Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mfundo Zazikulu za M’buku la Danieli

Mfundo Zazikulu za M’buku la Danieli

Mawu a Yehova Ndi Amoyo

Mfundo Zazikulu za M’buku la Danieli

BUKU lina lotanthauzira mawu a m’Baibulo (Holman Illustrated Bible Dictionary) limati: “Buku la Danieli lili m’gulu la mabuku ochititsa chidwi kwambiri m’Baibulo. M’bukuli muli choonadi chosasintha.” Nkhani zimene zili m’buku la Danieli zinayamba kuchitika mu 618 B.C.E., pamene Mfumu Nebukadinezara ya ku Babulo inafika ku Yerusalemu ndi kuzungulira mzindawo, ndipo inagwira ukapolo “ena a ana a Isiraeli,” n’kuwapititsa ku Babulo. (Danieli 1:1-3) Mmodzi wa ana amenewa anali Danieli, ndipo zikuoneka kuti panthawiyi n’kuti adakali mnyamata wosakwanitsa zaka 20. Nkhani yomaliza yolembedwa m’bukuli inachitika Danieli adakali ku Babulo. Panthawiyi, iye anali ndi zaka pafupifupi 100, ndipo Mulungu anamulonjeza kuti: “Udzapumula, nudzaima m’gawo lako masiku otsiriza.”​—Danieli 12:13.

Mbali yoyamba ya buku la Danieli inalembedwa mogwirizana ndi nthawi imene nkhanizo zinachitikira, ndipo zinalembedwa ngati kuti munthu akusimbira mnzake nkhani. Komano mbali yomaliza inalembedwa mosonyeza kuti Danieliyo ndiye akusimba nkhanizo. Bukuli linalembedwa ndi Danieli ndipo analembamo maulosi onena za maufumu olamulira dziko lonse amene adzakhalepo ndi kutha, za kubwera kwa Mesiya, ndiponso za zinthu zimene zikuchitika masiku ano. * Mneneri wokalambayo analembanso nkhani yofotokoza zochitika pazaka zambiri za moyo wake ndipo anasimba nkhani zimene zimatilimbikitsa kulambira Mulungu mokhulupirika. Uthenga wa m’buku la Danieli ndi wamoyo ndiponso wamphamvu.​—Aheberi 4:12.

KODI MBALI YOYAMBA YA BUKULI IKUTIPHUNZITSA CHIYANI?

(Danieli 1:1–6:28)

Chinali chaka cha 617 B.C.E. ndipo Danieli ndi anyamata anzake atatu, Sadrake, Mesaki, ndi Abedinego anali m’nyumba ya mfumu ya ku Babulo. Pazaka zonse zitatu zimene anali kuphunzira m’nyumba ya mfumu, anyamatawa anakhalabe okhulupirika kwa Mulungu. Patatha zaka 8, Mfumu Nebukadinezara analota maloto ovutitsa maganizo. Danieli anatchula malotowo kenaka n’kuwamasulira. Motero mfumuyo inafika povomereza kuti Yehova ndi “Mulungu wa milungu, ndi Mbuye wa mafumu, ndi wovumbulutsa zinsinsi.” (Danieli 2:47) Koma posakhalitsa, zikuoneka kuti Nebukadinezara anaiwala mfundo imeneyi. Tikutero chifukwa choti anzake atatu a Danieli atakana kulambira fano, mfumuyi inalamula kuti aponyedwe m’ng’anjo ya moto. Mulungu woona anapulumutsa anthu atatuwo, ndipo Nebukadinezara sakanachitira mwina koma kuvomereza kuti “palibe mulungu wina akhoza kulanditsa motero.”​—Danieli 3:29.

