Zosankha Zimene Zimabweretsa Chisangalalo
Zosankha Zimene Zimabweretsa Chisangalalo
“ZIKANAKHALA bwino ndikanati ndisachite zimenezi.” Kodi munayamba mwadandaulapo chonchi? Tonsefe timafuna kusankha bwino zinthu makamaka zimene zimakhudza kwambiri moyo wathu. Choncho, kodi tingamasankhe bwanji zinthu kuti tikhale osangalala pambuyo pake?
Choyamba, tiyenera kuyendera mfundo zodalirika. Kodi mfundo zotere zilipo? Anthu ambiri amaganiza kuti mfundo zimenezi sizipezeka. Ku United States, achinyamata ambiri amene ali m’chaka chawo chomaliza ku yunivesite atafunsidwa mafunso, atatu pa anayi alionse anati amakhulupirira kuti palibe chabwino ndi choipa. Akuti zimene munthu angaone kuti ndi zabwino kapena zoipa zimadalira zimene “iye amakonda komanso chikhalidwe chake.”
Kodi ndi bwino kuti munthu azingoyendera mfundo zakezake za makhalidwe kapenanso kumangotsatira mfundo zimene anthu ambiri amati n’zabwino? Ayi, si bwino. Ngati anthu angochita zimene akufuna, zotsatirapo zake zingakhale chipwirikiti. Kodi ndani angafune kukhala m’dziko lopanda malamulo, makhoti, kapena apolisi? Ndiponso, nthawi zambiri nzeru za anthu sizidalirika. Titha kusankha zinthu zimene tinaona kuti n’zabwino koma kenako n’kupeza kuti tinalakwitsa. Ndithudi, mbiri yonse ya anthu imasonyeza kuti Baibulo linanena molondola kuti: “Sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.” (Yeremiya 10:23) Choncho, kodi tingapeze kuti malangizo omwe angatithandize posankha zinthu zofunika pamoyo wathu?
Wolamulira wachinyamata yemwe tamutchula m’nkhani yoyamba uja anaganiza bwino kupita kwa Yesu kukapempha malangizo. Monga mmene taonera, Yesu poyankha funso la mnyamatayo anamuuza mfundo za Yohane 7:16) Choncho, tingaone kuti Mawu a Mulungu ndi odalirika ndipo angatithandize kusankha zinthu mwanzeru pamoyo wathu. Tiyeni tione mfundo zingapo za m’Mawu a Mulungu zimene ngati titazigwiritsa ntchito tingakhale osangalala.
m’Chilamulo cha Mulungu. Yesu anadziwa kuti Yehova Mulungu ndiye Gwero la nzeru, amenenso amadziwa zimene zili zoyenera kwa zolengedwa Zake. N’chifukwa chake Yesu ananena kuti: “Zimene ine ndimaphunzitsa si zanga ayi, koma ndi za amene anandituma.” (Zimene Tiyenera Kuchitira Anzathu
Mu ulaliki wake wotchuka wa paphiri, Yesu anatchula mfundo yofunika kwambiri yomwe ingatithandize kuchitira ena zinthu zabwino. Iye ananena kuti: “Zinthu zonse zimene mukufuna kuti anthu akuchitireni, inunso muwachitire zimenezo.”—Mateyo 7:12.
Ena amatembenuza mawu amenewa kuti: “Musachitire ena zinthu zimene simungafune kuti iwo akuchitireni.” Koma mawu amenewa n’ngosiyana ndi oyamba aja. Kuti mumvetse chifukwa chake, ganizirani fanizo la Yesu la Msamariya wachifundo. Myuda wina anamenyedwa pa msewu mpaka kutsala pang’ono kufa. Wansembe ndi Mlevi wina anamuona munthuyu koma anangomupitirira. Popeza kuti anthu amenewa sanavulaze nawo munthuyo, tinganene kuti anatsatira mawu akuti: “Musachitire ena zinthu zimene simungafune kuti iwo akuchitireni.” Koma mosiyana ndi zimene anachita awiriwa, Msamariya anaima ndi kum’thandiza munthuyo. Iye anamanga mabala ake n’kupita naye kunyumba ya alendo. Msamariyayu anachitira munthuyo zinthu zimene akanafuna kuti nayenso achitiridwe. Apa iye anachita zoyenera, chifukwa anatsatira mawu akuti: “Zimene mukufuna kuti anthu akuchitireni, inunso muwachitire zimenezo.”—Luka 10:30-37.
