Yang’ananibe pa Mphoto
Yang’ananibe pa Mphoto
“Ndikuyesetsa mpaka ndikapate mphoto.”—AFIL. 3:14.
1. Kodi mtumwi Paulo ankayembekezera mphoto yotani?
MTUMWI Paulo, yemwe amadziwikanso kuti Saulo wa ku Tariso, ankachokera ku banja lotchuka. Iye anaphunzitsidwa za chipembedzo cha makolo ake ndi Gamaliyeli, yemwe anali mphunzitsi wa Chilamulo wodziwika kwambiri. (Mac. 22:3) Tikhoza kunena kuti Paulo anali ndi tsogolo labwino kwambiri, koma iye anasiya chipembedzo chake n’kukhala Mkhristu. Ndipo anayamba kuyembekezera kulandira mphoto ya moyo wosatha ndiponso kudzakhala mfumu yosakhoza kufa komanso wansembe mu Ufumu wa Mulungu, kumwamba. Ufumu umenewo udzalamulira dziko lapansi la paradaiso.—Mat. 6:10; Chiv. 7:4; 20:6.
2, 3. Kodi Paulo anasonyeza bwanji kuti ankayamikira kwambiri mphoto yokakhala ndi moyo kumwamba?
2 Posonyeza kuti ankayamikira kwambiri mphoto imeneyi, Paulo anati: “Zinthu zimene zinali phindu kwa ine, zimenezo ndaziona kukhala zopanda phindu chifukwa cha Khristu. Zoonadi, ndimaona zinthu zonse kukhala zosapindulitsa, chifukwa cha kudziwa Khristu Yesu Ambuye wanga, kumene ndi kwa mtengo wopambanadi. Chifukwa cha iye, ndimaona zinthu zonse kukhala zosapindulitsa, ndipo ndimaziyesa mulu wa zinyalala.” (Afil. 3:7, 8) Paulo ataphunzira cholinga cha Yehova chokhudza anthu, anayamba kuona ngati zinyalala zinthu zimene anthu ambiri amaziona kuti n’zofunika, monga udindo, chuma, ntchito ndi kutchuka.
3 Kuyambira nthawi imeneyo, chinthu chimene Paulo ankachiona kuti ndi chofunika kwambiri chinali kudziwa Yehova ndi Yesu. Pofotokozanso za mfundo imeneyi, Yesu anapemphera kwa Mulungu kuti: “Moyo wosatha adzaupeza akamaphunzira ndi kudziwa za inu, Mulungu yekha woona, ndi za Yesu Khristu, amene inu munam’tuma.” (Yoh. 17:3) Mawu a Paulo opezeka pa Afilipi 3:14 amasonyeza kuti iye ankafunitsitsa kuti apeze moyo wosatha. Iye anati: “Ndikuyesetsa mpaka ndikapate mphoto ya chiitano cha Mulungu chopita kumwamba, chodzera mwa Khristu Yesu.” Ndithudi, maso ake anali pa mphoto ya moyo wosatha kumwamba monga mmodzi wa olamulira mu boma la Ufumu wa Mulungu.
Moyo Wosatha Padziko Lapansi
4, 5. Kodi anthu ambiri amene akuchita chifuniro cha Mulungu adzalandira mphoto yotani?
4 Ambiri mwa anthu amene asankha kuchita chifuniro cha Mulungu, ayenera kuyesetsa kuti adzalandire mphoto ya moyo m’dziko latsopano la Mulungu. (Sal. 37:11, 29) Yesu anasonyeza kuti chiyembekezo chimenechi n’chodalirika. Iye anati: “Osangalala ali iwo amene ali ofatsa, popeza adzalandira dziko lapansi.” (Mat. 5:5) Yesu ndiye woyamba kulandira dziko lapansili, monga mmene lemba la Salmo 2:8 limanenera, ndipo iye adzakhala ndi olamulira anzake kumwamba okwana 144,000. (Dan. 7:13, 14, 22, 27) Ndipo anthu onga nkhosa amene adzakhale padziko lapansi adzalandira Ufumu umene ‘unakonzedwera iwo kuchokera pa kukhazikitsidwa kwa dziko.’ (Mat. 25:34, 46) Sitikukayikira kuti zimenezi zidzachitika chifukwa Mulungu, yemwe analonjeza zimenezi, “sanganame.” (Tito 1:2) Ifenso tiyenera kukhala ndi chidaliro ngati chimene Yoswa anali nacho kuti Mulungu amakwaniritsa malonjezo ake. Iye anauza Aisiraeli kuti: “Pa mawu okoma onse Yehova Mulungu wanu anawanena za inu sanagwa padera mawu amodzi; onse anachitikira inu, sanasowapo mawu amodzi.”—Yos. 23:14.