Nebukadinezara analotanso maloto ena okhala ndi tanthauzo lapadera. Iye anaona mtengo waukulu, umene unadulidwa ndipo chitsa chake anachimanga ndi mkombero wachitsulo kuti mtengowo usaphukire. Danieli anafotokoza tanthauzo la malotowo. Mbali ya malotowo inakwaniritsidwa pamene Nebukadinezara anapenga kenaka n’kukhalanso bwino. Patatha zaka zambiri, Mfumu Belisazara anakonza phwando lalikulu n’kuitana akuluakulu a muufumu wake. Iye anachitira Mulungu mwano pogwiritsa ntchito ziwiya zomwe zinatengedwa m’kachisi wa Yehova. Usiku womwewo, Belisazara anaphedwa ndipo Dariyo Mmedi anakhala mfumu. (Danieli 5:30, 31) M’masiku a Dariyo, Danieli anali ndi zaka zoposa 90. Komabe akuluakulu ena anakonza chiwembu choti aphe mneneri wokalambayu. Koma Yehova anam’pulumutsa “ku mphamvu ya mikango.”​—Danieli 6:27.

Kuyankha Mafunso a M’Malemba:

1:11-15—Kodi kudya zakudya zamasamba n’kumene kunachititsa kuti anyamata achiyudawo azioneka bwino? Ayi. Palibe chakudya chimene chingasinthe munthu pa masiku 10 okha. Motero Yehova ndiye anachititsa kuti anyamatawa azioneka bwino ndipo anawadalitsa m’njira imeneyi chifukwa cha kukhulupirika kwawo.​—Miyambo 10:22.

2:1—Kodi Nebukadinezara analota liti za fano lalikulu? Nkhani ya m’bukumu imanena kuti munali mu “chaka chachiwiri cha Nebukadinezara mfumu.” Nebukadinezara anakhala mfumu mu 624 B.C.E. Motero chaka chachiwiri cha ulamuliro wake chinayamba mu 623 B.C.E., patatsala zaka zambiri kuti agonjetse Yuda. N’chifukwa chake zili zodziwikiratu kuti Danieli sakanakhala ali ku Babulo panthawiyi n’kumamasulira maloto aja. Zikuoneka kuti “chaka chachiwiri” chimenechi chinali chaka chachiwiri kuchokera mu 607 B.C.E., pamene ufumu wa Babulo unawononga Yerusalemu n’kukhala ufumu wolamulira dziko lonse lapansi.

2:32, 39—Kodi akutanthauzanji ponena kuti ufumu wa siliva unali wochepa pouyerekezera ndi mutu wa golidi, ndiponso kuti ufumu wa mkuwa unali wochepa pouyerekezera ndi wa siliva? Mbali ya siliva ya fanolo inkaimira ufumu wa Amedi ndi Aperisi womwe unali wochepa pouyerekezera ndi wa Babulo, womwe unaimiridwa ndi mutu wa golidi. Ufumu wa Amedi ndi Aperisi unali wochepa chifukwa choti si ndiwo unagonjetsa Yuda. Ufumu umene unabwera pambuyo pa ufumu wa Amedi ndi Aperisi unali wa Girisi, womwe unaimiridwa ndi mkuwa. Ufumuwu unali wochepa kuuyerekezera ndi wa Amedi ndi Aperisi, monga mmenenso mkuwa ulili mwala wamtengo wochepa pouyerekezera ndi siliva. Ngakhale kuti ufumu wa Agiriki unali waukulu zedi, ufumuwu sunakhale ndi mwayi womasula anthu a Mulungu kuukapolo monga anachitira Amedi ndi Aperisi.

4:10, 11, 20-22—Kodi mtengo waukulu womwe Nebukadinezara analota unkaimira chiyani? Poyamba mtengowo unkaimira Nebukadinezara monga mfumu ya ufumu wolamulira dziko lonse lapansi. Komabe, mtengowo unaimiranso chinthu china chachikulu kwambiri chifukwa choti ufumu wake unafika ku “chilekezero cha dziko lapansi.” Lemba la Danieli 4:17 limasonyeza kuti pali kugwirizana pakati pa ufumuwo ndi Mulungu “Wam’mwambamwamba.” Zimenezi zikutithandiza kuona kuti mtengowo ukuimiranso ulamuliro wa Yehova m’chilengedwe chonse, makamaka padziko lapansi. Choncho, malotowa anakwaniritsidwa mbali ziwiri. Mbali yoyamba inali yokhudza ufumu wa Nebukadinezara ndipo yachiwiri inali yokhudza ulamuliro wa Yehova.

