‘Ndiyeseni, Yehova’
‘Ndiyeseni, Yehova’
‘YEHOVA amayesa mitima.’ (Miyambo 17:3) Zimenezi ziyenera kutilimbikitsa kwambiri tonsefe. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa chakuti mosiyana ndi anthufe, amene timaweruza makamaka mwa zooneka ndi maso, Atate wathu wakumwamba ‘amayang’ana mumtima.’—1 Samueli 16:7.
Ndipotu, ngakhale eniakefe sitingadziwe bwinobwino zolinga zathu zenizeni ndiponso maganizo a pansi pamtima wathu. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti “mtima [wathu] ndiwo wonyenga koposa, ndi wosachiritsika,” ndipo palibe angathe kuudziwa. Koma Mulungu yekha amaudziwa, chifukwa iye anati: “Ine Yehova ndisanthula mtima, ndiyesa impso.” (Yeremiya 17:9, 10) Inde, Yehova amadziwa bwino “mtima” wathu, kuphatikizapo zolinga zathu, komanso “impso” zathu, kutanthauza maganizo a pansi pamtima wathu.
N’chifukwa Chiyani Akhristu Amayesedwa?
Ndiyetu n’zosadabwitsa kuti kalekale, Mfumu Davide inapempha Mulungu kuti: “Mundiyesere, Yehova, ndipo mundisunthe; yeretsani impso zanga ndi mtima wanga.” (Salmo 26:2) Kodi Davide anali wangwiro pa zochita ndi zolankhula zake, moti sankaopa kuyesedwa ndi Yehova? N’zodziwikiratu kuti mofanana ndi tonsefe, Davide anali wopanda ungwiro ndipo sankatha kutsatira mfundo za Mulungu popanda kuphonyetsako chilichonse. Chifukwa cha zofooka zake, Davide anachita machimo akuluakulu angapo, komabe iye ‘anayenda ndi mtima wowona.’ (1 Mafumu 9:4) Motani? Anatero mwa kulola kudzudzulidwa ndi kusintha zochita zake. Mwa kuchita zimenezi, iye anasonyeza kuti ankakondadi Yehova, ndipo anali wodzipereka ndi mtima wonse kwa Iye.
Nanga bwanji ifeyo masiku ano? Yehova amadziwa kuti ndife opanda ungwiro ndipo tingathe kuchimwa m’zolankhula ndi zochita zathu. Koma ngakhale kuti iye angathe kudziwiratu tsogolo lathu, sikuti amalemberatu mmene moyo wa munthu udzakhalire. Iye, mwa kukoma mtima kwake, anatilenga ndi ufulu wotha kusankha zochita, ndipo satikakamiza kusankha zimene iyeyo akufuna.
Komabe, nthawi zina Yehova amayesa umunthu wathu ndiponso zolinga zathu. Iye angachite zimenezi mwa kulola zochitika kapena mavuto ena kuti zisonyeze maganizo ndi zolinga zathu. Zimenezi zimatipatsa mwayi wosonyeza kudzipereka ndi kukhulupirika kwathu kwa Yehova. Mayesero amene Yehova amalola, angasonyeze kulimba kwa chikhulupiriro chathu. Angaonetse ngati tili “okwanira ndi opanda chilema m’mbali zonse, osaperewera kanthu.”—Yakobe 1:2-4.
Nkhani ya Mmene Chikhulupiriro Chinayesedwera Kalekale
Chikhulupiriro ndi zolinga za atumiki a Yehova zakhala zikuyesedwa kuyambira kalekale. Taganizirani za Abulahamu. Baibulo limati: “Mulungu anamuyesa Abulahamu.” (Genesis 22:1) Pamene mawu amenewa ananenedwa, n’kuti chikhulupiriro cha Abulahamu mwa Mulungu chitayesedwa kale. Zaka zambiri mawuwa asananenedwe, Yehova anauza Abulahamu kuti achoke mu mzinda wotukuka wa Uri ndi banja lake, n’kupita ku dziko lina lomwe iye sankalidziwa. (Genesis 11:31; Machitidwe 7:2-4) Abulahamu, yemwe n’kutheka kuti anali ndi nyumba yakeyake ku Uri, sanagule malo akeake ku Kanani, komwe anakhalako zaka zambiri. (Aheberi 11:9) Popeza Abulahamu anali munthu woyendayenda, n’kutheka kuti iye ndi banja lake akanavutika ndi njala, ndiponso kuvutitsidwa ndi achifwamba, ngakhalenso olamulira achikunja a m’dera lomwe anakakhala. Nthawi yonseyi, chikhulupiriro cha Abulahamu chinaoneka kuti chinali cholimba kwambiri.