Tingagwiritse ntchito mfundo imeneyi m’zochitika zosiyanasiyana ndipo zotsatira zake zingakhale zosangalatsa. Mwachitsanzo, kodi mungatani ngati banja lina litasamukira kwanuko? Kodi mungapite ku nyumba kwawo n’kukawalandira? Kodi mungawathandize kudziwa bwino malo awo atsopanowo ndi kuwafotokozera zomwe angafune kudziwa? Ngati mutachita zimenezi, mungayambe kugwirizana ndi alendowo. Ndiponso, mungasangalale chifukwa chodziwa kuti mwachita zimene Mulungu amafuna. Kumeneku ndiye kuchita zinthu mwanzeru.
Tizikonda Ena Posankha Zochita
Kuwonjezera pa mfundo imene takambirana ija, Yesu anaperekanso malangizo ena amene tiyenera kutsatira posankha zochita. Atafunsidwa kuti atchule lamulo lalikulu kwambiri m’Chilamulo cha Mose, Yesu anati: “‘Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi maganizo ako onse.’ Limeneli ndilo lamulo lalikulu koposa komanso loyamba. Lachiwiri, lofanana nalo ndi ili, ‘Uzikonda mnansi wako mmene umadzikondera wekha.’ Chilamulo chonse chagona pa malamulo awiri amenewa, kuphatikizaponso Zolemba za aneneri.”—Mateyo 22:36-40.
Usiku wina, kutangotsala tsiku limodzi kuti Yesu aphedwe, iye anapatsa ophunzira ake “lamulo latsopano” loti azikondana wina ndi mnzake. (Yohane 13:34) N’chifukwa chiyani Yesu anati lamulo limeneli ndi latsopano? Kodi Yesu sanali atanenapo kale kuti kukonda mnansi ndi limodzi mwa malamulo awiri amene Chilamulo chonse chagona? M’Chilamulo cha Mose chimenechi, Aisiraeli analangizidwa kuti: “Uzikonda mnansi wako monga udzikonda wekha.” (Levitiko 19:18) Koma Yesu anafuna kuti ophunzira ake azichita zoposa pamenepa. Usiku womwe uja, Yesu anauza ophunzira ake kuti iye watsala pang’ono kupereka moyo wake chifukwa cha iwo. Ndiyeno anawauza kuti: “Lamulo langa ndi ili, mukondane wina ndi mnzake mmene inenso ndakondera inu. Palibe amene ali ndi chikondi choposa ichi, chakuti wina n’kupereka moyo wake chifukwa cha mabwenzi ake.” (Yohane 15:12, 13) Lamulo limeneli linalidi latsopano chifukwa limafuna kuti munthu aziika zofuna za ena patsogolo pa zofuna zake.
Pali njira zosiyanasiyana zosonyezera kuti timakondadi anthu ena, m’malo mongofuna
zathu zokha. Mwachitsanzo, tinene kuti mukufuna kumvera nyimbo ndiye mwaikweza kwambiri kuti musangalale, koma mukusokoneza anzanu. Kodi mungalole kuitsitsa kuti musasokoneze anzanuwo? M’mawu ena, kodi mungaike zofuna za anzanu patsogolo pa zanu?Taganiziraninso nkhani iyi: Tsiku lina Mboni za Yehova zinafika pa nyumba ya munthu wina ku Canada. Kunja kunkazizira kwambiri ndiponso kunkagwa chipale chofewa. Akukambirana, munthuyo ananena kuti sanachotse chipale chofewa pabwalo la nyumba yakeyo chifukwa choti amadwala nthenda ya mtima. Patatha ola limodzi, munthuyu anamva phokoso la mafosholo. A Mboni awiri aja anali atabwera kudzakonza njira yopita ku nyumba yake. Munthuyo analemba kalata ku ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Canada ndipo kalatayo inati: “Lero ndaona ndi maso anga chikondi chenicheni chachikhristu. Zomwe zachitikazi, zasintha kwambiri mmene ndimaonera anthu ndipo zandichititsa kuti ndiziyamikira kuposa kale ntchito yanu ya padziko lonse.” Ndithudi, tikasankha kuchitira anthu ena zinthu zabwino ngakhale zitakhala zazing’ono, iwo angayamikire kwambiri. Mukamachitira ena zabwino, inunso mumasangalala kwambiri.
Tizikonda Mulungu Posankha Zochita
Tikamasankha zochita, tiyenera kuganizira lamulo limene Yesu anati ndi lalikulu kwambiri pa malamulo onse, lakuti tizikonda Mulungu. Yesu ananena mawuwa kwa Ayuda omwe anali mtundu wodzipereka kale kwa Yehova. Komabe, Mwisiraeli aliyense payekha anafunika kusankha kuti atumikire Mulungu ndi moyo wonse komanso mtima wonse.—Deuteronomo 30:15, 16.