4:16, 23, 25, 32, 33​—Kodi “nthawi zisanu ndi ziwiri” zinkaimira nthawi yotalika motani? N’zosachita kufunsa kuti panapita nthawi yaitali kuti Mfumu Nebukadinezara asinthiretu maonekedwe ake. Zimenezi zikutanthauza kuti “nthawi zisanu ndi ziwiri” sizinkaimira masiku enieni asanu ndi awiri. Motero, nthawi zimenezi zinkatanthauza zaka zenizeni zisanu ndi ziwiri za masiku 360 chaka chilichonse, kutanthauza kuti masiku 2,520. Pa mbali yachiwiri ya ulosi umenewu, “nthawi zisanu ndi ziwiri” zinkaimira zaka 2,520. (Ezekieli 4:6, 7) Nthawi zimenezi zinayambira mu 607 B.C.E. pamene Yerusalemu anawonongedwa, ndipo zinatha mu 1914 C.E. pamene Yesu anaikidwa kukhala Mfumu kumwamba.​—Luka 21:24.

6:6-10​—Popeza munthu angathe kupemphera atakhala m’njira ina iliyonse yoyenerera, kodi sichikanakhala chinthu chanzeru kuti Danieli azipemphera mobisa kwa masiku 30 aja? Aliyense ankadziwa zoti Danieli ankapemphera katatu patsiku. N’chifukwa chake anthu amene anam’konzera chiwembu anaganiza zoti akhazikitse lamulo loletsa kupempheralo. Motero Danieli akanati asinthe pang’ono chizolowezi chakechi, akanachititsa anthu ena kuona kuti wagonjera ndiponso walephera kutumikira Yehova mokhulupirika.

Zimene Tikuphunzirapo:

1:3-8. Khama la Danieli ndi anzake lofunitsitsa kukhala okhulupirika kwa Yehova limasonyeza kuti anthuwa anaphunzitsidwa bwino kwambiri ndi makolo awo. Makolo oopa Mulungu akamaika zinthu zauzimu patsogolo m’moyo wawo n’kumaphunzitsanso ana awo kuchita chimodzimodzi, m’posavuta kuti anawo athe kulimbana ndi mayesero ndiponso mavuto osiyanasiyana amene angakumane nawo ku sukulu kapena kwina kulikonse.

1:10-12. Danieli anamvetsa chifukwa chimene “mkulu wa adindo” ankaopera mfumu ndipo anasiya kum’pempha mkuluyu kuti akawanenere mawu kwa mfumu. Komabe, pambuyo pake Danieli anapita kwa “kapitawo,” amene mwina akanatha kuvomera mosavuta kuti awathandize. Tikakhala pa vuto linalake, tizichita zinthu monga anachitira Danieli; mwanzeru, momvetsetsana, ndiponso moganizira ena.

2:29, 30. Monga Danieli, nafenso tiziyamikira kwambiri Yehova chifukwa cha zonse zimene timadziwa, makhalidwe athu onse, ndi luso lililonse limene tili nalo chifukwa cha kuphunzitsidwa Baibulo.

3:16-18. N’zokayikitsa kuti Aheberi atatuwo akanachita zinthu molimba mtima chonchi akanakhala kuti anali ndi chizolowezi chodya zinthu zoletsedwa. Nafenso tiziyesetsa kukhala “okhulupirika m’zinthu zonse.”​—1 Timoteyo 3:11.

4:24-27. Polengeza uthenga wa Ufumu, umene umaphatikizapo chilango chimene Mulungu adzapereke, pamafunika kuti tikhale ndi chikhulupiriro ndiponso olimba mtima ngati Danieli. Iye anasonyeza makhalidwe amenewa ponena zimene zichitikire Nebukadinezara ndiponso zimene mfumuyi inayenera kuchita kuti ‘nthawi ya mtendere wake italike.’

