Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Udindo Wapadera wa Yesu Pokwaniritsa Cholinga cha Mulungu

Udindo Wapadera wa Yesu Pokwaniritsa Cholinga cha Mulungu

Udindo Wapadera wa Yesu Pokwaniritsa Cholinga cha Mulungu

“Ine ndine njira ndi choonadi ndi moyo. Palibe amene amafika kwa Atate osadzera mwa ine.”​—YOH. 14:6.

1, 2. N’chifukwa chiyani tiyenera kudziwa bwino udindo wapadera wa Yesu pokwaniritsa cholinga cha Mulungu?

KWA zaka zochuluka anthu ambiri akhala akuyesetsa kuchita zinthu zosiyana ndi anzawo, koma ndi ochepa amene amakwanitsa. Ndipo pa anthu ochepawo amene amachita zinthu mwapadera moti amasiyanadi ndi anzawo ndi ochepetsetsa. Koma Yesu Khristu, Mwana wa Mulungu, ndi wapadera m’njira zambiri.

2 N’chifukwa chiyani tiyenera kudziwa bwino udindo wapadera wa Yesu? Chifukwa chakuti udindo wa Yesu umakhudza kwambiri ubwenzi wathu ndi Atate wathu wakumwamba Yehova. Ndipo Yesu anati: “Ine ndine njira ndi choonadi ndi moyo. Palibe amene amafika kwa Atate osadzera mwa ine.” (Yoh. 14:6; 17:3) Tiyeni tikambirane mfundo zina zosonyeza mmene Yesu alili wapadera. Kuchita zimenezi kutithandiza kumvetsa udindo umene ali nawo pokwaniritsa cholinga cha Mulungu.

“Mwana Wobadwa Yekha”

3, 4. (a) N’chifukwa chiyani Yesu ali wapadera pa udindo wake monga Mwana wobadwa yekha? (b) Kodi udindo umene Yesu anali nawo polenga zinthu ndi wapadera motani?

3 Sikuti Yesu wangokhala “mwana wa Mulungu” basi ngati mmene Satana ananenera pomuyesa. (Mat. 4:3, 6) Moyenerera Yesu amatchedwa kuti “Mwana wobadwa yekha wa Mulungu.” (Yoh. 3:16, 18) Mawu a Chigiriki amene anawamasulira kuti “wobadwa yekha” amatanthauza kuti “amene alibe wofanana naye, amene ali yekha,” “amene anabadwa yekhayekha m’banja mwawo,” kapena “wapadera.” Yehova ali ndi ana auzimu mamiliyoni ambirimbiri, ndiye zikutheka bwanji kuti Yesu anabadwa “yekhayekha m’banja mwawo”?

4 Yesu ndi wapadera chifukwa chakuti ndi yekhayo amene analengedwa mwachindunji ndi Atate wake. Iye ndi Mwana woyamba kubadwa. Ndipotu ndiye “woyamba kubadwa wa chilengedwe chonse.” (Akol. 1:15) Iyenso ndi “woyamba wa chilengedwe cha Mulungu.” (Chiv. 3:14) Udindo wa Mwana wobadwa yekha ameneyu pa ntchito yolenga ndi wapaderanso. Iye sanali Mlengi kapena Woyambitsa chilengedwe koma Yehova anamugwiritsira ntchito polenga zinthu zina zonse. (Werengani Yohane 1:3.) Mtumwi Paulo analemba kuti: “Kwa ife Mulungu alipo mmodzi yekha basi amene ndi Atate. Iye ndi amene zinthu zonse zinachokera mwa iye, ndipo ifeyo ndife ake. Ndipo pali Ambuye mmodzi, Yesu Khristu, amene zinthu zonse zinakhalapo kudzera mwa iye, ndipo ifeyo kudzera mwa iyeyo.”​—1 Akor. 8:6.

5. Kodi Malemba amasonyeza bwanji kuti Yesu ndi wapadera?

5 Komabe, Yesu ndi wapadera m’njira zinanso zambiri. M’Malemba muli mayina ambiri amene amafotokoza udindo wake wapadera pokwaniritsa cholinga cha Mulungu. Tsopano tikambirana mayina ena asanu amene ali m’Malemba Achigiriki Achikhristu onena za Yesu.