5 Moyo m’dziko latsopano la Mulungu sudzakhala wamavuto ngati mmene zilili masiku ano. Sikudzakhala nkhondo, kuphwanya malamulo, umphawi, kupanda chilungamo, matenda ndi imfa. Anthu nthawi imeneyo adzakhala angwiro ndipo adzakhala m’paradaiso. Moyo udzakhala
wabwino kwambiri kuposa mmene tingaganizire. Ndithudi, tsiku lililonse lidzakhala losangalatsa kwambiri. Imeneyitu ndi mphoto yapamwamba kwambiri.6, 7. (a) Kodi Yesu anachita chiyani posonyeza zimene tingayembekezere m’dziko latsopano la Mulungu? (b) Kodi anthu amene anamwalira adzakhala bwanji ndi moyo watsopano?
6 Pamene Yesu anali padziko lapansi, Mulungu anamupatsa mphamvu ya mzimu woyera kuti achite zinthu zabwino posonyeza zimene zidzachitike m’dziko latsopano. Mwachitsanzo, iye anauza munthu wofa ziwalo kuti ayende. Munthuyo anali atadwala kwa zaka 38. Baibulo limati munthuyo anayenda. (Werengani Yohane 5:5-9.) Panthawi inanso Yesu anakumana ndi “munthu wakhungu chibadwire” ndipo anamuchiritsa. Kenaka munthuyu atafunsidwa kuti afotokoze yemwe wamuchiritsa, anayankha kuti: “Sizinamveke n’kale lonse kuti wina watsegula maso a munthu amene anabadwa wakhungu. Munthu uyu akanapanda kuchokera kwa Mulungu, sakanatha konse kuchita kanthu.” (Yohane 9:1, 6, 7, 32, 33) Yesu anatha kuchita zimenezi chifukwa anapatsidwa mphamvu ndi Mulungu. Kulikonse kumene iye anapita “anachiritsa amene anafunikira kuchiritsidwa.”—Luka 9:11.
7 Sikuti Yesu anangochiritsa odwala ndi opuwala, iye anaukitsanso akufa. Mwachitsanzo, mtsikana wina wazaka 12 atamwalira, makolo ake anali ndi chisoni chachikulu. Koma Yesu anati: “Buthuwe, ndikunena ndi iwe Dzuka!” Ndipo iye anadzuka. Kodi mukuganiza kuti makolo a mtsikanayu komanso anthu amene anaona zimenezi anamva bwanji? (Werengani Maliko 5:38-42.) M’dziko latsopano la Mulungu mudzakhala ‘kusangalala kwadzaoneni’ anthu ambirimbiri akamadzaukitsidwa, chifukwa “kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama omwe.” (Machitidwe 24:15; Yohane 5:28, 29) Anthu amenewa adzayamba moyo watsopano ndipo adzapatsidwa mwayi wokhala ndi moyo wosatha.
8, 9. (a) Kodi n’chiyani chidzachitikire uchimo wotengera kwa Adamu mu Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Khristu? (b) Kodi anthu akufa adzaweruzidwa pa zifukwa ziti?