5:30, 31. Mawu a ‘m’nyimbo yantchintchi [ya ndakatulo] ya mfumu ya ku Babulo’ anakwaniritsidwa. (Yesaya 14:3, 4, 12-15) Satana Mdyerekezi, amene kunyada kwake kunali kofanana ndi kwa ufumu wa Babulo, adzalangidwanso m’njira yochititsa manyazi yotereyi.​—Danieli 4:30; 5:2-4, 23.

KODI MASOMPHENYA AMENE DANIELI ANAONA AMASONYEZA CHIYANI?

(Danieli 7:1–12:13)

Danieli anaona masomphenya ake oyamba mu 553 B.C.E., ali ndi zaka za m’ma 70. Iye anaona zilombo zinayi zikuluzikulu zimene zinkaimira maufumu amene akhala akulamulira dziko lonse kuyambira nthawi yake mpaka panopo. M’masomphenya iye anaona kumwamba kuli “wina ngati mwana wa munthu” ndipo anapatsidwa “ulamuliro wosatha.” (Danieli 7:13, 14) Patatha zaka ziwiri, Danieli anaona masomphenya okhudza Mediya ndi Perisiya, Girisi, ndiponso ulamuliro wina umene unadzakhala “mfumu ya nkhope yaukali.”​—Danieli 8:23.

M’chaka cha 539 B.C.E., ufumu wa Babulo unagwa, ndipo Dariyo, mfumu ya Amedi anakhala mfumu ya Akasidi. Danieli anapemphera kwa Yehova kuti zinthu zibwerere mwakale kwawo kumene anachokera. Ali m’kati mopemphera, Yehova anatumiza mngelo Gabrieli kuti akathandize Danieli ‘kuzindikira mwaluntha’ za kubwera kwa Mesiya. (Danieli 9:20-25) Ndiyeno chapakati pa chaka cha 536 ndi 535 B.C.E., Ayuda ochepa anabwerera ku Yerusalemu. Koma anthu ena anayamba kulimbana nawo pantchito yawo yomanga kachisi. Zimenezi zinam’vutitsa maganizo kwambiri Danieli. Motero anapemphera za nkhaniyi ndipo Yehova anam’tumizira mngelo waudindo waukulu. Mngeloyo atam’limbikitsa Danieli, anamuuzanso ulosi wonena za kulimbirana mphamvu pakati pa mfumu ya kumpoto ndi mfumu ya kum’mwera. Kulimbana kwa mafumu awiriwa kunayamba pa nthawi imene ufumu wa Alesandro Wamkulu unagawidwa n’kuperekedwa kwa akazembe ake anayi n’kufika pa nthawi imene Kazembe Wamkulu, Mikayeli, “adzauka.”​—Danieli 12:1.

Kuyankha Mafunso a M’Malemba:

8:9—Kodi “dziko lokometsetsa” likuimira chiyani? Pankhani imeneyi “dziko lokometsetsa” likuimira mmene Akhristu odzozedwa alili padziko lapansi panthawi ya ulamuliro wapadziko lonse wa Britain ndi America.

8:25—Kodi “kalonga wa akalonga,” ndani? Mawu achiheberi akuti sar, omwe anawamasulira kuti “kalonga,” kwenikweni amatanthauza kuti “mfumu,” kapena “wamkulu.” Mawu akuti “kalonga wa akalonga” amangonena za Yehova Mulungu basi, yemwe ali Mfumu ya akalonga onse aungelo, kuphatikizapo “Mikaeli, wina wa akalonga omveka.”​—Danieli 10:13.

9:21—N’chifukwa chiyani Danieli anatchula mngelo Gabrieli kuti “munthu”? N’chifukwa choti Gabrieli anaonekera kwa iye monga munthu, monganso anachitira m’mbuyo pamene anaonekera kwa Danieliyo m’masomphenya.​—Danieli 8:15-17.