“Mawu”

6. N’chifukwa chiyani Yesu ali woyenera kutchedwa kuti “Mawu”?

6 Werengani Yohane 1:14. N’chifukwa chiyani Yesu amatchedwa kuti “Mawu” kapena kuti Logosi? Dzina limeneli limasonyeza ntchito imene wakhala akugwira kuyambira pamene zolengedwa zina za nzeru zinalengedwa. Yehova anagwiritsa ntchito Mwana wake popereka uthenga ndi malangizo kwa ana ena auzimu komanso kwa anthu padziko lapansi. Mfundo yakuti Yesu ndi Mawu kapena kuti Womulankhulira Mulungu inasonyezedwa bwino ndi zimene Khristu anauza Ayuda. Iye anati: “Zimene ine ndimaphunzitsa si zanga ayi, koma ndi za amene anandituma. Ngati munthu akufuna kuchita chifuniro cha wonditumayo, adzadziwa za chiphunzitsochi ngati chili chochokera kwa Mulungu, kapena ngati ndimalankhula za m’maganizo mwanga.” (Yoh. 7:16, 17) Yesu amatchedwabe kuti “Mawu a Mulungu” ngakhale pambuyo pobwerera ku ulemerero wake wa kumwamba.​—Chiv. 19:11, 13, 16.

7. Kodi tingatsanzire bwanji kudzichepetsa kwa Yesu kumene amasonyeza pa udindo wake monga “Mawu”?

7 Tangoganizirani tanthauzo la dzina limeneli. Ngakhale kuti Yesu ndi wanzeru kwambiri kuposa zolengedwa zonse za Yehova, iye sadalira nzeru zakezo. Iye amalankhula zochokera kwa Atate wake, ndipo nthawi zonse zonena zake zimachititsa ena kuganizira za Yehova osati za iye mwini. (Yoh. 12:50) Chimenechitu ndi chitsanzo chabwino kwambiri kwa ife. Ifenso tapatsidwa mwayi wamtengo wapatali woti ‘tilengeze uthenga wabwino wa zinthu zabwino.’ (Aroma 10:15) Kuzindikira chitsanzo cha Yesu cha kudzichepetsa kungatithandize kupewa kulankhula za m’maganizo athu. Tikamalalikira uthenga wa m’Malemba umenewu womwe ndi wopulumutsa moyo, sitiyenera ‘kupitirira zinthu zolembedwa.’​—1 Akor. 4:6.

“Amen”

8, 9. (a) Kodi mawu akuti “amen” amatanthauza chiyani, ndipo chifukwa chiyani Yesu amatchedwa kuti “Amen”? (b) Kodi Yesu anakwaniritsa bwanji udindo wake monga “Amen”?

8 Werengani Chivumbulutso 3:14. N’chifukwa chiyani Yesu amatchedwa “Amen”? Mawu akuti “amen” anachokera ku mawu Achiheberi amene amatanthauza kuti “zikhale momwemo” kapena kuti “ndithudi.” Ndipo tsinde la mawu Achiheberiwo limatanthauza “kukhala wokhulupirika” kapena “wodalirika.” Mawu amenewanso amagwiritsidwa ntchito pofotokoza kuti Yehova ndi wokhulupirika. (Deut. 7:9; Yes. 49:7) Ndiyeno kodi Yesu ndi wapadera motani akamatchulidwa kuti “Amen”? Taonani mmene lemba la 2 Akorinto 1:19, 20 limayankhira funso limeneli. Lembali limati: “Pakuti Mwana wa Mulungu, Khristu Yesu, amene analalikidwa pakati panu . . . , sanakhale Inde kenako Ayi, koma mwa iye, Inde wakhalabe Inde. Pakuti malonjezo a Mulungu, kaya akhale ochuluka chotani, akhala Inde kudzera mwa iye. Choteronso, kudzera mwa iye, “Amen” amanenedwa kwa Mulungu kuti Mulungu alandire ulemerero kudzera mwa ife.”

9 Yesu ndi “Amen” wa malonjezo onse a Mulungu. Chifukwa choti Yesu ali padziko lapansi sanachimwe ndiponso anafa imfa yansembe, anatsimikizira kuti malonjezo onse a Yehova Mulungu adzakwaniritsidwa. Komanso anatsegula njira yokwaniritsira malonjezowo. Mwa kukhala wokhulupirika, Yesu anatsutsa mawu a Satana olembedwa m’buku la Yobu. Satana anati ngati munthu atasauka, kuvutika kapena kuyesedwa, angasiye kutumikira Mulungu. (Yobu 1:6-12; 2:2-7) Pa zolengedwa zonse za Mulungu, Mwana woyamba kubadwayu ndi amene akanapereka yankho losatsutsika pa bodza limeneli. Komanso Yesu anapereka umboni wabwino zedi pa nkhani yofunika kwambiri yakuti, Yehova ali ndi ufulu wolamulira chilengedwe chonse ndipo mwakutero anasonyeza kuti ali ku mbali ya Atate wakewo.

