Mfundo Zazikulu za M’buku la Machitidwe
Mawu a Yehova Ndi Amoyo
Mfundo Zazikulu za M’buku la Machitidwe
BUKU la Machitidwe limafotokoza mwatsatanetsatane za kukhazikitsidwa ndi kukula kwa mpingo wachikhristu. Bukuli linalembedwa ndi Luka, ndipo lili ndi nkhani zochititsa chidwi zosonyeza ntchito imene Akhristu anachita kwa zaka 28, kuyambira mu 33 C.E. mpaka mu 61 C.E.
Chigawo choyamba cha buku la Machitidwe chimafotokoza kwambiri zimene mtumwi Petulo anachita, pamene chigawo chomaliza chimafotokoza za mtumwi Paulo. Pogwiritsa ntchito mawu akuti “ife,” Luka anasonyeza kuti analipo pamene zinthu zina zinali kuchitika. Uthenga wa m’buku la Machitidwe ungatithandize kuzindikira kufunika kwa Mawu a Mulungu ndi mphamvu ya mzimu wake woyera. (Aheb. 4:12) Uthengawu ungatithandizenso kukhala odzipereka ndiponso ungalimbitse chikhulupiriro chathu mu zimene Ufumu udzachita.
PETULO AGWIRITSA NTCHITO “MAKIYI A UFUMU”
Atalandira mzimu woyera, atumwi anayamba kulalikira molimba mtima. Petulo anagwiritsa ntchito “makiyi a ufumu wa kumwamba” oyamba kutsegula mwayi kwa Ayuda ndi anthu olowa Chiyuda kuti ‘alandire mawu’ ndi kulowa mu Ufumu. (Mat. 16:19; Mac. 2:5, 41) Chifukwa cha chizunzo ophunzira anabalalika, koma zimenezi zinathandiza kuti ntchito yolalikira ifalikire m’madera ambiri.
Atamva kuti anthu ku Samariya alandira mawu a Mulungu, atumwi ku Yerusalemu anatumiza Petulo ndi Yohane. Petulo anatsegula mwayi wolowa Ufumu kwa Asamariya, ndipo pamenepa anagwiritsa ntchito makiyi achiwiri. (Mac. 8:14-17) Mwina patadutsa chaka chimodzi Yesu ataukitsidwa, Saulo wa ku Tariso anasintha modabwitsa. Mu 36 C.E., Petulo anagwiritsa ntchito makiyi achitatu, ndipo mphatso yaulere ya mzimu woyera inathiridwa pa anthu osadulidwa amitundu.—Mac. 10:45.
Kuyankha Mafunso a M’Malemba:
2:44-47; 4:34, 35—N’chifukwa chiyani okhulupirira anali kugulitsa zinthu zawo ndi kugawira ena ndalama zimene anapeza? Anthu ambiri amene anakhulupirira anali ochokera m’madera akutali ndipo analibe ndalama zokwanira zokhalira ku Yerusalemu. Komabe anasankha kukhalako nthawi yaitali kuti aphunzire zambiri zokhudza chipembedzo chawo chatsopano ndi kulalikira ena. Pofuna kuthandiza anthu amenewa, Akhristu ena anagulitsa katundu wawo ndipo ndalama zake anagawira osowa.
4:13—Kodi n’chifukwa chiyani anthu ananena kuti Petulo ndi Yohane anali osaphunzira? Sikuti iwo anali osaphunzira, koma anali kutchedwa “osaphunzira ndiponso anthu wamba” chifukwa chakuti sanapite ku sukulu za Arabi kukaphunzira zachipembedzo.
5:34-39—Kodi Luka anadziwa bwanji zimene Gamaliyeli ananena mseri ku Bungwe Lalikulu la Ayuda? Mwina anadziwa mwa njira zitatu izi: (1) Anamva kwa Paulo, yemwe anali wophunzira wa Gamaliyeli; (2) anafunsa munthu wina wachifundo amene anali m’Bungwe Lalikulu la Ayuda, monga Nikodemo; (3) anadziwa zimenezi pouziridwa ndi Mulungu.
