Chitirani Umboni Bwino Lomwe
Chitirani Umboni Bwino Lomwe
“Anatilamula kuti tilalikire kwa anthu, ndi kupereka umboni wokwanira.”—MAC. 10:42.
1. Pamene Petulo ankalankhula ndi Korneliyo, kodi ananena za ntchito iti?
MKULU wa asilikali wa ku Italiya anasonkhanitsa abale ake ndi anzake. Ndipo zimene zinachitika pa tsikuli, chinali chiyambi cha kusintha kwakukulu pa zochita za Mulungu ndi anthu. Munthu woopa Mulungu ameneyu anali Korneliyo. Mtumwi Petulo anauza gulu limene linasonkhanalo kuti atumwi analamulidwa, ‘kulalikira kwa anthu, ndi kupereka umboni wokwanira’ wonena za Yesu. Umboni umene Petulo anachitira pa tsikuli unali ndi zotsatira zabwino kwambiri. Anthu akunja osadulidwa analandira mzimu wa Mulungu, anabatizidwa ndipo anakhala ndi chiyembekezo chokakhala mafumu limodzi ndi Yesu kumwamba. Izitu, zinali zotsatira zabwino kwambiri za umboni wokwanira umene Petulo anachitira.—Mac. 10:22, 34-48.
2. Kodi timadziwa bwanji kuti si atumwi 12 okha amene analamulidwa kuchitira umboni?
2 Zimenezi zinachitika mu 36 C.E. Koma zaka ziwiri izi zisanachitike, munthu amene ankatsutsa Chikhristu kwadzaoneni, anaona zinthu zimene zinasintha moyo wake. Saulo wa ku Tariso anali pa ulendo wopita ku Damasiko. Ali panjira, Yesu anamuonekera ndipo anamuuza kuti: “Nyamuka, ulowe mu mzindawo, ndipo udzauzidwa zoyenera kuchita.” Kenako Yesu anauza wophunzira wina dzina lake Hananiya kuti Saulo adzachitira umboni “kwa amitundu, ngakhalenso kwa mafumu ndi ana a Isiraeli.” (Werengani Machitidwe 9:3-6, 13-20.) Hananiya atakumana ndi Saulo anamuuza kuti: “Mulungu wa makolo athu akale wakusankha iwe . . . pakuti udzakhala mboni yake kwa anthu onse.” (Mac. 22:12-16) Kodi Saulo yemwe anadzakhala Paulo, anatani posonyeza kuti ankaona kuti ntchito imeneyi ndi yofunika kwambiri?
Anachitira Umboni Bwino Lomwe
3. (a) Kodi tikambirana nkhani iti? (b) Kodi akulu a ku Efeso anatani atalandira uthenga wa Paulo ndipo anasonyeza chitsanzo chabwino chotani?
3 Zikanakhala zosangalatsa kukambirana mwatsatanetsatane zonse zimene Paulo anachita. Koma panthawi ino tiyeni tikambirane zimene Paulo ananena mu 56 C.E. Nkhani imeneyi ili m’chaputala 20 cha buku la Machitidwe. Paulo anakamba nkhani imeneyi chakumapeto kwa ulendo wake wachitatu waumishonale. Iye atatsika pa Mileto lomwe ndi doko la nyanja ya Ejani, anatumiza uthenga kwa akulu a mpingo wa Efeso kuti abwere. Efeso anali pamtunda wa makilomita 50, koma ulendowu unkatalika chifukwa chakuti misewu yake inali yozungulira kwambiri. N’zachionekere kuti akulu a ku Efeso anali osangalala atalandira uthenga wa Paulo. (Yerekezerani ndi Miyambo 10:28.) Komabe iwo anayenera kukonzekera ulendo wopita ku Mileto. N’kutheka kuti ena anafunika kutsanzika kuntchito kapena kusiya kaye kukagulitsa malonda awo. Akhristu ambiri masiku ano, amachitanso chimodzimodzi pofuna kuti asaphonye chigawo chilichonse cha msonkhano wachigawo umene umachitika chaka chilichonse.
