Kodi Mukukumbukira?
Kodi Mukukumbukira?
Kodi mwapindula powerenga magazini aposachedwapa a Nsanja ya Olonda? Tayesani kuyankha mafunso otsatirawa:
• Kodi okhulupirira nyenyezi anakaona Yesu liti?
Baibulo lina limati: “Okhulupirira nyenyezi sanakaone Yesu ali modyera ziweto usiku womwe iye anabadwa monga anachitira abusa aja. Iwo anakamuona patatha miyezi ingapo.” Nthawi imeneyi Yesu anali “mwana wamng’ono” ndipo anali kunyumba osati kukhola. (Mat. 2:7-11) Okhulupirira nyenyezi aja akanakhala kuti anapatsa Yesu golidi ndi mphatso zina zamtengo wapatali usiku umene iye anabadwa, kodi Mariya akanapereka nsembe ya nkhunda ziwiri zokha kukachisi patangotha masiku 40?—1/1, tsamba 31.
• Kodi munthu angatani kuti akhale ndi moyo waphindu?
Mwina mungadzifunse kuti, ‘Kodi ndingasinthe moyo wanga kuti ndikhale ndi zinthu zochepa?’ Izi ndi zimene Amy anachita. Iye anali wolemera koma sanali kusangalala. Anazindikira kuti kufunafuna ntchito yapamwamba m’dzikoli kukanamuwonongera chikhulupiriro. Choncho, iye anayamba kuika zinthu za Ufumu patsogolo ndipo anachita upainiya kwa nthawi ndithu. Iye anati, “Moyo wanga panopo ndi watanthauzo kwambiri kusiyana ndi mmene unalili panthawi imene ndinali kugwirira ntchito dzikoli.”—1/15, tsamba 19.
• Kodi ndi chiyani chingathandize amayi kukhala ndi moyo wosangalala?
Amayi ambiri amapita kuntchito. Ena amachita zimenezi kuti adyetse banja lawo, enanso kuti adziimire paokha kapena kuti agule zimene mtima wawo umalakalaka. Koma ena amatero chifukwa chongosangalala ndi ntchito yawo. Amayi amene amatsatira mfundo zachikhristu amagwira ntchito yaikulu panyumba, makamaka pamene ali ndi mwana wakhanda. Amayi ena asankha kugwira ntchito nthawi yochepa kapena kusiya kumene kuti asamalire bwino banja lawo, ndipo amakhala ndi moyo wosangalala.—2/1, masamba 28-31.
• Kodi “m’badwo” umene Yesu ananena pa Mateyo 24:34 ndi uti?
Nthawi zambiri, Yesu anagwiritsa ntchito mawu akuti “m’badwo,” polankhula ndi anthu oipa kapena pofotokoza za anthu oipa. Koma sanatero palembali pamene anali kulankhula ndi ophunzira ake, amene anali pafupi kudzozedwa ndi mzimu woyera. Iwo ndiwo akanatha kudziwa tanthauzo la zimene iye ananena pa Mateyo 24:32, 33. Choncho zikuoneka kuti Yesu anali kunena otsatira ake odzozedwa, kalelo komanso masiku ano.—2/15, masamba 23-24.
• Malinga ndi Agalatiya 3:24, kodi Chilamulo chinakhala bwanji namkungwi?
Kale pachikhalidwe cha Aroma ndi Agiriki, namkungwi ankakhala wantchito wokhulupirika amene anali kusamalira mwana mogwirizana ndi zofuna za bambo a mwanayo. Mofanana ndi namkungwi, Chilamulo chinali kuteteza Ayuda ku zinthu zoipa monga kukwatirana ndi anthu akunja. Komanso monga namkungwi, Chilamulo chinali chakanthawi chabe, ndipo chinagwira ntchito mpaka Khristu atafika.—3/1, masamba 18-21.
• Malinga ndi Yakobe 3:17, kodi tiyenera kukhala ndi makhalidwe otani?
Pokhala anthu oyera, tiyenera kukana zinthu zoipa mwamsanga. (Gen. 39:7-9) Tiyenera kukhalanso amtendere, kupewa ndewu kapena khalidwe losokoneza mtendere. Choncho tonse tingachite bwino kudzifunsa kuti: “Kodi ndimadziwika ngati munthu wodzetsa mtendere kapena wosokoneza mtendere? Kodi ndimakhalira kukangana ndi ena? Kodi sindichedwa kukhumudwa kapena kukhumudwitsa ena? Kodi ndimakhululuka msanga ndipo sindiumirira kuti anthu ena atsatire mfundo zanga?—3/15, masamba 24-25.
• Kodi n’chifukwa chiyani Yesu anachiritsa munthu wakhungu pang’onopang’ono? (Maliko 8:22-26)
Baibulo silitchula chifukwa chenicheni. Koma Yesu anachiritsa munthu wakhunguyo pang’onopang’ono mwina ndi cholinga chakuti maso ake azolowere kuwala. Ngati chifukwa chake ndi chimenechi, ndiye kuti Yesu anamuganizira kwambiri munthuyo.—4/1, tsamba 30.