7:59—Kodi Sitefano anali kupemphera kwa Yesu? Ayi. Munthu ayenera kulambira Yehova yekha basi. Choncho, mapemphero akenso ayenera kupita kwa Yehova Mulungu yekha. (Luka 4:8; 6:12) Sitefano ankatha kuchonderera Yehova m’dzina la Yesu, koma zimene zinachitika apa zinali zapadera. (Yoh. 15:16) Panthawiyi, Sitefano anaona masomphenya a “Mwana wa munthu ali chiimirire kudzanja lamanja la Mulungu.” (Mac. 7:56) Sitefano anali kudziwa bwino kuti Yesu anali atapatsidwa mphamvu zotha kuukitsa akufa. Choncho, malinga ndi tanthauzo lake lenileni la mawu a Chigiriki, iye sanapemphere kwa Yesu koma ‘anaitana’ Yesuyo, kumupempha kuti asunge mzimu wake.
Zimene Tikuphunzirapo:
1:8. Ntchito ya padziko lonse yolalikira yomwe ikuchitika ndi olambira Yehova singatheke popanda thandizo la mzimu woyera.
4:36–5:11. Yosefe wa ku Kupuro anapatsidwa dzina lakuti Baranaba, lomwe limatanthauza “Mwana wa Chitonthozo.” N’kutheka kuti atumwi anam’patsa dzinali chifukwa chakuti iye anali wokoma mtima, wachifundo ndi wokonda kuthandiza ena. Tiyenera kutengera chitsanzo chake osati cha Hananiya ndi Safira, amene anachita zinthu mwachinyengo ndi mosaona mtima.
9:23-25. Kuzemba adani athu kuti tipitirizebe kulalikira si mantha.
9:28-30. Ngati kulalikira ku madera ena kapena kwa anthu ena kungatiike pangozi monga kumenyedwa, kuyesedwa kuchita choipa, kapena kusokoneza ubale wathu ndi Mulungu, tiyenera kukhala anzeru ndi kusankha bwino malo ndi nthawi yolalikira.
9:31. Panthawi yomwe kuli mtendere, tiyenera kuyesetsa kulimbitsa chikhulupiriro chathu mwa kuphunzira ndi kusinkhasinkha. Zimenezi zingatithandize kuyenda moopa Yehova pogwiritsa ntchito zimene tikuphunzira ndiponso kukhala achangu mu utumiki.
UTUMIKI WA PAULO
Mu 44 C.E., Agabo anabwera ku Antiokeya kumene Baranaba ndi Saulo anakhala akuphunzitsa “chaka chonse.” Agabo analosera kuti kudzakhala “njala yaikulu,” imene inadzachitika patatha zaka ziwiri. (Mac. 11:26-28) “Atamaliza utumiki wopereka thandizo ku Yerusalemu,” Baranaba ndi Saulo anabwerera ku Antiokeya. (Mac. 12:25) Mu 47 C.E., patatha zaka 12 kuchokera pamene Saulo anatembenuka, Baranaba ndi Saulo anatumizidwa ndi mzimu woyera paulendo wa umishonale. (Mac. 13:1-4) Mu 48 C.E., anabwerera ku Antiokeya, kumene m’mbuyomo “anaikizidwa m’kukoma mtima kwa m’chisomo cha Mulungu.”—Mac. 14:26.
Kenako patapita miyezi 9, Paulo (wotchedwanso Saulo) anasankha Sila kuti aziyenda naye ndipo anayamba ulendo wake wachiwiri. (Mac. 15:40) Ali pa ulendowu, Timoteyo ndi Luka anakumana ndi Paulo ndi kupitira limodzi. Luka anatsala ku Filipi pamene Paulo anapitirira kukafika ku Atene mpaka ku Korinto, kumene anakumana ndi Akula ndi Purisikila. Paulo anakhala kumeneko chaka ndi miyezi 6. (Mac. 18:11) Iye anasiya Timoteyo ndi Sila ku Korinto, kenako anatenga Akula ndi Purisikila ndipo anayenda ulendo wapanyanja kupita ku Suriya kumayambiriro kwa 52 C.E. (Mac. 18:18) Akula ndi Purisikila anaperekeza Paulo mpaka ku Efeso, kumene iwo anatsala.
Atatha nthawi ndithu ku Antiokeya wa ku Suriya, Paulo anayamba ulendo wake wachitatu mu 52 C.E. (Mac. 18:23) Ku Efeso “mawu a Yehova anapitirira kufalikira ndi kupambana.” (Mac. 19:20) Paulo anatha pafupifupi zaka zitatu kumeneko. (Mac. 20:31) Pofika pa Pentekosite wa mu 56 C.E., Paulo anali ali ku Yerusalemu. Atagwidwa, analalikira molimba mtima kwa akuluakulu a boma. Ndipo atapita ku Roma, mtumwiyu anali pa ukaidi wapanyumba kwa zaka ziwiri (cha m’ma 59-61 C.E.), ndipo ali kumeneko anapeza njira zolalikirira Ufumu ndi kuphunzitsa “za Ambuye Yesu Khristu.”—Mac. 28:30, 31.