8 Anthu adzaukitsidwa osati ndi cholinga choti awonongedwe. Oukitsidwawo sadzaweruzidwa pa machimo amene anachita asanamwalire. (Aroma 6:7) Mu Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Khristu, nsembe ya dipo idzagwira ntchito ndipo pang’ono ndi pang’ono anthu omvera olamuliridwa ndi Ufumu umenewu adzakhala angwiro. Pamapeto pake adzamasulidwa ku mavuto onse obwera chifukwa cha tchimo la Adamu. (Aroma 8:21) Yehova ‘adzameza imfa ku nthawi yonse; ndipo Ambuye Mulungu adzapukuta misozi pankhope zonse.’ (Yes. 25:8) Mawu a Mulungu amanenanso kuti ‘mipukutu idzafunyululidwa,’ kusonyeza kuti anthu amene adzakhale ndi moyo nthawi imeneyo adzapatsidwa malangizo atsopano. (Chiv. 20:12) Dziko lapansi likamadzakonzedwa kukhala paradaiso, “okhala m’dziko lapansi adzaphunzira chilungamo.”—Yes. 26:9.
9 Anthu amene adzaukitsidwe sadzaweruzidwa chifukwa cha uchimo umene anatengera kwa Adamu, koma chifukwa cha zimene iwo adzasankha kuchita. Lemba la Chivumbulutso 20:12 limanena kuti: “Akufa anaweruzidwa malinga ndi zolembedwa m’mipukutuyo, mogwirizana ndi ntchito zawo,” kutanthauza zimene adzachite ataukitsidwa. Kunena zoona, zimenezi zikusonyeza kuti Yehova ndi wachilungamo, wachifundo komanso wachikondi kwambiri. Ndiponso zinthu zopweteka zimene anthu anakumana nazo m’dziko lakaleli “sizidzakumbukika, pena kulowa mumtima.” (Yes. 65:17) Chifukwa chophunzira zinthu zatsopano zolimbikitsa komanso chifukwa chokhala ndi zinthu zabwino zokhazokha, iwo sadzavutika maganizo ndi zinthu zoipa zimene ankakumana nazo. Zinthu zakalezo sadzazikumbukira. (Chiv. 21:4) Zimenezi zidzachitikiranso “khamu lalikulu” limene lidzapulumuke Aramagedo.—Chiv. 7:9, 10, 14.
10. (a) Kodi moyo m’dziko latsopano la Mulungu udzakhala wotani? (b) Kodi muyenera kuchita chiyani kuti muziyang’anabe pa mphoto?
10 M’dziko latsopano la Mulungu, anthu sadzadwalanso kapena kufa. “Wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala.” (Yes. 33:24) Choncho, anthu okhala m’dziko lapansi latsopano azidzadzuka m’mawa uliwonse ali athanzi, kuyembekezera kusangalala ndi zochitika za tsikulo. Azidzagwira ntchito ya tsikulo mosangalala ndi kucheza ndi anthu abwino okhaokha, omwe amawakonda. Moyo umenewu ndi mphoto yosangalatsa kwambiri. Tengani Baibulo lanu ndi kuwerenga ulosi wopezeka pa Yesaya 33:24 ndi pa Yesaya 35:5-7. Ndipo yerekezerani kuti zimene mukuwerengazo zikuchitira inuyo. Kuchita zimenezi kungakuthandizeni kuyang’anabe pa mphoto.
Ena Omwe Anasiya Kuyang’ana pa Mphoto
11. Fotokozani chiyambi chabwino cha ulamuliro wa Solomo.
11 Pamene tadziwa mphoto imene tikuyembekezera, timafunika kuchita khama kuyang’anabe pa mphotoyo, chifukwa ngati sitichita khama, tingaiwale. Mwachitsanzo, Solomo atakhala mfumu ya Isiraeli, anapemphera kwa Mulungu modzichepetsa kuti amupatse mtima wanzeru ndi wozindikira n’cholinga chakuti athe kuweruza anthu a Mulungu moyenerera. (Werengani 1 Mafumu 3:6-12.) Baibulo limati: “Mulungu anam’patsa Solomo nzeru ndi luntha lambiri.” Zoonadi, “nzeru ya Solomo inaposa nzeru za anthu onse a kum’mawa, ndi nzeru zonse za ku Aigupto.”—1 Maf. 4:29-32.