10. Kodi tingatsanzire bwanji Yesu pa udindo wake wapadera monga “Amen”?

10 Kodi tingatsanzire bwanji Yesu pa udindo wake wapadera monga “Amen”? Tingachite zimenezi mwakukhala okhulupirika kwa Yehova ndi kuchirikiza ulamuliro wake. Tikamatero ndiye kuti tikuchita zimene timapemphedwa pa Miyambo 27:11. Lembali limati: “Mwananga, khala wanzeru, nukondweretse mtima wanga; kuti ndimuyankhe yemwe anditonza.”

“Mkhalapakati wa Chipangano Chatsopano”

11, 12. N’chifukwa chiyani udindo wa Yesu monga Mkhalapakati uli wapadera?

11 Werengani 1 Timoteyo 2:5, 6Yesu “ndi mkhalapakati mmodzi, pakati pa Mulungu ndi anthu.” Iye ndi “mkhalapakati wa chipangano chatsopano.” (Aheb. 9:15; 12:24) Komatu Mose nayenso amatchedwa mkhalapakati wa chipangano cha Chilamulo. (Agal. 3:19) Ndiyeno n’chifukwa chiyani tinganene kuti udindo wa Yesu monga Mkhalapakati ndi wapadera?

12 Mawu a chinenero choyambirira amene anamasuliridwa kuti “mkhalapakati” ankagwiritsidwa ntchito pa nkhani zokhudza malamulo. Ndipo amanena za Yesu monga Mkhalapakati wovomerezeka mwalamulo (kapena tinganene kuti loya) wa chipangano chatsopano chimene chinachititsa kuti mtundu watsopano wa “Isiraeli wa Mulungu” ubadwe. (Agal. 6:16) Mtundu watsopano umenewu wapangidwa ndi Akhristu odzozedwa ndi mzimu omwe ndi “ansembe achifumu” akumwamba. (1 Pet. 2:9; Eks. 19:6) Chipangano cha Chilamulo chimene Mose anali mkhalapakati wake, sichinachititse kuti mtundu ngati umenewu ubadwe.

13. Kodi udindo wa Yesu monga Mkhalapakati umaphatikizapo chiyani?

13 Kodi udindo wa Yesu monga Mkhalapakati umaphatikizapo chiyani? Yehova amagwiritsa ntchito mtengo wa magazi a Yesu pa anthu a mu chipangano chatsopano. Chifukwa cha zimenezi Yehova amawaona kuti mwalamulo ndi olungama. (Aroma 3:24; Aheb. 9:15) Motero Mulungu amawavomereza kulowa mu chipangano chatsopano kuti adzakhale ansembe ndiponso mafumu kumwamba. Monga Mkhalapakati wawo, Yesu amawathandiza kukhalabe oyera pamaso pa Mulungu.​—Aheb. 2:16.

14. N’chifukwa chiyani Akhristu onse ayenera kuyamikira udindo wa Yesu monga Mkhalapakati, kaya akhale opita kumwamba kapena ayi?

14 Nanga bwanji za anthu amene sali m’chipangano chatsopano omwe akuyembekezera kudzakhala padziko lapansi? Ngakhale kuti sali mu chipangano chatsopano, iwo amapindula ndi chipanganochi. Iwo amakhululukidwa machimo awo ndipo amayesedwa olungama komanso amakhala mabwenzi a Mulungu. (Yak. 2:23; 1 Yoh. 2:1, 2) Kaya tili ndi chiyembekezo chopita kumwamba kapena chodzakhala padziko lapansi, tili ndi zifukwa zomveka zoyamikirira udindo wa Yesu monga Mkhalapakati wa chipangano chatsopano.

“Mkulu wa Ansembe”

15. N’chifukwa chiyani udindo wa Yesu monga Mkulu wa Ansembe ndi wosiyana ndi wa akulu ansembe ena?

15 Anthu ambiri m’mbuyomu anakhalapo pa udindo wa mkulu wa ansembe. Koma Yesu ndi Mkulu wa Ansembe wapadera. N’chifukwa chiyani zili choncho? Paulo anati: “Iye safunikira kupereka nsembe tsiku ndi tsiku za machimo a iye mwini choyamba, kenako za anthu ena, monga amachitira akulu a ansembe. (Iye anachita zimenezi kamodzi kwatha pamene anadzipereka nsembe.) Pakuti Chilamulo chimaika amuna okhala ndi zofooka kukhala akulu a ansembe. Koma mawu a lumbiro onenedwa pambuyo pa Chilamulo anaika Mwana, amene anakhalitsidwa wangwiro kosatha.”​—Aheb. 7:27, 28. *