Kenako Yehova anapatsa Abulahamu mayeso ovuta kwambiri. Iye anati: “Tengatu mwana wako, wamwamuna wayekhayo, Isaki, amene ukondana naye, . . . num’pereke iye . . . nsembe yopsereza.” (Genesis 22:2) Kwa Abulahamu, Isaki sanali mwana wamba. Iye anali mwana mmodzi yekha amene anabereka ndi mkazi wake Sara ndipo anali mwana wolonjezedwa. Malingana ndi lonjezo la Mulungu, Abulahamu ankayembekezera kuti chifukwa cha mwana ameneyu “mbewu” yake idzalandira dziko la Kanani ndipo anthu ambiri adzadalitsidwa. Ndipotu, Isaki anali mwana amene Abulahamu ankayembekezeka kukhala naye ndipo anabadwa Mulungu atapanga chozizwitsa.—Genesis 15:2-4, 7.
Mungathe kuona mmene zinalili zovuta kwa Abulahamu kumvetsa tanthauzo la lamulo limeneli. Kodi Yehova ankafuna nsembe ya munthu? N’chifukwa chiyani Yehova analola kuti Abulahamu akhale ndi mwana atakalamba kale, kenako n’kumuuza kuti apereke nsembe mwana yemweyo? *
Abulahamu anamvera lamuloli mosanyinyirika ngakhale kuti sanamvetse bwinobwino mayankho a mafunso amenewa. Ulendo wopita ku phiri lomwe linasankhidwa unam’tengera masiku atatu. Paphiripo anamangapo guwa la nsembe n’kuika nkhuni pamwamba pake. Pachimake pa mayesowo Abulahamu anatenga mpeni, koma atangotsala pang’ono kupha mwana wakeyo, Yehova kudzera mwa mngelo anamuletsa, n’kumuuza kuti: “Tsopano ndidziwa kuti iwe umuopa Mulungu, pakuti sunandikanize ine mwana wako, mwana wako wayekha.” (Genesis 22:3, 11, 12) Taganizirani mmene Abulahamu anasangalalira ndi mawu amenewo. Maganizo a Yehova pa chikhulupiriro cha Abulahamu anali olondola. (Genesis 15:5, 6) Zitatero, Abulahamu anapereka nsembe nkhosa yamphongo, m’malo mwa Isaki. Kenako Yehova anatsimikizira lonjezo la pangano lonena za mbewu ya Abulahamu. M’pake kuti Abulahamu anayamba kudziwika kuti ndi bwenzi la Yehova.—Genesis 22:13-18; Yakobe 2:21-23.
Chikhulupiriro Chathunso Chimayesedwa
Tonsefe timadziwa kuti masiku ano atumiki onse a Mulungu sangapewe mayesero. Komabe mayesero amene timakumana nawo amakhala amene Yehova walola kuti achitike osati zimene iye angatiuze kuti tichite.
Mtumwi Paulo analemba kuti: “Onse ofuna kukhala ndi moyo wodzipereka kwa Mulungu mwa Khristu Yesu, nawonso adzazunzidwa.” (2 Timoteyo 3:12) Akhristu angazunzidwe ndi ophunzira nawo sukulu, anzawo, achibale, oyandikana nawo nyumba kapenanso akuluakulu aboma amene auzidwa zonama. Kuzunzidwa kumeneku kungaphatikizepo kunenedwa mawu achipongwe, kumenyedwa kapenanso kuwasokonezera njira yopezera zofunika pamoyo. Akhristu oona amakumananso ndi mavuto amene anthu ena onse amakumana nawo, monga matenda, kukhumudwa ndi kuchitiridwa chinyengo. Mavuto onsewa amayesa chikhulupiriro cha munthu.
Mtumwi Petulo anafotokoza za ubwino woyesedwa chikhulupiriro. Iye anati: “Mayesero amitundumitundu akukuchititsani chisoni, kuti chikhulupiriro chanu choyesedwa, chimene chili chamtengo wapatali kuposa golide amene amawonongekabe ngakhale kuti anadutsa m’moto, chidzakhale chifukwa cha kutamandidwa kwanu, ulemerero, ndi ulemu pa vumbulutso la Yesu Khristu.” (1 Petulo 1:6, 7) Zoonadi, zimene mayesero amachita pa moyo wa munthu n’zofanana ndi kuyenga golide pamoto. Poyenga golide, zoipa zonse zimachoka ndipo pamatsala golide wabwino. N’chimodzimodzinso ndi chikhulupiriro chathu. Tikakumana ndi mayesero, chikhulupiriro chathucho chimakhala ngati chayengedwa.
Mwachitsanzo, pangakhale mavuto chifukwa cha ngozi kapena tsoka lachilengedwe. Koma anthu amene ali ndi chikhulupiriro cholimba sada nkhawa mopitirira muyeso. Amalimbikitsidwa ndi mawu a Yehova akuti: “Mulimonse sindidzakusiyani, ngakhale kukutayani konse.” (Aheberi 13:5) Iwo amapitiriza kuika patsogolo zinthu zauzimu ndipo amakhulupirira kuti Yehova Mulungu adzadalitsa zimene angachite pofuna kupeza zinthu zimene akufunikiradi pamoyo wawo. Chikhulupiriro chawo chimawathandiza kupirira nthawi za mavuto ndiponso sadzivutitsa kwambiri ndi nkhawa zosayenera.