4. Kodi Paulo ankalalikira bwanji pa zaka zimene anali ku Efeso?
4 Kodi mukuganiza kuti Paulo anali kuchita chiyani ku Mileto pa masiku atatu kapena anayi amene ankayembekezera akuluwo? Kodi mukanakhala inuyo bwenzi mukutani? (Yerekezerani ndi Machitidwe 17:16, 17.) Mawu a Paulo kwa akulu a ku Efeso angatithandize kudziwa zimene ankachita panthawi imene ankawayembekeza. Iye anawafotokozera chizolowezi chake cha kulalikira uthenga wabwino ngakhale masiku oyambirira amene anali ku Efeso. (Werengani Machitidwe 20:18-21.) Podziwa kuti panalibe amene akanakana iye anati: “Mukudziwa bwino lomwe mmene ndinakhalira nanu nthawi zonse kuchokera tsiku loyamba limene ndinaponda m’chigawo cha Asiya. . . . Ndachitira umboni bwino lomwe.” Iye anatsimikiza mtima kugwira ntchito imene Yesu anamupatsa. Kodi anakwanitsa bwanji kuchita zimenezi ku Efeso? Njira imodzi imene anapangira zimenezi ndi kulalikira kulikonse kumene Ayuda akanapezeka. Luka analemba kuti pamene Paulo anali ku Efeso, cha m’ma 52 mpaka 55 C.E, “anali kukamba nkhani ndi kuwakopa” m’sunagoge. Ndipo pamene Ayuda anapitiriza “kuumitsa mitima yawo osakhulupirira,” Paulo anayamba kukalalikira kwa anthu ena a mumzindawo. Motero tingati iye analalikira kwa Ayuda ndi kwa Agiriki mumzinda waukuluwu.—Mac. 19:1, 8, 9.
5, 6. N’chifukwa chiyani tinganene motsimikiza kuti Paulo ankalankhula ndi anthu osakhulupirira polalikira ku nyumba ndi nyumba?
5 Anthu ena amene anakhala Akhristu, m’kupita kwa nthawi anayenerera kukhala akulu ndipo ndi amene Paulo analankhula nawo ku Mileto. Iye anawakumbutsa njira imene anagwiritsa ntchito polalikira. Iye anati: “Komatu sindinakubisireni chilichonse chopindulitsa, kapena kuleka kukuphunzitsani poyera komanso ku nyumba ndi nyumba.” Masiku ano, anthu ena amanena kuti palembali Paulo ankangotanthauza za kuyenda ndi kulimbikitsa anthu omwe anali kale okhulupirira. Koma zimenezi si zoona. Mawu akuti ‘kuphunzitsa poyera komanso ku nyumba ndi nyumba,’ kwenikweni amatanthauza kulalikira kwa anthu osakhulupirira. Zimenezi zikuoneka bwino m’mawu amene Paulo ananena pambuyo pake, kuti analalikira “kwa Ayuda ndi kwa Agiriki omwe, za kulapa pamaso pa Mulungu ndi chikhulupiriro mwa Ambuye wathu Yesu.” Mwachionekere Paulo ankalalikira kwa anthu osakhulupirira amene ankafunika kulapa ndi kukhulupirira Yesu.—Mac. 20:20, 21.
6 Katswiri wina atasanthula bwino Malemba Achigiriki Achikristu, anathirirapo ndemanga pa lemba la Machitidwe 20:20. Iye ananena kuti: “Paulo anakhala zaka zitatu ku Efeso. Anafika pakhomo lililonse ndipo analalikira pafupifupi anthu onse. (vesi 26) Ichitu ndi chifukwa cha m’Malemba cholalilikirira ku nyumba ndi nyumba komanso poyera.” Kaya Paulo anafikadi pa nyumba iliyonse ngati mmene katswiriyu ananenera kapena ayi, mfundo ndi yakuti iye anafuna kuwakumbutsa akulu a ku Efesowo mmene anali kulalikirira komanso zotsatira zake. Luka analemba kuti: “Onse okhala m’chigawo cha Asiya anamva mawu a Ambuye, Ayuda ndi Agiriki omwe.” (Mac. 19:10) Koma kodi n’chifukwa chiyani ananena kuti “onse” okhala m’chigawo cha Asiya anamva uthengawo, ndipo kodi zimenezi zikutiuza chiyani pantchito yathu yolalikira?
