? Chimene chingachititse ndi mtima wodziimba mlandu mopitirira malire ndi thanzi lofooka. Ngati ndi choncho, ndi bwino kupemphera ndi kupuma mokwanira. Tisalole Satana kutifooketsa kuti tileke kutumikira Mulungu. Popeza kuti Yehova sasangalala ndi imfa ya munthu woipa, sasangalalanso munthu akasiya kumutumikira. Choncho ngati tikuopa kuti tachimwira mzimu woyera, tiyenera kupitiriza kuwerenga Mawu a Mulungu, makamaka malemba otonthoza monga Masalmo. Tiyenera kupitirizabe kusonkhana ndi kulalikira za Ufumu. Kuchita zimenezi kungatithandize kukhala “olimba m’chikhulupiriro” ndi kupewa nkhawa yakuti mwina tachita tchimo losakhululukidwa.—Tito 2:2.
20. Kodi ndi mafunso ati amene angathandize munthu kuona kuti sanachimwire mzimu woyera?
20 Aliyense amene akuopa kuti wachimwira mzimu woyera ayenera kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndanyoza mzimu woyera? Kuchokera pamene ndinalapa tchimo langa, kodi ndasintha maganizo anga ndi kukhalanso wosalapa? Kodi ndikukhulupirira kuti Mulungu amakhululuka? Kodi ndine wampatuko amene wakana kuwala kwauzimu?’ Mafunso amenewa angathandize munthu kuzindikira kuti sananyoze mzimu woyera, ndipo si wampatuko. Munthuyo angakhale wolapa, ndipo angamakhulupirire kuti Yehova ndi wokhululuka. Ngati ali wotere, ndiye kuti sanachimwire mzimu woyera wa Yehova.
21. Kodi nkhani yotsatira idzayankha mafunso otani?
21 N’zosangalatsadi kuzindikira kuti sitinachimwire mzimu woyera. Komabe, pali mafunso ena okhudza mzimu woyera amene tidzakambirana m’nkhani yotsatira. Mwachitsanzo, tingadzifunse kuti: ‘Kodi mzimu woyera ukunditsogoleradi ineyo? Kodi zipatso zake zimaonekera pa moyo wanga?’
Kodi Mungayankhe Bwanji?
• Kodi n’chifukwa chiyani tinganene kuti ndi zotheka kuchimwira mzimu woyera?
• Kodi kulapa kumatanthauza chiyani?
• Kodi ndani anachimwira mzimu Yesu ali pa dziko lapansi?
• Kodi nkhawa yakuti tachita tchimo losakhululukidwa tingaithetse bwanji?
[Mafunso]
[Chithunzi patsamba 17]
Anthu amene ananena kuti Yesu anachita zozizwitsa ndi mphamvu ya Satana anachimwira mzimu woyera
[Chithunzi patsamba 18]
Ngakhale kuti anakana Yesu, Petulo sanachite tchimo losakhululukidwa