16. N’chifukwa chiyani nsembe ya Yesu ilidi yapadera kwambiri?

16 Yesu anali munthu wangwiro ngati mmene analili Adamu asanachimwe. (1 Akor. 15:45) Pachifukwa chimenechi, Yesu anali munthu yekhayo amene akanatha kupereka nsembe yangwiro komanso yokwanira, moti singafunike kubwerezedwa. M’chilamulo cha Mose, nsembe zinkaperekedwa tsiku ndi tsiku. Nsembe zonsezo ndiponso ntchito zonse zimene ansembe ankagwira zinali kuimira zimene Yesu anali kudzakwaniritsa. (Aheb. 8:5; 10:1) Motero Yesu ndi Mkulu wa Ansembe wapadera chifukwa chakuti anakwaniritsa zimene anthu ena sakanatha kuchita komanso chifukwa chakuti adzatumikira pa udindo umenewu kosatha.

17. N’chifukwa chiyani tiyenera kuyamikira udindo wa Yesu monga Mkulu wa Ansembe, ndipo tingachite bwanji zimenezi?

17 Udindo wa Yesu monga Mkulu wa Ansembe ndi wofunika kwambiri kwa ife kuti tiyanjidwe ndi Mulungu. Ndipotu tili ndi Mkulu wa Ansembe wabwino kwambiri. Paulo analemba kuti: “Sitili ndi mkulu wa ansembe amene sangatimvere chisoni pa zofooka zathu, koma amene wayesedwa m’zonse ngati ifeyo, napezekabe wopanda uchimo.” (Aheb. 4:15) Kunena zoona, kuyamikira mfundo imeneyi kuyenera kutilimbikitsa kuti ‘tisadzikhalire moyo wa ife eni, koma tikhalire moyo iye amene anatifera.’​—2 Akor. 5:14, 15; Luka 9:23.

“Mbewu” Yolonjezedwa

18. Kodi ndi ulosi uti umene unanenedwa Adamu atachimwa, ndipo ndi zinthu ziti zokhudza ulosiwo zimene zinavumbulidwa pambuyo pake?

18 Anthu atachimwa mu Edeni, zinaoneka ngati palibe chabwino chifukwa anataya ubwenzi wawo ndi Mulungu, moyo wosatha, chimwemwe komanso Paradaiso. Koma Yehova Mulungu analosera za Mpulumutsi. Yehova anatchula mpulumutsi ameneyu kuti “mbewu.” (Gen. 3:15) Kwa nthawi yaitali maulosi ambiri a m’Baibulo anatchula za Mbewu. Komabe nthawi imeneyo mbewuyo inali isanadziwike kuti adzakhala ndani. Mbewuyo inali kudzachokera ku mbadwa ya Abulahamu, Isake ndi Yakobo komanso mu mzere wa Mfumu Davide.​—Gen. 21:12; 22:16-18; 28:14; 2 Sam. 7:12-16.

19, 20. (a) Kodi ndani amene ali Mbewu yolonjezedwa? (b) N’chifukwa chiyani tinganene kuti mbewu yolonjezedwa si Yesu yekha?

19 Kodi Mbewu yolonjezedwa imeneyi inali ndani? Yankho la funso limeneli lili pa Agalatiya 3:16. (Werengani.) Komabe kumapeto kwa chaputala chomwechi, mtumwi Paulo anauza Akhristu odzozedwa kuti: “Ndiponso, ngati muli a Khristu, mulidi mbewu ya Abulahamu, olandira cholowa malinga ndi lonjezolo.” (Agal. 3:29) Popeza kuti Yesu ndi amene ali Mbewu yolonjezedwa, zikutheka bwanji kuti ena akhalenso mbewu imeneyi?