7. Kodi ntchito yolalikira ya Paulo inakhudza bwanji anthu ena amene iye sanawalalikire mwachindunji?
7 Chifukwa chakuti Paulo ankalalikira poyera komanso ku nyumba ndi nyumba anthu ambiri anamva uthenga wake. Kodi mukuganiza kuti anthu onse amene anamvetsera uthengawo anali kungokhala ku Efeso komweko, osapita kumadera ena kukachita malonda, kukacheza ndi achibale kapena kukapumula kumalo enaake? Zimenezi sizingatheke. N’chimodzimodzinso masiku ano, anthu ambiri amasamukira kumalo ena pa zifukwa zimenezi ndipo mwina inunso mwatero. Ndiponso, kalelo anthu ena anali kuchoka kumadera ena kubwera ku Efeso kudzacheza kapena kudzachita malonda. Ndipo n’kutheka kuti pamene anali kumeneko, anakumana ndi Paulo kapena anamumva akulalikira. Ndiyeno kodi anthu amenewa anali kuchita chiyani akabwerera kwawo? Anthu amene anaphunzira choonadi anali kuchitiranso umboni kwa ena. Ngakhale anthu amene sanakhulupirire, mwina ankauza anzawo zimene anamva ku Efeso. Pamapeto pake, achibale, oyandikana nawo kapena ogwira nawo ntchito anamva choonadi ndipo mwina ena anakhulupirira. (Yerekezerani ndi Maliko 5:14.) Kodi zimenezi zikusonyeza chiyani pa zotsatira za ntchito yanu yochitira umboni bwino lomwe?
8. Kodi zinatheka bwanji kuti anthu a ku chigawo chonse cha Asiya amve uthenga wa choonadi?
8 Ponena za nthawi yake yoyambirira imene analalikira ku Efeso, Paulo analemba kuti ‘khomo la ntchito yaikulu linamutsegukira.’ (1 Akor. 16:8, 9) Kodi ndi khomo liti limene linamutsegukira, ndipo linamutsegukira motani? Utumiki wa Paulo ku Efeso unachititsa kuti uthenga wabwino ufike ku madera ena. Taganizirani za mzinda wa Kolose, Laodikaya ndi Herapoli. Mosiyana ndi mzinda wa Efeso, mizinda imeneyi sinali m’mphepete mwa nyanja. Paulo sanapite ku mizinda imeneyi koma anthu a kumeneko anamva uthenga wabwino. Epafura anali wochokera kudera lakumeneku. (Akol. 2:1; 4:12, 13) Kodi Epafura anakhala Mkhristu atamva Paulo akulalikira ku Efeso? Baibulo silinena. Koma pamene Epafura anali kulalikira kudera la kwawolo, ayenera kuti anali kulalikira m’malo mwa Paulo. (Akol. 1:7) Mwina uthenga wa Chikhristu unafikanso ku Filadefiya, Sade ndi ku Tiyatira pa zaka zimene Paulo anali kulalikira ku Efeso.
9. (a) Kodi Paulo ankafunitsitsa kuchita chiyani? (b) Tchulani lemba la chaka cha 2009.
9 Akulu a ku Efeso anali ndi umboni wokwanira wovomerezera mawu a Paulo akuti: “Komabe, sindiuyesa kanthu moyo wanga, kuuona ngati wamtengo wapatali kwa ine ayi. Chimene ndikungofuna ndi kumaliza njira yanga, ndi utumiki umene ndinaulandira kwa Ambuye Yesu basi, kuchitira umboni bwino lomwe za uthenga wabwino wa kukoma mtima kwa m’chisomo cha Mulungu.” Mawu amenewa ndi olimbikitsa kwambiri ndipo m’pamene pachokera lemba la chaka cha 2009 lakuti, “Kuchitira umboni bwino lomwe za uthenga wabwino.”—Mac. 20:24.
Kuchitira Umboni Bwino Lomwe Masiku Ano
10. Tikudziwa bwanji kuti nafenso tiyenera kuchitira umboni bwino lomwe?
10 Lamulo la ‘kulalikira kwa anthu, ndi kupereka umboni wokwanira’ silinaperekedwe kwa atumwi okha. Yesu ataukitsidwa analankhula ndi ophunzira pafupifupi 500 amene anasonkhana ku Galileya ndipo anawalamula kuti: “Choncho pitani mukapange ophunzira mwa anthu a mitundu yonse. Muziwabatiza m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la mzimu woyera, kuwaphunzitsa kusunga zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu.” Lamulo limeneli limapitanso kwa Akhristu oona masiku ano chifukwa Yesu ananena kuti: “Ndipo dziwani ichi! Ine ndili nanu pamodzi masiku onse mpaka mapeto a dongosolo lino la zinthu.”—Mat. 28:19, 20.
