N’zotheka Kupirira Zinthu Zopanda Chilungamo
N’zotheka Kupirira Zinthu Zopanda Chilungamo
KODI ndani wa ife amene sanayambe wachitiridwapo zinthu zopanda chilungamo? Ngakhale kuti munthu angathe kungoganizira kuti wachitiridwa zinthu zopanda chilungamo, koma nthawi zina zimakhala zenizeni.
Ena akatichitira zinthu zopanda chilungamo, mtima umatiwawa ndipo nthawi zina zingathe kusokoneza ubwenzi wathu ndi Mulungu. Mwina tingafunitsitse kukonza zimene zalakwikazo. Chifukwa chiyani? Chifukwa chimodzi n’chakuti Mlengi wathu, Yehova Mulungu, yemwe “ndi wopanda chisalungamo,” anapatsa anthu mtima wokonda chilungamo. (Deuteronomo 32:4; Genesis 1:26) Koma nthawi zina pangachitike zinthu zimene tingaone kuti n’zopanda chilungamo. Munthu wina wanzeru anati: “Ndinabweranso tsono ndi kupenyera nsautso zonse zimachitidwa kunja kuno; ndipo taona, misozi ya otsenderezedwa, koma analibe wakuwatonthoza; ndipo akuwatsendereza anali ndi mphamvu koma iwowa analibe wakuwatonthoza.” (Mlaliki 4:1) Ndiyeno tingatani ngati tachitiridwa zinthu zopanda chilungamo?
Kodi Kuchita Zinthu Zopanda Chilungamo N’kutani?
Kupanda chilungamo ndi kuchita zinthu mosatsatira mfundo zolungama. Kodi n’kuti kumene anthu angapeze mfundo zachilungamo? N’zodziwikiratu kuti Mlengi wathu, yemwe ndi wolungama ndiponso wosasintha, ali ndi ufulu wotisonyeza mfundo zolungama ndi zosalungama. Kwa iyeyo, kuyenda “m’malemba a moyo” kumaphatikizapo ‘kusachita chosalungama.’ (Ezekieli 33:15) Motero, Yehova atalenga munthu woyamba, anam’patsa chikumbumtima, chomwe ndi mphamvu yachibadwa yom’thandiza kuzindikira cholungama ndi chosalungama. (Aroma 2:14, 15) Kuwonjezera pamenepo, m’Mawu ake Baibulo, Yehova anafotokozamo mfundo zothandiza kuzindikira cholungama kapena chosalungama.
Koma bwanji ngati tikuona kuti tachitiridwa zinthu zopanda chilungamo? Zikatero tingachite bwino kuiganizira mofatsa nkhaniyo kuti tione ngati tachitiridwadi zinthu zopanda chilungamo. Mwachitsanzo, taonani zimene zinachitikira mneneri wachiheberi, Yona. Yehova anam’tuma kuti akachenjeze anthu a ku Nineve za tsoka limene anthuwo anatsala pang’ono kukumana nalo. Poyamba, Yona anathawa ntchito imene anapatsidwayo. Koma kenako anapita ku Nineve ndi kukachenjeza anthu a mu mzindawo za tsokalo. Anthuwo atalabadira chenjezolo, Yehova anakonza zoti asawononge mzindawo. Kodi Yona anamva bwanji ndi zimenezi? Baibulo limati: “Sikudakomera Yona konse, ndipo anapsa mtima.” (Yona 4:1) Iye anaganiza kuti Yehova sanachite chilungamo m’pang’ono pomwe.
N’zodziwikiratu kuti Yehova, amene amatha kuona za mumtima ndiponso ‘amakonda chilungamo ndi chiweruzo,’ sanalakwitse chilichonse pankhaniyi. (Salmo 33:5) Yona anafunika kungodziwa kuti maganizo a Yehova pankhaniyi anali olungama. Ngati tikuganiza kuti tachitiridwa zinthu zopanda chilungamo, tingadzifunse kuti, ‘Kodi zingatheke kuti Yehova akuona nkhaniyi mosiyana ndi mmene ine ndikuionera?’