Kuyankha Mafunso a M’Malemba:
14:8-13—Kodi n’chifukwa chiyani anthu ku Lusitara anatcha “Baranaba . . . kuti Zeu, koma Paulo anamutchula kuti Hereme”? Zeu anali mkulu wa milungu ya Agiriki, ndipo mwana wake Hereme anali kudziwika ndi kudziwa kulankhula. Popeza kuti Paulo ndiye analankhula kwambiri, anthu a ku Lusitara anamutcha Hereme ndipo Baranaba anamutcha Zeu.
16:6, 7—N’chifukwa chiyani mzimu woyera unaletsa Paulo ndi anzake kulalikira ku chigawo cha Asiya ndi ku Bituniya? Antchito anali ochepa. Choncho, mzimu woyera unawatsogolera kuti akalalikire ku madera obala zipatso kwambiri.
18:12-17—Kodi n’chifukwa chiyani anthu atayamba kumenya Sositene, Bwanamkubwa Galiyo sanawaletse? Popeza kuti Sositene anali mtsogoleri wa gulu lolimbana ndi Paulo, mwina Galiyo anaganiza kuti m’pake kuti Sositene amenyedwe. Ngakhale ndi choncho, zikuoneka kuti zotsatira zake zinali zabwino chifukwa Sositene anatembenuka kukhala Mkhristu. Patapita nthawi Paulo ananena za Sositene kuti ndi “m’bale wathu.”—1 Akor. 1:1.
18:18—Kodi Paulo analumbira chiyani? Akatswiri ena amati Paulo analumbira zokhala Mnaziri. (Num. 6:1-21) Komabe Baibulo silinena zimene Paulo analumbira. Ndiponso Malemba sanena ngati Paulo anapanga lumbiro lakelo asanatembenuke kapena atatembenuka, kapena ngati iye anali kuyamba kuchita zimene analumbirazo kapena kusiya. Mulimonsemo, kupanga lumbiro limeneli sikunali kulakwa.
Zimene Tikuphunzirapo:
12:5-11. Tiyenera kupempherera abale athu.
12:21-23; 14:14-18. Herode sanakane kulandira ulemerero womwe unafunika kupita kwa Mulungu yekha basi. Mosiyana ndi Herode, Paulo ndi Baranaba anakanitsitsa kutamandidwa ndi kupatsidwa ulemu wosawayenerera. Tisamafune ulemerero pa zilizonse zimene tingachite potumikira Yehova.
14:5-7. Kuchita zinthu mwanzeru kungatithandize kuti tipitirizebe kutumikira.—Mat. 10:23.
14:22. Akhristu amadziwa kuti angakumane ndi masautso. Iwo sagonja pa chikhulupiriro chawo kuti athawe masautsowo.—2 Tim. 3:12.
16:1, 2. Akhristu achinyamata ayenera kuchita khama pazinthu zauzimu ndi kudalira Yehova kuti awathandize kukhala ndi mbiri yabwino.
16:3. Tiyenera kuchita zonse zimene tingathe, zogwirizana ndi Malemba, kuti anthu alandire uthenga wabwino.—1 Akor. 9:19-23.
20:20, 21. Kulalikira nyumba ndi nyumba ndi kofunika kwambiri pa utumiki wathu.
20:24; 21:13. Kukhalabe wokhulupirika kwa Mulungu ndi kofunika kwambiri kuposa moyo wathu.
21:21-26. Tizikhala okonzeka kulandira malangizo ndi mtima wonse.
25:8-12. Akhristu masiku ano ayenera kugwiritsa ntchito makhoti “pa kuteteza uthenga wabwino ndi kuutsimikizira mwalamulo.”—Afil. 1:7.
26:24, 25. Tiyenera kulengeza “mawu a choonadi ndiponso anzeru” ngakhale kuti “munthu wa kuthupi” amawaona ngati opusa.—1 Akor. 2:14.
[Chithunzi patsamba 30]
Kodi ndi liti pamene Petulo anagwiritsa ntchito “makiyi a ufumu”?
[Chithunzi patsamba 31]
Ntchito ya padziko lonse yolalikira singatheke popanda thandizo la mzimu woyera