11. Kodi Mboni za Yehova zimadziwika ndi ntchito yofunika iti?
11 Akhristu achangu amapitirizabe kumvera lamulo limeneli mwa kuyesetsa “kuchitira umboni bwino lomwe za uthenga wabwino.” Njira yaikulu yochitira zimenezi ndi kulalikira ku nyumba ndi nyumba ndipo izi ndi zimene Paulo anauza akulu a ku Efeso. David G. Stewart, Jr. ananena m’buku lake lonena za kuchita bwino ntchito ya umishonale lomwe linatuluka mu 2007, kuti: “Njira imene a Mboni za Yehova amagwiritsa ntchito pophunzitsa aliyense m’gulu lawo mmene angauzire ena za zikhulupiriro zawo imakhala yogwira mtima kwambiri kuposa [kumangolalikira ku gome]. Mboni za Yehova zambiri zimasangalala ndi ntchito youza ena zimene amakhulupirira.” Kodi zotsatira zake ndi zotani? David G. Stewart, Jr. anapitiriza kuti: “Pa kafukufuku amene ndinachita mu 1999 m’mizinda iwiri ya kum’mawa kwa Ulaya, ndinapeza kuti anthu awiri kapena anayi okha pa anthu 100 alionse ndi amene anafikiridwapo ndi anthu a tchalitchi cha Latter-day Saints, kapena amishonale a tchalitchi chimenechi. Koma anthu oposa70 pa 100 alionse ananena kuti anafikiridwapo ndi a Mboni za Yehova, ndipo ambiri mwa iwo anati anafikiridwa maulendo angapo.”
12. (a) N’chifukwa chiyani timapita “maulendo angapo” kunyumba za m’gawo lathu? (b) Kodi mungafotokoze chitsanzo cha munthu amene anasintha maganizo ake n’kuyamba kumvetsera uthenga wathu?
12 N’kutheka kuti anthu a m’dera lanu afikiridwanso chimodzimodzi. Inuyo mukuchita nawo ntchito imeneyi, ndipo polalikira ku nyumba ndi nyumba “mwakhala mukukumana” ndi amuna, akazi ndi achinyamata. Mwina anthu ena sangamvetsere ngakhale kuti mwawalalikira “maulendo angapo.” Ena angamvetsere pang’ono chabe mukamakambirana nawo lemba kapena mfundo ina ya m’Baibulo. Koma ena mwakhala mukuwalalikira bwinobwino ndipo amamvetsera mwachidwi. Zonsezi zikhoza kuchitika pamene “mukuchitira umboni bwino lomwe za uthenga wabwino.” Mwina inunso mukudziwa zitsanzo za anthu ambiri amene anasonyeza chidwi chochepa atafikiridwa “maulendo angapo,” koma kenako anasintha. N’kutheka kuti pali chinachake chimene chinawachitikira iwo kapena mnzawo chomwe chinawapangitsa kuti asinthe maganizo ndi mitima yawo ndi kuyamba kumvetsera choonadi. Ndipo panopa iwo ndi abale ndi alongo athu. Motero simuyenera kusiya ngakhale ngati panopo simukupeza anthu ambiri achidwi. Sitiyembekeza kuti aliyense angabwere m’choonadi. Koma zimene Mulungu amayembekeza kwa ife ndi zakuti tikhale achangu, komanso akhama pochitira umboni bwino lomwe.
Zotsatira Zimene Sitingazidziwe
13. Kodi kulalikira kwathu kungakhale ndi zotsatira zotani zimene sitingazidziwe?
13 Utumiki wa Paulo sunangokhudza anthu okhawo amene anawathandiza kukhala Akhristu. N’chimodzimodzinso ndi ife. Nthawi zonse timayesetsa kugwira nawo ntchito yolalikira kunyumba ndi nyumba, kuchitira umboni kwa anthu ambiri mmene tingathere. Timalankhula za uthenga wabwino kwa anzathu oyandikana nawo, amene timagwira nawo ntchito, anzathu a kusukulu ndiponso achibale athu. Kodi timadziwa zotsatira zake zonse? Kwa ena pangakhale zotsatira zabwino pasanapite nthawi yaitali. Pamene kwa ena mbewu za choonadi sizimera koma kenako, zimazika mizu m’mitima ya anthu ena n’kukula. Ngakhale kuti si nthawi zonse pamene izi zingachitike, anthu amene timawalalikira angakauze anzawo zimene tawauza, zimene timakhulupirira komanso khalidwe lathu. Ndiyeno zimenezi, n’zimene zingachititse kuti mbewu ya choonadi ikamere m’mitima ya anthu enawo.
14, 15. Kodi kulalikira kwa m’bale wina kunali ndi zotsatira zotani?