20 Mamiliyoni ambiri amanena kuti ndi mbadwa za Abulahamu ndipo ena afika pochita zinthu ngati aneneri. Zipembedzo zina zimanena motsimikiza kuti aneneri awo ndi mbadwa za Abulahamu. Koma kodi onsewo ndi Mbewu yolonjezedwadi? Ayi. Monga mmene mtumwi Paulo ananenera mouziridwa, si mbadwa zonse za Abulahamu zimene zingakhale Mbewu yolonjezedwa. Ndipo ndi zoona kuti si mbadwa zonse za Abulahamu zimene zinagwiritsidwa ntchito kuti anthu adalitsidwe. Mbewu yodalitsa anthu imeneyi ikanachokera kwa Isake yekha. (Aheb. 11:18) Pamapeto pake zinadziwika kuti Yesu Khristu amene anali mbadwa ya Abulahamu, ndiye anali mbali yoyamba ya mbewu yolonjezedwa. * Ndipo anthu onse amene anali m’gulu la makolo ake analembedwa m’Baibulo. Ena onse anadzakhala mbali yachiwiri ya mbewu ya Abulahamu chifukwa chakuti ndi ake “a Khristu.” Choncho udindo wa Yesu pokwaniritsa ulosi umenewo ndi wapaderadi.

21. Kodi ndi chiyani chimakuchititsani chidwi ndi mmene Yesu wakwaniritsira udindo wake wapadera pa cholinga cha Yehova?

21 Kodi taphunzira chiyani pa zimene takambirana zokhudza udindo wapadera wa Yesu pokwaniritsa cholinga cha Yehova? Kuyambira pamene analengedwa, Mwana wobadwa yekha wa Mulungu ameneyu ndi wapadera ndipo palibe wina wofanana naye. Komabe Mwana wapadera wa Mulungu ameneyu, amene anadzakhala Yesu, nthawi zonse wakhala akutumikira modzichepetsa mogwirizana ndi chifuniro cha Atate wake. Ndipo iye sanayesepo kudzifunira yekha ulemerero. (Yoh. 5:41; 8:50) Chimenechitu ndi chitsanzo chabwino kwambiri kwa ife masiku ano. Mofanana ndi Yesu, chikhale cholinga chathu ‘kuchita zonse ku ulemerero wa Mulungu.’​—1 Akor. 10:31.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 15 Katswiri wina wamaphunziro a Baibulo ananena kuti mawu amene anamasuliridwa kuti “kamodzi kwatha,” amafotokoza mfundo yofunika ya m’Baibulo chifukwa “amasonyeza kuti imfa ya Khristu ndi yapadera ndipo singafanane ndi ina ili yonse.”

^ ndime 20 Ayuda m’nthawi ya atumwi ankadziona kuti ndi mtundu woyanjidwa ndi Mulungu, chifukwa chakuti anali mbadwa za Abulahamu. Komabe iwo ankayembekezera kuti kudzabwera munthu mmodzi amene adzakhale Mesiya kapena kuti Khristu.​—Yoh. 1:25; 7:41, 42; 8:39-41.

Kodi Mukukumbukira?

• Kodi mwaphunzira chiyani za udindo wapadera wa Yesu pa mayina ake ena? (Onani bokosi.)

• Kodi mungamutsanzire bwanji Mwana wapadera wa Yehova?

[Mafunso]

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 15]

Mayina Ena Osonyeza Udindo Wapadera wa Yesu Pokwaniritsa Cholinga cha Mulungu

Mwana Wobadwa Yekha. (Yoh. 1:3) Ndi Yesu yekha amene analengedwa mwachindunji ndi Atate wake.

Mawu. (Yoh. 1:14) Yehova amagwiritsa ntchito Mwana wake ngati Wom’lankhulira popereka mauthenga ndi malangizo kwa zolengedwa zina.

Amen. (Chiv. 3:14) Chifukwa choti Yesu ali padziko lapansi sanachimwe ndiponso anafa imfa yansembe, anatsimikizira kuti malonjezo onse a Yehova Mulungu adzakwaniritsidwa. Komanso anatsegula njira yokwaniritsira malonjezowo.

Mkhalapakati wa Chipangano Chatsopano. (1 Tim. 2:5, 6) Yesu monga Mkhalapakati wovomerezeka watheketsa kubadwa kwa mtundu watsopano womwe ndi “Isiraeli wa Mulungu.” Mtundu umenewu ndi Akhristu amene adzakhale “ansembe achifumu” kumwamba.​—Agal. 6:16; 1 Pet. 2:9.

Mkulu wa Ansembe. (Aheb. 7:27, 28) Yesu yekha ndi amene akanatha kupereka nsembe yangwiro imene singafunike kubwerezedwa. Iye angathe kutimasula ku imfa komanso kutiyeretsa ku uchimo ndi zotsatira zake zonse.

Mbewu Yolonjezedwa. (Gen. 3:15) Yesu Khristu ndi mbali yoyamba ya mbewu yolonjezedwa. Ena onse amene anakhala mbali yachiwiri ya mbewu ya Abulahamu, ndi ‘ake a Khristu.’​—Agal. 3:29.