12. Kodi Yehova anapereka chenjezo lotani kwa anthu amene anali kudzakhala mafumu a Isiraeli?
12 M’mbuyomo Yehova anali atachenjeza kuti aliyense amene anali kudzakhala mfumu, ‘asadzadzichulukitsire akavalo’ ndiponso ‘asadzadzichulukitsire akazi, kuti ungapatuke mtima wake.’ (Deut. 17:14-17) Kuchulukitsa akavalo kukanasonyeza kuti mfumuyo ikudalira kwambiri zida za nkhondo poteteza mtundu wake m’malo modalira Yehova monga Mtetezi. Ndipo kuchulukitsa akazi kunali koopsa chifukwa ena mwa akaziwo akanachokera ku mitundu yachikunja imene inkalambira milungu yonyenga, ndipo akazi amenewa akanapatutsa mfumuyo n’kusiya kulambira Yehova.
13. Kodi Solomo analephera bwanji kuyamikira zimene anapatsidwa?
13 Solomo sanamvere machenjezo amenewa. M’malomwake, iye anachita ndendende zimene Yehova ananena kuti mafumu asamachite. Iye 1 Maf. 4:26) Analinso ndi akazi 700 ndi enanso 300 apambali. Ndipo ambiri mwa akaziwa anali ochokera ku mitundu yachikunja yoyandikana nayo. Amenewa “anapambutsa mtima wake atsate milungu ina; ndipo mtima wake sunakhala wangwiro ndi Yehova.” Solomo anayamba kulambira konyenga kwa mitundu yachikunja kumene akazi ake achilendowa anamuphunzitsa. Chifukwa cha zimenezi, Yehova ananena kuti ‘adzang’amba ufumu’ wa Solomo, kuuchotsa kwa iye.—1 Maf. 11:1-6, 11.
anapeza akavalo ndiponso apakavalo ambirimbiri. (14. Kodi chinachitika n’chiyani chifukwa cha kusamvera kwa Solomo ndi mtundu wa Isiraeli?
14 Solomo anaiwala kuti anali ndi mwayi waukulu woimira Mulungu woona. Mfumuyi inalowerera m’kulambira konyenga. Patapita nthawi mtundu wonse unapanduka ndipo unawonongedwa mu 607 B.C.E. Kenako Ayuda anayambiranso kulambira koona. Komabe, patapita zaka mazana ambiri, Yesu ananena kuti: “Ufumu wa Mulungu udzachotsedwa kwa inu ndi kuperekedwa kwa mtundu wobala zipatso zake.” Ndipo zimenezi zinachitikadi. Yesu anati: “Tsopano tamverani! Nyumba yanu akunyanyalirani.” (Mat. 21:43; 23:37, 38) Chifukwa cha kusakhulupirika, mtunduwu unataya mwayi wapadera woimira Mulungu woona. Mu 70 C.E., magulu a nkhondo a Roma anawononga Yerusalemu ndi kachisi wake ndipo Ayuda ambiri amene anatsala anakhala akapolo.
15. Tchulani zitsanzo za anthu amene anaiwala zinthu zimene zinali zofunika kwambiri.
15 Yudasi Isikariyoti anali mmodzi wa atumwi 12 a Yesu. Iye ankamva mfundo zapamwamba zimene Yesu ankaphunzitsa ndipo ankaona zozizwitsa zimene Yesu ankachita mothandizidwa ndi mzimu woyera wa Mulungu. Komabe Yudasi sanatchinjirize mtima wake. Iye anali ndi udindo wosunga bokosi la ndalama za Yesu ndi atumwi 12. Koma “anali wakuba . . . ndipo anali kutengamo ndalama zoponyedwa mmenemo.” (Yoh. 12:6) Dyera lake litafika pachimake, iye anakonza chiwembu ndi ansembe akulu achinyengo kuti apereke Yesu ndi ndalama zokwana 30 zasiliva. (Mat. 26:14-16) Munthu wina amene anasiya kuyang’ana pa mphoto anali Dema mnzake wa mtumwi Paulo. Iye sanatchinjirize mtima wake. Paulo anati: “Dema wandisiya ine chifukwa chokonda dongosolo ili la zinthu.”—2 Tim. 4:10; werengani Miyambo 4:23.
