N’chifukwa Chiyani Mulungu Walola Kuti Zoipa Zizichitika?
N’chifukwa Chiyani Mulungu Walola Kuti Zoipa Zizichitika?
SIMUNGACHITE kuyenda mtunda wautali kuti muone zinthu zoipa kapena anthu akuvutika. Asilikali ngakhalenso anthu wamba amafa pa nkhondo. Chiwawa ndi umbanda zili paliponse. Mwina inu mwavutikapo chifukwa cha tsankho ndi kupanda chilungamo. Chifukwa cha zimene mwaona ndi kukumana nazo, muyenera kuti munafunsapo kuti: ‘N’chifukwa chiyani Mulungu walola kuti zoipa zizichitika?’
Anthu sanayambe lero kufunsa funso limeneli. Zaka pafupifupi 3,600 zapitazo, Yobu yemwe anali mtumiki wokhulupirika wa Mulungu, anafunsa kuti: “Oipa akhaliranji ndi moyo?” (Yobu 21:7) Ndiponso zaka pafupifupi 2,600 zapitazo, mneneri Yeremiya, chifukwa chokhumudwa kwambiri ndi zochita za anthu m’dziko lake, anafunsa kuti: “Chifukwa chanji ipindula njira ya oipa? Chifukwa chanji akhala bwino onyengetsa?” (Yeremiya 12:1) Yobu ndi Yeremiya ankadziwa kuti Mulungu ndi wolungama. Koma onsewa anafuna kudziwa chifukwa chake padziko pali zoipa zambiri chonchi. Mwina nanunso zimenezi zimakudabwitsani.
Anthu ena amaganiza kuti Mulungu ndi amene amachititsa zoipa ndiponso kuvutika kwa anthu. Ena amadzifunsa kuti: ‘Ngati Mulungu ali wamphamvu yonse, wolungama ndiponso wachikondi, kodi n’chifukwa chiyani sakuthetsa zoipa ndi kuvutika? N’chifukwa chiyani walola kuti zoipa zizichitika mpaka pano?’ Nkhani yotsatirayi iyankha mafunso amenewa ndiponso mafunso ena ofunika kwambiri.
[Mawu a Chithunzi patsamba 3]
AP Photo/Adam Butler