Mfundo yakuti mayesero angasonyeze mbali zina zofooka pa chikhulupiriro chathu ingatithandize ngati pambuyo pa mayeserowo tikuona kufunika koti tikonze mbali zofookazo. Tingachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndingalimbitse bwanji chikhulupiriro changa? Kodi ndiyenera kuwonjezera nthawi yophunzira ndi kusinkhasinkha mozama Mawu a Mulungu? Kodi ndimagwiritsa ntchito mokwanira mwayi wosonkhana ndi okhulupirira anzanga? Kodi ndimadzidalira m’malo mouza Yehova Mulungu nkhawa zanga?’ Komatu, kudziunika mwa njira imeneyi ndi chiyambi chabe.
Kuti munthu alimbitse chikhulupiriro chake angafunike kukulitsa chidwi chophunzira zinthu zauzimu, n’kukhala munthu ‘wolakalaka mkaka wosasukuluka wa mawu.’ (1 Petulo 2:2; Aheberi 5:12-14) Tiyenera kuyesetsa kukhala ngati munthu amene wamasalmo anamufotokoza kuti: “M’chilamulo cha Yehova muli chikondwerero chake; ndipo m’chilamulo chake amalingirira usana ndi usiku.”—Salmo 1:2.
Kuti zimenezi zitheke pamafunika zinthu zambiri, osati kungowerenga Baibulo basi. Ndibwino kuganizira zimene Mawu a Mulungu amatiuza n’kumatsatira malangizo ake. (Yakobe 1:22-25) Tikatero, chikondi chathu pa Mulungu chidzakula, mapemphero athu adzakhala osapita m’mbali ndi ochokera pansi pamtima, ndipo tidzakhala ndi chikhulupiriro cholimba mwa iye.
Phindu la Chikhulupiriro Choyesedwa
Tikazindikira kuti chikhulupiriro n’chofunika kwambiri kuti Mulungu atiyanje, tidzayesetsa kwambiri kuchilimbitsa. Baibulo limatikumbutsa kuti: “Popanda chikhulupiriro n’kosatheka kum’kondweretsa Mulungu. Pakuti amene akum’fikira Mulungu ayenera kukhulupirira kuti iye alikodi, ndi kuti amakhala wopereka mphoto kwa anthu om’funafuna ndi mtima wonse.” (Aheberi 11:6) Choncho maganizo athu ayenera kukhala ngati munthu amene anapempha Yesu kuti: “Limbitsani chikhulupiriro changa!”—Maliko 9:24.
Kuyesedwa kwa chikhulupiriro chathu kungalimbikitsenso anthu ena. Mwachitsanzo, pamene wokondedwa wa Mkhristu wina wamwalira, chikhulupiriro chake cholimba m’malonjezo a Mulungu akuti akufa adzauka chimamulimbikitsa. Mkhristuyo amalira, koma ‘sachita chisoni mofanana ndi mmene onse opanda chiyembekezo amachitira.’ (1 Atesalonika 4:13, 14) Anthu ena akaona mmene chikhulupiriro cha Mkhristuyo chamulimbikitsira, angazindikire kuti iye akudziwadi zinthu zofunika kwambiri. Zimenezi zingawapatse chidwi chofuna kukhala ndi chikhulupiriro changati chimenechi, ndipo angafune kuphunzira Mawu a Mulungu n’kukhala ophunzira a Yesu Khristu.
Yehova amadziwa kuti chikhulupiriro choyesedwa n’chopindulitsa kwambiri. Mayesero a chikhulupiriro chathu angatithandizenso kuona ngati chikhulupiriro chathucho chilidi champhamvu. Mayeserowo amatithandiza kudziwa ngati chikhulupiriro chathu n’chofooka, n’kuona mmene tingachilimbitsire. Pomaliza, kupirira mayesero mokhulupirika kungathandize ena kukhala ophunzira a Yesu. Choncho tiyeni tiyesetse kukhalabe ndi chikhulupiriro champhamvu, chimene pambuyo poti chayesedwa m’njira zosiyanasiyana ‘chidzakhale chifukwa cha kutamandidwa kwathu, ulemerero, ndi ulemu pa vumbulutso la Yesu Khristu.’—1 Petulo 1:7.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 11 Tanthauzo lophiphiritsa la “nsembe” ya Isaki mungalipeze mu Nsanja ya Olonda ya July 1, 1989, tsamba 22.
[Chithunzi patsamba 13]
Ntchito za Abulahamu zosonyeza chikhulupiriro zinapangitsa kuti akhale bwenzi la Yehova
[Zithunzi patsamba 15]
Mayesero angasonyeze ngati chikhulupiriro chathu chilidi champhamvu
[Mawu a Chithunzi patsamba 12]
From the Illustrated Edition of the Holy Scriptures, by Cassell, Petter, & Galpin