Phunziro kwa Aliyense
16, 17. (a) Kodi tikulimbana ndi zinthu ziti zomwe ndi zamphamvu kwambiri? (b) Koma kodi chingatithandize ndi chiyani kulimbana ndi chilichonse chimene Satana angatichitire?
16 Mtumiki aliyense wa Mulungu ayenera kuganizira mofatsa zitsanzo za m’Baibulo. Tikutero chifukwa Baibulo limatiuza kuti: “Tsopano zinthu zimenezi zinali kuwagwera monga zitsanzo, ndipo zinalembedwa kuti zitichenjeze ife amene mapeto a madongosolo a zinthu atifikira.” (1 Akor. 10:11) Panopa tikukhala m’masiku otsiriza a dongosolo la zinthu loipali.—2 Tim. 3:1, 13.
17 Satana Mdyerekezi, yemwe ndi “mulungu wa dongosolo lino la zinthu,” akudziwa kuti “wangotsala ndi kanthawi kochepa.” (2 Akor. 4:4; Chiv. 12:12) Iye angachite chilichonse chimene angathe kuti anyengerere atumiki a Yehova n’cholinga choti awasiyitse kukhala Akhristu okhulupirika. Satana ndi amene akulamulira dzikoli ndiponso ali ndi mphamvu pa njira zimene dzikoli limafalitsira nkhani. Komabe anthu a Yehova amapeza “mphamvu yoposa yachibadwa” ndipo mphamvu imeneyi imaposa mphamvu ya Satana. (2 Akor. 4:7) Tiyenera kudalira mphamvu imeneyi yochokera kwa Mulungu kuti itithandize kulimbana ndi chilichonse chimene Satana angatichitire. Choncho tikulimbikitsidwa kupitirizabe kupemphera, ndi chidaliro chakuti Yehova “adzapereka mowolowa manja mzimu woyera kwa amene akum’pempha.”—Luka 11:13.
18. Kodi dziko lilipoli tiyenera kuliona bwanji?
18 Timalimba mtima chifukwa chodziwa kuti dongosolo lonse la Satana lidzawonongedwa posachedwapa, koma Akhristu oona adzapulumuka. Baibulo limati: “Dziko likupita limodzi ndi chilakolako chake, koma wochita chifuniro cha Mulungu akhalabe kosatha.” (1 Yoh. 2:17) Choncho, kungakhale kupanda nzeru kuti mtumiki wa Mulungu aziganiza kuti m’dongosolo la zinthu lilipoli angapeze chinthu chaphindu kuposa ubwenzi wake ndi Yehova. Dziko la Satanali lili ngati sitima imene ikumira. Koma Yehova wapereka mpingo wachikhristu umene uli ngati boti lopulumutsira atumiki ake okhulupirika. Pamene akupita ku dziko latsopano, iwo amakhulupirira lonjezo lakuti: “Ochita zoipa adzadulidwa: Koma iwo akuyembekeza Yehova, iwowa adzalandira dziko lapansi.” (Sal. 37:9) Choncho, yang’ananibe pa mphoto yabwino kwambiri imeneyi.
Kodi Mukukumbukira?
• Kodi mphoto imene Paulo ankayembekezera kulandira ankaiona bwanji?
• Kodi anthu amene adzakhale ndi moyo wosatha padziko lapansi adzaweruzidwa mogwirizana ndi chiyani?
• Kodi chinthu chanzeru chimene inuyo muyenera kuchita panopa n’chiyani?
[Mafunso]
[Chithunzi pamasamba 12, 13]
Kodi mukamawerenga nkhani za m’Baibulo, mumadziyerekezera mukulandira mphoto?