9:27—Kodi ndi chipangano chotani chimene chinali “cholimba ndi ambiri” mpaka kumapeto kwa mlungu wa chi 70 wa milungu ya zaka, kapena kuti mu 36 C.E.? Chipangano cha chilamulo chinatha mu 33 C.E. pamene Yesu anapachikidwa. Koma powasungirabe Aisiraeliwo pangano limene anapangana ndi Abulahamu mpaka mu 36 C.E., Yehova anawonjezera nthawi imene anayanja mtunduwu mwapadera ndipo anatero chifukwa choti iwowa anali mbadwa za Abulahamu. Pangano la Abulahamu likugwirabe ntchito panopo kwa “Isiraeli wa Mulungu.”​—Agalatiya 3:7-9, 14-18, 29; 6:16.

Zimene Tikuphunzirapo:

9:1-23; 10:11. Chifukwa chakuti Danieli anali wodzichepetsa, wodzipereka kwa Mulungu, wokonda kuphunzira Mawu a Mulungu ndiponso kupemphera, iye anali ‘wokondedwa kwambiri.’ Makhalidwe omwewa ndi amenenso anam’thandiza kukhala wokhulupirika kwa Mulungu mpaka imfa yake. Nafenso tiziyesetsa kutsanzira Danieli.

9:17-19. Ngakhale kuti timapempherera za kubwera kwa dziko latsopano la Mulungu, limene ‘mudzakhale chilungamo,’ mfundo imene tiyenera kuiganizira kwambiri izikhala ya kuyeretsa dzina la Yehova ndi kukweza ulamuliro wake. Tisamaganizire kwambiri za kuthetsa mavuto ndi mikwingwirima imene tikukumana nayo.​—2 Petulo 3:13.

10:9-11, 18, 19. Potsanzira mngelo amene anapita kwa Danieli, ifenso tizilimbikitsana pothandizana zinthu ndi kuuzana mawu olimbikitsa.

12:3. M’masiku otsiriza ano “aphunzitsi,” kutanthauza kuti Akhristu odzozedwa, akhala ‘akuwala monga zounikira,’ ndipo ‘atembenuza ambiri kuti atsate chilungamo,’ kuphatikizapo “khamu lalikulu” la “nkhosa zina.” (Afilipi 2:15; Chivumbulutso 7:9; Yohane 10:16) Panthawi ya Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Khristu m’pamene odzozedwa adzafike pachimake ‘ponyezimira ngati nyenyezi,’ chifukwa adzachita nawo ntchito yopereka madalitso onse a nsembe ya dipo kwa anthu omvera Mulungu padziko lapansi. Anthu a “nkhosa zina” ayenera kukhulupirika kwa odzozedwa, ndi kuwamvera pa chilichonse ndi mtima wawo wonse.

Yehova ‘Amadalitsa Amene Amamuopa’

Kodi buku la Danieli limatiphunzitsa chiyani za Mulungu amene timalambira? Taganizirani maulosi omwe ali m’bukuli amene anakwaniritsidwa kale ndiponso amene akwaniritsidwe m’tsogolo. Maulosi amenewatu amasonyeza momveka bwino kuti Yehova amakwaniritsa mawu ake.​—Yesaya 55:11.

Kodi nkhani za m’buku la Danieli zomwe si maulosi zimatiuza chiyani za Mulungu wathu? Anyamata anayi achiheberi amene anakana kutengera moyo wa anthu a m’nyumba ya mfumu ya ku Babulo “anawapatsa chidziwitso ndi luntha.” (Danieli 1:17) Mulungu woona anatumiza mngelo amene anapulumutsa Sadrake, Mesaki, ndi Abedinego m’ng’anjo ya moto. Danieli nayenso anapulumutsidwa m’dzenje la mikango. Ndithudi, Yehova ‘amathandiza ndi kuteteza anthu amene amamukhulupirira’ ndipo ‘amadalitsa amene amamuopa.’​—Salmo 115:9, 13.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Ngati mukufuna kudziwa tanthauzo la vesi lililonse la m’buku la Danieli, onani buku la Samalani Ulosi wa Danieli! lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Chithunzi patsamba 18]

Kodi n’chifukwa chiyani Danieli anali ‘wokondedwa kwambiri’?