14 Mwachitsanzo, taganizirani zimene zinachitikira Ryan ndi mkazi wake Mandi amene amakhala ku Florida, m’dziko la United States. Ryan analalikira mwamwayi kwa munthu amene ankagwira naye ntchito. Munthuyo anali Mhindu ndipo ankachita chidwi ndi kavalidwe komanso kalankhulidwe ka Ryan. Mwa zina, iwo anakambirana za kuuka kwa akufa komanso za mmene akufa alili. Tsiku lina madzulo m’mwezi wa January, munthuyu anafunsa mkazi wake Jodi ngati akudziwa chilichonse chokhudza Mboni za Yehova. Mkaziyo anali wakatolika ndipo ananena kuti, chomwe amadziwa n’chakuti a Mboni amalalikira “khomo ndi khomo.” Kenako Jodi anafufuza pa Intaneti mawu akuti “Mboni za Yehova” ndipo anafika pa adiresi yathu ya www.watchtower.org. Kwa miyezi ingapo, Jodi anawerenga nkhani zokhudza Mboni za Yehova pa Intanetipo. Iye anawerengaponso Baibulo ndi nkhani zina zimene zinkamuchititsa chidwi.
15 Kenako Jodi anakumana ndi Mandi poti onse anali a namwino. Mandi anasangalala kuyankha mafunso amene Jodi anali nawo. M’kupita kwa nthawi anakambirana nkhani zambiri za m’Baibulo, ndipo Jodi anavomereza phunziro la Baibulo la panyumba. Pasanapite nthawi yaitali anayamba kupezeka ku misonkhano ku Nyumba ya Ufumu. Pofika mu October, Jodi anakhala wofalitsa wosabatizidwa ndipo anabatizidwa mu February chaka chotsatira. Iye analemba kuti: “Ndine wosangalala kwambiri tsopano ndipo ndine wokhutira kuti ndapeza choonadi.”
16. Kodi zimene zinachitikira m’bale wina ku Florida zikutiphunzitsa chiyani pa khama lathu lochitira umboni bwino lomwe?
16 Poyamba Ryan sanadziwe kuti kulalikira munthu mmodzi kungachititse munthu wina kubwera m’choonadi. Koma zimene zinachitikazi, zinamuthandiza Ryan kudziwa zotsatira za khama lake ‘pochitira umboni bwino lomwe.’ Mwina inuyo mumalalikira khomo ndi khomo, kuntchito, kusukulu kapena mwamwayi ndipo simungadziwe kuti njira zimenezi zikuthandiza anthu ena kumva uthenga wabwino. Paulo sanadziwe zotsatira zonse za kulalikira kwake “m’chigawo cha Asiya.” Nanunso simungadziwe zotsatira zonse za ntchito yanu yolalikira. (Werengani Machitidwe 23:11; 28:23.) Choncho ndi bwino kwambiri kupitiriza kulalikira.
17. Kodi mukufunitsitsa kuchita chiyani mu chaka cha 2009?
17 M’chaka cha 2009, tiyeni tonse tiyesetse kugwira ntchito yathu yochitira umboni ku nyumba ndi nyumba komanso m’njira zina. Tikatero tidzatha kulankhula ngati Paulo, amene anati: “Sindiuyesa kanthu moyo wanga, kuuona ngati wamtengo wapatali kwa ine ayi. Chimene ndikungofuna ndi kumaliza njira yanga, ndi utumiki umene ndinaulandira kwa Ambuye Yesu basi, kuchitira umboni bwino lomwe za uthenga wabwino wa kukoma mtima kwa m’chisomo cha Mulungu.”
Kodi Mungayankhe Bwanji?
• Kodi mtumwi Petulo ndi mtumwi Paulo komanso anthu ena mu nthawi yawo anachitira umboni motani?
• N’chifukwa chiyani tinganene kuti sitingadziwe zotsatira zonse za ntchito yathu yolalikira?
• Kodi lemba la chaka cha 2009 ndi loti chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani lili loyenera?
[Mafunso]
[Mawu Otsindika patsamba 19]
Lemba la chaka cha 2009 ndi lakuti: “Kuchitira umboni bwino lomwe za uthenga wabwino.”—Mac. 20:24.
[Chithunzi patsamba 17]
Akulu a ku Efeso ankadziwa kuti Paulo anali ndi chizolowezi chochitira umboni ku nyumba ndi nyumba
[Chithunzi patsamba 18]
Kodi khama lanu pochitira umboni bwino lomwe lidzakhala ndi zotsatira zotani?