Choncho, zinthu zimene mumasankha kuchita zimasonyeza ngati mumakonda Mulungu kapena ayi. Mwachitsanzo, mukayamba kudziwa Baibulo ndi kuona kuti malangizo ake ndi othandiza, nanunso mumakhala ndi udindo wosankha zochita. Kodi mungakonde kuyamba kuphunzira Baibulo mwadongosolo n’cholinga choti mukhale wophunzira wa Yesu? Mutatero mudzakhala wosangalala, chifukwa Yesu anati: “Osangalala ali iwo amene amazindikira zosowa zawo zauzimu.”—Mateyo 5:3.
Sitikudziwa ngati wolamulira wachinyamata uja ananong’oneza bondo ndi zimene anasankha. Koma tikudziwa mmene Petulo anamvera atatsatira Yesu Khristu kwa zaka zambiri. Petulo atatsala pang’ono kufa cha mu 64 C.E, analimbikitsa okhulupirira anzake kuti: “Chitani chilichonse chotheka kuti [Mulungu] adzakupezeni opanda thotho, opanda chilema ndiponso muli mu mtendere.” (2 Petulo 1:14; 3:14) N’zoonekeratu apa kuti Petulo sananong’oneze bondo chifukwa cha zimene anasankha zaka 30 m’mbuyomo ndipo analimbikitsanso ena kuti asasiye zimene iwo anasankha.
Tingamvere malangizo a Petulo mwa kusankha kuchita zimene zimafunika kuti tikhale ophunzira a Yesu ndiponso kutsatira malamulo a Mulungu. (Luka 9:23; 1 Yohane 5:3) Zimenezi zingaoneke zovuta koma ganizirani lonjezo lolimbikitsa la Yesu lakuti: “Bwerani kwa ine, nonsenu ogwira ntchito yolemetsa ndi olemedwa, ndipo ndidzakutsitsimutsani. Senzani goli langa ndipo phunzirani kwa ine, pakuti ndine wofatsa ndi wodzichepetsa, ndipo mudzapeza chitsitsimutso cha miyoyo yanu. Pakuti goli langa ndi lofewa ndipo katundu wanga ndi wopepuka.”—Mateyo 11:28-30.
Taganizirani zimene zinamuchitikira Arthur. Ali ndi zaka 10, anayamba kuphunzira kuimba vayolini kuti adzakhale katswiri woimba. Atafika zaka 14, anayamba kudziwika ndipo ankakaimba ku malo osiyanasiyana. Komabe, iye sanali wosangalala. Bambo ake ankakhala ndi mafunso ofuna kudziwa cholinga cha moyo, ndipo ankaitana kunyumba kwawo aphunzitsi a zachipembedzo koma mayankho awo sanawagwire mtima. M’banja mwawo, ankakambirana ngati Mulungu alipo ndiponso chifukwa chake amalola zoipa. Kenako, bambo a Arthur anayamba kukambirana nkhani zimenezi ndi a Mboni za Yehova. Zimene ananena zinawagwira mtima ndipo banja lawo lonse linayamba kuphunzira nawo Baibulo.
Patapita nthawi, Arthur anazindikira kuchokera m’Malemba chifukwa chake Mulungu amalola zoipa kuchitika ndipo anamvetsa bwino cholinga cha moyo. Iye ndi anthu ena atatu a m’banja mwake anasankha kuchita chinthu chimene mpaka pano sanong’oneza nacho bondo. Anadzipereka kwa Yehova. Iye anati: “Ndine wosangalala kwambiri chifukwa Yehova wandithandiza kudziwa choonadi ndipo wandipulumutsa ku moyo wampikisano umene ndi wofala kwa akatswiri oimba. Kuti apambane, oimba ambiri amachita chilichonse ndi zoipa zomwe.”
Arthur amakondabe kuimba vayolini kuti asangalatse anzake, koma si kuti moyo wake wonse wagona pa zimenezi. M’malo mwake, cholinga chachikulu pamoyo wake ndicho kutumikira Mulungu. Iye amagwira ntchito pa ofesi ya nthambi ina ya Mboni za Yehova. Mosiyana ndi wolamulira wachinyamata uja, mungasankhe kumvera pempho la Yesu loti mukhale wophunzira wake monga mmene anachitira Arthur ndi anthu ena ambiri. Zimenezi zingakuthandizeni kukhala wosangalala kwambiri.
[Chithunzi patsamba 6]
Zosankha zanu zingathandize kwambiri anthu ena
[Chithunzi patsamba 7]
Kodi mwasankha kuphunzira Baibulo ndi kukhala wotsatira wa Yesu?