Kuchitiridwa Zinthu Zopanda Chilungamo
Baibulo lili ndi nkhani zambiri za anthu amene anachitiridwapo zinthu zopanda chilungamo. Tingaphunzire zambiri mwa kuona zimene anthuwo anachita atakumana ndi mavuto awowo. Taganizirani za Yosefe, amene abale ake ansanje anam’gulitsa n’kukakhala kapolo ku Iguputo. Ali ku Iguputo, mkazi wa mbuye wake anayesa kum’kopa Yosefe kuti agone naye, ndipo atakanidwa, mkaziyo ananamizira Yosefe kuti amafuna kum’gwiririra. Chifukwa cha zimenezi Yosefe anaponyedwa m’ndende. Komabe, iye anali ndi chikhulupiriro cholimba kuposa unyolo umene anam’manga nawo m’ndendemo. Iye sanalole kuti zinthu zopanda chilungamo zimene anthu anam’chitira zim’fooketse mwauzimu kapena kuti asiye kum’dalira kwambiri Yehova.—Genesis 37:18-28; 39:4-20; Salmo 105:17-19.
Munthu wina amene anachitiridwa zinthu zopanda chilungamo anali Naboti. Iye anachitiridwa chiwembu ndi Yezebeli, mkazi wa Mfumu Ahabu ya Isiraeli. Mfumu Ahabu inkafunitsitsa kwambiri malo akufupi ndi nyumba yake, omwe anali cholowa cha Naboti. Popeza kuti Mwisiraeli sankaloledwa kupatsa munthu wina cholowa chake, Naboti anakana pempho la mfumuyo loti igule malowo. (Levitiko 25:23) Zitatero, mkazi woipa wa Ahabu anapeza anthu oti apereke umboni wonama wakuti Naboti wanyoza Mulungu ndiponso mfumu. Motero Naboti ndi ana ake aamuna anaphedwa. Taganizirani mmene Naboti anamvera pamene anthu ankanyamula miyala kuti amuphe nayo.—1 Mafumu 21:1-14; 2 Mafumu 9:26.
Komatu zitsanzo tatchulazi sizingafanane n’komwe ndi zinthu zopanda chilungamo zimene anthu anachitira Khristu Yesu. Pachigamulo choti aphedwe, anthu anagwiritsa ntchito mabodza ndiponso anam’zenga mlandu mosatsatira malamulo. Bwanamkubwa wachiroma amene ankaweruza mlanduwo sanalimbe mtima n’kuweruza mwachilungamo. (Yohane 18:38-40) Zoonadi, Satana anachitira Khristu Yesu zinthu zopanda chilungamo zoipitsitsa, kuposa munthu wina aliyense.
Yesaya 55:8, 9) Yosefe anapulumutsa anthu a m’banja lake, chifukwa choti anagulitsidwa n’kukakhala kapolo. Iye anakhala woyang’anira chakudya ku Iguputo njala yaikulu yomwe inakhudza banja lake isanagwe. Yehova akanapanda kulola kuti Yosefe achitiridwe zinthu zopanda chilungamo, iye sakanapezeka kundende. Kundendeko n’kumene anamasulira maloto a akaidi ena awiri, ndipo pambuyo pake mmodzi wa akaidiwo anadzafotokozera Farao za Yosefe, ndipo zimenezo n’zimene zinathandiza kuti Yosefe akhale woyang’anira chakudya.—Genesis 40:1; 41:9-14; 45:4-8.
Kodi zochitika zimenezi zikusonyeza kuti Yehova sasamala anthu akamachitiridwa zinthu zopanda chilungamo? Ayi. Yehova sanaone zochitikazi ngati mmene anthu angazionere. (Nanga bwanji za Naboti? Pankhani iyinso, tayesani kuiona ngati mmene Yehova anaionera. M’maganizo a Yehova, amene angathe kuukitsa akufa, Naboti anali moyo, ngakhale pamene mtembo wake unali kwala pansi. (1 Mafumu 21:19; Luka 20:37, 38) Panopa, Naboti akudikirira nthawi imene Yehova adzamuukitse, koma nthawi yonse imene yadutsayi sikuti ndi yaikulu kwa Naboti, chifukwa akufa sadziwa kalikonse. (Mlaliki 9:5) Komanso, Yehova anabwezera zinthu zopanda chilungamo zimene Ahabu anachitira Naboti, mwa kulanga Ahabu ndi banja lake lonse.—2 Mafumu 9:21, 24, 26, 35, 36; 10:1-11; Yohane 5:28, 29.
Pankhani ya Yesu, n’zoona kuti iye anafa. Koma Mulungu anamuukitsa n’kum’patsa udindo wapamwamba “kuposa boma lililonse, ulamuliro uliwonse, amphamvu onse, azimbuye onse, ndi dzina lililonse loperekedwa kwa wina aliyense.” (Aefeso 1:20, 21) Zinthu zopanda chilungamo zimene Satana anachitira Khristu Yesu sizinalepheretse Yehova kupatsa mphoto Mwana wakeyo. Yesu anali ndi chikhulupiriro chakuti Yehova atafuna angathe kum’pulumutsa nthawi yomweyo pa mlandu wopanda chilungamowo. Komabe, Khristu ankadziwanso kuti Yehova ali ndi nthawi yokwaniritsira Malemba ndiponso yothetsera zinthu zonse zopanda chilungamo.
N’zoona kuti Satana ndi omutsatira ake akhala akuchitira anthu olungama zinthu zopanda chilungamo, koma m’kupita kwa nthawi Yehova wakhala akukonza zinthu ndipo adzateronso m’tsogolo muno. Choncho, pa chinthu chilichonse chimene anthu atichitira mopanda chilungamo, tiyenera kudalira Mulungu kuti ndiye adzakonze zinthu.—Deuteronomo 25:16; Aroma 12:17-19.
Chifukwa Chimene Yehova Angalolere Kuti Anthu Atichitire Zinthu Zopanda Chilungamo
Yehova angakhale ndi zifukwa zosakonzera vuto linalake. Monga mbali ya maphunziro achikhristu, iye angalole kuti anthu atichitire zinthu zopanda chilungamo. N’zoona kuti ‘Mulungu sayesa [munthu] ndi zoipa.’ (Yakobe 1:13) Komabe, iye angalole kuti vuto linalake lichitike, ndipo anthu amene amaphunzirapo kanthu akachitiridwa zinthu zopanda chilungamo iye angawalimbikitse. Baibulo limatitsimikizira kuti: “Mutavutika kanthawi, Mulungu wa kukoma mtima konse kwa m’chisomo . . . iye mwiniyo adzamalizitsa kwatsalaku m’kuphunzitsidwa kwanu; adzakulimbitsani, adzakupatsani mphamvu.”—1 Petulo 5:10.
Komanso, Yehova akalola kuti anthu atichitire zinthu zopanda chilungamo, zingawapatse mpata anthuwo woti alape. Patangotha milungu ingapo Yesu ataphedwa, Ayuda ena amene anamvetsera malangizo a Petulo “analasidwa nawo mtima.” Ayuda amenewa analabadira mawu a Mulungu n’kubatizidwa.—Machitidwe 2:36-42.
N’zoona kuti si anthu onse ochita zinthu zopanda chilungamo amene angalape. Ena mwina angapitirize kuchita zinthu zoipa kwambiri. Koma lemba la Miyambo 29:1 limati: “Yemwe aumitsa khosi atadzudzulidwa kwambiri, adzasweka modzidzimuka, palibe chom’chiritsa.” Inde, Yehova m’tsogolo muno adzalanga anthu amene sakusiya makhalidwe oipa.—Mlaliki 8:11-13.
Zilibe kanthu kuti zingatitengere nthawi yaitali motani kuti tiiwale zinthu zopanda chilungamo zimene anthu atichitira, koma tisakayikire kuti Yehova akudziwa mmene angatithandizire pavuto lathulo. Ndipo iye adzathetsa zinthu zonse zopanda chilungamo zimene anthu angatichitire m’dongosolo lino la zinthu. Komanso, anatilonjeza mphoto yaikulu kwambiri, imene ndi moyo wosatha m’dziko latsopano momwe “mudzakhala chilungamo.”—2 Petulo 3:13.
[Chithunzi pamasamba 16, 17]
Mukuganiza kuti Naboti anamva bwanji anthu akum’chitira zinthu zopanda chilungamo m’pang’ono pomwe?